23-0219 Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe

Uthenga: 65-0822M Khristu Akuwululidwa Mu Mawu Ake Omwe

PDF

BranhamTabernacle.org

Nkhosa zanga zazing’ono,

Moni kwa inu ndi inu pama foni awa, zabwino kwambiri.Ndine wothokoza kwambiri kwa Ambuye inu mukhoza kukhala mnyumba mwanu momwe, kusonkhana mu malo anu, mipingo yanu, ndi kumva bulaliki. Kulikonse kumene liwu langa likubwera, lekani gulu laling’ono ilo lidalitsidwe.

Lero, ndikufuna kukulemberani kalata yachikondi yochokera pansi pamtima kuti ndikulimbikitseni. Inu ndinu amene Mulungu anasankha kuti mukhale Mkwati Wake kuchokela kuchiyambi cha dziko; inu mukumvera matepi aya. Ine ndikuuzani inu nthawi zambiri, matepi aya ndi anu okha, ndinu osonkhana anga. Ine ndiribe udindo pa zomwe Mulungu anapatsa atumiki ena kuti azidyese; Ndili ndi udindo pa mtundu wa Chakudya chomwe ndimakupatsirani. Matepi aya ndi a inu, mpingo wanga yekha, amene Mulungu wandipatsa kukala mbusa. Ndi Manna obisika, winayo sangakhoze kutenga Izo.

Tsopano, ngati anthu ena akufuna kupanga haibridi chakudya ndi zinthu kunja uko, asiyeni iwo atenge vumbulutso kuchokera kwa Mulungu ndi kuchita zomwe Mulungu akuwauza iwo kuti azichita, azidya pa chirichonse chimene iwo akufuna. Ndichita zomwezo. Koma Mauthenga awa nkwa inu nokha.

Ine ndikuyesera mwakukhoza kwanga kukhala ndi Mawu, kwa inu amene mwayikidwa mmanja mwanga kuchokera kwa Mulungu, chifukwa nkhosa zimafuna chakudya cha nkhosa. “Nkhosa Zanga zimamva Liwu Langa.” Ndipo ndicho chimene ife timakhalira moyo, Mawu aliwonse amene atuluka. Osati Mawu chabe nthawi ndi nthawi, koma Mawu aliwonse amene atuluka kuchokera mkamwa mwa Mulungu. Ndi chimene inu oyera mtima mumakhala nayho.

Aliyense ayenera kukhala ndi chinachake chimene angagwire .Chinachake chiyenera kukhala chomangirira, mwa kuyankhula kwina, chodalirapo. Ndipo aliyense ayenera kukhala nacho mtheradi kapena mtheradi. Kwa ine, ndi kwa iwo amene ine ndikuyembekeza kuti ine ndikuwatsogolera kwa Khristu, ndi mwa Khristu, Baibulo ndilo chochidalira chathu.

Tsopano, ife tikuzindikira kuti Mulungu anatitumizira ife aneneri Ake. Umo ndi momwe Iye aliri ndi kubweretsa Mawu Ake kwa anthu, kupitila mu milomo ya mneneri Wake. Tsopano mu masiku otsiriza ano, Iye walonjeza kuti adzadziwonetsera Yekha mu chidzalo kachiwiri, cha thupi Lake, mu Mzimu. Ndi Mulungu Mwiniwake mu mawonekedwe a chilembo, mawonekedwe a mneneri, akuwonetseredwa mu thupi.

Ine ndiyenera kukhala lyonse mu Kukhalapo kwa analemba ndi cholembera changa chokonzeka nthawi iliyonse kuti nilembe chirichonse chimene Iye anena. Ine ndimayika maganizo anga pa maganizo Ake; osati zomwe munthu amaganiza, zomwe m’badwo ukuganiza, zomwe mpingo ukuganiza, zomwe ufumu ukuganiza. Maganizo a Mulungu okha! Ndimangofotokoza maganizo a Mulungu ku Mawu.

Pamene Mulungu awulula maganizo Ake kwa ine, ine ndimazifotokoza izo mu Mawu kwa inu pa tepi, “KUKAMBA KWA AMBUYE.” Izo siziri, “Kukamba kwa ine.” Ndi, “KUKAMBA KWA AMBUYE!” Ine ndingakhoze kokha kuwatanthauzira Iwo monga Analemba anivomeleza ine kuti ndikutanthauzire kwa inu; pakuti Iwo ali Mawu osalephera a Mulungu.

