Uthenga: 65-0822M Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe
- 26-0621 Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe
- 24-0908 Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe
- 23-0219 Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe
- 21-1024 Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe
- 21-0530 Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe
- 19-1013 Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe
- 17-1112 Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe
Wokondedwa mfumukazi
Ndipo Mkwatibwi lero ndi wotengedwa kuchokera ku thupi la Khristu, amene ali kuchita ndi kupanga basi ndendende monga Iye anati Iye akanati adzachite kwa tsiku lino, Mkwatibwi, Mfumukazi; Mfumu ndi Mfumukazi.
Pamene Yesu anakhala Mawu onsewo, ndiye kuti tinali gawo la Iye KALE. Palibe mdierekezi, palibe mphamvu, palibe chomwe chingatichotsere zimenezo.Chimenecho ndicho chimango cha moyo.
Ndi chitsitsimutso chotani chomwe Mkwatibwi akukhala nacho ndi Uthenga uliwonse womwe ife tikumva. Izo ndi zopitilira mawu aumunthu ku fotokoza. Palibe mthunzi uliwonse wa kukayika, Mulungu watisankha ife ndipo watipatsa ife Vumbulutso LENI LENI la Mawu Ake a lero. Chifukwa chake, tikudziwa kuti ndife ndani, Mfumukazi Yake.
Liwu la Mulungu likulankhula ndi Mkwatibwi Wake pa matepi likumupanga kukhala wangwiro Mkwatibwi Wake. Palibe utumiki wina, palibe liwu lina; palibe chomwe chingapange kukhala wangwiro Mkwatibwi Wake koma Mulungu Mwiniwake akulankhula kudzera m’milomo ya munthu mwachindunji kwa Mkwatibwi Wake. Ena angafune cholowa m’malo, koma Mkwatibwi Wake sadzakhutira ndi china chilichonse koma LIWU Lake, kalata Yake yachikondi kwa Mkwatibwi Wake; chifukwa Nkhosa Zake zimangofuna kumva liwu Lake.
Anthu amati timaika kutsimikizira kwambiri pa mneneri. Izo zili choncho za chilendo kuti anthu savomereza kuti Atate Wamkulu Wakumwamba Mwiniwake anasamala kwambiri mngelo Wake kotero kuti anaika kufunika kwakukulu pa chilichonse chokhudza iye; momwe ankavalira, momwe ankachitira zinthu, khalidwe lake, machitidwe ake.
Anamuvekanso zovala zomwe ankavala; chibadwa chake, cholinga chake, chilichonse momwe ankayenera kukhalira, anasankhidwa mwangwiro ndi Mulungu Mwiniwake chifukwa cha ife…ndiyeno mkumati ife timaika kutsimikizira kwambiri pa mneneri.
Kwa ife, Liwu lomwe lili pa matepi si liwu la munthu, komanso sililankhulidwa ndi munthu, kubweretsedwa ndi munthu, kapena silingavumbulutsidwe ndi munthu. Ndi Liwu la Mulungu lomwe lawululidwa ndi Mulungu Mwiniwake, Wotanthauzira Wake, Khristu akudziwulula Yekha mu Mawu Ake.
Ena amatha kumva, koma sazindikira mokwanira. Inu mutha kuwauza, kuwawonetsa, koma Iwo mophweka sangathe kuwona. Ife timawakonda, kuwapempherera, koma zomwe Mulungu watiwululira ndi Ungwiro Wake.
Pano Pali choyesera cha Litimasi pa kugawikana kwakukulu pakati pa Mkwatibwi wa Khristu lero omwe iwo amati ali ndi Vumbulutso lowona la Uthenga waukulu uwu wa nthawi yotsiriza.
Tanthauzo la choyesera cha Litimasi: Chimodzi, fundo yotsimikizika, funso, kapena chochitika chomwe chimawulula mwachangu mtundu weniweni, maonekedwe, kapena udindo wa chinthu china (kapena winawake).
Ndiloleni ine ndinene kaye izo mobwereza, ndimakhulupirira mu utumiki weniweni woyitanidwa ndi Mulungu. Pali kufunika, ndi malo, pa udindo uliwonse. Lemba limati utumiki wa amuna awa ndi wopangitsa oyera mtima kukhala angwiro, koma silinena kuti utumiki uliwonse wofutukuka pasanu udzapangitsa oyera mtima kukhala angwiro. M’bale Branham amatiuza momveka bwino kuti utumiki mu m’badwo uliwonse umasochera, ndiye kodi IWO angapange bwanji Mkwatibwi kukhala wangwiro?
Pali Iwo ambiri, alaliki ambiri, aphunzitsi, atumwi ndi aneneri omwe alalikira kuti amakhulupirira Uthenga wa nthawi yotsiriza uwu ndipo kuti M’bale Branham anali Liwu la Chivumbulutso 10:7, omwe tsopano iwo akunena kuti ndi zabodza, iye ndi wonyenga, ife ndife a mwano.
