Category Archives: Uncategorized

25-0216 Sabata La Makumi Asanu Ndi Chiwiri La Daniele

Uthenga: 61-0806 Sabata La Makumi Asanu Ndi Chiwiri La Daniele

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Akuyang’anira Ndinso Akuyembekenzera,

Pali chisangalalo pakati pa Mkwatibwi kuposa kale. Tili pa kuyembekezera kwakukulu; Chaka chathu chachisangalalo chikukonzekera kuti chichitike. Mkwatibwi wayembekezera motalika kwambiri kuti tsiku ili lifike. Mapeto a nyengo ya m’badwo wa Amitundu yafika ndipo chiyambi cha muyaya ndi Ambuye wathu chiyamba posachedwapa.

Ife tikumvetsa nthawi yomwe tikukhalamo pa kumva Mawu. Nthawi yatha. Nthawi ya Mkwatulo yayandikira. Tafika. Mzimu Woyera wabwera ndi kuwulula kwa Mkwatibwi Wake zinthu zonse zazikulu, zakuya, zinthu za zinsisi.

Ife tiri mu kusimidwa, kufunafuna Mulungu; kudzikonzekeretsa tokha. Tataya zinthu zonse za dziko lino. Zosamalira za moyo uno sizitanthauza kanthu kwa ife. Chikhulupiriro chathu chafika patali kwambiri kuposa kale lonse. Mzimu Woyera ukumupatsa Dona Wake wosankhidwa Chikhulupiriro chokwatulitsa, kotero Iye akhoze kubwera ndi kumuchotsa Iye.

191 Masabata sikisite naini awa analondolera mwangwiro; kupita kwina kwa Ayuda kumalondolera mwangwiro; m’badwo wa mpingo umalondolera mwangwiro. Ife tiri pa mapeto a nthawi, nthawi yotsiriza, m’badwo wa mpingo wa Laodikaya, kutha kwa iwo. Atumiki nyenyezi onse alalikira uthenga wawo. Iwo wapita kunja. Ife tikungogubuduka.

Ndi nthawi yodabwitsa bwanji yomwe Ife tikukhalamo. Ndi nthawi yovuta kwambiri pamene m’dani akulimbana ndi aliyense kuposa kale. Iye akuponya zonse zimene ali nazo kwa ife. Iye ali mu kusimidwa, chifukwa akudziwa kuti nthawi yake yafika kumapeto.

Koma panthawi yomweyomweyo, Ife sitinakhalepo osangalala kwambiri mmiyoyo yathu.

• Sitinakhalepo pafupi ndi Ambuye.
• Mzimu Woyera amadzaza mum’tsempha uliwonse wa thupi lathu.
• Chikondi chathu pa Mau ake sichinakhale chokulirapo.
• Vumbulutso lathu la Mau ake limadzaza moyo wathu.
• Tikugonjetsa mdani aliyense ndi Mau.

NDIPO, sitinakhalepo otsimikiza kwambiri kuti ndife ndani:

• OKONZEDWERATU
• OSANKHIDWA
• OSANKHIDWA
• Mbewu Yachifumu
• OKOMA APA MTIMA
• AMUYAYA, IWO OVALA MWINJIRO WOYERA, MAYI JÉZU, OMVETSERA KU MATEPI, OWUNIKILIKIDWA, NAMWALI WOLANGIDWA, WODZAZIDWA NDI MZIMU, WOSAGONJETSEDWA, WOKHAZIKITSIDWA KWAUZIMU, WOSAIPITSIDWA, MKWATIBWI WA MAWU NAMWALI.

Mchiyani Chikubwera chotsatira ? Mwala ukubwera. Tikuyang’ana, kuyembekenzera ndi kupemphera mphindi iliyonse tsiku lililonse. Palibenso china chilichonse chovuta koma kudzikonzekeretsa tokha pa kubwera kwake.

Sikuti, “Tikuyembekeza choncho”, TIKUDZIWA. Kulibenso zokaikitsa zochuruka zina zilizonse. Mu M’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso kudzakhala kuti kwatha, ndipo tidzakhala kuti tili kumbali inayo ndi okondedwa athu onse ndi IYE pa Mgonero wathu wa Ukwati.

NDIPO ICHO NDI CHIYAMBI CHABE …NDIPO KULIBE MAPETO!!

Bwerani mudzakonzekere Mgonero wa Chikwati uwu nafe Lamlungu lino pa 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene Mulungu akuyankhula kupyolera mwa mngelo Wake wamphamvu, yemwe Iye anamutuma kuti adzatsogolere Mkwatibwi Wake, monga iye akuuzira, ndi kuwulula, zinsinsi zonse za Mulungu.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga: 61-0806 – Sabata La Makumi Asanu Ndi Awiri La Daniele

25-0209 Cholinga Chofutukuka Pasanu Ndi Kamodzi Cha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele

Uthenga: 61-0730E Cholinga Chofutukuka Pasanu Ndi Kamodzi Cha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wa kukondwera,

Tayang’ana nkhope zathu Kumwamba m’mapemphero ndi mapembedzero kuti tipeze tsiku ndi ola lomwe tikukhalamo.

