Uthenga: 65-0815 Ndipo Osadziwa Izo Ayi
- 26-0614 Ndipo Osadziwa Izo Ayi
- 24-0901 Ndipo Osadziwa Izo Ayi
- 23-0212 Ndipo Osadziwa Izo Ayi
- 21-1017 Ndipo Osadziwa Izo Ayi
Okondedwa Iwo Osankhidwa
Kubadwa kwatsopano ndi Khristu, ndi vumbulutso. Mulungu wawululira kwa iwe chinsinsi chachikulu ichi, ndipo kumeneko ndi Kubadwa kwatsopano. Tsopano kodi iwe ungachite chiyani pamene ungalibweretse gulu lonselo pamodzi? kumene vumbulutso likumakhala mwangwiro mu chiyanjano,
Mulungu akusonkhanitsa gulu lake lonse la Mphungu pamodzi mumgwirizano wangwiro akuulula Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake.
Njira ya Mulungu ya kukhala ndi mfumu, monga Davide anali, inali yolondola, ndipo inu mumakhala ndi chimake chimodzi cha lingaliro. Monga mtsogoleri mmodzi ndi gulu la atsekwe, kapena zina zotero, inu simungakhoze kutenga awiri kapena atatu a iwo. Ndiye, inu mukawasokoneza iwo palimodzi, inu mumabwera ndi lingaliro la mtundu uliwonse.
Ndiye ife tiyenera kuchita chiyani, Ambuye?
Chinthu chokha chimene inu muyenera kuchita ndicho kungopangitsa Liwu Langa kudziwika; iwo akulidziwa ilo, pakuti nkhosa Zanga zimadziwa Liwu Langa.”
Kodi Liwu Lanu Langwiro la Lero Ndi Liti, Ambuye?
Ngati ine ndinakukhumudwitsani mwa kunena zimenezo, mundikhululukire, koma, ndinamvelera kuti mwina icho chinazembedwa, koma, Ine ndine Liwu la Mulungu kwa inu.
Ife timakhulupirira zimenezo ndi mtima wathu wonse. Umu ndi momwe ife timamvera, Ambuye
Iwo sasowa kutsimikizira chirichonse mwasayansi, kapena kumufunsa Msaduki aliyense kapena Mfarisi, kapena china chirichonse, za izo. Ine ndinanena izo, iwo akhulupirira izo, pakuti nkhosa Zanga zimamva Liwu Langa.
Kodi Liwu lomwe lili pa matepi kwa Mkwatibwi Wanu ndi lotani?
Ili ndi Liwu la Mulungu mu mawonekedwe a kalata, chifukwa Ili ndi vumbulutso lathunthu la Yesu Khristu, Chipangano Chakale ndi Chatsopano zitayikidwa palimodzi. Ameni. Apo inu muli.
Kodi matepi akadali ofunikirabe lero?
Ine ndikudziwa kuti, ndikadzachoka pa dziko lapansi lino, matepi awo ndi mabuku awo azidzakhalapobe, ndipo ambiri a inu anthu aang’ono mudzapeza, mu masiku akudza, kuti izi ndi chimodzimodzi Choonadi,
Ambuye, ife tikukhulupirira kuti matepi ndi mabuku ndi moyo wanu, utumiki wanu wamoyo womwe munamusiyira Mkwatibwi Wanu.
N’chifukwa chiyani matepi ndi LIWU LOFUNIKA KWAMBIRI kuti ife timve?
Ife tiri mu m’badwo wachinyengo kwambiri umene ife tinakhalamo konse. “Iwo ukananyenga Osankhidwa omwe ngati izo zikanakhala zotheka,” chifukwa iwo ali nako kudzoza, iwo akhoza kuchita chirichonse monga ena onse.
Aliyense amene adzawonjezere mawu amodzi kwa Awa, kapena kutenga Mawu amodzi kwa Iwo.” Iwe uyenera kukhala nawo mtheradi penapake.
