Category Archives: Uncategorized

26-0426 Kuyesa Kuti Umuchitire Mulungu Ntchito Mopanda Kukhala Chifuniro Cha Mulungu

Uthenga: 65-0718M Kuyesa Kuti Umuchitire Mulungu Ntchito Mopanda Kukhala Chifuniro Cha Mulungu

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wosamalidwa,

Ola lachedwa. Nthawi yafika. Chisankho chiyenera kupangidwa. Mulungu akuchenjeza ana Ake. Ambuye Mulungu wathu walengeza ndi kutsimikizira kwa ife chomwe Choonadi Chake chili ndi Mawu Ake, ndi Mzimu Wake. Osati ndi mphamvu, osati ndi nkhondo, koma ndi Mzimu Wanga, ndipo Mawu Anu ndi Choonadi.

Iye watsimikizira kwathunthu kwa Mkwatibwi lero kuti Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi nthawi zonse.Iye watiwonetsa ndi kutiwululira kuti Uthenga ndi mthenga wa ora ali ofanana. Iye wativumbulutsira zinsinsi Zake zonse zomwe zinali zobisika mu Mawu. Iye watitsimikizira Izi ndi Mzimu Wake Woyera. Palibe funso m’maganizo mwathu, m’mitima kapena m’miyoyo yathu. Mawu Ake pa matepi ndi PAKUTI ATERO AMBUYE KWA MKWATIBWI WAKE.

Mulungu nthawi zonse walola njira zambiri kubwera kwa Iye.Iye amapanga chifuniro Chake chongololera kukhala chifuniro Chake Changwiro. Iye mongaso nthawi zonse wapereka CHIFUNIRO CHANGWIRO NDI NJIRA YABWINO KWA ANA AKE. Ambiri amayesa kubwera mwanjira yosiyana pochitira Mulungu ntchito popanda kukhala chifuniro Chake changwiro.Izo Zingawonekere ndikumveka ngati chifuniro Chake changwiro, koma izo sizili monga ndi Mawu Ake.

Ngakhale munthu wamkulu, wodzozedwa kumene, wochokera ku Kukhalapo kwa Mulungu, adapeza vumbulutso loti achite china chake kwa Mulungu, ndipo amafuna kuchichitira Mulungu; koma vumbulutso lomwe anali nalo linali lolakwika.

Aliyense wa ife ayenera kupeza njira Yake yangwiro yoperekedwa. Kodi ife tingadziwe bwanji kuti tili mu chifuniro Chake changwiro ngati wina wodzozedwadi, wochokera ku kukhalapo kwa Mulungu, ndi vumbulutso, si ali mu chifuniro changwiro cha Mulungu?

Pali NJIRA IMODZI YOKHA YODZIWIRA YA CHOWONADI, ndipo Mulungu wapereka njira imeneyo kwa Mkwatibwi Wake.

Liwu la Mulungu Mwiniwake lawuza mpingo uno, ndi inu nonse anthu omwe muli pa matepi, ndi anthu omwe ali olumikizidwa pa intaneti m’madera ena a dziko lapansi, nthawi imeneyo ndi TSOPANO. Iye anatiuza ife kuti timvere mwatcheru Kwambiri zomwe iye anali kunena , ndipo kuti ife TISALEPHERE.

Chotero ine ndikunena, mu Dzina la Yesu Khristu! Musati inu muwonjezere kanthu kamodzi. Musati mutenge, kuyika malingaliro anu omwe mwa Iwo. Inu muzingonena chimene chikunenedwa pa matepi awo. Inu muzingochita chimodzimodzi chimene Ambuye Mulungu wakulamulirani kuti muchite. Musati muwonjezere kwa Iwo.

Iye sananene kuti, ndipo izo sizikutanthauza kuti alaliki sangalalikire Mawu, aphunzitsi sangaphunzitse Mawu, kapena abusa kapena aneneri ife tichite zomwe tayitanidwira kuchita; iwo ayenera, ine ndiyenera.Ife tayitanidwa ndi kudzozedwa kuti tichite zimenezo.Ife tiyenera kuloza ndi kubwereza Uthenga uwu ndi mthenga kwa anthu, chifukwa iwo ndiwo Mawu a tsiku lathu.

Koma Iye akutiuza momveka bwino kuti tonsefe a ife tikhoza kudzozedwa, ndi kudzozedwa kolondola, kudzazidwa ndi Mzimu Wake Woyera, ndi vumbulutso latsopano, ndikukhala kunja Kwa chifuniro Chake. Mu tsiku lathu lino, Iye wapereka NJIRA YANGWIRO yodziwira motsimikiza kuti mukumva Liwu la Mulungu, lochokera kwa Mulungu Mwiniwake. Ndiyo njira YOKHAYO yangwiro.

Utumiki suyenera kungotchula mobwereza kokha ndi kulalikira Uthenga uwu, koma ife tiyenera kusewera Liwu la Mulungu pa matepi kwa anthu. Palibe KUDZOZA KWAKUKULU kuposa kumva Liwu la Mulungu. Palibe njira ina yodziwira popanda mthuzi wa kukayikira kuti zomwe ife tikumva ndi NDIZOMWEZODI zomwe Mulungu ananena.

Mu tsiku lino, mosiyana ndi tsiku lina lililonse mu mbiri ya dziko lapansi, Mulungu wapereka njira yomwe imapangitsa kuti zikhale zosatheka kuphonya izo, ngati inu ndinu Mkwatibwi Wake Wokonzedweratu.Iyo yatsimikiziridwa ndi kuwululidwa ndi Lawi la Moto Mwiniwake kuti ndi Liwu la Mulungu Mwiniwake likulankhula mwachindunji ku Mpingo Wake.