Monga sizinachitikepo kale lonse, ife tikukhala pamodzi mu malo amwambamwamba, kuchokera kuzungulira dziko, kumva Mulungu akulankhula ndi kuwulula Mawu Ake kwa ife kupyolera mwa mngelo Wake wamphamvu wamthenga. Mngelo wapadziko lapansi wamthenga yemwe Atate anamutumiza kwa Mkwatibwi Wake mu tsiku lotsiriza ili kuti awulule Mawu Ake.

Gabrieli ndi mngelo wa anthu osankhidwa a Mulungu, Ayuda. Koma kwa Mkwatibwi Wake wa Amitundu, Melkizedeki Iyemwini anabwera ndipo anayankhula kupyolera mu thupi la munthu mwa mngelo wapadziko lapansi wotchedwa William Marrion Branham, kotero kuti Iye akhoze kulankhula ndi kuwulula Mawu Ake ONSE kwa Mkwatibwi Wake wokondedwa wapamtima.

Iye anali nalo ilo likujambulidwa, kusungidwa, ndi kusamaliridwa, kotero kuti Mkwatibwi akakhale ndi Chakudya Chake chauzimu, Manna obisika, mmanja mwawo miniti iliyonse ya tsiku lirilonse mpaka mapeto a nthawi.

Mkati mwathu ndimodzazidwa ndi kudzoza komweko pomwe tikunva Liwu la Mulungu kuwulula Mawu Ake kwa ife. Momwe Iye amavumbulutsira Mawu Ake kuti tithe kuwona bwino bwino ndi kumvetsetsa tanthauzo lake. Ilo likuwulula ola lomwe tikukhalamo, Limatiuza ife amene tiri ndi chimene chiti chichitike posachedwapa; Mkwatulo wathu ukubwera posachedwa.

Iye akuwululira kwa Mkwatibwi Wake zomwe ziti zichitike pano pa dziko lapansi pamene ife tiri naye Iye pa Mgonero wa Chikwati. Momwe Iye adzatsegula maso akhungu a osankhika ake; iwo amene Iye anawachititsa khungu chifukwa cha Mkwatibwi Wake wa Amitundu.

Abwenzi anga, ndikudziwa mmene tatopela ndi dziko lino ndipo tikulakalaka za kudza kwake kudzatichotsa, koma tiyeni tisangalale ndi kuyamikira zimene zikuchitika pakali pano pamaso pathu.

Tiyeni tikweze manja athu mmwamba, mitima yathu, mawu athu, ndi kukondwera. Osati kokha kuti tikuyembekezera zimene Iye ati atichitire posachedwapa, koma tiyeni tikondwere ndi zimene Iye akutiululira ndi kutichitira ife TSOPANO.

Iye akutiuza ife kuti ndife Mkwatibwi Wake wokonzedweratu akulumikizana limodzi ndi Iye ndi Mawu Ake. Iye akutitsimikizira mobwereza bwereza, ife tiri mu Chifuniro Chake changwiro pokhala ndi Liwu Lake, Mawu Ake, mngelo Wake. Iye Watipatsa ife CHIKHULUPIRIRO chodziwa ndi kuzindikira cha chomwe Ife tiri:
MAWU AKE OKHALA MTHUPI.

Tilibe kanthu koti tizikawopa; tilibe kanthu koti tizidandaula nako; tilibe kanthu koti kazitikwiyitsa. Kodi ndikudziwa bwanji zimenezo? MULUNGU ANANENA CHOMWECHO! CHONCHO TIYENI TIKONDWERE, KHALANI OSANGALALA, KHALANI OYAMIKILA; MAWU AMOYO AMAKHAKHALA NDI KUKHALA PAKATI PATHU. NDIFE MBEWU YAKE YAPAMWAMBA YAUFUMU.

Ine Zoonadi Ndikukhulupirira kuti Ambuye akuyeneranso kukhala wokondwa kudziwa kuti nthawi yafika ndipo tadzikonzekeretsa tokha pokhala wowona ndi mokhulupirika ku Mawu Ake.

Monga mnyamata wamng’ono yemwe anayang’ana pa kalilole kwa nthawi yake yoyamba, ife tikuyang’ana mu Mawu Ake, kuwona yemwe ife TILI. Ambuye…NDI INE. Ine ndine Mkwatibwi wa Mawu Anu amoyo. Ine Ndine amene munasankha. Ine ndiri mwa Inu, Inu muli mwa ine, ndife amodzi.

Kodi Ife sutingakondwerere bwanji ndi kukhala anthu osangalala kwambiri amene anakhalapo padziko lapansi? Oyera ndi aneneri onse tisanakhalepo ife ankafuna kukhala mu tsiku lino ndi kuwona malonjezo awa akukwanilitsidwa. Koma mwa CHISOMO cha Mulungu, Iye anatiika IFE kuno.

