Kubadwa kwatsopano ndi Khristu, ndi vumbulutso. Mulungu wawululira kwa iwe chinsinsi chachikulu ichi, ndipo kumeneko ndi Kubadwa kwatsopano. Tsopano kodi iwe ungachite chiyani pamene ungalibweretse gulu lonselo pamodzi? kumene vumbulutso likumakhala mwangwiro mu chiyanjano,
Mulungu akusonkhanitsa gulu lake lonse la Mphungu pamodzi mumgwirizano wangwiro akuulula Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake.
Njira ya Mulungu ya kukhala ndi mfumu, monga Davide anali, inali yolondola, ndipo inu mumakhala ndi chimake chimodzi cha lingaliro. Monga mtsogoleri mmodzi ndi gulu la atsekwe, kapena zina zotero, inu simungakhoze kutenga awiri kapena atatu a iwo. Ndiye, inu mukawasokoneza iwo palimodzi, inu mumabwera ndi lingaliro la mtundu uliwonse.
Ngati ine ndinakukhumudwitsani mwa kunena zimenezo, mundikhululukire, koma, ndinamvelera kuti mwina icho chinazembedwa, koma, Ine ndine Liwu la Mulungu kwa inu.
Ife timakhulupirira zimenezo ndi mtima wathu wonse. Umu ndi momwe ife timamvera, Ambuye
Iwo sasowa kutsimikizira chirichonse mwasayansi, kapena kumufunsa Msaduki aliyense kapena Mfarisi, kapena china chirichonse, za izo. Ine ndinanena izo, iwo akhulupirira izo, pakuti nkhosa Zanga zimamva Liwu Langa.
Kodi Liwu lomwe lili pa matepi kwa Mkwatibwi Wanu ndi lotani?
Ili ndi Liwu la Mulungu mu mawonekedwe a kalata, chifukwa Ili ndi vumbulutso lathunthu la Yesu Khristu, Chipangano Chakale ndi Chatsopano zitayikidwa palimodzi. Ameni. Apo inu muli.
Kodi matepi akadali ofunikirabe lero?
Ine ndikudziwa kuti, ndikadzachoka pa dziko lapansi lino, matepi awo ndi mabuku awo azidzakhalapobe, ndipo ambiri a inu anthu aang’ono mudzapeza, mu masiku akudza, kuti izi ndi chimodzimodzi Choonadi,
Ambuye, ife tikukhulupirira kuti matepi ndi mabuku ndi moyo wanu, utumiki wanu wamoyo womwe munamusiyira Mkwatibwi Wanu.
N’chifukwa chiyani matepi ndi LIWU LOFUNIKA KWAMBIRI kuti ife timve?
Ife tiri mu m’badwo wachinyengo kwambiri umene ife tinakhalamo konse. “Iwo ukananyenga Osankhidwa omwe ngati izo zikanakhala zotheka,” chifukwa iwo ali nako kudzoza, iwo akhoza kuchita chirichonse monga ena onse.
Aliyense amene adzawonjezere mawu amodzi kwa Awa, kapena kutenga Mawu amodzi kwa Iwo.” Iwe uyenera kukhala nawo mtheradi penapake.
Motero, Mtheradi wathu chiyenera kukhala Mawu a Mulungu.Inu mwatiululira kuti Mawu a Mulungu ndi Liwu la Mulungu ndi ofanana. Liwu ndi malingaliro enieni a Mulungu olankhulidwa, monga momwe munachitira ndi aneneri pamene munalemba Baibulo; koma m’masiku otsiriza ano, munasunga Mawu Anu, Liwu lanu, powajambula ndikuwayika pa tepi. Choncho, Liwu Lanu lolankhulidwa pa matepi ndi Mtheradi kwa Mkwatibwi.
Ndipo ngati mpingo uli mtheradi wanu, inu simumalabadira zimene aliyense anena. Ndiwo mtheradi wanu. O Mulungu, thandizani izi kuti zimire mkati! Kwa ine, chinthu chonse ncholakwika. Mawu a Mulungu ndiwo mtheradi. Chirichonse chimeme Mawu anena, ndiye ndiko kulondola.
Iye anali kuyembekezera kuti iwo amuitanire Iye. Ndicho chimene Iye akuyembekezera usikuuno, kuti inu mumuitanire Iye. Zindikirani, pamene ophunzira awo anamuitanira Iye umo ku chiyanjano chawo kuzungulira gome,
Kodi wina anganene bwanji, kulungamitsa, kapena kupereka zifukwa, iwo amene akunena kuti iwo akukhulupirira Uthenga wa nthawi yotsiriza, kuti asasewere matepi m’matchalitchi awo pamene ali ndi mwayi womva LIWU LIMENE LA MULUNGU? Ndi Mawu omwe Mulungu analankhula kudzera m’milomo ya munthu kudzera mwa mneneri wake wodzozedwa. LIWU LOKHALO lomwe latsimikiziridwa ndi Lawi la Moto, lotsimikiziridwa mwa kudziwa zinsinsi zomwe za mumtima, lotsimikiziridwa ndi zizindikiro ndi zodabwitsa, kuti NDI Liwu la Mulungu kwa m’badwo uno.
Kodi wina angapange bwanji zifukwa, kufotokozera, kapena kusakhala ndi chilakolako chomva Liwu la Mulungu nthawi iliyonse akasonkhana?
Ambuye, musandilole ine kuti ndisatenge Liwu Lanu pa matepi mwachibwana. Mundilole ine nthawi zonse ndilengeze ku dziko lonse lapansi Ndi Liwu LOKHA lomwe ayenera kumva. Mundilole ndilengeze kwa Mkwatibwi Wanu, CHONSE CHOMWE AKUFUNIKA NDI LIWU LANU PA MATEPI.
