22-1225 Kuchita Manyazi

Uthenga: 65-0711 Kuchita Manyazi

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwati Rebekah,

Atate anatumiza mtumiki wake wokhulupirika, Eliezere, kukasanka Mkwati Wake Rebeka. Ife tamuziba iye, mtumiki Wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri, William Marrion Branham, yemwe Iye anamutuma kuti: Amuyitane, Asonkhanitse, Atsogolere ndipo potsiriza Atidziwitse ife, kwa Iye.

Iye watipatsa ife kutsanulidwa kwakukulu kwa Mphamvu Yake Yofulumizitsa ndipo watifikitsa ife kuziba udindo wathu, malo athu, ndi maudindo athu, pokhala anthu oitanidwa, olekanitsidwa ndi dziko, odzipereka kwa Mulungu. Iye akutitsogolera ndi kutitsogolera mu zinthu zomwe timachita ndi kunena, kubweretsa ulemu ndi ulemerero ku Dzina Lake.

Palibe kanthu, paliponse, kangatilekanitse ife kwa Izo, PALIBE. Ndife otetezedwa Kwamuyayaya mu Ufumu wa Mulungu. Atate watidinda Chidindo Chake ife mpaka kumapeto kwa kopita kwathu.

Satana amatikhonya ISE kuseni ndi usiku. Iye amanena chirichonse kwa ife, ndipo amatitsutsa ife, ndipo amayesa kutipangitsa ife kuganiza kuti ife sitiri Mkwati ameneyo. Amaponya chilichonse m’njira yathu kuyesa kutisokoneza, monga matenda ndi mavuto, koma sitimumvera. Mphamvu yofulumizitsa iyo ili TSOPANO mwa ife ndipo ife tasindikizidwa ndi kukhazikika pa Mawu amenewo. Tikutoloka pa kamelo yathu, kuthamangira kwa Iye popita ku Mgonero wathu waukulu wa Ukwati.

Sitichita manyazi ndi zomwe timakhulupirira; m’malo mwake, ife tikufuna kuti dziko lidziwe, IFE NDIFE ANTHU AMATEPI AMENE AMAKHULUPIRIRA MAWU ONSE OLANKHULIDWA NDI MNENERI WAKE WOKHULUPIRIKA WA ELIEZA yemwe Iye anamutuma kuti akamuitane ndi kutsogolera MKWATI WAKE WA REBEKA. Ife sitimawonjezeranso kapena kuchotsa Mawu AMODZI. Uthenga uwu ndi Mtheradi wathu.

Angakhoze bwanji munthu yemwe ali wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, wodzaza ndi Mphamvu ya Mulungu, ndi chikondi cha Mulungu mu mtima mwake, kulankhula kwa munthu maminiti pang’ono chabe ndi kusakamba chinachake cha Uthenga umene iye wangowumva kumene pa Tepi?

Mukakumana ndi anthu amene amadzinenera kuti ndi okhulupirira mu Uthenga wa nthawi yotsiriza ino, mukhoza kuyankhula nawo maminiti pang’ono chabe ndipo mukhoza kudziwa kumene iwo akuyima pa kuliza matepi. Iwo mwina ndi Anthu a Tepi kapena ayi.

Ndi shosaganizila kuti amaona kuti ndi chamanyazi, kapenanso cholakwika, ngati munganene kuti mumaliza matepi kutchalitchi kwanu kapena kunyumba. Iwo amamverera kuti ndi zotsutsana ndi Mawu ndipo osati Njira yoperekedwa ndi Mulungu. Mumaonesedwa pansi chifukwa mumati ndinu “Munthu Watepi”.
[12/24, 12:38 PM] Br moya: Atumiki omwe amaliza matepi m’mipingo yawo amatsutsidwa, ndipo amaitanidwa aulesi. Ndipo ngati inu mumvetsera kwa tepi yomweyo pa nthawi yomweyo, chabwino, sindinu nkomwe mtumiki, ndinu chipembedzo, kapena wopempela munthu.