Sitingadikire:

Uuu, mai! [M’bale Branham akuwombetsa manja ake—Mkonzi.] Psyuu! Mwa kuyankhula kwina, pamene mdani akhala atachotsedwa, mapeto a tchimo abwera, kubweretsamo kwa chilungamo chosatha kutabwera, Satana akusindikizidwira mu dzenje lopandamalire, ndipo chidziwitso cha Ambuye chidzaphimba dziko lapansi monga madzi aphimbira nyanja. Ameni! Ulemerero kwa Mulungu! Izo zikubwera, m’bale, izo zikubwera!

Kodi ndi Kudzoza kotani kumene kudzakhala kukuchitika Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, pamene ife tidzasonkhana palimodzi kuchokera kuzungulira dziko kuti tidzamve mngelo wa Mulungu, Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi, kutibweretsera ife Uthenga: Cholinga Chofutukuka Pasanu ndi Kamodzi Cha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele 61-0730E.

M’bale. Joseph Branham

25-0202 Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele

Uthenga: 61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Osankhidwa,

Ndi nthawi ya dzinja yabwino bwanji yomwe takhala tili nayo tikamaphunzira mibadwo isanu ndi iwiri ya mipingo, kenako Mulungu akuululanso zochuluka kwa ife mu Bukhu la Chibvumbulutso cha Yesu Khristu. Momwe machaputala atatu oyamba a Chibvumbulutso anali mibadwo ya mpingo, kenako momwe Yohane adatengedwera kunka ku mwamba mmutu wa 4 ndi 5 ndikutisonyeza zinthu zomwe zinali mkudza.

Mu mutu wa 6., Iye anaulula momwe Yohane adatsikira dziko lapansi kuti aone zinthu zomwe zikuchitika kuchokera ku mutu wa 6. Kuyambira mutu 19 wa buku la Chivumbulutso.

Mkwatibwi adzakhala wodalitsika bwanji Lamlungu pamene tikumva Liwu la Mulungu likulankhula kudzera mwa mngelo wake Wamphamvu wachisanu ndi chiwiri akutiuza ife chomwe chiti chiwululidwe patsogolo.

Ndine wokondwa kwambiri kunena kuti tsopano tiyamba kuphunzira kwakukulu masabata makumi asanu ndi awiri a Daniel. Mneneri ananena kuti icho chimangilira uthenga wonse tisanapite mu Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri; Malipenga 7; Matsoka atatu; mkazi wovala dzuwa; kutulutsa a m’dierekezi wofiira; handiredi ndi forte-foro sauzande atasindikizidwa apo ; Zonse zikuchitika pakati pa nthawi ino.

Buku la Danieli ndi ndendende kalendala ya m’badwo ndi nthawi yomwe tikukhalamo ino, ndipo chingawoneke chovuta bwanji, Mulungu adzachiswa icho ndikuchipanga icho kukhala chophweka kwa ife.

Ndipo Mulungu akudziwa kuti ndizomwe ndikufuna tsopano, kuti nditonthoze anthu ake ndikuwauza chomwe chili pafupi, Onse a iwo m’mawa uno ndipo kudutsa ku mayiko omwe matepi awa adzapita, Pa dziko lonse lapansi, kuti tili kumapeto a nthawi.

Ndife anthu osankhidwa a Mulungu omwe akukhumba ndi kupempherera tsikulo ndi Ola limenelo. Ndipo maso athu akuyang’anila kumwamba, ndipo tikuyembekezera Iye kudza Kwake.

Tiyeni tonse tikhale ngati Danieli ndikuyang’ana nkhope zathu kumwamba, popemphera ndi mapembedzero, monga tikudziwa pa kuwerenga mawu ndi kumva Liwu lake, Kubwera kwa Ambuye kukuyandikira msanga; Tili kumapeto.

Tithandizeni Atate kuika cholemera chilichonse kumbali, tchimo lililonse, kusakhulupirira kwakung’ono kulikonse komwe kungatibwezere ife mmbuyo. Tsopano tiyeni tikambirane za mayitanidwe apamwamba, podziwa kuti nthawi yathu ndi yochepa.

Uthengawu Wapita kulinkonse. Chilichonse chakonzeka tsopano; Tikuyembekezera ndi kupuma. Mpingo wasindikizidwa. Oipa akuchita zoipa kwambiri. Mipingo ikukhala mpingo wokhuthala, koma oyera anu akubwera pafupi ndi inu.

Tili ndi Liwu likufuula m’chipululu, likuitana anthu kubwerera ku uthenga wa pachiyambi; Kubwerera ku zinthu za Mulungu. Timamvetsetsa mwa vumbulutso izi zinthu zomwe zikuchitika.

Bwerani mudzalumikizane nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00PM nthawi ya ku Jeffersonville , pomwe Mulungu akuwululira Mawu Ake kwa ife, pamene tikuyamba kuphunzira kwakukulu za buku la Danieli.