Ife timakonda kuyanjana. Timakonda kulankhula za Inu ndi kutchula zidutswa za Mawu Anu, koma palibe china chachikulu chomwe inu mukanachita kwa Mkwatibwi Wanu kuposa kutipatsa Mawu Anu pamwamba pa Mawu, Vumbulutso la Liwu Lanu, kenako kuzindikira YEMWE IFE TILI, MKWATIBWI WANU WOKHULUPIRIKA.
Momwe ine ndingapitirire ndi kupitilira, ndikusonkhana pa vumbulutso lalikulu lomwe Mulungu watipatsa ife. Palibe mapeto; koma chinthu chachikulu chomwe ine ndingachite ndikukuitanani inu kuti mubwere mudzamve nokha Liwu la Mulungu ndi gawo la Mkwatibwi Lamlungu pa 12:00 PM, nthawi ya Jeffersonville, pomwe tidzanva: 65-0815 – Ndipo Osadziwa Izo Ayi.
Wokondedwa Namwali wamng’ono wa Khristu, Mawu, Gulu la Nkhosa, Mkwatibwi:
Momwe mitima yathu inasangalalira kwambiri titamva mngelo wake wamphamvu akulengeza kuti ndife Mbewu ya Mulungu yokonzedweratu yomwe singachite china chilichonse koma kutsatira Liwu Lake. Izo zimatanthauza zambiri kuposa moyo kwa ife. Inu mukhoza kutenga miyoyo yathu, koma inu simungathe kutenga Liwu Lake. Ife ndife amodzi ndi Mawu Ake. Ife Ndife amodzi ndi Liwu Lake. Ife ndife amodzi ndi Iye.
Izo zikuwoneka zachilendo kwa ife kotero kuti ife sitikumvetsedwa bwino komanso kupangidwa msangulutso chifukwa ife timati timakhulupirira mu nkusewera matepi; kuti ilo ndi Liwu la Mulungu likulankhula ndi Mkwatibwi Wake. Satana ali ndi anthu wanyengedwa kotero iwo amaganiza kuti mwa ife kulengeza kuti ndife mpingo wa tepi, ndi chinthu chinachake chosemphana ndi Mawu, cholakwika, ndipo tikusocheretsedwa, pomwe nthawi zonse Ndi njira yangwiro yoperekedwa ndi Mulungu kwa Mkwatibwi Wake.
Kodi iyo ingakhale njira ina bwanji? Ngati inu mutatanthauzira molakwika Mawu amodzi omwe adalankhulidwa,inu mwatayika.Iwo angakhale ndi chifukwa ndinso cholinga choyenera, koma ndikukhala olakwa. Wina akhoza kudzozedwa ndi Mzimu Woyera koma nkukhalabe wolakwa.
Ngati Mulungu akanakhala kuti sanapereke njira yoti Mkwatibwi Wake amve yekha Mawu onse, ndiye kuti pakanakhala njira ina. Koma Iye wapereka njira kwa munthu aliyense padziko lapansi kuti akhale ndi mwayi womva Mawu akulankhula kwa iwo mwachindunji popanda kufunikira kutanthauzira, kufotokozera, kapena malongosoledwe. Izo zonse ndi Pakuti Atero Ambuye…MFUNDO!
Ife tonse timavomereza kuti tiyenera kukhala ndi Mawu kuti tikhale Mkwatibwi Wake.
Ine ndikukhulupirira kuti chirichonse chimene ife timachisowa chinalembedwa momwemu Umu, zikungosowa kuti zitanthauziridwe ndi Mzimu Woyera. Ine sindikukhulupirira kuti munthu aliyense pa dziko lapansi ali nawo ufulu woika kutanthauzira kwake kwake ku Mawu. Mulungu samasowa aliyense kuti atanthauzire Mawu Ake. Iye ndi Wodzitanthauzira Iye Mwini. Iye anati Iye akanadzachita izo, ndipo Iye akuzichita izo.
Mwachinvekere, Ambuye walankhula ndi kuulula kwa Mkwatibwi Wake kuti palibe njira ina yokhalira Mkwatibwi Wake wosankhidwa koma kukhala ndi Mawu Ake. Mulungu mwiniwake amatanthauzira Mawu Ake Omwe, ndipo palibe wina amene ali ndi ufulu wowonjezera kutanthauzira kwake pa Iwo.
Mawu amanenanso kuti MNENERI Wake ndiye womasulira Mawu Ake. Iye ndi Liwu la Mulungu kwa anthu. Zimene iye amanena ndi Mawu a tsiku lathu.
Mwa kumvetsera Liwu la Mulungu pa matepi, ife timakhala kuti ulosi ukukwaniritsidwa. Palibe china chilichonse champhamvu kwambiri, chopatulika kwambiri, chokwaniritsidwa kwambiri, palibe changwiro kwambiri kuposa kumvetsera Liwu lotsimikiziridwa la Mulungu likulankhula nanu.
Pamene ena anganene kuti palibe chilichonse ku izo, Mphungu zikusonkhana ndikusangalala ndi chisangalalo chachikulu chopitilira, ndi chitsimikizo kuti zikusunga Mawu a Mulungu. Iye anatiuza ife ngati muli ndi makina a tepi, sonkhanitsani gulu la anthu pamodzi, ndipo sewerani iyo, ndipo mvetserani mwatcheru. Mwa chisomo ndi chifundo Chake, ndicho ndendende chomwe ife tikuchita.