Kwa zaka zikwizikwi, ana a Mulungu akhala akulakalaka ndikukhala nayo njala yakumva Liwu la Mulungu pa Iwo eni.Momwe iwo bwanji anakhumba akanakhalapo tsiku limene lija pamene Yesu analalikira kwa zikwizikwi paphiri. Kumva momwe Iye analankhulira Mawu Ake mwachikondi ndi chifundo. Kumva momwe Iye anayikila kutsimikiza pa Mawu aliwonse. Momwe Iye analankhulira ndi kulimbikitsa mitima yawo.

Ife tili amoyo tsopano ndipo tili mu mkupezeka kwa Mulungu kumva Liwu la Mulungu.

Tsiku lina posachedwa sitidzabwerera ku moyo wamtundu uwu kachiwiri. Tidzabwerera ngati munthu wosafa. Uchimo udzachotsedwa. Satana adzamangidwa kwa zaka chikwi ndipo tidzakhala padziko lapansi lino lomwe Ambuye Mulungu wathu watipatsa.

Ife ndife athunthu handiredi peresenti. Ife sitidakhalepo osangalala kapena mochuluka osakhalapo ndi mafunso m’miyoyo yathu. Ife ndife mmodzi ndi Iye ndi Mawu Ake. Ife ndife Mawu Ake. IFE TILI MU CHIFUNIRO CHAKE CHANGWIRO MWAKUKHALABE NDI LIWU LAKE, MAWU AKE. Iye adzabweranso tsiku lina lililonse tsopano kuti adzatitenge ife limodzi naye.

Zikomo inu Ambuye Yesu!

Ambuye Mulungu wanu wawonetsera kwa inu chomwe chiri Choonadi. Ambuye Mulungu wanu watsimikizira chomwe chiri Choonadi, mwa Mawu Ake ndi mwa Mzimu Wake. “Si mwa mphamvu, si mwa nkhondo, koma mwa Mzimu Wanga.” Ndipo, Mzimu, “Mulungu akufuna iwo amene ampembedza Iye mu Mzimu ndi Choonadi.” “Mawu Anu ali Choonadi.” Ndipo Iye watsimikizira mwathunthu kuti Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi nthawizonse. Iye wawonetsera Mbewu ya madzulo kwa inu. Iye wawululira Iyo kwa inu, mu Mawu. Iye wayitsimikizira Iyo kwa inu, mwa Mzimu Wake.

Ndi mtima wanga wonse ine ndikukuitanani aliyense wa inu kuti mubwere kudzalumikana ndi gawo la Mkwatibwi Wake pamene tikulumikizana kuchokera padziko lonse lapansi nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, kuti tidzamve Liwu Lake likulankhula kudzera mwa mthenga wake wachisanu ndi chiwiri wa mngelo ndikutibweretsera ife Uthenga: Kuyesa Kuti Umuchitire Mulungu Ntchito Mopanda Kukhala Chifuniro cha Mulungu 65-0718M.

M’bale Joseph Branham

Malemba Owerenga Musanamve Uthenga:
Deuteronomo 4:1-4 / 4:25-26
1 Mbiri 13
1 Mbiri 15:15
Masalimo 22
Mariko Woyera 7:7
Yoweli 2:28
Amosi 3:7
Malaki 3
Mateyu Woyera 11:1-15
1 Akorinto 13:1

26-0419 Kusankha Kwa Mkwatibwi

Uthenga: 65-0429E Kusankha Kwa Mkwatibwi

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wosankhidwa,

Pamene ife tikumvetsera Uthenga uwu, Kusankha Kwa Mkwatibwi, ena amaganiza kuti mneneri akungolankhula ndi kutilangiza za khalidwe ndi thunthu limene mwamuna ayenera kuyang’ana akamasankha mkazi amene akufuna kukhala mkazi wake. Izo ndi zoona, iye akutero, koma pali kalata yeniyeni yobisika yachikondi m’Mawu Ake. Zimene Iye akuulula kwa Mkwatibwi Wake ndi zozama kwambiri. Mulungu akulankhula ndi iye mwachindunji, kumuuza zomwe ankafuna mwa Iye, ndi chifukwa chake Iye anamusankha iye kuchokera pachiyambi. Iye anafuna kuti Iye adziwe kuti wamusankha iye kukhala MKWATIBWI WAKE WOKONDEDWA WOKOMA MTIMA yemwe Iye ankafuna kugawana naye Umuyaya Wake.

Pachiyambi, Mulungu anali kufunafuna Mkwatibwi amene adzakhala ndi Khalidwe Lake lomwelo. Mzimu Wake womwewo ukanadzaonekera mwa Iye. Iye anafuna Mkwatibwi amene akanadzakhala wodzipereka kwambiri kwa Iye, ndi Mawu Ake olonjezedwa,Kufikira mpaka Maganizo omwe anali mwa Iye adzakhale mwa Iye. Iye ayenera kuumbidwa monga momwe Iye alili.

Iye anafuna kuti Iye akhale thupi Lake lomwelo, mafupa omwewo, Mzimu womwewo, chilichonse chomwecho, basi chimodzimodzi monga Iye. Awiriwa a iwo adzakhala M’MODZI.

Iye sakanakhala wa chimasomaso mmaso mwake . Iye sakananyengereredwa ndi ma liwu ena aliwonse. Iye akanakhala woona mtima komanso wokhulupirika kwa Iye, mosasamala kanthu za zomwe wina anganene. Iye akanamutenga Iye pa Mawu Ake. Chilichonse chimene Iye adanena, AKANAKHULUPIlIRA MAWU ONSE, zilibe kanthu kaya ndi motalika bwanji zingatenge kuti zikwaniritsidwe, iye Akanakhulupirira izo. Iye akanakhalabe ndi Mawu Ake.