M’bale. Joseph Branham

61-0730M – Malangizo a Gabriel kwa Daniel

25-0126 Chibvumbulutso, Mutu Faivi Gawo II

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Akupumula,

Ili ndilo Dzinja labwino kwambiri m’miyoyo yathu. Kudza kwa Ambuye kuli pafupi kumene. Ife tasindikizidwa ndi Mzimu Woyera; Chisindikizo cha Mulungu cha chivomerezo chakuti zonse zimene Kristu anafera ndi zathu.

Ife tsopano tiri ndi chikole cha cholowa chathu, Mzimu Woyera. Icho ndi Ndichitsimikizo, malipiro ochepera, kuti talandiridwa mwa Khristu. Ife tikupumula mu malonjezo a Mulungu, tikugona mu kutentha kwa Dzuwa Lake lowala; Mawu Ake otsimikiziridwa, kumvetsera ku Liwu Lake.

Ndicho chikole cha chipulumutso chathu. Ife Sitikudandaula ngati tipita Kumeneko kapena ayi, IFE TIKUPITA! Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Mulungu ananena chomwecho! Mulungu analonjeza ndipo ife tiri nacho chikole. Ife talandira kale Icho ndipo Khristu watilandira ife.

Palibe njira yothawira kwa Izo…m’malo mwake, tiri kumeneko! Zomwe tiyenera kuchita ndikungodikira; Iye ali pansi akuchita Chiwombolo Chachibale pakali pano. Ife tiri nacho chikole chake pakali pano. Ife tikungoyembekezera nthawi imene Iye abwereso Kwa Ife. Kenako, m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso tonse tidzapita ku Phwando la Ukwati.

Kungoganizira zonse zimene zili pa tsogolo pa ife. Malingaliro athu sangatengere zonse mkati. Tsiku ndi tsiku Iye akuwulula zambiri za Mawu Ake, kutsimikizira kuti malonjezo aakulu awa ndi athu.

Dziko likugwa; moto, zivomezi, ndi chipwirikiti kulikonse, koma amakhulupirira kuti ali ndi mpulumutsi watsopano amene adzapulumutsa dziko lapansi, ndikubweretsa m’badwo wawo wagolide. Talandira kale Mpulumutsi wathu ndipo takhala tikukhala mu nyengo yathu ya M’badwo wa Golide.

Tsopano Iye akutikonzekeretsa ife ku Chibvumbulutso chochuluka pamene ife tikulowa mu mutu wa Fayifi wa Chivumbulutso. Iye akukhazikitsa chochitika apa cha kutsegula kwa Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri. Monga momwe iye anachitira mu mutu 1 wa Chivumbulutso, kutsegula njira ya Mibadwo Isanu ndi iwiri ya Mpingo.

Kodi zina zonse za Dzinja zidzakhala bwanji kwa Mkwatibwi? Tiyeni tiwone mwachidule:

Tsopano, ndilibe nthawi. Ine Ndazilemba izo pano. nkhani ina pa izo apa, koma msonkhano wathu wotsatira ife tisanalowe mu izi mwinamwake pamene ine ndidzachoka kutchuthi changa kapena nthawi ina, ine ndikufuna kuti nditenge masabata makumi asanu ndi awiri awa a Daniele ndi kumangiriza izo mkati momwe muno, ndi kuzisonyeza izo pamene izo zitengera izo ku chisangalalo cha Chipentekoste, ndi kuzibweretsa izo m’mbuyo kumene ndi miliri isanu ndi awiri iyo Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri kuti zitsegulidwe pano ife tisanapite, ndi kusonyeza kuti izo ziri pa mapeto, izi…

Ndi nthawi yodabwitsa bwanji yomwe Ambuye wasungira Mkwatibwi Wake. Kudzivumbulutsa Yekha mu Mawu Ake kwa ife kuposa kale. Kutilimbikitsa kuti ndife osankhidwa ake amene Iye akuwadzera. Kutiuza ife kuti tiri mu chifuniro Chake Changwiro pakukhala ndi Liwu Lake, ndi Mawu Ake.

Kodi tikuchita chiyani? Osati chinthu chimodzi, Kungopumula! Kudikirira! Palibenso ntchito zolemetsa, palibenso zokhumudwitsa, TIKUPUMULA PA IZO!

Bwerani mudzapumule nafe Lamlungu lino pa 12:00 p.m., nthawi ya mu Jeffersonville, pamene ife tikumva Liwu la Mulungu LOTSIMIKIZILIDWA likutibweretsera ife Uthenga:
61-0618 – “Chivumbulutso, Mutu Fayifi Gawo II”.

M’bale. Joseph Branham

25-0112 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo III

Uthenga: 61-0108 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo III

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Akumuyaya,

Ndi nthawi yoti tivule chovala chathu chankhondo ndi kuvala kuganiza kwanu kwa uzimu, chifukwa Mulungu akukonzekera kuti amupatse Mkwatibwi Wake Vumbulutso lochuluka la Mawu Ake.