Mulungu watiyitana kutitulutsa ife mu m’badwo woyipa uno chifukwa cha Dzina Lake. Ife tikukumana ndi mayeso ndi mayesero ambiri kuposa kale lonse. Satana ali panjira yomenyera nkhondo monga iye akudziwa kuti nthawi yake ili kumapeto. Inu mungakhoze kumadzifunsa nokha kuti, kodi ine ndingamadutse bwanji mu zinthu zonse izi, ndipo Kodi Ine ndine Mkwatibwi Wake?
Inu muli kupangidwa kuwonetseredwa, kuyesedwa, ndi kutsimikizira kwa Satana, NDIFE MKWATIBWI WAKE. Ndife Mawu mu thupi. Ife tikhoza kulankhula Mawu ndipo izo zidzafika pochitika. Izo Ndi PAKUTI ATERO AMBUYE.
Tili ndi Liwu la Mulungu likulankhula mwachindunji kwa Satana ndi kumuuza iye:
Satana, iwe wagonjetsedwa. Iwe ndi wabodza. Ndipo, monga wantchito wa Mulungu, ndi monga antchito, ife tikulamulira kuti mu Dzina la Yesu Khristu, kuti iwe umvere Mawu a Mulungu, ndipo utuluke mwa anthu, chifukwa izo zinalembedwa, “Mu Dzina Langa iwo adzatulutsa ziwanda.”
Palibe chonga ichi chomwe chinachitikapo mu m’mbiri ya dziko lapansi. Nchiyani chomwe chakopa anthu awa kuti agwirizane onse nthawi imodzi kuti amve Liwu limenelo lakuyitana lomutulutsa kwa Mkwatibwi Wake? Ndi Mulungu akukwaniritsa Luka 17:30. Ndi Mulungu akukwaniritsa Chivumbulutso 10:7. Ndi Mulungu akuwulula Ahebri 13:8, Melkizedeki mu thupi la munthu, monga momwe Iye adachitira kwa Abrahamu.
Iwo akudikira ndi kudabwa, Kodi Iye adzalankhula chiyani? Kodi Chidzachitika nchiyani Iye akadzayamba kulankhula? Iwo amafuna kukhalapo pa kulumikizana Kwa pa telefoni kuti apeze chilichonse chimene Iye akunena. Iwo amafuna icho. Iwo amafuna kuchimva icho chonse nthawi imodzi ndi Mkwatibwi padziko lonse lapansi. Pakuti iwo amakhulupirira kuti iye ndiye liwu limene Mulungu anasankha kukhala Liwu Lke kuti liyitane kumutulutsa ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake.
Ngakhale kuti ali kutali kosiyana kwa maola ambiri mu nthawi, koma onse ali pamodzi ngati CHIMODZI, akumvetsera, akumvetsera Liwu limenelo likulankhula nawo kuchokera ku Tchalitchi chawo cha panyumba. Akukhala munkupezekapo kwa Mwana wamamuna, akucha ndikuyembekezera Kubwera kwa Mesiya.
Mitima yawo ikuthamanga. Mzimu Woyera ukuwaulula zomwe zikuchitika. Mulungu wakhala akuyembekezera kufikira mpaka lero kuti awonetse Mawu Ake ndikusonkhanitsa Mkwatibwi Wake. Izo Zikuchitika, ndipo iwo ndi gawo la Izo. Chowonadi cha zomwe zikuchitika chikugwera m’mitima yawo. Iwo awerenga za izo m’Malemba kwa zaka mazana ambiri, koma tsopano ndi zenizeni. Vumbulutso la Mawu likuonekera kudzera mwa iwo. Maulosi a mneneri akukwaniritsidwa.
Pamene iwo akukhala pansi pa kudzoza kwakukulu kwa Liwu Lake lamphamvu, Iye amalengeza kwa iwo kuti akonzekere; pakuti usikuuno Iye apempherera aliyense wa iwo. Iye amatiuza kuti akayamba kupemphera, muyike manja pa odwala, chifukwa Mulungu alipo paliponse, kulikonse komwe ali: ku Texas, ku California, ku Arizona, South America, ngakhale m’nyumba za m’nkhalango mbali ina ya dziko lapansi. Kulikonse kumene iwo akulumikizidwa pa intaneti, ikani manja pa wina ndi mnzake tikayamba kupemphera ndipo Mulungu adzachiritsa aliyense wa iwo, ngati akhulupirira, pakuti Ndi Pakuti Atero Ambuye.
Iwo akumvetsa tsopano kuti m’mibadwo yonse ndi mneneri aliyense amene anakhalapo kapena amene adzakhalapo, padzakhala anthu enaake omwe adakonzedweratu kuti amve Uthenga umenewo, ndipo amenewo adzautsatira iwo. Iwo Sadzavomera gulu. Iwo Sadzavomera ndi kutsutsidwa kwa wosakhulupirira amene amati ndi njira yolakwika kapena si njira yoperekedwa ndi Mulungu. Iwo alibe mkangano ndi iwo.Iwo ali ndi chinthu chimodzi chomwe AYENERA KUCHITA, ndicho kukhulupirira ndipo kuti apeze gawo lililonse la Iwo momwe iwo angathere, kuulowetsamo monga Mariya amene anakhala pa Mapazi a Yesu. Iwo Sachita manyazi, iwo amanyadira kwambiri kunena kuti iwo ndi mnyamata wa tepi kapena kuti mtsikana wa tepi amene amakanikiza kusewera.
Liwu limenelo lawachenjeza kale kuti padzakhala odzozedwa pa nthawi yotsiriza omwe adzakhala ndi kudzoza kwakukulu, Mzimu Woyera. Adzatchula mobwereza mneneri ndi Uthenga wa nthawiyo; akunena kuti ndi okhulupirira, koma ali odzozedwa abodza.