Iye akanakonda Iye, ndipo Iye yekhayo. Iye sanafunikire kumupatsa iye chuma chambiri, iye anali ndi Ngale yamtengo wapatali, Vumbulutso lenileni la Iye. Iye akanadziwa, iwo anali M’MODZI ndipo ndi ofanana. Mzimu Wake ukanakhala mwa Iye. Chilichonse chimene Iye akanafuna, Iye akanamupatsa Iye; chomwe Iye ankayenera kuchita chinali kupempha ndi kukhulupirira, ndipo Iye akanachita icho.

Iye ankadziwa kuti Iye akanapita kwa nthawi yaitali kuti akamumangire nyumba yomwe ikanakhala ndi chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ankayimanga iyo momwe Iye akanakondera. Iye ankadziwa tsiku lina Iye adzabweranso kwa Iye, monga momwe Iye analonjezera, ndiye kuti adzakhala ndi Mgonero Waukwati waukulu kwa zaka chikwi. Kenako, adzapita limodzi ku Nyumba yokongola imene Iye adamumangira iye kuti akhale Kwamuyaya.

Palibe china chilichonse chomwe chingakhale chovuta kwa Iye. Iye Sadzafuna china chilichonse. Iye adzakhala choncho wokhutira ndi wokhutsidwa ndi pokhala ndi Vumbulutso podziwa yemwe Iye ali, ndi kuti Iye ndi ndani. Iye anadziwa kuti Iye adzasunga Mawu Ake. IYE ADZAKWANIRITSIDWA, PODZIWA KUTI IYE NDIYE YOMWE IYE ANASANKHA KUTI AKHALE MKWATIBWI WAKE.

Abale ndi alongo anga, Mulungu wamphamvu wa Kumwamba ndi dziko lapansi anayang’ana kupitilira mumuyaya ndipo WAKUSANKHANI… INU KUKHALA MKWATIBWI WAKE WOSANKHIDWA WOKOMA MTIMA.

Ine ndikukuitanani inu kuti mubwere mudzalumikizane nane limodzi ndi gawo la Mkwatibwi Wake Lamlungu lino, pamene Iye akulankhula kudzera mwa mngelo wake wamphamvu ndikutiuza kuti ndife Mkwatibwi Wake Wosankhidwa.

M’bale Joseph Branham

Uthenga:   65-0429E  Kusankha Kwa Mkwatibwi
Nthawi: 12:00 P.M. Nthawi ya ku Jeffersonville

Malemba:
Genesis 24:12-14
Yesaya 53:2
Chivumbulutso 21:9

26-0412 Kodi Mulungu Amasintha Konse Malingaliro Ake Pa Mawu Ake?

Uthenga: 65-0418E Kodi Mulungu Amasintha Konse Malingaliro Ake Pa Mawu Ake?

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Ofulumizitsidwa,

Momwe mitima yathu inakondwera monga Mphungu kumapeto kwa sabata ino ya Isitala. Tsiku ndi tsiku, kudzoza kwake kunali kukukulirakulirabe kwambiri. Mgonero, Kuikidwa m’manda, Ungwiro, kenako chimake chachikulu chomwe Iye anatiwumbirako: Ndikutuluka kwa Dzuwa…ULEMERERO, IYE WAUKA ndipo ali ndi moyo mwa aliyense wa ife. Iye anali kuulula Mawu Ake kwa aliyense wa ife monga momwe sitinamvepo kale. Kudzoza kunadzaza mitima yathu, kukhalapo kwake kunadzaza mlengalenga; zinkaoneka ngati Kukwatulidwa kunali pafupi.

Iye anatiuza zomwe zinachitika zaka 2000 zapitazo, kenako zomwe zinali kuchitika mu 2026. Yesu anali Mbewu yoyamba ya Tirigu wa Mulungu yomwe inaukitsidwa kwa akufa. Iye anaukitsidwa ndi Mphamvu ya Mulungu yofulumizitsa. Mulungu anafulumizitsa moyo Wake, anamuukitsa Iye kwa akufa, ndipo Iye anali zipatso zoyamba za iwo omwe anagona. Anali woyamba kufika kukucha, Mtolo wa Mulungu womwe unaweyulidwa ngati chikumbutso cha kuyamika Mulungu, kukhulupirira kuti enafe tidzabwera. Icho chinali chizindikiro.

KENAKO IYE ANATIWULULIRA ZIMENE ZILI KUCHITIKA LERO. Monga momwe Iye anaweyulidwa pa Tsiku la Pentekoste pamene kunamveka mkokomo wochokera Kumwamba ngati kuweyula, mphepo yamphamvu yothamanga ikuweyulira pa anthu. Inaweyulidwiranso pamwamba pa anthu monga momwe Iye analonjezera mu Luka 17:30 ndi Malaki 4, pamene M-w-a-n wa munthu adzawululidwa ndi kuweyulidwanso pa anthu.