Alipo ena ambiri amene amayesa kunikopela ine, monga ansembe, ndi zina zotero. Ndipo amachita chiyani? Ingosokonezani, ndizo zonse. Iwo sakhoza kuchita izo. Mulungu anandituma ine, mneneri Wake, kuti ndidzamutsogolere Mkwati Wake; osati munthu wina, kapena osati gulu la amuna.

Mawu omwe ndikunena, ndi momwe ndimachitira, adzachititsa khusaona ena, koma adzatsegula maso a ena. Iye anandivalika ine mu mtundu wa diresi limene ine ndifunika ndivale, chikhalidwe changa, chikhumbo changa, chirichonse basi momwe ine ndiyenera kukhalira. Anakusankhirani ine mwabwino. Ena amaima ndi kuyang’ana ndi kunena, “Chabwino, sindingathe. Pali…ine—ine sindikukhoza kuwona.” Iwo achititsidwa khusaona.

Adzaulula kwa amene Iye adzaulula. Iye anapangidwa kotero kuti Iye akhoza kudzibisa Yekha mu Lemba, kwa wazamulungu wochenjera kwambiri amene alipo. Iye akhoza kungodzibisa Yekha, kukhala apo pomwe mu Lemba, ndipo iwo akhoza kuyang’ana utali wa tsiku lonse ndipo osachiwona icho; kuyang’anani moyo wonse, ndipo osachiwona icho. Iye akhoza kungodzibisa Yekha, kunkhala pamenepo.

Chofunikira tsopano ndi iwo amene alandira Uthenga mu mitima yawo, ayenera kunkala mu Kukhalapo kwa Mwana, kuti akachepe. Lisani matepi ndiyeno lolani Mwana aphike zobiriwira zonse mwa inu, kukupangani inu Akhristu okhwana.

Pamene iye anabwera nthawi yoyamba, iye anali munthu. Pamene iye anabwera nthawi yachiwiri; ndi magawo awiri, iye anali munthu. Pamene iye anabwera mu mawonekedwe a Yohane M’batizi, iye anali munthu. Iye analonjeza kubwera tsiku lino ndi kukhala moyo ndi kudziulula Yekha kamodzinso mwa munthu; Mwana wa munthu akukhala m’thupi la munthu.

Ife tsopano tiri mu m’badwo wa Maso, aulosi, wa Malaki 4. Palibe china chatsalira kuti icho chibwere koma Iye Mwiniwake kuti alowe mu zimenezo, ’chifukwa ndicho chinthu chotsiriza chimene chiripo.

Mvetserani ana ankhosa anga, inu amene Mulungu wandipatsa ine kwa m’busa. Nthawi lachedwa. Iye azabwela posachedwa, Mkwati Wake. Khalani nawo matepi amenewo, ayo siyafunika kutanthauzira.

Ine ndikukuitanani inu a Mphungu aang’ono kuti mubwere mudzalumikizana nane ndi chinthu chokha chimene chidzabweretse Mkwati Wake pamodzi Lamlungu lino, pa 12:00 p.M., nthawi ya Jeffersonville. Mudzamva Kukamba kwa Ambuye pamene Mulungu akulankhula kupyolera mwa ine ndi kuwulula: Khristu Akuwululidwa Mmawu Ake 65-0822M.

Kumbukirani, KHALANI NDI UTUMIKI WA TEPI.LISANI MATEPI TSIKU LONSE.

M’bale Branham

Malemba o werenga pamene mukalibe kumva Uthenga:

Eksodo 4:10-12
Yesaya 53:1-5
Yeremiya 1:4-9
Malaki 4:5
Luka 17:30 St
Yohane Woyera 1:1 / 1:14 / 7:1-3 / 14:12 / 15:24 / 16:13
Agalatiya 1:8
2 Timoteyo 3:16-17
Ahebri 1:1-3 / 4:12 / 13:8
2 Petulo 1:20-21
Chivumbulutso 1:1-3 / 10:1-7 / 22:18-19