Iwo adzakhala pafupi kwambiri ndi kudzoza kwenikweni komwe kukadati kunyenge osankhidwa omwe ngati n’kotheka, koma Iwo akudziwa kuti iwo sanganyengedwe, chifukwa iwo NDI MAWU. Iwo ndi Mkwatibwi weniweni amene anakhala ndi Mawu a Mulungu.
Liwu limenelo likulengeza kwa iwo kuti mu tsiku lino ilo Silidzakhala ndimu, kapena mphesa. Zimenezo zingakhale zosavuta kuzindikira kusiyana. Koma lidzakhala tangelo, theka la ndimu, theka la lalanje, mtundu wosakanikirana. Lidzawoneka ngati lalanje, koma silidzakhala lili ilo, chifukwa nthambi yatsopanoyo idzakhala handiredi peresenti ngati yapachiyambi. Iwo ADZAKHALA ndi Liwu Mawu apachiyambi. Iwo sadzatenga mlowammalo. Iwo Adzakhala ndi iye amene, Mulungu mwini wake adalengeza kuti ndi LIWU LAKE, MAWU AKE, otsimikiziridwa ndi Lawi la Moto.
Kodi chikuchitika nchiyani?
Mbewu ya Mulungu yokonzedweratu singachite china chilichonse koma kutsatira ndi kumvetsera Liwu limenelo, chifukwa limatanthauza zambiri kuposa moyo kwa iwo. Inu mukhoza kutenga miyoyo yawo, koma inu simungathe kutenga Liwu limenelo.
Bwerani mudzalumikizane nafe ndikukhala gawo la ulosi wa mneneri womwe ukukwaniritsidwa Lamlungu lino pa 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tikumva Malemba akuwonetseredwa.
M’bale Joseph Branham
Uthenga: 65-0725E “Kodi Ndi Chiyani Chokopa Pa Phiri?”
Mutu wokha wa Uthenga wa sabata ino ukuwulula kuzindikira Mzimu Woyera kwa Mkwatibwi. Kuganiza kuti padzakhala amuna odzozedwa enieni omwe adzauka m’masiku ano, ndi kudzoza kwenikweni kwa Mzimu Woyera womwewo womwe unali pa mneneri wathu, koma kukhala abodza.
Mawu amatiuza kuti adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa, kulandira mvula yomweyo, madalitso omwewo monga mneneri weniweni. Anthu adzasiya Mawu enieni otsimikiziridwa a tsikulo kupita ku zilakolako zawo, kudziunjikira aphunzitsi, okhala ndi zoyabwa mmakutu. Zidzakhala pafupi kwambiri ndi Mawu enieni mpaka zidzangokhala pafupifupi kunyenga Osankhidwa.
Kodi kudzoza kumeneko kudzakhala pafupi bwanji? Kodi zidzakhala zosavuta kuzindikira chomwe chili chowonadi ndi chomwe chili chabodza? Mneneri anatiuza kuti Mfumu Davide, munthu wotsatira mtima womwe wa Mulungu, wokhala ndi kudzoza pa iye, adapeza vumbulutso loona; koma ilo linali lolakwika.
CHIYANI!! Lolani chimenecho chilowe mkati mwakanthawi. Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu inali ndi kudzoza kwenikweni ndi vumbulutso loona, koma linali lolakwika! Ana a nkhosa a Mulungu ayenera kukhala maso kwambiri kuti adziwe kuti zomwe akumva ndi kudzoza koona kapena kwabodza; pakuti malo awo amuyaya akupumulira pa zigamulo izi.
Ife tikudziwa kuti Mulungu waika atumiki ambiri odzozedwa kuti athandize kutsogolera ndi kusunga Mkwatibwi Wake m’Mawu. Mawu Ake amanena choncho, ndipo ife tili oyamikira kwambiri Ambuye chifukwa cha aliyense wa iwo. Iwo ayitanidwa kukhala abusa pa nkhosa zawo.Iwo ayenera kuwasunga iwo m’Mawu. Pochita izi, iwo sayenera kulephera kusewera Liwu Lokhalo lotsimikiziridwa la Mulungu kwa nkhosa zawo.
Monga momwe ife tangomvera kumene momwe munthu aliyense angalakwire, ngakhale ali ndi kudzoza koona ndi vumbulutso loona. Koma Mkwatibwi akhoza kukhala otsimikiza konse, chifukwa Mulungu wapereka njira yangwiro yomwe iwo nthawi zonse angakhoze kuti amve KUDZOZA KOWONA, VUMBULUTSO LOWONA, PAKUTI ATERO AMBUYE WOWONA; KOKHA KANIKIZANI KUSEWERA.
Kumene kuli Nyama, kumeneko ndi komwe ife Mphungu tidzasonkhanako. Kumene kuli Nyama yatsopano, Mawu amu nyengo, Uthenga wa ola. Ndipo palibe malo atsopano odyera Manna amenewo kuposa kumva Liwu la Mulungu akulankhula Iyemwini.
Awo ndi Mawu Ake. “Munthu sadzakhala moyo ndi mkate wokha, koma ndi Mawu onse.” Mwaona? Okonzedweratu amadziwa izi. “Mawu achirendo, kapena liwu lachirendo, iwo sadzalitsatira.”
Chifukwa chomwe ife sitidzanyengedwa, ndipo sitinganyengedwe, ndi ndichifukwa chakuti ife ndife Mawu omwe ali ndi vumbulutso ili. Ife sitingakhale china chilichonse. Ife sitingamve china chilichonse. Ife Sitikudziwa china chilichonse.