Tsopano, Mwana wa munthu ndi Ndani? “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu. Ndipo Mawu anasandulika thupi, ndipo anadzakhala pakati pathu.” Ndipo ngati kuphunzitsa konse kumene ife tiri nako, ndi kutsimikizira kwa Mawu a Mulungu; mwa Mawu a Mulungu, mwa zizindikiro, ndi zodabwitsa, ife tikuziwona lero, kuti mu Bukhu la—la Luka apa, kuti monga ife tangobwereza kumene, kapena—Luka mutu wa 17 ndi ndime ya 30; ndi Malaki 4, ndi Malemba osiyanasiyana amene ife tikuwadziwa, kuti Mawu amenewo akuweyulidwanso pa anthu, kuti miyambo yakufa ya anthu yafa, ndipo Mwana wa Mulungu ali moyo kachiwiri ndi ubatizo wa Mzimu Woyera pakati pathu pomwe, ndipo akutipatsa ife Moyo.

Mzimu Woyera unapitirizabe kuweyulira ndi kuweyulirabe, kuulula ndi kuulula Mawu Ake… Mphamvu, machitidwe, Mphamvu yofulumizitsa…

Kenako, pamene zinaoneka ngati sizingakule kwambiri, Iye anatiuza kuti:

Iye anandilola ine kuyang’ana kudutsa katani, ndipo ine ndinakuonani inu nonse kumeneko. “Onse amene iwe unawakonda, ndi onse amene anakukonda iwe, iwo aperekedwa kwa iwe.” Mukuona? Ine ndinawawona iwo paliponse kumeneko monga choncho. Chinali chiyani chimenecho? Mphamvu Yofulumizitsa.

IYE ANATIONA IFE KUMENEKO!! Kupitirira katani ya nthawi….ife tinali KUMENEKO ndi iye; okondedwa athu onse omwe adatsogola…abambo, amayi, ana. Ife tidali nawo pamodzi ndi onse omwe sitinakumanenawopo: Mose, Eliya, Petro, Paulo….tinali tonse pamodzi.

Kenako, monga momwe basi wokondedwa Mzimu Woyera Iye ali wokongola, Iye sankafuna kutiiwala ife odwala, ovutika maganizo komanso omenyedwa, choncho Iye anadziweyula iyemwini pa ife kuti aliyense achiritsidwe ku chilichonse chomwe tinkachifuna.

Anthu awa, amene ali nzika zimzathu za Ufumu, eni a Mphamvu zofulumizitsa, fulumizitsani Iyo kwa iwo, Ambuye, pakali pano. Ndipo mulole Mzimu upite kuchokera kwa mphungu kupita kwa mphungu, kuchokera ku Mawu kupita ku Mawu, mpaka chidzalo cha Yesu Khristu chitawonetseredwa mu thupi lirilonse, ku zakuthupi, zauzimu, kapena chosowa chirichonse chimene iwo akuchisowa, pamene ife tikuyikana manja athu pa wina ndi mzake. Mu Dzina la Yesu Khristu.

Mawu amenewo. Liwu limenelo. CHILICHONSE chimene ife tikufuna chili pa matepi, Mkwatibwi. Mulungu sasintha malingaliro ake pa Mawu Ake. Palibe dontho limodzi kapena Mutu umodzi omwe ungasinthidwe, kotero Iye anapanga njira kuti Mkwatibwi Wake amve NDENDENDE ndi makutu awo chimene Iye amafuna alankhule Kwa iwo.

Mulungu walankhula ndi Mkwatibwi Wake ndipo wawulula CHILICHONSE. Izo zili zojambulidwa. Mkwatibwi ayenera kubwera kwa Mkwati; Iyo ndiyo njira Yake yangwiro yoperekedwa yomwe yapangidwira lero.Izo ndi PAKUTI ATERO AMBUYE.

Kodi Mulungu amasintha konse malingaliro Ake pa Mawu Ake? AYI. Iye ali ndi CHIFUNIRO CHANGWIRO NDI CHIFUNIRO CHONGOLOLERA. Mkwatibwi ayenera kukhala mu CHIFUNIRO Chake CHANGWIRO. Palibe Chifuniro changwiro china, kapena malo angwiro, kuposa kumva Liwu la Mulungu mwachindunji kuchokera kwa Mulungu Mwiniwake.

Kuitana kwanga kwa wina aliyense wa inu ndikuti mudzalumikizane nafe Lamlungu pa 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, kudzanva Liwu la Mulungu likutibweretsera Mawu Oyera. Palibe kufunikira koganizira, kungokhala kumbuyo basi ndi kumanena AMEN KU MAWU ALIWONSE….palibe malo ena omwe zingachitikire, ndi kokha mwa KUKANIKIZA KUSEWERA.

M’bale Joseph Branham.

Uthenga: 65-0418E — Kodi Mulungu Amasintha Konse Malingaliro Ake pa Mawu Ake?

Tiyamba ndi ndime 61.

Malemba Oti muwerenge musanamve Uthenga:
Eksodo mutu wa 19
Numeri 22:31
Mateyu Woyera 28:19
Luka 17:30
Chivumbulutso mutu wa 17

ISITALA 2026- MWAMBO WA MGONERO WA PADELA NDI KUSAMBITSANA MAPAZI

Okondedwa Azanga Nzika Za Ufumu,

Isitala iyi ikulonjeza kukhala Isitala yayikulu kwambiri yomwe Mkwatibwi adakhalapo nayo. Ife Takhala tikukhala pamaso pa Mwana, tikucha, tikuzindikira kuti ndife ndani. Chidzalo cha Yesu Khristu chikupangidwa kuonetseredwa mwa wina aliyense wa ife pamene Mawu Ake, Liwu Lake, likufuula, kuchokera Kwa Mphungu yaikulu kupita kwa ti ana ta mphungu, kutiitana ife ku Mgonero Wathu wa Ukwati.