Awa anali atumiki olemekezeka kwambiri okhala ndi mipingo yayikulu omwe adayenda padziko lonse lapansi ndikutumikira. Amaonedwa ngati atsogoleri akuluakuku mu utumiki wofutukuka pasanu, akulalikira m’misonkhano ndi m’matchalitchi ku United States konse. Iwo anali ndi utumiki waukulu pamaso pa anthu, ndipo anawatsatira ndikuwakhulupirira kuti anali amuna akuluakulu a Mulungu.
Ndiye pali atumiki masiku ano omwe amadziwika kwambiri ngati atumiki enieni awutumiki wofutukuka pasanu omwe amati akukhulupirira Uthengawu mwa kutchula mobwereza ndi kuulalikira iwo, koma iwo amanenanso kuti Uthenga uwu si uli Mtheradi. Masiku a Uthenga wa munthu mmodzi anatha. Utumiki wofutuka pasanu tsopano ndiwomwe woti umupange Mkwatibwi kukhala wangwiro, ndipo ndikolakwika kusewera matepi mu tchalitchi, kubwereza mawu ochepa.
Tikudziwa kuti padzakhala odzozedwa abodza mu nthawi yotsiriza; mneneri anatichenjeza kuti tichenjere nawo. Utumiki wawo udzakhala odzoza. Iwo adzakhala ndi Mzimu Woyera, motero iwo azizatchula mobwereza Uthenga wa ola lino. Adzakhala PAFUPI KWAMBIRI moti iwo akanadzanyenga osankhidwa omwe ngati n’kotheka.
Izo si zipembedzo zimenezo. Iwo sanayambe anyengapo osankhidwa. Chifukwa chake, ziyenera kukhala pafupi kwambiri kuposa pamenepo. Izi sizikutanthauza kuti mtumiki ALIYENSE wasochera, osati mwanjira iliyose ayi. Pali amuna akuluakulu a Mulungu omwe amalalikira ndi kuphunzitsa choonadi, koma pali chinthu china chomwe wokhulupirira aliyense ayenera kuzindikira ndikudzifunsa:
Kodi mtumiki amene mukumutsatira angalakwitse?
Kodi inu munganene kuti ameni ku mawu onse amene iye amalalikira?
Kodi inu mumakhulupirira kuti Mawu aliwonse amene iye amaphunzitsa ndi Pakuti Atero Ambuye?
Kodi liwu lake ndi Liwu lofunikira kwambiri lomwe inu muyenera kumva?
Kodi iye angalalikire chinthu cholakwika?
Kodi iye angalakwitse ngakhale atalalikira Uthenga kwa zaka 30? Kodi iye angalephere?
Kodi iye angakuuzeni zinthu zolakwika?
Kodi iye anganyengedwe?
Tsopano dzifunseni mafunso omwewo okhudza Mawu a Mulungu otsimikiziridwa omwe mungamve pa matepi.
Kodi Uthenga womwe uli pa matepi ungalakwitse: AYI
Kodi inu mungakhulupirire ndi kunena AMENI ku Mawu aliwonse amene iye akunena? INDE
Kodi ilo lingalephere? AYI
Kodi iye angalalikire zinthu zolakwika? AYI
Kodi ilo lingakuuzeni inu chinthu cholakwika? AYI
Kodi inu mungaike malo anu okhazikika pa Mawu onse amene mukumva…INDE!!!
Kodi ilo Ndi Liwu La Mulungu: INDE
N’chifukwa chiyani ine ndikunena zinthu zimezi? Kusonyeza kuti anthu ONSE akhoza, ndipo amachita, kulakwitsa, koma LIWU LA MULUNGU pa matepi silingalakwitse. Ndicho chifukwa chake ndi LIWU LOFUNIKA KWAMBIRI LIMENE INU MUYENERA KUMVA. Ndicho chifukwa chake utumiki uyenera kusewera matepi ku mipingo yawo. Ndi NJIRA YANGWIRO YOPEREKEDWA ndi Mulungu imene wapangira Mkwatibwi Wake.
Ndithudi, ndikukhulupirira kuti inu mungamve ena, koma Liwu lokhalo limene Inu MUYENERA KUMVA ndikukhulupirira Mawu onse ndi Liwu lomwe lili pa matepi. Liwu limenelo ndi LIMODZI LOKHALO limene tinganene AMEN ku Mawu onse.
Ili ndi lamulo la Mulungu, inu muyenera kukhulupirira Mawu onse, ndipo Mawu omwe mumamva pa matepi ndi MAWU OKHAWO amene wotsimikiziridwa ndi Lawi la Moto kuti ndi choonadi. Mulungu anati William Marrion Branham ndiye womasulira waumulungu yekhayo wa Mawu Ake, chifukwa Si mawu ake, Ndi Mawu a Mulungu.
Musasinthe kadontho kamodzi kapena kachidutswa. Palibe munthu amene ali wangwiro moteromo; Liwu la Mulungu lokha ndilo langwiro moteromo. Ngakhale pamene ife sitikumvetsa zomwe tikumva, tiyenera kungokhulupirira kuti ndi Mawu a Mulungu otsimikiziridwa kwa Mkwatibwi Wake.