Iye adzakhala akuvumbulutsa kwa ife zinsinsi zonse zakale. Iye adzatiuza zimene zidzachitike m’tsogolo. Zomwe ena onse m’Baibulo adangowona kapena kumva, Iye adzawulula tsatanetsatane wa chilichonse chaching’ono cha Mawu Ake ndi tanthauzo lake kwa ife.

Tidzamva ndi kumvetsa tanthauzo la zizindikiro za m’Baibulo: Zolengedwa Zamoyo, Nyanja Yagalasi, Mkango, Mwana wa Ng’ombe, Munthu, Mphungu, Mpando Wachifundo, Alonda, Akuluakulu, Ma liwu, Chirombo Chakuthengo Chosawetedwa, Zorengedwa za Moyo.

Tidzamva ndikumvetsetsa zonse za alonda a Chipangano Chakale. Yuda: Mlonda wa Kum’maŵa; Efraimu: Mlonda Wa Kumadzulo; Rueben: Mlonda waku Mmwela; ndi Dani: Mlonda wa Kumpoto.

Palibe chimene chikanakhoza kubwera paliponse mozungulira mpando wachifundo umenewo popanda kuwoloka mafuko amenewo. Mkango, luntha la munthu; Ng’ombe: kavalo wantchito; Mphungu: Kuthamanga kwake.

Momwe Kumwamba, dziko lapansi, pakati, ndi pozungulira, iwo anali alonda. Ndipo pamwamba pake panali Lawi la Moto. Palibe chinakhudza mpando wachifundo uwo popanda kudutsa mafuko amenewo.

Tsopano pali alonda a Chipangano Chatsopano: Mateyu, Marko, Luka ndi Yohane, kupita molunjika patsogolo. Chipata chakum’maŵa chimayang’aniridwa ndi mkango, chipata chakumpoto chimayang’aniridwa ndi chiwombankhanga chowuluka, Yohane, m’vangeri. Ndiye sing’anga wa mbali iyi, Luka, munthuyo.

Mauthenga anai a Uthenga Wabwino amateteza Madalitso a Chipentekoste ndi Lemba lirilonse kukhalira khonde ndendende zomwe iwo ananena. Ndipo tsopano Machitidwe a atumwi akuwonetsera lero ndi Mauthenga anai kuti Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi nthawizonse.

Pamene wodzozedwa woona wa Mulungu ayankhula, Ilo ndi Liwu la Mulungu! Ife tikungofuna kufuula, “Woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye!”

Palibe basi njira yopitira kutali kwa Icho. Ndipotu, ife sitingathe kuchoka kwa Icho, chifukwa Icho sichingatichokere kwa ife. Ndife odindidwa chisindikizo mpaka tsiku la chiombolo chathu. Palibe mtsogolo, palibe kalikonse, zowopsa, njala, ludzu, imfa, kapena CHINTHU, chimene chingatilekanitse ife ku chikondi cha Mulungu chimene chiri mwa Khristu Yesu.

Asanaikidwe maziko a dziko maina athu anayikidwa pa Bukhu la Moyo wa Mwanawankhosa kuti tiwone Kuwala UKU, kulandira Liwu Ili, kukhulupirira Uthenga Uwu, kulandira Mzimu Woyera wa tsiku lathu ndi kuyenda mwa Iwo. Pamene Mwanawankhosa anaphedwa, MAYINA ATHU anayikidwa pa Bukhu pa nthawi yomweyo Dzina la Mwanawankhosa linayikidwa pamenepo. ULEMERERO!!

Kotero, palibe chimene chingatilekanitse ife ku Uthenga uwu. Palibe chimene chingatilekanitse ife ku Liwu limenelo. Palibe chimene chingatenge Vumbulutso la Mawu Awa kwa ife. Ndi zathu. Mulungu anatiyitana ife ndipo anatisankha ife ndipo anatikonzeratu ife. Zonse ndi za Ife, Ndi zathu.

Pali njira imodzi yokha yopezera zonsezi. Inu Mukuyenera kutsukidwa ndi madzi a Mau. Inu mukuyenera kumva Mawu inu musanalowe mmenemo. Ndipo pali njira imodzi yokha imene inu mungafikire kwa Mulungu, ndiyo mwa Chikhulupiriro. Ndipo Chikhulupiriro chimadza pakumva, kumva Mawu a Mulungu, amene akunyezimiritsidwa kuchokera ku Malo Opatulikitsa kupita kwa mthenga wa m’badwowo.

Kotero, apa, mngelo wa m’badwo wa mpingo akunyezimira m’madzi awo Yemwe Munthu uyu ali muno, akunyezimiritsa chifundo Chake, Mawu Ake, chiweruzo Chake, Dzina Lake. Zonse zikuwonetseredwa muno pamene inu mumalekanitsidwa ndi kuzikhulupirira Izo. Kodi mukumvetsa?