Chaka chilichonse nthawi ino Mkwatibwi amakhala pansi pa kuyembekezera kwakukulu kwa Isitala ilimkudza kumapeto kwa sabata. Nthawi yomwe Iye adzatigwirizanitsa kuchokera padziko lonse lapansi kwa masiku anayi mopitiliza, kumulambira Iye, kumuyamika Iye, kumutamanda Iye; chifukwa Iye wauka ndipo akukhala mwa wina aliyense wa ife. Mkwati ndi Mkwatibwi akukhala M’MODZI.

Iye akutipatsa ife nthawi yapaderayi kuti titsekere kunja zinthu zonse za dziko lapansi zomwe zatizungulira ife ndikukhala basi ndi Iye . Palibe zosokoneza za dziko lino, pamene tikupanga dziko lathu ndi Iye. Tsekani zitseko zathu, zimitsani zathu zonse zamagetsi ndi chilichonse chomwe chimatisokoneza kwa Iye.

Chikhumbo chachikulu chomwe wina aliyense wa ife ali nacho ndikukhala pafupi ndi Iye. Ife tikufuna kukhala moyo wodzipereka kwambiri kwa Iye; kukhala nthawi zonse mu chifuniro Chake changwiro. Kukhala okonzeka Kukubwera Kwake. Palibe chilichonse m’dziko lino, kapena m’moyo wathu, chofunika kwambiri kuposa ichi.

Iye watipatsa mwayi wapaderawu kuti tingokhala ndi Iye, kulankhula ndi kusinkhasinkha za Iye. Kukhala pamaso Pake ndikutsegula mitima yathu kwa Iye. IZO ZIDZAKHALA ZOSINTHA MOYO KWA MKWATIBWI WAKE!

Iye akudziwa kuti zingakhale zovuta kwa ena a inu omwe muli ndi ana, banja, ndi maudindo ena omwe tili nawo, koma ngati tigwiritsa ntchito mphindi iliyonse yaulere tiyenera kulankhula ndi Iye, kuyandikira kwa Iye, kutsegula mitima yathu kwa Iye, padzakhala kusintha kwakukulu mu kuyenda kwathu ndi Iye, mpaka sitidzakhalanso chimodzimodzi.

Monga momwe Iye adachitira m’tsiku la Mose pamene Iye adawakhazika ana Ake m’nyumba zawo, magazi anali atapakidwa ndipo anali kudzipangitsa Iwo eni kukonzekera Kutuluka kwawo; momwemonso sabata yapadera iyi ya Isitala yomwe Iye adakonza idzakhala ya aliyense wa ife.

Ulendo wathu udzakhala motere:

LACHINAYI

Unali Lachinayi usiku pamene Ambuye Yesu adadya Mgonero Womaliza ndi ophunzira Ake, pokumbukira Paskha asanatuluke ana a Israeli. Ndi mwayi waukulu bwanji womwe ife tili nawo wolankhulana ndi Ambuye m’nyumba zathu, kumapeto kwa sabata yathu yopatulika, ndikupempha Iye kuti atikhululukire ife machimo athu, ndi kutipatsa zonse zomwe tikufunikira paulendo wathu.

Atate Wakumwamba, tikuyamikira nthawi ino, nthawi inaso yosonkhana pamodzi, mbali ino ya Umuyaya. Ndipo ife tikuyang’anira m’mawa uno kuti mphamvu zatsopano zichokere kwa Inu, kutipatsa kulimba mtima paulendo womwe uli patsogolo. Ife tasonkhana monga momwe ana Achiheberi adachitira m’mawa kwambiri, kuti titenge mana omwe adaperekedwa kwa iwo usiku wonse, kuti awathandize tsiku lotsatira. Ife tasonkhana kuti tidye Mana a uzimu, m’mawa uno, kutipatsa mphamvu paulendo.

Tiyeni tonse tiyambe pa nthawi ya 6:00 PM. pa nthawi yanu yapafupi kuti mumve Mgonero 62-0204, kenako mneneriyo adzatitengera ku Utumiki wathu wapadera wa Mgonero ndi Kutsukana Mapazi ku m’maliziro a tepiyo, yomwe idzaseweredwa pa pulogalamu ya Lifeline (mu Chingerezi), kapena mutha kupanga dawunilodi utumikiwu mu Chingerezi kapena mu zilankhulo zina podina ulalo womwe uli pansipa.

LACHISANU

Tiyeni ife tipite ku pemphero ndi mabanja athu nthawi ya 9:00 AM, ndipo kenako nthawi ya 12:00 PM, kupempha Ambuye kuti akhale nafe ndikudzaza nyumba zathu ndi Mzimu Woyera pamene tikudzipereka ife eni kwa Iye.

Malingaliro athu abwerere m’mbuyo ku tsiku lija ku Kalvari, zaka zoposa 2000 zapitazo, ndikuwona Mpulumutsi wathu atapachikidwa pamtanda. Tiyeni tikumbukire mtengo waukulu umene Iye analipira chifukwa cha ife. Iye anali Mwana wa Mulungu wopanda uchimo, koma anayenera kuvutika monga momwe panalibe munthu wina aliyense akanavutikira, chifukwa machimo athu anaikidwa pa Iye.

Iye anayenera kumutumiza ku gehena wolangidwa (Mukuona?), chifukwa Iye ananyamula machimo athu. Ndipo Khristu anafa, osati wolungama; Khristu anafa wochimwa. Mukuona? Khristu sanachimwepo Iye mwini, koma Iye ananyamula machimo athu pa Iye.

Kenako pa 12:30 PM, tiyeni tilumikizane pamodzi m’nyumba zathu ndikunva 57- 0419 Ungwiro.