Ine ndikuganiza anthu onse aja omwe anachita conekiti pa telefoni mu mipingo ndi nyumba zawo, akumvetsera kwa M’bale Branham onse pa nthawi imodzi, iwo ayenera kuti anali achipembedzo nawonso. Ayenera kuti sianali mu pulogalamu la Mulungu. Sanachite manyazi NDIPO NAIFE.

Patawi chabe zochepa mukalankhula ndi anthu, amakudziwitsani pomwepo pomwe ayima: Inde, timadinikiza kuliza. Inde, timamvetsera matepi Lamlungu mu Mpingo kapena nyumba zathu. Inde, tepi yomweyo, na nthawi yomweyo.

Chifukwa chiyani ena amati, “Timapita kutchalitchi Lamlungu m’mawa, Lamlungu usiku, ndi Lachitatu usiku. Tili ndi abusa abwino; Iye amazifotokoza momveka bwino komanso momveka bwino kuti ife timvetse. Iye akufotokoza Uthenga kuti ine ndiwumvetse Iwo. Inu muyenera kukhala ndi utumiki kuti mukhale Mkwati. M’bale Branham sananene kuti mukaziliza matepi mu mpingo.”

Munena chiyani ndiye chofunikira kwambiri? Zomwe alaliki amanena, zomwe M’bale Joseph akunena, kapena zomwe Liwu lomwe la Mulungu likunena pa Tepi? Mtheradi wanu ndi chiyani? Kodi pa Tepi pali chiyani, kapena zomwe wina akunena?

Utumiki ndi wabwino, ndipo mu Mawu. Timawafuna. Koma CHOFUNIKA KWAMBIRI ndi chiyani, kulalikira kapena Matepi?

Ngati Matepi sali chinthu chofunikira kwambiri mu moyo wanu waumuntu, mu moyo wa mpingo wanu, ndiye chinachake chalakwika. Inu mwachoka pa Chifuniro Chabwino cha Mulungu. BWELANI MU NJILA.

Pamene munthu akomana konse ndi Mulungu; osati mu ntchito zina zokhudza maganizo, ziphunzitso za chipembedzo cikhulupililo kapena ciphunziso zozilimbikitsa, koma akafika pa malo monga mmene Mose anacitila. Kumbuyo kwadesati, kuyenda maso ndi maso ndi Mulungu Wamphamvuzonse, ndipo iwe umawona Liwu likulankhula kwa iwe, kosapusana ndi Mawu ndi lonjezo la ntawi, pali chinachake chikuchita kwa iwe! Mwaona, inu simukuchita nawo manyazi Iwo, Iwo amachita chinachake kwa inu.

Masiku atu, chofimba chachikhalidwe chimenecho chang’ambika. Apa payima Lawi la Moto, likuwonetsera Mawu a tsiku lino. Umulungu aphimbidwa mu thupi la munthu. Ulemerero wa Shekinah wa lero. Mulungu ayima ndi kuyankhula pamaso pathu, aphimbidwa mu thupi la munthu.

Mose anali nawo Mawu. Tsopano kumbukirani, Mawu ana wonetseredwa, Mose anali Mose kachiwiri. Mwaona? Koma pamene Mawu amenewo anali mwa iye kuti aperekedwe, iye anali Mulungu; chabwino, iye sanali Mose panonso. Iye anali nawo Mawu a Ambuye a m’badwo umenewo.

Khrisimasi yomwe ife a Rebeka tidzakhala nayo Lamlungu lino. Tsiku lonse, nthawi zosiyanasiyana tsiku lonse. Tidzamva Eliezere wathu akuitana Mkwati wake ndipo tidzakhala tikumuuza kuti sitikuchita manyazi.

Ambuye akupatseni inu Khrisimasi yabwino, yodzazidwa ndi “KUKHALA KWAKE”.

Bro. Joseph Branham

Uthenga: 65-0711 Manyazi

Lemba: Marko 8:34-38