Motero, Mtheradi wathu chiyenera kukhala Mawu a Mulungu.Inu mwatiululira kuti Mawu a Mulungu ndi Liwu la Mulungu ndi ofanana. Liwu ndi malingaliro enieni a Mulungu olankhulidwa, monga momwe munachitira ndi aneneri pamene munalemba Baibulo; koma m’masiku otsiriza ano, munasunga Mawu Anu, Liwu lanu, powajambula ndikuwayika pa tepi. Choncho, Liwu Lanu lolankhulidwa pa matepi ndi Mtheradi kwa Mkwatibwi.
Anthu saganiza kuti ndikofunikira kusewera Liwu m’tchalitchi chawo masiku ano. Amaphunzitsidwa m’matchalitchi awo kuti M’bale Branham sananene kuti azisewera matepi m’tchalitchi, iwo amangofuna basi kumva mtumiki wautumiki ndi kungowabwerezera zidutswa za Mawu.
Ndipo ngati mpingo uli mtheradi wanu, inu simumalabadira zimene aliyense anena. Ndiwo mtheradi wanu. O Mulungu, thandizani izi kuti zimire mkati! Kwa ine, chinthu chonse ncholakwika. Mawu a Mulungu ndiwo mtheradi. Chirichonse chimeme Mawu anena, ndiye ndiko kulondola.
Iye anali kuyembekezera kuti iwo amuitanire Iye. Ndicho chimene Iye akuyembekezera usikuuno, kuti inu mumuitanire Iye.
Zindikirani, pamene ophunzira awo anamuitanira Iye umo ku chiyanjano chawo kuzungulira gome,
Kodi wina anganene bwanji, kulungamitsa, kapena kupereka zifukwa, iwo amene akunena kuti iwo akukhulupirira Uthenga wa nthawi yotsiriza, kuti asasewere matepi m’matchalitchi awo pamene ali ndi mwayi womva LIWU LIMENE LA MULUNGU? Ndi Mawu omwe Mulungu analankhula kudzera m’milomo ya munthu kudzera mwa mneneri wake wodzozedwa. LIWU LOKHALO lomwe latsimikiziridwa ndi Lawi la Moto, lotsimikiziridwa mwa kudziwa zinsinsi zomwe za mumtima, lotsimikiziridwa ndi zizindikiro ndi zodabwitsa, kuti NDI Liwu la Mulungu kwa m’badwo uno.
Kodi wina angapange bwanji zifukwa, kufotokozera, kapena kusakhala ndi chilakolako chomva Liwu la Mulungu nthawi iliyonse akasonkhana?
Ambuye, musandilole ine kuti ndisatenge Liwu Lanu pa matepi mwachibwana. Mundilole ine nthawi zonse ndilengeze ku dziko lonse lapansi Ndi Liwu LOKHA lomwe ayenera kumva. Mundilole ndilengeze kwa Mkwatibwi Wanu, CHONSE CHOMWE AKUFUNIKA NDI LIWU LANU PA MATEPI.
Ife timakonda kuyanjana. Timakonda kulankhula za Inu ndi kutchula zidutswa za Mawu Anu, koma palibe china chachikulu chomwe inu mukanachita kwa Mkwatibwi Wanu kuposa kutipatsa Mawu Anu pamwamba pa Mawu, Vumbulutso la Liwu Lanu, kenako kuzindikira YEMWE IFE TILI, MKWATIBWI WANU WOKHULUPIRIKA.
Momwe ine ndingapitirire ndi kupitilira, ndikusonkhana pa vumbulutso lalikulu lomwe Mulungu watipatsa ife. Palibe mapeto; koma chinthu chachikulu chomwe ine ndingachite ndikukuitanani inu kuti mubwere mudzamve nokha Liwu la Mulungu ndi gawo la Mkwatibwi Lamlungu pa 12:00 PM, nthawi ya Jeffersonville, pomwe tidzanva: 65-0815 – Ndipo Osadziwa Izo Ayi.
M’bale Joseph Branham
Malemba oti muwerenge:
Chivumbulutso 3:14-19
Akolose 1:9-20