Kenako tiyeni tilumikizane pamodzi m’pemphero mwachangu nthawi yomweyo pambuyo pa utumiki, pokumbukira kupachikidwa kwa Ambuye wathu.

LOWERUKA

Tiyeni tonse tibwere pamodzi mu pemphero nthawi ya 9:00 AM ndi 12:00 PM, ndikukonzekeretsa mitima yathu zinthu zazikulu zomwe Iye adzatichitira pakati pathu.

Ine ndikumva Iye akunena kuti, “Satana, bwera kuno!” Iye ndiye Bwana tsopano. Akufikira, akutenga kiyi ya imfa ndi gehena m’mbali mwake, naipachika pambali Pa Iye Mwini. “Ine ndikufuna nditumikire kukudziwitsani inu. Mwakhala wonyenga kwa nthawi yayitali. Ine ndine Mwana wa Mulungu wamoyo wobadwa kwa namwali. Magazi anga akadali onyowa pamtanda, ndipo ngongole yonse yathunthu yalipidwa! Iwe Siwulinso ndi ufulu mkomwe. Iwe wavulazidwa. Ndipatse ine makiyi amenewo!”

Kenako nthawi ya 12:30 PM, tonse tidzasonkhana pamodzi kuti timve Mawu: 57-0420 Kuikidwa M’manda.

Ndi tsiku la KALATA YOFIWIRA kwambiri bwanji yomwe iyo ili kwa Mkwatibwi Wake padziko lonse lapansi.

Ndiye tiyeni tigwirizanenso pamodzi mu pemphero nthawi yomweyo utatha utumiki.

LAMULUNGU

Tiyeni tidzuke kaye m’mawa monga momwe M’bale Branham adachitira m’mawa pamene bwenzi lake laling’ono, phwiti, adamudzutsa iye nthawi ya 5:00 AM. Tiyeni ife tingoyamika Ambuye chifukwa choukitsa Yesu kwa akufa:

Masiku asanu m’mawa uno, bwenzi langa laling’ono lofiira linaulukira pawindo ndipo linandidzutsa ine. Zikuoneka kuti mtima wake waung’ono unaphulika, ndikunena, “Iye Wauka.”

Nthawi ya 9:00 AM tiyeni tigwirizanenso mu Tcheni chathu cha pemphero, kupemphererana wina ndi mnzake ndikukonzekera kumva Liwu la Mulungu.

Nthawi ya 9:30 AM, Ife tidzasonkhana pamodzi kuti timve Uthenga wathu wa Isitala: 65-0418M Ndi Kutuluka kwa Dzuwa.

Nthawi ya 12:00 PM tidzakweza mawu athu kwa Iye kumuyamika chifukwa cha Mphamvu Yofulumizitsa.

Nthawi ya 3:00 PM, tiyeni tigwirizanenso m’pemphero, kumuyamika chifukwa cha MAPETO A SABATA YODABWISTSA YOMWE IYE WATIPATSA IFE NDI IYE NDI MKWATIBWI WAKE KUZUNGULIRA DZIKO LONSE LA PANSI.

Kwa abale ndi alongo anga akunja, monga chaka chatha, ine ndikufuna kukuitanani kuti mugwirizane nafe pa nthawi ya ku Jeffersonville, nthawi zonse zamapemphero pa ndondomekoyi. Ine ndikuzindikira, komabe, kuti kusewera Matepi Lachinayi, Lachisanu, ndi Loweruka masana pa nthawi ya ku Jeffersonville kungakhale kovuta kwambiri kwa ambiri a inu, choncho chonde musazengereze kusewera Mauthenga amenewo panthawi yomwe ingakhale yoyenera kwa inu. Komabe, ndikufuna kuti tonse tigwirizane Lamlungu nthawi ya 9:30 AM, nthawi ya ku Jeffersonville, kuti timve Uthenga wathu wa Lamlungu pamodzi.

Ndikufunanso kukuitanani inu ndi ana anu kuti mukhale nawo m’mapulojekiti a Creations, kulemba manyuzipepala, ndi maphikidwe, omwe banja lanu lonse lingasangalale nawo limodzi. Tikuganiza kuti mudzawakonda chifukwa onse akuchokera pa MAWU omwe tidzakhala tikuva kumapeto kwa ndondomeko kwa sabata ino.

Zidziwitso pa za kakonzedwe ka mwambo wa mgonero , zinthu zomwe zidzafunike pa mapulojekiti a Creations, ndi zidziwitso zina, onani maulalo omwe ali pansipa.

Tiyeni ife titseke mafoni athu kumapeto kwa sabata ya Isitala kupatula kujambula zithunzi, kumvetsera Zobwereza Za Pa Tsiku, ndikusewera matepi kuchokera ku pulogalamu ya Table, pulogalamu ya Lifeline, kapena ulalo wopangidwa dawunilodi.

Iwo ndi ulemu waukulu kwa ine kukuitanani inu ndi banja lanu kuti mudzabwere pamodzi ndi Mkwatibwi kuzungulira padziko lonse lapansi kumapeto kwa sabata yodzaza ndi KUPEMBEDZA, MATAMANDO NDI MACHIRITSO. Ine ndikukhulupirira kuti ndikwenikweni ndi kumapeto kwa sabata komwe kudzasintha moyo wanu kwamuyaya.

M’bale Joseph Branham

26-0329 Kodi Melkizedeki Uyu Ndi Ndani?

Uthenga: 65-0221E Kodi Melkizedeki Uyu Ndi Ndani?

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi wa Moyo Wamuyaya,

Kodi Liwu limene likulankhula nafe pa matepi ndi ndani?

