23-0319 Kusankha Kwa Mkwatibwi

Uthenga: 65-0429E Kusankha Kwa Mkwatibwi

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa umozi mu Miliyoni,

Ndakhala ndikulidirirani nthawi yayitali. Ndinu wokondedwa Wanga wokondedwa, ndipo ndimakukondani kwambiri. Monga ndinakulonjezani, ndakhala ndikukupangilani Nyumba yatsopano kumene Tidzakhala pamodzi Muyaya. Ndapanga chilichonse chimodzimodzi monga inu mumakonda iwo.

Ine ndikhoza tsopano kuyang’ana pa inu ndi kuwona, inu ndinu chinyezimiro cha Ine. Inu muli ndi khalidwe Langa lomwe, mnofu Wanga, Mafupa Anga, Mzimu Wanga womwewo, Chirichonse Changa chomwecho, chimodzimodzi basi. mwakhala amodzi ndi Ine.

Ndinatumiza mngelo Wanga wamphamvu padziko lapansi kuti adzakuitaneni kuti utuluke mu Edeni wa Satana. Ine ndinamutuma iye kotero kuti akakhoze kufotokoza maganizo anga, makhalidwe Anga, ndi kukuuzani inu za zinthu zimene ziri kubwela. Ndinasebenzesa kamwa kake ndi mawu ake pofotokoza. Pabuyo ponena izo, Ine ndinazifikitsa izo, chifukwa Miyamba ndi dziko lapansi zidzapita, koma Mawu Anga kwa inu sadzalephera konse.

Ndinadziwa kuti pamene munandimva Ine ndikulankhula, kusebenzesa mawu a mngelo Wanga, mudzadziwa mkati mwa mtima wanu, amene sanali iyeyo, amene anali kulankhula ndi inu. Ndinali Ine ndikukutumizirani kalata yachikondi, ndikukuuzani inu, Ine ndakusankhani inu kuti mukhale Mkwati wapamtima Wanga wokondedwa.

Pamaso panga palibe wina monga imwe. Palibe amene angatenge malo anu. Wakhala woona ndi wokhulupirika kwa Ine. Ndikayang’ana pa inu, Mtima wanga ukusefukira ndi chisangalalo.

Ndikakuuzani, samalani kwambiri wokondedwa, zomwe mukumvera, padzakhala odzozedwa ambiri omwe amagwiritsa ntchito Mawu Anga, koma ndi abodza. Munamvetsetsa chenjezo Langa la Chibvumbulutso ndipo munakhala boona ndi wokhulupirika ku Mawu Anga.

Ndinanyadira kwambiri pamene munapemphera mowona mtima za mpingo umene mumasonkhana nawo. Ndinakuuzani kuti mupange chisankho choyenera, ndikukupatsani zitsanzo za zomwe mpingo wanbwino uli. Munakumbukira pamene ndinanena kuti onse amanyamula mizimu, ndikusankha mpingo wanbwino.

Ndinakuuzani kuti samalani kwambiri ndi m’busa wanu. Kotero inu mungolingalira mmene mtima Wanga unalumpha ndi chisangalalo pamene ndinakuona mukukhala ndi abusa amene ndinatuma kuti akubweretseni inu kwa Ine. Inu mumadziwa kuti unali Mzimu Wanga Woyera ukukhala mwa mneneri Wanga kuti akutsogolereni inu kwa Ine.

Ndikukumbukira tsiku limene munali okondwa kwambiri, ndi kukondwa kwambiri, pamene ndinaitana mngelo Wanga pamalo okwezeka kuti ndimusonyeze chithunzithunzi cha inu. Tinayima pamenepo ndikukuwonani mukamaguba nyimbo ya
Patsogolo asilikari Achikhristu pamaso pathu.

Iye anakonda momwe inu nonse munabvala mu zobvala za mtundu wanu kuchokera kumene inu munachokera; monga Switzerland, Germany, ndi padziko lonse lapansi. Lililonse mu tsitsi lanu lalitali lomwe linali lokonzedwa bwino kwambiri. Masiketi anu anali pansi bwino. Ndinali wonyada ndi wokondwa kukuwonetsani inu nonse kwa iye, kotero kuti abwerere ndikukulimbikitsani ndikukuuzani kuti adakuwonani Kumeneko.

Liso lirilonse linali pa Ife. Pamene atsikana ochepa, kumbuyo kwa mzerewo, anayamba kuyang’ana malo ena, anakuwa kuti, “Usachite zimenezo! Osachoka pa sitepe!

Pamene ndinakuuzani kuti ndikusungirani chakudya kuti mudye, munadziwa bwino zomwe ndikunena. Inu mumafuna kukhala Mkwati Wanga wa Namwali wa Mawu Anga. Sindinagwirepo ukucheza ndi wina aliyense. Nthawi zonse ndinali Ine, Mawu Anga. Zimenezo zinandisangalatsa Ine kwambiri.

Ndakusankhani, IWE, kuti ukhale Mkwati Wanga. Inenso ndimakukondani kwambiri, monga mmene mumandikondera Ine. Musataye mtima, khalani olimbikitsidwa, sangalalani, sangalalani, tsiku likuyandikira lomwe ndidzabwera kudzabwera kwa inu. Ndi nthawi yodabwitsa bwanji yomwe Tidzakhala nayo.

Kwa nonse a inu, LAPANI, dziko lapansi likuomba. Tsiku lina Los Angeles adzakhala ali pansi pa nyanja, monga ine ndinakuuzani inu kuti izo zikankhala. Mkwiyo wanga ukugwera pansi pake pomwe. Sindigwiranso mchengawo nthawi yayitali. Mudzalowa m’nyanja kuya kwa kilomita imodzi, mpaka ku Salton Sea. Zidzakhala zoyipa kuposa tsiku lomaliza la Pompeii.

Ndiyeretsa dziko lapansi ndi moto posachedwa. Ndidzaphaya zonse zomwe zili pamwamba pake ndi pansi pake. Mukuona zimene zikuchitika padziko lonse, monga ndinakuuzani. Inu mukuwona Mkwati Wanga akulumikizana pamodzi kuzungulira Mawu Anga, monga Ine ndinakuuzani inu.

Tsopano ndi nthawi. Tsopano ndi nyengo. Dzikonzekereni nokha!

Nthawi la mkwiyo Wake lili pa dziko lapansi. Thawani pamene nthawi ikaliko yothawa, ndi kubwera mwa Khristu.

Inu mukuyitanidwa kuti mubwere kudzalumikizana nafe, gawo la Mkwati Wake, pamene ife tikudzikonzekeretsa tokha Kubwera Kwake, pakumva Liwu la Mulungu likulankhula kwa ife ndi kutibweretsera ife Uthenga: Kusankhidwa Kwa Mkwati 65-0429E Lamlungu lino pa 12:00. P.M., nthawi ya Jeffersonville.

M’Bale. Joseph Branham

Genesis 24:12-14
Yesaya 53:2
Chivumbulutso 21:9