23-0326 Chilumikizo Chosawoneka Cha Mkwatibwi Wa Khristu

Uthenga: 65-1125 Chilumikizo Chosawoneka Cha Mkwatibwi Wa Khristu

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Dona Wosankhidwa,

Kodi mungapatse chiyani kuti Ambuye Yesu abwere kunyumba kwanu Lamlungu lino, kukhala pansi pa kama panu, kuyang’ana inu m’maso mwanu ndikulankhula ndi inu mwachindunji?

Simunathe kulankhula. Simukufuna kulankhula. Chomwe mungafune kuchita ndikungoyang’ana pa Iye ndi kulira. Mumaopa ngakhale kutsegula pakamwa panu. Kodi munganene chiyani? M’maganiso anu inu munkhala mukuganiza, Ambuye, ine sindine woyenera kuti Inu mukhale muno mu nyumba yanga. Ndine wotsikitsitsa mwa otsika. Ndakulepherani nthawi zambiri, Ambuye, koma Ambuye, ndimakukondani kwambiri.

Mukadzazindikira mu mtima mwanu, Iye akudziwa ndendende zomwe ndikuganiza, palibe chobisika kwa Iye. Iye amadziwa zinsinsi zomwe za mtima wanga.

Pamene muyang’ana m’Maso Ake amtengo wapatali, mumawona chikondi choterocho ndi chifundo. Angakhale akulankhula kwa inu osatsegula nkomwe pakamwa pake. Mungakhale mukuganiza, Iye ali pano, m’nyumba mwanga, ndi ine.

Mtima wanu ungayambe kuthamanga kwambiri, pamene munawona kuti Iye ali pafupi kunena chinachake kwa inu. Zonse mwakamodzi, Liwu lokoma kwambiri lomwe inu mukalibe mwalimvapo likanati, “Wokondedwa wanga wapamtima, usadandaule, dzina lako liri pa Bukhu la Moyo wa Mwanawankhosa Wanga. Osati bukhu lakale la chilumikizano chanu chachirengedwe, koma Bukhu Langa la Mkwati latsopano. Ndi satifiketi yaukwati wanu ndi Ine.

Wokondedwa wanga, simunakhululukidwe machimo anu onse ndi zolephera zanu zokha, koma kwa Ine, ndinu WOLUNGAMA. M’maso Anga, simunachitepo cholakwika chilichonse.

Ndiwe mwana Wanga wamtengo wapatali, wabwino, wopanda uchimo. Inu mwaima woyera; Mkwati Wanga wosaipitsidwa yemwe watsukidwa ndi Madzi a Magazi Anga Omwe.

Pasanakhale ngakhale mwezi, nyenyezi, kapena molekyu, munali Mwana Wanga ndi mwana wamkazi. Inu ndinu mawonetseredwe a thupi la zikhumbo zomwe zinali mwa Ine pachiyambi.

Jini lanu lauzimu linali mwa Ine chifukwa ndinu chionetsero cha makhalidwe Anga, maganizo Anga. Inu munali ngakhale mwa Ine asanaikidwe maziko a dziko.

Inu ndinu Mkwati Wanga wauzimu yemwe wakhala ali mu Kukhalapo kwa Mwana, akucha, pakumvetsera ku Mawu Anga. Tsopano mwayamba kukhala ndi chitsitsimutso, kubwereranso ndi kudzifoletsa nokha ndi Mawu Anga. Ndinu Mkwati Wanga Wosankhidwa.

Tsopano muli ndi mgwirizano wauzimu ndi ine. Thupi lanu likukhala Mawu, ndipo Mawu akukhala thupi; kuwonetseredwa ndi kutsimikiziridwa. Zomwe ndidakuuzani kuti zichitike mu tsiku lino, zikuchitika, tsiku ndi tsiku. Mawu kukhala Mawu.

Inu muli nalo Vumbulutso loona la tsiku lotsiriza lino: kusonkhanitsa kwa Mkwati Wanga pamodzi mwa Uthenga uwu. Palibe m’badwo wina umene ine ndinaulonjeza Iwo. Ine ndinalonjeza Izo kwa inu, mu m’badwo uno: Malaki 4, Luka 17:30, Yohane Woyera 14:12, Yoweli 2:38.

Tidzakhala ndi Phwando lachiyamiko Lamlungu lino pamene ndidzakuuzani zambiri. Ndikhala ndi inu maola ambiri, ndikuyanjana ndi kudya pa Mawu Anga. Ndikutsimikizirani kuti pakukhala ndi Mawu Anga, mneneri Wanga, Mawu Anga, kutyanka kuliza, muli mu Chifuniro Changa chabwino.

Ine ndinawauza iwo mu Mawu Anga, Ine ndaima pakhomo, ndipo ndikugogoda. Ngati wina amva MAU anga, nakatsegula chitseko, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine. Ambiri sangamve ndikutsegula chitseko chawo, koma mwa Chivumbulutso, mwatsegula chitseko chanu ndikundilandira Ine mkati.