Musati musiye kumvetsera kwa matepi, ingokhalani nawo Iwo. Fufuzani Izo ndi Mawu ndi kuwona ngati Izo ziri zolondola. Ndiyo Njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero.

Bwerani mudzakhale nafe Dzinja ili pamene tikulumikizana pamodzi kuchokera ku dziko lonse lapansi ndikumva Liwu la Mulungu likuwululira Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake kuposa kale. Palibe kudzoza kwakukulu kuposa kukanikiza kusewera ndi kumvetsera ku Liwu Lake.

Kuchokera pansi pamtima, nditha kunena kuti: Ndine wokondwa kunena kuti ndine Mmodzi wa Iwo ndi aliyense wa inu.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga: 61-0108 – “Chivumbulutso, Mutu Foro Gawo III”
Nthawi: 12:00 PM. Jeffersonville nthawi

24-1229 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo I

Uthenga: 60-1231 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo I

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Oyera Ovala Mwinjiro Woyera,

Tikamamva Liwu la Mulungu likuyankhula nafe, chinachake chimachitika mkati mwa moyo wathu.  Thupi lathu lonse limasinthidwa ndipo dziko lotizungulira likuwoneka kuti likutha. 

Kodi munthu angakhoze bwanji kufotokoza zomwe zikuchitika mu mitima yathu, malingaliro athu, ndi moyo wathu, pamene Liwu la Mulungu livundukula Mawu Ake ndi Uthenga uliwonse umene timamva?

Monga mneneri wathu, timamva kuti takwatulidwira kumwamba kwachitatu ndipo mzimu wathu ukuwoneka kuti ukuchoka mu thupi lachivundi ili. Palibe mawu ofotokozera zomwe timamva pamene Mulungu akutiululira Mawu ake kuposa kale. 

Yohane anaikidwa pa chisumbu cha Patmo ndipo anapemphedwa kuti alembe zimene anaona ndi kuziika mu bukhu lotchedwa Chivumbulutso, kotero izo zikanadzapita kupyola mu mibadwo. Zinsinsi zimenezo zakhala zobisika mpaka zidaululidwa kwa ife kupyolera mwa mthenga Wake wosankhidwa wa 7.  

Ndiye Yohane anamva Liwu lomwelo pamwamba pa iye ndipo anakwatulidwira kumwamba kwachitatu. Liwu lija linamuwonetsa iye mibadwo ya mpingo, kudza kwa Ayuda, kutsanulidwa kwa miliri, Mkwatulo, Kudza kachiwiri, Zakachikwi, ndi Kwawo Kwamuyaya kwa opulumutsidwa Ake. Iye anamutengera iye mmwamba ndipo anabwereza chinthu chonsecho kwa Yohane monga Iye anati Iye akanadzachita. 

Koma kodi Yohane anaona ndani pamene anaona kubwerezako? Palibe amene amadziwa mpaka lero.  

Chinthu choyamba chimene anaona pakubwera chinali Mose. Iye anaimira oyera mtima akufa amene adzaukitsidwa; mibadwo isanu ndi umodzi yonse yomwe inagona.
Koma si Mose yekha amene anaima pamenepo, komanso Eliya anali pamenepo. 

Kodi Eliya amene anali kuyima anali ndani? 

Koma Eliya anali kumeneko; m’thenga wa tsiku lotsiriza, ndi gulu lake, la osandulika, okwatulidwa.

ULEMELERO…HALELUYA…Kodi Yohane adamuwona atayimapo ndani? 

Osati wina koma mthenga wa mngelo wa 7 wa Mulungu, William Marrion Branham, ndi GULU LAKE LA OSANDULIKA, OKWATULIDWA… ALIYENSE WA IFE!!

Eliya ankayimira oyeramtima akufa…Ine ndikutanthauza Mose, ndi kuwukitsidwa. Eliya ankayimira gulu losandulika. Kumbukirani, Mose anali woyamba, ndipo kenako Eliya. Eliya anali woti adzakhale mthenga wa tsiku lotsiriza, kuti ndi iye ndi gulu lake kukanadzabwera chiwukitsiro…kukanadzabwera…chabwino, ukanadzabwera Mkwatulo, ine ndikutanthauza. Mose anabweretsa chiwukitsiro ndipo Eliya anabweretsa gulu Lokwatulidwa. Ndipo, pamenepo, onse a iwo anayimiriridwa pomwepo.

Lankhulani za kuvundukula, kuwulula, ndi Chivumbulutso. 

Apa Iwo uli! Ife tiri nawo Iwo kumene ndi ife tsopano, Mzimu Woyera, Yesu Khristu, yemweyo dzulo, lero, ndi nthawizonse. Ndinu…Iwo ukulalikira kwa inu, Iwo ukukuphunzitsani inu, Iwo ukuyesera kuti ukufikitseni inu kuti muwone chimene chiri cholondola ndi cholakwika. Ndi Mzimu Woyera Mwiniwake ukuyankhula kupyolera mu milomo ya munthu, ukugwira ntchito pakati pa anthu, kuyesa kusonyeza chifundo ndi chisomo.