“INE NDINE!” Osati “Ine ndinali, kapena ndidzakhala ndiri.” INE NDINE,” tensi yapakalipano, Mawu tsopano. Osati Mawu amene analipo, kapena Mawu amene ati adzabwere; Mawu amene alipo tsopano. Mwaona? Inu mwamvetsa zimenezo? “INE NDINE!” “INE NDINE” ali Mawu. “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu.” Ndi kulondola uko? “INE NDINE.” “Mulungu anandituma ine monga mneneri Wake, kuti ndidzatsimikizire izi kuti ziri zoona. Ine ndine yankho kwa Mawu awa, chotero, pamene Iye anabwera pansi pano ndi kuchita izi.”
Yesu anati, “Tsopano, izo zidzabwereza kachiwiri mu masiku otsiriza,” onani, kumadzitcha chinthu chomwecho.
Ambuye alemekezeke. Kakamba za chitsimikizo cha Mkwatibwi. Pomwe inu mukhala ndi Vumbulutso ili, ndiyeno inu mudzadziwa kuti inu muli wosankhidwa Wake, Okonzedweratu , Mkwatibwi wake wokomamtima.
Mwa kumvetsera Liwu la Mulungu pa matepi, ife tikumvetsera Mwana wa Munthu, amene ndi Khristu. Iye ndiye amene ife tikumudya. Ife sitikudya munthu; munthu, mawu ake adzalephera. Koma ife tikudya Thupi la Mawu a Mwana wa Munthu losalephera.
Ngati inu mukufuna kukhala otsimikiza Wani Handiredi peresenti kuti inu mukumvetsera ku Pakuti Atero Ambuye, bwerani mudzakhale nawo gawo la Mkwatibwi Lamlungu lino pa 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumva Liwu la Mulungu likutiululira zonse zokhudza iwo odzozedwa ps nthawi yotsiriza.
M’bale. Joseph Branham
Uthenga: Iwo Odzozedwawo Pa Nthawi Yotsiriza 65-0725M
Tsopano, ine ndikuganiza kuti palibe kulemekeza kokwanira kumene tikanakhoza kupereka kwa mayi.
Mayi athu ndiye oyamba nafe, ndipo anapatsidwa udindo waukulu wa zomwe ife tidzakhale komanso njira yomwe ife tiyenera kuyendamo. Iye anapatsidwa udindo kuchokera Kwa Mulungu woti atiyike ife panjira yoyenera. Ndicho chifukwa chake mayi ali nako mwapadela , kukhudza kochepa komwe kwapatsidwa kwa iye kuchokera kwa Mulungu.
Ndi dalitso lapadera bwanji lomwe lili mu nkhokwe la ife la Lamlungu lino, pamene ife tikupereka ulemu kwa Amayi onse, pamene ife tidzamva mngelo wachisanu ndi chiwiri wa Mulungu akufotokoza chikondi ndi ulemu womwe amayi athu ali nawo m’mitima mwathu.
Ife tikudziwa kuti tsiku lililonse ndi Tsiku la Anakubala, koma Lamlungu lino tidzapereka ulemu wapadera kwa Amayi onse pamene ife tidzamva mneneri wathu akupereka ulemu kwa iwo monga momwe iye adayankhula zaka 67 zapitazo pa tsiku lomwelo lofanana , pa 10 Meyi , 1959.
Liwu lomwe ife tonse timakonda kumva lidzalankhula Lamlungu lino, ndipo lidzatibweretsera ife Uthenga Wapadera wa Kalata Yachikondi, wa Mkwatibwi wa Yesu Khristu yekha.
Liwu limenelo linangolankhula ku dziko lapansi ndikuwachenjeza iwo kuti, “Musayese kundichitira Ine ntchito mopanda kukhala chifuniro Changa. Ndili ndi njira yangwiro yoperekedwa imene ine ndakupangirani inu, Mkwatibwi Wanga. Kumbukirani Mawu Anga, inu muzingonena zimene Ine ndalankhula pa matepi Anga, chifukwa inu mukulowa mu chiweruzo. Chifundo chakanidwa. Koma kondwerani, ndipo khalani oyamikira, chifukwa ine ndapereka ndi kukupatsani inu Chakudya Chobisika, Chakudya Chauzimu, kuti inu mukhale ndi moyo pa ubwino ndi chifundo cha Vumbulutso la Yesu Khristu.
Tsopano muli chilala m’dzikololi lomvera Liwu Langa . Iwo samakumvetsani inu chifukwa inu mumati ndinu anthu a Tepi, ndipo mukufuna kungomva Liwu Langa pa Matepi; koma ndakuitanani kukutulutsani inu ndipo ndakuwululirani inu njira Yanga yangwiro yoperekedwa ya lero.
Inu simunadziphatikize ndi osakhulupirira panthawi ya chilala. Ine ndakupatsani Liwu Langa kuti likuthandizeni. Mwa kusewera Liwu Langa, mgolo wanu siwudzapita wopanda kanthu, ngakhale mtsuko wanu siwudzauma, mpaka tsiku limene ine ndidzabwera ndikukutengani ngati Mkwatibwi wanga.
Ndicho chifukwa chake Ine ndinali ndi Liwu Langa likujambulidwa, kotero kuti inu muKhale ndi malo angwiro operekedwa oti mupiteko, komwe kulibe cholakwika, palibe chifukwa chofuna kutanthauzira, basi Liwu Loyera la Mulungu. Malo omwe mungapiteko kuti mumve ndendende zomwe Ine ndanena: Pakuti Atero Ambuye.
Ine ndidzalankhula nanu momveka bwino Lamlungu.Ine Ndikufuna kuti inu musadzaiwale zomwe ndidzalankhule nanu. Matepi awa ndicho Chakudya Chanu Chauzimu mu Nyengo Ino. Ndi cholemera kwambiri kwa ena a iwo; sangathe kuchidya icho. Icho sichinawululidwe kwa iwo, koma Ine ndakusankhani INU, ndipo ndakupatsani inu Vumbulutso la njira Yanga Yangwiro yoperekedwa.