Ife tingathe kudziwa yankho la funso limenelo kudzera ku vumbulutso lochokera kwa Mulungu. Mkwatibwi Wake wokonzedweratu yekha ndiye amene adzakhala ndi Vumbulutso limenelo. Chifukwa chake, tiyenera kufufuza Mawu Ake kuti timvetse amene Iye anati anali ndani: Wotanthawuzira yekha wa Mawu Ake. Ndani angamatule ndi kuwulula Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri? Ndani angawulule zinsinsi zonse zobisika za m’Baibulo? Ndani adzaitana ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake? Ndani adzakhala ndi Liwu losalephera?

Malingana ndi Mawu, si wina koma Melikizedeki, Iyemwini. Munthu wopanda bambo kapena mayi, Amene analibe chiyambi kapena mapeto a masiku. Mulungu, Amene anakhala thupi ndipo anadya nyama ndi mkate wa chimanga, anamwa mkaka wa batala, ndipo analankhula ndi Abrahamu. Iye anali Munthu wokhala ndi umunthu, wokhala ndi thupi la munthu.

Mawu omwewo anati Melikizedeki, Munthu ameneyo, umunthu umenewo, adzakhala ndi moyo ndi kudziulula Yekha kachiwiri mu thupi la munthu monga momwe anachitira kwa Abrahamu, kenako kachiwiri mwa Yesu Khristu; koma lero, mu mthenga wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri wa Chivumbulutso 10:7. Mzimu Wake udzanyeketsa kachisi wapadziko lapansi kuti Iye athe kulankhula ndi kudziulula kwa Mkwatibwi Wake. Mulungu mwiniwake akukhala ndi kulankhula mu thupi la munthu. Mbewu yake yoyamba yobwezeretsedwa kwathunthu inali itacha mokwanira. Dongosolo lathunthu la Mulungu linafika; Mulungu ndi munthu anali Mmodzi. Mulungu anali kulankhula ndi Mkwatibwi Wake pakamwa ndikupita ku khutu monga momwe anachitira kwa Abrahamu.

Iye anadza mkati nakhala mmenemo, mwa Munthu wa Melkezedeki. Ndiye, kenako, ife sitinamvenso za Melkizedeki, chifukwa Iye anadzakhala Yesu Khristu. Melkizedeki anali Wansembe, koma Iye anadzakhala Yesu Khristu. Tsopano, inu munalidutsa ilo. Chifukwa, mmawonekedwe awo, Iye ankadziwa zinthu zonse, ndipo inu simunakhozebe kudziwa izo.

KOMABE…!! Ndiyeno Kodi ifeyo ndife ndani?

Maso athu, thunthu lathu, chilichonse chomwe ife tinali, tinali m’maganizo Ake pachiyambi. Pasanakhalepo Mngelo, nyenyezi, Kerubi, kapena china chilichonse. Iye anaganiza, Iye analankhula, ndipo ndife tili pano.

Uko ndi kusakhala nawo malire. Ife sitingakhoze kumvetsa izo mmaganizo mwathu, koma ndizo Mulungu. Mulungu, wopanda malire!

Pakuti tinali mwa Iye pachiyambi, kodi n’chiyani chomwe chimachitika kwa ife moyo wa padziko lino lapansi utatha?

Pamene mwinjiro wa thupi uwu wavulidwa, pali thupi lachibadwa, fiofane, thupi osati lopangidwa ndi manja, ngakhalenso kuti lobadwa mwa mkazi, limene ife timapitako.

Ndiye thupi ilo limabwereranso ndi kukatenga thupi la ulemerero.

Kodi ndi zinthu zodabwitsa zanji zomwe zili mu nkhokwe za Mkwatibwi Wake. Taonani zomwe zikuchitika pakali pano pamene Iye akuwululira Mawu Ake Kwa ife kuposa kale lonse. Kukamba za kalata yachikondi kwa Mkwatibwi Wake! Ndi tsiku lotani lomwe ife tikukhalamo.

Ife tili ndi Vumbulutso ndipo tikudziwa kuti ndi Melikizedeki, Liwu la Mulungu, likulankhula nafe pa matepi. Ife tili ndi Vumbulutso, ndi njira yoperekedwa ndi yangwiro ya Mulungu ya lero. Kotero, IFE TIMADZIWA YEMWE IYE ALI NDIPO NDIFE MKWATIBWI WAKE.

Vumbulutso limenero likukulirakulirabe tsiku lililonse. Tsiku lililonse likadutsa limatibweretsera chisangalalo chochuluka, vumbulutso lochuluka. Mkwatibwi akudzikonzekeretsa yekha pokhala pamaso pa Liwu Lake, pamene Iye akutiuza kuti Ife ndi ndani, mochuluka momwe Iye amatikondera Ife, momwe Iye sangathe kuyembekezera kukhala nafe!!!

Bwerani, dzikonzekeretseni nokha nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pa chomwe chikukonzekera kuchitika, pamene ife tikumvetsera Liwu la Melikizedeki.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 65-0221E “Kodi Melikizedeki Uyu Ndi Ndani?”

Malemba Owerenga:
Genesis Chaputala 18
Eksodo 33:12-23
Yohane Woyera 1:1
Aroma 8:1
2 Akorinto 5:1
1 Atesalonika 4:13-18
Timoteo Woyamba 3:16 / 6:15
Ahebri 7:1-3 /13:8
Chivumbulutso 10:1-7 / 21:16

26-0322 Chikwati Ndi Chilekano

Uthenga: 65-0221M Chikwati Ndi Chilekano

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wotengedwa, Wosankhidwa, ndinso Wokonzedweratu:

Ine ndikukumbukira pomwe ndinali mnyamata wachichepere ndikukula, ndikuyesera kusankha tepi yoti ndimvere. Pamene ndinali kuwerenga mitu yomwe ndimaganiza nthawi zonse, Ine sindinkafuna kumvera Chikwati ndi Chilekano, chifukwa zimenezo zinalibe chochita ndi ine; zinali za anthu okwatira okha.