Ndife Oyera Ovala Mwinjiro Woyera amene mngelo wake anawaona akuchokera ku dziko lonse lapansi kudzadya Mkate wa Moyo. Tili pa kutomeledwa ndipo wokwatitsidwa ndi Iye ndipo tamva kupsompsona kwa Iye kwa chikwati mu mtima mwathu. Ife tinadzilonjeza tokha kwa Iye, ndi ku Liwu Lake lokha. Tilibe, ndipo sitidzadzidetsa ndi mawu ena aliwonse.

Mkwatibwi akukonzekera kukwera mmwamba monga Yohane anachitira; mu Kukhalapo kwa Mulungu. Tidzakwatulidwa pa Mkwatulo wa Mpingo. Momwe izo zimangozungulira moyo wathu! 

Kodi Iye atiululira chiyani motsatira? 

Ziweruzo; mwala wa sardine, ndi chimene umaimira; idachita gawo lotani. Yaspi, ndi miyala yonse yosiyana. Iye adzazitenga zonse izi mmusi kupyola mu Ezekieli, kubwerera ku Genesis, kubwerera ku Chivumbulutso, kubwera mmusi pakati pa Baibulo, kuzimangiriza izo palimodzi; miyala yonseyi ndi mitundu yosiyanasiyana.

Ndi Mzimu Woyera womwewo, Mulungu yemweyo, kusonyeza zizindikiro zomwezo, zodabwitsa zomwezo, kuchita chinthu chomwecho basi monga Iye analonjezera. Ndi Mkwatibwi wa Yesu Khristu akudzikonzekeretsa Yekha pakumva Liwu Lake.

Ife tikukulandirani inu kuti mulumikizane nafe pamene ife tikulowa mu malo ammwambamwamba pa 12:00 p.M., nthawi ya Jeffersonville, kuti tidzamve Eliya, mthenga wa Mulungu mu m’badwo wotsiriza uno, akuwulula zinsinsi zimene zakhala zobisika mu mibadwo yonse.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga:  60-1231 Chivumbulutso,Mutu Foro Gawo I 

Chonde kumbukirani Uthenga wathu wa Chaka Chatsopano, Lachiwiri usiku: Mpikisano 62-1231. Palibe njira yabwinoko yoyambira Chaka Chatsopano.

24-1222 Mphatso Yokulungidwa ya Mulungu

Uthenga: 60-1225 Mphatso Yokulungidwa ya Mulungu

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkazi Wa JEZU,

O Mwanawankhosa wa Mulungu, Inu ndinu Mphatso yayikulu yokulungidwa ya Mulungu ku dziko. Inu mwatipatsa ife Mphatso yaikulu kwambiri imene inayamba yaperekedwapo, Inu eni. Inu musanalenge nyenyezi yoyamba, Inu musanalenge dziko lapansi, mwezi, mphavu ya dzuwa, Inu munatidziwa ife ndi kutisankha ife kukhala mkwatibwi wanu

Pamene Inu munatiwona ife pamenepo, Inu munatikonda ife. Ife tinali mnofu wa mnofu Wanu, fupa la fupa Lanu; ife tinali gawo la Inu. Momwe Inu munatikondera ife ndi kufuna kuyanjana nafe. Munafuna kugawana nafe Moyo Wanu Wamuyaya. Kenako Tidadziwa pamenepo, tidzakhala Anu m’kazi wa JEZU.

Inu munawona kuti ife tidzalephera, kotero Inu munayenera kutipatsa njira yotibwezeretsa ife . Tinali otayika komanso opanda chiyembekezo. Panali njira imodzi yokha, Munayenera kukhala “Chilengedwe Chatsopano”. Mulungu ndi munthu anayenera kukhala Mmodzi. Inu munayenera kuti mukhale ife, kuti ife tikhoze kukhala Inu. Chotero, Inu munaika dongosolo lanu lalikulu zaka zikwi zapitazo m’munda wa Edeni.

Inu mwakhala olakalaka kwambiri kukhala nafe, Mkwatibwi Wanu wangwiro wa Mawu, koma Inu munadziwa poyamba kuti Inu munayenera kutibwezeretsa ife ku zonse zomwe zinatayika pachiyambi. Munadikirira ndikudikirira ndi kudikirira mpaka kufikila tsiku lino kuti mumalize dongosolo Lanu.

Tsiku lafika. Kagulu kakang’ono kamene mudakawona pachiyambi kali pano. Wokondedwa wanu yemwe amakukondani Inu ndi Mawu Anu kuposa china chilichonse.

Inali nthawi yoti Inu mubwere ndi kudziulula Nokha mu thupi la umunthu monga Inu munachitira ndi Abrahamu, ndipo monga Inu munachitira pamene Inu munakhala Chirengedwe chatsopano. Momwe Inu munali kufunitsitsa za tsiku lino kotero kuti Inu mukhoze kuwulula kwa ife zinsinsi Zanu zonse zazikulu zimene zinali zobisika kuchokera ku maziko a dziko.