Kwa inu, Ndi Chakudya Chobisika, komwe mukukhala ndi ubwino ndi chifundo cha Mawu Amoyo.
Pamene Ine ndinali kukhala m’thupi mwa Mwana wanga wa mamuna, iwo mophweka sanathe kuvomereza yemwe ine ndinali: Mulungu ndi munthu. Kenako ine ndinalonjeza kuti ndidzabweranso m’masiku otsiriza ndikukhalanso m’thupi la munthu monga momwe ndinachitira Abrahamu asanakhalepo, ndipo ine ndidzatsika pansi ndikudziveka ndekha m’thupi la munthu monga momwe ine ndinachitira nthawi imeneyo.
Izi ndi zomwe iwo adaphonya, nthawi imeneyo ndi tsopano, koma ine sindikufuna kuti inu muiwale. Chakudya chosungidwa chimene ine ndikukudyetsani inu, ndi mthenga wanga, ndi ofanana. Inu Simungathe kuwalekanitsa iwo. Uthenga ndi mthenga ndi ofanana.Ine ndinakuuzani inu m’Mawu Anga zomwe ndikanachita mu tsiku ili. Ndicho chifukwa chake ndi chifuniro changa kuyika Liwu Langa m’matchalitchi anu, m’nyumba zanu, kulikonse komwe inu mupita; chifukwa ndilo Liwu lofunikira kwambiri lomwe inu muyenera kumva. Ndi Liwu LOKHALO lotsimikiziridwa lomwe limalankhula Pakuti Atero Ambuye.
Chifundo chakhala chikukanidwa. Tsopano inu mukukhala pa Mawu Anga.Ine ndakupatsani inu Vumbulutso la yemwe Ine Ndili ndi yemwe INU muli. Sipayenera kukhala mthunzi umodzi wa kukayika m’mitima ndi m’maganizo mwanu. Inu ndinu Mkwatibwi Wanga Wosankhidwa, Wosankhidwiratu, Wokonzedweratu. Ndinu Mawu Anga Olankhulidwa omwe anali mwa Ine pachiyambi.
Inu muli ndi mwayi wopeza machiritso a matupi athu pamene madokotala alephera; Ndi chimodzi mwa Zakudya zomwe ine ndinalonjeza ndi kukupatsani inu m’masiku otsiriza.
Ine ndinalonjeza kuulula zinsinsi za mitima yanu ndikuchita izi. Ine ndiri mwa inu. Inu ndinu gawo la Ine, ndipo Ine ndine gawo la inu. Zizindikiro izi zidzawatsata iwo amene akhulupirira.
Lamlungu lino Ine ndidzakhala ndikugwirizanitsa Mkwatibwi Wanga kuchokera kuzungulira pa dziko lonse lapansi ndi Liwu Langa. Ine ndidzakuwuzani inu kuti muyike manja anu pa wina ndi mnzake. Musadzadzipempherere nokha, mudzapempherere amene mwamusanjika manja anu pa iye, chifukwa iwo akukupemphererani inu. Ife tidzapemphera limodzi, ndipo sipadzakhala munthu wofooka kulikonse padziko lonse lapansi ngati inu mudzakhulupirira.
Satana, iwe wagonjetsedwa! Yesu Khristu anakugonjetsa iwe! Iye anawuka kwa akufa ndipo akuyima pakati pa ife usikuuno, kutsimikizira Uthenga uwu wa masiku otsiriza. Tuluka mwa anthu awa! Asiye iwo, mu Dzina la Yesu Khristu! “Mu Dzina Langa iwo adzaturutsa adierekezi,” ndipo iwe watulutsidwa. Mu Dzina la Yesu Khristu asiye osonkhana awa!
Padzakhala machiritso akuchitika kuzungulira pa dziko lonse lapansi kuposa kale lonse.
Ine ndikuyitana dziko lonse lapansi kuti lidzabwere kudzalumikizana nafe Lamlungu lino pa 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, ndikudzamva Uthenga ndi mthenga Wake akutibweretsera ife Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake, Chakudya Chobisika cha Mkwatibwi.
M’bale Joseph Branham
Uthenga: Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake 65-0718E
Ola lachedwa. Nthawi yafika. Chisankho chiyenera kupangidwa. Mulungu akuchenjeza ana Ake. Ambuye Mulungu wathu walengeza ndi kutsimikizira kwa ife chomwe Choonadi Chake chili ndi Mawu Ake, ndi Mzimu Wake. Osati ndi mphamvu, osati ndi nkhondo, koma ndi Mzimu Wanga, ndipo Mawu Anu ndi Choonadi.
Iye watsimikizira kwathunthu kwa Mkwatibwi lero kuti Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi nthawi zonse.Iye watiwonetsa ndi kutiwululira kuti Uthenga ndi mthenga wa ora ali ofanana. Iye wativumbulutsira zinsinsi Zake zonse zomwe zinali zobisika mu Mawu. Iye watitsimikizira Izi ndi Mzimu Wake Woyera. Palibe funso m’maganizo mwathu, m’mitima kapena m’miyoyo yathu. Mawu Ake pa matepi ndi PAKUTI ATERO AMBUYE KWA MKWATIBWI WAKE.