Kenako tsiku lina, pamene ndimamvetsera Chikwati ndi Chilekano, Atate anandipatsa Vumbulutso la Uthenga umenewo. Kudzoza Kwake kunabwera mumtima mwanga. Iye akulankhula nane. Uthenga uwu NDI wa ine. Iye akundiuza ine kuti Iye anandisankha ine maziko a dziko la pansi asanakhazikitsidwe. Uwu ndi mwambo wa ukwati wanga. Ine Sindikufuna wina koma Iye. Ine ndine woona mtima komanso wokhulupirika kwa Iye, ndi Mawu Ake, ndi Liwu Lake, LOKHALO. Ife ndife M’MODZI.

Zoonadi Uthenga uwu unali kwa abale ndi alongo ambiri omwe anali okwatirana ndipo tsopano analekana, ndipo Iye anali kuwauza iwo chomwe anali kuyenera kuchita; koma panali tanthauzo la patali LOKWANIRA NDI LALIKULU kwambiri, lalikulu kwambiri, lamphamvu kwambiri.

Panali Mwamuna m’modzi, ndipo Iye anali kuyitana ndi kulankhula kwa Ake ambiri, mkwatibwi wosankhidwa. LIWU LA MULUNGU LINALI KUITANA WAKE WOYERA, WOSAWONONGEDWA, NAMWALI MKWATIBWI WA MAWU. Mmodzi amene sanakhudzidwe kapena kuipitsidwa ndi munthu. Mmodzi woona mtima komanso wokhulupirika kwa Iye ndi Mawu Ake okha. Mmodzi amene anakhutitsidwa kwathunthu ndi Iye ndi Mawu Ake.

Mwa Chisomo ndi Chifundo Chake, lero tinganene, popanda mthuzi umodzi wa kukayika, IFE NDIFE NAMWALI WAKE MKWATIBWI WA MAWU. ULEMERERO!!

Iye ankafuna kutsimikiza kuti sipadzakhala malire omasuka pankhani yoitana Mkwatibwi Wake, kotero Iye anabwera yekha ndikukhala m’thupi la munthu kuti awulule Mawu Ake ndikuitana Mkwatibwi Wake kwa Iyemwini. Iye anali Elieza amene akanasankha Mkwatibwi Wa Iyemwini.

Kuti titsimikizire kuti palibe njira yoti tisokonezedwe ndi amene anali kutifunsira ukwati, Iye mwini anatsimikizira chotengera chake chosankhidwa mwa kulankhula naye kuchokera mu mphepo yamkuntho yopachikidwa pamtengo. Kenako Iye analankhula naye moonekera pa Mtsinje wa Ohio pamaso pa anthu zikwizikwi.

Iye ngakhaleso anajambulidwa chithunzi chake pamodzi ndi Iye kotero onetsani ndi kuliwuza dziko lonse lapansi , INE NDINAKUWUZANI INU KUTI INE NDIKANADZABWERANSO NDI KUDZAKHALA NDI MOYO MU THUPI. IYE NDIYE AMENE INE NDINASANKHA KUKHALAMO NDI MOYO, KUTI NDIKUITANENI INU KUTI MUKHALE MKWATIBWI WANGA. SI IYE; NDI INE NDIKULANKHULA KUDUTSIRA MWA IYE. INE NDIKUNGOGWIRITSA NTCHITO LIWU LAKE KUTI LIKHALE LIWU LANGA KWA INU. INE NDIYE AMENE NDAKUYITANANI INU KUTI MUKHALE MKWATIBWI WANGA WANGWIRO.

Vumbulutso la Uthenga Uwu, Mawu Ake, Liwu Lake, ndipo tsopano chomwe amene IFE tili ndizopitirira mawu a munthu kuti ayesere kufotokoza. Ine ndikudziwa kuti inu mukudziwa chenicheni chomwe ine ndikunena. Kukwatulidwa mu Chikhulupiriro kukuchitika. Mkwatibwi akudzikonzekeretsa yekha pokhala mu mkupezeka kwa Mulungu Mwiniwake, kukhala wangwiro.

Ndi mwayi waukulu kwambiri wotani womwe dziko lapansi lili nawo womva Liwu la Mulungu likulankhula ndi iwo; kukhala pansi ndi kumvetsera Mawu pa Mawu pamene Iye akulankhula ndi kuwulula Mawu Ake ndikutiuza amene ife tili. Palibe china choponsa kukhala mumkupezeka Kwake, choncho bwerani mudzalumikizane nafe Lamlungu nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumumva Iye akulankhula ndi Mkwatibwi Wake, Uthenga, “Chikwati Ndi Chilekano” 65-0221M.

M’bale Joseph Branham

Malemba owerenga musanamve Uthenga:

Mateyu Woyera 5:31-32 / 16:18 / 19:1-8 / 28:19
Machitidwe 2:38
Aroma 9:14-23
Timoteo Woyamba 2:9-15
Akorinto Woyamba 7:10-15 / 14:34
Ahebri 11:4
Chivumbulutso 10:7
Genesis mutu 3
Levitiko 21:7
Yobu 14:1-2
Yesaya 53
Ezekieli 44:22