Inu mumanyadira kwambiri Mkwatibwi Wanu. Momwe Inu mumakondera kumuwonetsera Iye ndi kumuuza Satana, “Ziribe kanthu zomwe iwe ungayese kuchita kwa iwo, iwo sadzasuntha; iwo sadzanyengerera pa Mawu Anga, Liwu Langa. Iwo ali MKWATIBWI WANGA WA MAWU Angwiro.” Iwo ndi okongola kwambiri kwa Ine. Tangoyang’anani pa iwo! Kupyolera mu mayeso awo onse ndi mayesero, iwo amakhala okhulupirika ku Mawu Anga. ndidzawapatsa mphatso yosatha. Zonse zomwe ndili, ndipereka kwa iwo. TIDZAKHALA AMODZI.

Zonse Zomwe tinganene n’zakuti: “JEZU, TIMAKUKONDANI. Tiloleni ife tikulandireni Inu munyumba mwathu. Tiloleni ife tikudzozeni Inu ndi kusambitsani mapazi anu ndi misozi yathu ndi kuwapsyopsyona iwo. Tifuna Tikuuzeni momwe timakukonderani Inu.”

Zonse zomwe ife tili, tikupereka kwa Inu JEZU. Imeneyo ndiyo mphatso yathu kwa Inu JEZU. Timakukondani. Timakukondani Inu. Ife tikukupembedzani Inu.

Ine ndikukuitanani aliyense wa inu kuti adzakhale nafe Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, ndi kumulandira JEZU munyumba mwanu, mu mpingo wanu, mu galimoto yanu, kulikonse kumene inu mungakhale, ndi kulandira Mphatso yaikulu kwambiri imene inayamba yapatsidwapo kwa munthu; Mulungu Mwiniwake akuyankhula ndi kuyanjana ndi inu.

M’bale. Joseph Branham

60-1225 Mphatso Yokulungidwa ya Mulungu

CHIDZIWITSO CHAPADERA

Wokondedwa Mkwatibwi,

Ambuye wayika pamtima wanga kukhala ndi Uthenga Wapadera ndi Utumiki wa Mgonero pa Madzulo a Chaka Chatsopano kachiwiri chaka chino. Ndi chinthu chachikulu chiti chimene tingachite, abwenzi, kuposa kumva Liwu la Mulungu likulankhula kwa ife, kutenga nawo mbali pa Mgonero wa Ambuye, ndi kuperekanso miyoyo yathu ku utumiki Wake pa kulowa mu m’Chaka Chatsopano. Idzakhala nthawi yopatulika bwanji kutsekera dziko kunja, ndi kulumikizana ndi Mkwatibwi pa kusonkhana kwapadera kumeneku mu Mawu, pamene tikunena kuchokera mu mitima yathu, “Ambuye, tikhululukireni ife zolakwa zathu zonse zomwe takhala tikuchita chaka chonse; tsopano tikuyandikira kwa Inu, ndikufunsani ngati mudzatigwira dzanja ndi kutitsogolera chaka chomwe chikubwerachi. Mulole ife tikutumikireni Inu kuposa kale lonse, ndipo ngati icho chiri mu Chifuniro Chanu Chaumulungu, mulole icho chikhale chaka cha Mkwatulo waukulu umene uti uchitike. Ambuye, ife tikungofuna kuti tipite Kwathu kukakhala ndi Inu mu Muyaya.” Ine Sindili onyalanyaza kudikira kusonkhana mozungulira Mpando wachifumu Wake ku msonkhano wapadera wodziperekanso uwu, alemekezeke Yehova.

Kwa okhulupilira okhala mu dera la Jeffersonville, Ine ndikufuna kudzayamba tepi nthawi ya 7:00 pm pa nthawi ya kwathu kuno. Uthenga wonse ndi Mgonero udzakhala pa Wailesi ya Liwu panthawiyo, monga tinachitira m’mbuyomu. Tidzakhala ndi mapaketi a vinyo a Mgonero omwe adzapezeke Lachitatu, pa Disembala 18, kuyambira 1:00 – 5:00 pm, kuti mudzawatengere ku nyumba ya YFYC.

Kwa inu amene mumakhala kunja kwa dera la Jeffersonville, chonde khalani ndi chiyanjano chapadera chimenechi panthawi yomwe ndi yabwino kwa inu kwanuko. Tidzakhala nayo linki yotengera Uthenga ndi Chiyanjano cha Mgonero posachedwapa.

Pamene tikuyandikira Tchuthi cha Khrisimasi, ndikufuna ndikufunireni inu ndi banja lanu Nyengo ya Tchuthi YABWINO NDI YOTETEZEKA, ndi Khrisimasi yabwino, yodzaza ndi chisangalalo cha Ambuye Yesu woukitsidwayo… LIWU.

Mulungu akudalitseni,

M’bale Joseph

Gwero: https://branhamtabernacle.org/en/bt/F6/110067