Mulungu nthawi zonse walola njira zambiri kubwera kwa Iye.Iye amapanga chifuniro Chake chongololera kukhala chifuniro Chake Changwiro. Iye mongaso nthawi zonse wapereka CHIFUNIRO CHANGWIRO NDI NJIRA YABWINO KWA ANA AKE. Ambiri amayesa kubwera mwanjira yosiyana pochitira Mulungu ntchito popanda kukhala chifuniro Chake changwiro.Izo Zingawonekere ndikumveka ngati chifuniro Chake changwiro, koma izo sizili monga ndi Mawu Ake.
Ngakhale munthu wamkulu, wodzozedwa kumene, wochokera ku Kukhalapo kwa Mulungu, adapeza vumbulutso loti achite china chake kwa Mulungu, ndipo amafuna kuchichitira Mulungu; koma vumbulutso lomwe anali nalo linali lolakwika.
Aliyense wa ife ayenera kupeza njira Yake yangwiro yoperekedwa. Kodi ife tingadziwe bwanji kuti tili mu chifuniro Chake changwiro ngati wina wodzozedwadi, wochokera ku kukhalapo kwa Mulungu, ndi vumbulutso, si ali mu chifuniro changwiro cha Mulungu?
Pali NJIRA IMODZI YOKHA YODZIWIRA YA CHOWONADI, ndipo Mulungu wapereka njira imeneyo kwa Mkwatibwi Wake.
Liwu la Mulungu Mwiniwake lawuza mpingo uno, ndi inu nonse anthu omwe muli pa matepi, ndi anthu omwe ali olumikizidwa pa intaneti m’madera ena a dziko lapansi, nthawi imeneyo ndi TSOPANO. Iye anatiuza ife kuti timvere mwatcheru Kwambiri zomwe iye anali kunena , ndipo kuti ife TISALEPHERE.
Chotero ine ndikunena, mu Dzina la Yesu Khristu! Musati inu muwonjezere kanthu kamodzi. Musati mutenge, kuyika malingaliro anu omwe mwa Iwo. Inu muzingonena chimene chikunenedwa pa matepi awo. Inu muzingochita chimodzimodzi chimene Ambuye Mulungu wakulamulirani kuti muchite. Musati muwonjezere kwa Iwo.
Iye sananene kuti, ndipo izo sizikutanthauza kuti alaliki sangalalikire Mawu, aphunzitsi sangaphunzitse Mawu, kapena abusa kapena aneneri ife tichite zomwe tayitanidwira kuchita; iwo ayenera, ine ndiyenera.Ife tayitanidwa ndi kudzozedwa kuti tichite zimenezo.Ife tiyenera kuloza ndi kubwereza Uthenga uwu ndi mthenga kwa anthu, chifukwa iwo ndiwo Mawu a tsiku lathu.
Koma Iye akutiuza momveka bwino kuti tonsefe a ife tikhoza kudzozedwa, ndi kudzozedwa kolondola, kudzazidwa ndi Mzimu Wake Woyera, ndi vumbulutso latsopano, ndikukhala kunja Kwa chifuniro Chake. Mu tsiku lathu lino, Iye wapereka NJIRA YANGWIRO yodziwira motsimikiza kuti mukumva Liwu la Mulungu, lochokera kwa Mulungu Mwiniwake. Ndiyo njira YOKHAYO yangwiro.
Utumiki suyenera kungotchula mobwereza kokha ndi kulalikira Uthenga uwu, koma ife tiyenera kusewera Liwu la Mulungu pa matepi kwa anthu. Palibe KUDZOZA KWAKUKULU kuposa kumva Liwu la Mulungu. Palibe njira ina yodziwira popanda mthuzi wa kukayikira kuti zomwe ife tikumva ndi NDIZOMWEZODI zomwe Mulungu ananena.
Mu tsiku lino, mosiyana ndi tsiku lina lililonse mu mbiri ya dziko lapansi, Mulungu wapereka njira yomwe imapangitsa kuti zikhale zosatheka kuphonya izo, ngati inu ndinu Mkwatibwi Wake Wokonzedweratu.Iyo yatsimikiziridwa ndi kuwululidwa ndi Lawi la Moto Mwiniwake kuti ndi Liwu la Mulungu Mwiniwake likulankhula mwachindunji ku Mpingo Wake.
Kwa zaka zikwizikwi, ana a Mulungu akhala akulakalaka ndikukhala nayo njala yakumva Liwu la Mulungu pa Iwo eni.Momwe iwo bwanji anakhumba akanakhalapo tsiku limene lija pamene Yesu analalikira kwa zikwizikwi paphiri. Kumva momwe Iye analankhulira Mawu Ake mwachikondi ndi chifundo. Kumva momwe Iye anayikila kutsimikiza pa Mawu aliwonse. Momwe Iye analankhulira ndi kulimbikitsa mitima yawo.
Ife tili amoyo tsopano ndipo tili mu mkupezeka kwa Mulungu kumva Liwu la Mulungu.
Ife ndife athunthu handiredi peresenti. Ife sitidakhalepo osangalala kapena mochuluka osakhalapo ndi mafunso m’miyoyo yathu. Ife ndife mmodzi ndi Iye ndi Mawu Ake. Ife ndife Mawu Ake. IFE TILI MU CHIFUNIRO CHAKE CHANGWIRO MWAKUKHALABE NDI LIWU LAKE, MAWU AKE. Iye adzabweranso tsiku lina lililonse tsopano kuti adzatitenge ife limodzi naye.
Zikomo inu Ambuye Yesu!
Ambuye Mulungu wanu wawonetsera kwa inu chomwe chiri Choonadi. Ambuye Mulungu wanu watsimikizira chomwe chiri Choonadi, mwa Mawu Ake ndi mwa Mzimu Wake. “Si mwa mphamvu, si mwa nkhondo, koma mwa Mzimu Wanga.” Ndipo, Mzimu, “Mulungu akufuna iwo amene ampembedza Iye mu Mzimu ndi Choonadi.” “Mawu Anu ali Choonadi.” Ndipo Iye watsimikizira mwathunthu kuti Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi nthawizonse. Iye wawonetsera Mbewu ya madzulo kwa inu. Iye wawululira Iyo kwa inu, mu Mawu. Iye wayitsimikizira Iyo kwa inu, mwa Mzimu Wake.