Sagwirizana ndi kuliza Mawu Anga m’mipingo yawo. Ngati iwo analeka Mzimu Woyera ufufuze mumaganozo awo ndi Mawu, iwo agati anavomereza. Kumuleka Khristu, Mawu odzozedwa, afufuze chikumumtima chanu chomwe. Mulekeni Iye alowe mwa inu, muwone ngati Izo ziri zolondola kapena ayi.

Ine ndinakuuzani inu kuti sichizankhala chipembedzo kumibweretseni inu pamodzi, iwo sangakhoze nkomwe kugwirizana pa Mawu amodzi kapena awiri mu Baibulo. Kodi ine ndinayamba ndakuuzanipo inu kuti lidzakhala gulu la amuna? Ayi! Ine ndinakuuzani inu kuti Iwo unali Uthenga wa Munthu MMODZI; ndipo mudamvera ndi kumvera.

Popeza sanamvere ndi kuvomereza pulogalamu yanga yoyambirira kuyambira pachiyambi, ndinawatumizira alaliki, aphunzitsi, atumwi, abusa ndi aneneri. Koma iwo anatumizidwa kuti akaloze anthu KUBWERA ku pulogalamu yanga yoyamba ndi yabwino, Mngelo Wanga wamphamvu. Pakuti Ilo ndi Liwu la Mulungu kwa inu.

Iwo ndi odzozedwa, koma ine ndiri ndi MNENERI MMODZI MTUMIKI OTI AKUTSOGOLERI INU. MZIMU WOYERA NDI MNENERI. Kodi Ine sindinakuuzeni inu nthawi zambiri, MAWU ANGA OLANKHULA KUPYOLERA MWA IYE SAFUNA KUTANTHAUZIRA, OSAWONJEZERA KAPENA KUCHOTSA CHONCHO CHILICHONSE CHONENA, AKUNGONENA ZIMENE IYE ANANENA PA MATEPI AWO? Ameneyo ndi mneneri, Mzimu Woyera akukutsogolerani inu.

Iye ndi amene Ine ndinamutuma kuti adzakuitane iwe kuti ukhale Mkwati Wanga. Iye ndi amene adzakuonetseni kwa Ine. Iye ndi yemwe ine ndinayima naye pamene ine ndinamuwonetsa iye chithunzithunzi cha inu, Mkwati Wanga. Ine ndinakuuzani inu zonse za iye mu Chivumbulutso pamene ine ndinati, INE Yesu ndatumiza NGELO WANGA kuti adzachitire umboni kwa inu zinthu izi MU MIPINGO. Ndi INE, ndikungogwiritsa ntchito thupi lake ndi mawu ake kulankhula nanu. ”

Ndi tsiku lodabwitsa bwanji lomwe ife tikukhala limodzi ndi Iye. Sitinakhalepo osangalala kapena okhutira kwambiri m’mimweo yathu. Ichi ndi Ichi. Izi ndi zomwe takhala tikuyembekezera kwa moyo wathu wonse.

Mulibe mthunzi wa chikaiko m’mitima mwathu kapena m’maganizo mwathu. Pakuti ndi Uthenga uliwonse umene timamva, Iye amatiuza ife tiri mu chifuniro Chake chabwino. Pali Liwu limodzi lokha limene lidzakuyanjanitseni inu, kukupangitsani inu kukhala angwiro, ndi kukubweretsani inu pamodzi…Ine, INE NDIKULANKHULA KUPITILA MNENERI WANGA. OSATI MAWU AKE, MAWU ANGA. NDI NJIRA ANGA WOPEZEKA.

Gome yafalikira. Ilo ladzaza ndi kabichi, ndi mpiru, ndi radishes…MAWU PAMWAMBA PA MAWU, PAMWAMBA PA MAWU. Tidzakhala ndi Phwando lakuthokoza kuchila kale lonse. Padzakhala chisangalalo padziko lonse lapansi pamene Mkwati adzasonkhana mozungulira pamagome awo kuti amvetsere ku Liwu la Mulungu likulankhula kwa iwo. Nyumba zathu ndi mipingo idzadzazidwa ndi kupezeka kwake. Tidzakhala osalankhula kupatula Ulemerero wathu, Aleluya, lilemekezeke dzina la Yehova.

Bwerani mukhale gawo la Msonkhano wa Chiyamiko cha Banja la Mkwati, pamene Iye atidyetsa. Musachedwe, pamene tidzayamba kuchita phwando Lamlungu, ndendende 12:00 P.M., nthawi ya Jeffersonville. Iye adzakhala ali kumeneko, pakuti Iye anandiuza ine kuti Iye azankala pamene.

NDIZABWELA ndipo ndikhala ndikukuuzani zonse za Mgwirizano Wanu Wosaoneka Wa Mkwati Wa Khristu 65-1125.

Ndidzakuwonani pa gome.

M’Bale . Joseph Branham

AKA: Mkazi Wake Wosankhidwa.