Zoonadi, Mzimu Woyera ukutsogolera amuna a Mulungu. Zoonadi, Mzimu Woyera wawaitana iwo kuti akhale abusa ndi alaliki ndi aphunzitsi; nzoona, koma si angwiro. Koma Mulungu wapanga njira yoti mumve MAWU ANGWIRO nthawi iliyonse inu mukasonkhana.
Anthu, komanso utumiki, akufuna amlowa mmalo lero. Kodi inu mungaganizire wina kuchita kwa mtumiki zimene Iwo amachitira M’bale Branham?… “Ndikupatsani mphindi sate ndiye inu muyenera kuyima, ndili ndi uthenga womwe ndiyenera kubweretsa.
Inu mukhoza kumva matepi nthawi iliyonse. Ine ndikudziwa zomwe mpingo uwu uyenera kumva zomwe zikuchitika lero.” Ambiri ngakhale sangasewere ngakhale gawo la tepi, ndipo amati n’kulakwa kusewera Liwu la Mulungu m’matchalitchi awo.
Kodi wina aliyense amene ali ndi maganizo abwino angaganize mtumiki amene angapange chifukwa, chifukwa chilichonse, kuti asasewere Liwu la Mulungu m’tchalitchi chawo chifukwa iwo amakhulupirira kuti iwo ayenera kulalikira? Iwo amanena zimenezo, koma iwo sakhulupirira kuti ndi Liwu la Mulungu, kapena iwo sangapereke chifukwa chilichonse choti asasewere matepiwo.
Kodi wina anganene bwanji kuti amakhulupirira kuti ili ndi Liwu la Mulungu ndipo sangafune kulisewerera m’tchalitchi chawo? Kodi anthu amene amanena kuti amakhulupirira kuti ndi Liwu la Mulungu lomwe likulankhula ndipo safuna kuwawuza abusa awo kuti awasewere matepiwo m’matchalitchi awo? Chifukwa ali ndi mzimu womwewo.
Musakhale Nikodemo ndikunena kuti, “Ine ndikuona ndipo ine ndikukhulupirira ilo. Ndi Mwana wa Munthu akudziulula yekha mu thupi la munthu. Ndi Pakuti Atero Ambuye. Ndi Uthenga wangwiro. Ndi Liwu la Mulungu pa matepi, koma ine sindingathe kuchepetsa utumiki wanga ndikunena kuti Liwu limenelo ndilo lofunikira kwambiri kuti mpingo wanga umve.”
Abale ndi alongo, inu simungakhoze kugwirizana nane ndendende kokha pa izi. Ine sindikupempha inu kuti muchite zimenezo. Chinthu chokhacho, inu ingoganizirani izo. Zimene inu mundiuza ine, ine ndidzaziganizira izo. Ngati atumiki alankhula ku mpingo wawo kuti sakhulupirira kusewera matepi m’matchalitchi awo, palibe vuto, m’bale wanga. Inu muwadyetse chilichonse chomwe inu mukufuna.
Ine ndikuyesetsa mwa ubwino wanga kwambiri kuti ndikhale wolondola ndi Mawu, chifukwa nkhosa sizifuna china chilichonse koma chakudya cha nkhosa ndipo ife timakhulupirira kuti Liwu pa Matepi ndi Chakudya chathu cha Nkhosa. Ndicho chimene timakhala nacho moyo: Mawu aliwonse otuluka…Osati Mawu okha tsopano ndi kale; koma Mawu onse otuluka mkamwa mwa Mulungu olankhulidwa pa matepi; ndicho chimene ife timakhala nacho moyo.
Mulungu andikhululukire ine ndipo inu mundikhululukire ine ngati ine ndakukhumudwitsani Inu kapena ndanena china chake cholakwika. Ichi ndi chokhacho chimene ife timakhulupirira ndikuona kuti ndicho Choonadi chomwe ife timakhala nacho moyo. Mulungu watipatsa ife NJIRA YANGWIRO kuti ife timve Liwu Lake ndipo ife timalikonda ilo.
Monga mwachizolowezi, ine ndikuitana aliyense amene akufuna kuti adzalumikizane nafe kudzanva Liwu Limenelo pa nthawi yofanana, kuti adzagwirizane nafe pa 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, komwe tidzagwirizana ngati Gawo Limodzi kumva: 65-0822M Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe.
M’bale. Joseph Branham
Malemba Oyenera Kuwerenga Musanamve Uthenga:
Eksodo 4:10-12
Yesaya 53:1-5
Yeremiya 1:4-9
Malaki 4:5
Luka Woyera 17:30
Yohane Woyera 1:1 / 1:14 / 7:1-3 / 14:12 / 15:24 / 16:13
Agalatiya 1:8
2 Timoteo 3:16-17
Ahebri 1:1-3 / 4:12 / 13:8
2 Petro 1:20-21
Chivumbulutso 1:1-3 / 10:1-7 / 22:18-19