23-0312 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko

Uthenga: 64-0802 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwati Wapadziko Lapansi,

Malaki 4 ndi Mawu a Mulungu, ndipo Iwo abala a mtundu wake, IFE, Mkwati Wake. Ndi Mzimu Woyera, Umunthu wa Yesu Khristu, ukugwira ntchito, wokhazikitsidwa mu mitima yathu. Ife timafulumizitsidwa ku Mawu ONSE amene Iye analankhula, pakuti “Nkhosa Zanga zimamva Liwu Langa; mlendo sizimamtsata.”

Mwezi yapita aya yakhala yabwino making, kukonka mneneri mu Jeffersonville. Mulungu wakhala akulankhula kupyolera mwa mngelo Wake wamphamvu ndi kutidyetsa ife ndi Chakudya Chake chosungika kuchokera mu KOLOWE LAKE LIMODZI m’dziko lonselo. Iwo ndi Mana Obisika, niya Mkwati Wake basi.

Ndi Uthenga uliwonse umene timamva, timayanjana ndi kusangalala wina ndi mzake; “Ndikudziwa kuti ndamva Mauthenga awa nthawi zambiri m’mbuyomo, koma SINANDINAYAMBE kumva monga tsopano”. Nizoona ndi kasupe wa Madzi amoyo akutumphukira mkati mwathu. Sitingathe kudziletsa. Ndizo zonse zomwe tikufuna kukambirana. Sitinakhalepo otsimikiza m’miyeo yathu, kuti ndife ndani komanso komwe tikupita.

Palibenso kudabwa:
“Sindikudziwa basi. Ndachita zinthu zambiri zoipa m’moyo wanga. Ndamulephera Ambuye nthawi zambiri. Zikuoneka kuti ndalakwitsa nthawi zonse. ”

Palibenso chiyembekezo:
“Ndikukhulupirira kuti ndine mwana wa Mulungu. NDIKUFUNA kukhala. Ndikupemphera kuti ndine.”

Masiku amenewo ZONSE ZATHA. Tsopano TIKUDZIWA. Ulemerero kwa Mulungu!!

Kodi tikudziwa bwanji? Mulungu wakhala akuyankhula molunjika kwa ife mwa Liwu Lake pa matepi, kutiuza ife mobwereza bwereza, “Ine ndiri mwa inu, inu muli mwa Ine. Ndife AMODZI. Ndinakusankhani inu asanaikidwe maziko a dziko. Inu ndinu mnofu wa mnofu wanga, fupa la Fupa Langa.”

Ndi Uthenga wabwino umene Mulungu analankhula kwa ife Lamlungu kutiuza zonse za mmene dziko limene tikukhalamo siliri lathu, ndi Edeni wa Satana. Momwe iye anamunyenga Eva pachiyambi kuti amufunse ndi kukayika MAWU AMAMODZI. Iye anavula Chophimba Choyera cha Mulungu, ndipo anavala chophimba cha chidziwitso, ndiye maso ake anatseguka ndipo iye anadziwa kuti iye anali wosavala.

Satana anapotoza Mawu apachiyambi, ndipo tsopano wachititsa iye khunkala osaona kuti iye akali wosavala ndipo sakudziwa izo. Iye wakhala mfumukazi ya Satana ndipo dziko lapansili ndi ufumu wake wa Edeni.

Lamlungu, Mkwati wathu wa Kumwamba akufuna kukumbutsa Mkwati Wake wapadziko lapansi kumene Nyumba Yathu Yamtsogolo ili ndi momwe Idzakhalire. “Wokondedwa wokondedwa, tsopano popeza ndakuwuzani zonse za dziko lino ndi momwe liri Edeni wa Satana, ndikufuna ndikuuzeni ANSO za Kwanu Kwamtsogolo ndi Ine.

Ndikufuna ndikuuzeni mwabili vonse. Ndikudziwa kuti mwandimvapo Ine ndikukuuzani za Izo nthawi zambiri, koma yembekezani, nthawi ino zikhala ngati simunanmvepo Ine ndikukuuzani kale.

Ndikufuna kulowa mwatsatanetsatane. Ndikufuna kukuululirani kuti muli mu Chifuniro changa chanbwino pakukhala ndi Mawu Anga ndi mneneri Wanga. Ndikufuna kukupatsani choyimira cha zomwe mukuchita lero ngati mtundu wangwiro wa Mzinda watsopano womwe mudzakhalamo.

Ife ndithudi tilowa mu chinachake. Ine ndikhala ndikugwetsera inu kenakake kakang’ono; Ndikudziwa kuti mudzachigwira Icho. Inu mudzakhala mu Mzinda umenewo ndi Ine. Mneneri wanga adzakhala pafupi ndi inu. adzakhala mnansi wako. Inu mudzayenda m’misewu ya golide iyo ndi kumwa kuchokera ku Kasupe Wanga. Inu mudzakhala mukuyenda kulowa m’paradaiso wa Mulungu, ndi Angelo akugwedezeka ndi kuyimba nyimbo za fuko.

Inu mudzakhala ngale mu korona wa mneneri Wanga. Mudzapambana Chilichonse cha m’dziko Patsiku limenelo. Pali zambiri zomwe ndikufuna kukuwululirani Lamlungu. Ndi tsiku losangalatsa maningi lomwe tidzakhala limodzi”.

Ali ndi zambiri zotisungira masabata angapo akubwerawa, ngati sabwera kudzatitenga nthawiyo isanafike. Sabata ndi sabata, kutiuza ife, yemwe ife tiri, kumene ife tikupita, momwe Izo ziti zidzakhalire Kumeneko. Adzakhala akutitsogolera ku sabata laulemerero la Isitala lomwe takhala nalo, lodzaza ndi china chilichonse koma kumutamanda ndi kupempeza iye.

Ndi nthawi yosangalatsa eyi. Tikuwona uneneri ukukwaniritsidwa pamaso pathu. Ife tikuwona Mawu akuwonetseredwa MWA IFE. Kubwera Kwake kukhoza kukhala nthawi iliyonse. Tiyimirira pakhomo ndi maluwa m’manja mwathu. Timamva mahatchi akuthamanga komanso mchenga ukugwedezeka pansi pa mawilo.

Bokosi lakale liyimitsidwa posachedwa kwambiri. Tidzalumpa mu chitseko cha thupi lakale ili ndikuwulukira mmanja mwake. Iye adzatiyang’ana ife ndi kunena, “Zonse zatha tsopano, wokondedwa, ine ndikutengerani inu tsopano Kwanu Kutsogolo Kwanu.”

Mukuitanidwa kukhala nawo m’masiku opambana kwambiri amene dziko silinaonepo. Mphungu zidzakhala zikusonkhana kuchokera kozungulira dziko kuti zimve Liwu la Mulungu likulankhula kwa Mkwati Wake ndi kumuuza iye zonse za: Kwawo Kwamtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwati Wapadziko 64-0802, pa 12:00 P.M., nthawi ya Jeffersonville.

M’BALE . Joseph Branham

Chikumbutso: Musaiwale za Nthawi Yosungira Masana.

Malemba oti muwerenge musanamve Uthenga:
Mateyu 19:28
Yohane 14:1-3
Aefeso 1:10
2 Petro 2:5-6 / 3rd Mutu
Chivumbulutso 2:7; 6:14/21:1-14
Levitiko 23:36
Yesaya 4 Mutu 28:10 / 65:17-25
Malaki 3:6