Ndi mtima wanga wonse ine ndikukuitanani aliyense wa inu kuti mubwere kudzalumikana ndi gawo la Mkwatibwi Wake pamene tikulumikizana kuchokera padziko lonse lapansi nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, kuti tidzamve Liwu Lake likulankhula kudzera mwa mthenga wake wachisanu ndi chiwiri wa mngelo ndikutibweretsera ife Uthenga: Kuyesa Kuti Umuchitire Mulungu Ntchito Mopanda Kukhala Chifuniro cha Mulungu 65-0718M.
Pamene ife tikumvetsera Uthenga uwu, Kusankha Kwa Mkwatibwi, ena amaganiza kuti mneneri akungolankhula ndi kutilangiza za khalidwe ndi thunthu limene mwamuna ayenera kuyang’ana akamasankha mkazi amene akufuna kukhala mkazi wake. Izo ndi zoona, iye akutero, koma pali kalata yeniyeni yobisika yachikondi m’Mawu Ake. Zimene Iye akuulula kwa Mkwatibwi Wake ndi zozama kwambiri. Mulungu akulankhula ndi iye mwachindunji, kumuuza zomwe ankafuna mwa Iye, ndi chifukwa chake Iye anamusankha iye kuchokera pachiyambi. Iye anafuna kuti Iye adziwe kuti wamusankha iye kukhala MKWATIBWI WAKE WOKONDEDWA WOKOMA MTIMA yemwe Iye ankafuna kugawana naye Umuyaya Wake.
Pachiyambi, Mulungu anali kufunafuna Mkwatibwi amene adzakhala ndi Khalidwe Lake lomwelo. Mzimu Wake womwewo ukanadzaonekera mwa Iye. Iye anafuna Mkwatibwi amene akanadzakhala wodzipereka kwambiri kwa Iye, ndi Mawu Ake olonjezedwa,Kufikira mpaka Maganizo omwe anali mwa Iye adzakhale mwa Iye. Iye ayenera kuumbidwa monga momwe Iye alili.
Iye anafuna kuti Iye akhale thupi Lake lomwelo, mafupa omwewo, Mzimu womwewo, chilichonse chomwecho, basi chimodzimodzi monga Iye. Awiriwa a iwo adzakhala M’MODZI.
Iye sakanakhala wa chimasomaso mmaso mwake . Iye sakananyengereredwa ndi ma liwu ena aliwonse. Iye akanakhala woona mtima komanso wokhulupirika kwa Iye, mosasamala kanthu za zomwe wina anganene. Iye akanamutenga Iye pa Mawu Ake. Chilichonse chimene Iye adanena, AKANAKHULUPIlIRA MAWU ONSE, zilibe kanthu kaya ndi motalika bwanji zingatenge kuti zikwaniritsidwe, iye Akanakhulupirira izo. Iye akanakhalabe ndi Mawu Ake.
Iye akanakonda Iye, ndipo Iye yekhayo. Iye sanafunikire kumupatsa iye chuma chambiri, iye anali ndi Ngale yamtengo wapatali, Vumbulutso lenileni la Iye. Iye akanadziwa, iwo anali M’MODZI ndipo ndi ofanana. Mzimu Wake ukanakhala mwa Iye. Chilichonse chimene Iye akanafuna, Iye akanamupatsa Iye; chomwe Iye ankayenera kuchita chinali kupempha ndi kukhulupirira, ndipo Iye akanachita icho.
Iye ankadziwa kuti Iye akanapita kwa nthawi yaitali kuti akamumangire nyumba yomwe ikanakhala ndi chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ankayimanga iyo momwe Iye akanakondera. Iye ankadziwa tsiku lina Iye adzabweranso kwa Iye, monga momwe Iye analonjezera, ndiye kuti adzakhala ndi Mgonero Waukwati waukulu kwa zaka chikwi. Kenako, adzapita limodzi ku Nyumba yokongola imene Iye adamumangira iye kuti akhale Kwamuyaya.
Palibe china chilichonse chomwe chingakhale chovuta kwa Iye. Iye Sadzafuna china chilichonse. Iye adzakhala choncho wokhutira ndi wokhutsidwa ndi pokhala ndi Vumbulutso podziwa yemwe Iye ali, ndi kuti Iye ndi ndani. Iye anadziwa kuti Iye adzasunga Mawu Ake. IYE ADZAKWANIRITSIDWA, PODZIWA KUTI IYE NDIYE YOMWE IYE ANASANKHA KUTI AKHALE MKWATIBWI WAKE.
Abale ndi alongo anga, Mulungu wamphamvu wa Kumwamba ndi dziko lapansi anayang’ana kupitilira mumuyaya ndipo WAKUSANKHANI… INU KUKHALA MKWATIBWI WAKE WOSANKHIDWA WOKOMA MTIMA.
Ine ndikukuitanani inu kuti mubwere mudzalumikizane nane limodzi ndi gawo la Mkwatibwi Wake Lamlungu lino, pamene Iye akulankhula kudzera mwa mngelo wake wamphamvu ndikutiuza kuti ndife Mkwatibwi Wake Wosankhidwa.
M’bale Joseph Branham
Uthenga: 65-0429E Kusankha Kwa Mkwatibwi Nthawi: 12:00 P.M. Nthawi ya ku Jeffersonville