23-0226 Fyuluta Ya Munthu Woganiza

Uthenga: 65-0822M Fyuluta Ya Munthu Woganiza

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Osonkhana Ndi M’bale Branham,

Ndikufuna kuitana dziko kuti lisakane naife pa kulumikizanitsa Lamlungu lino pa 12:00 P.M., nthawi ya Jeffersonville, pamene ife a chiomba nkanga timasonkhana pamodzi mailosi mazana awiri aliwonse mu umodzi wa mipingo ya mneneri. Tidzamva Mulungu akulankhula kupitira mu mngelo mutumwa Wake wachisanu ndi chiwiri ndi kutiuza kuti:

Uthenga uwu, ndi Mauthenga ena onse amene ine ndimalankhula, walunjikidwa kwa osonkhana anga. Izo si za osonkhana anu koma ngati iwo akufuna kuti achilandire Icho. Koma Izo zalunjikidwa kwa anthu awa pano.

Iye akulankhula kwa ife, ULEMERERO, osonkhana ake. Osati inu amene mumati, “M’bale Branham ndi mneneri, koma iye si m’busa wanga. Abusa athu akuti kuliza matepi mu tchalitchi simolingana ndi Mawu amasiku ano.” “M’busa wathu amatiuza kuti tizimumvera. Molingana ndi Mawu, akutitsogolera ndi Mzimu Woyera tsopano.”

Mneneri anakulankhulani inu ndi abusa anu.

Kwa atumiki aliwonse pa malo aliwonse, nthawi iliyonse, izi sizinalunjikidwe monyozera ku ziphunzitso zanu, izi sizinalunjikidwe nkomwe kwa nkhosa zanu.

Sitifuna kukangana nanu abale ndi alongo. Ife tikumvetsa, Izo sizinalunjikidwe kwa inu, koma kwa ife, amene timakhulupirira kuti Mzimu Woyera wayika mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri mutumiki kuti akhale m’busa wathu ndi kutitsogolera ife, mpingo Wake. Ife timakhulupirira kuti kuliza matepi ndi NJIRA YAZOONA YOKHA. Mulichabebwino ndipo mukuchita zomwe mneneri wakuuzani kuti muchite:

Ndipo ine nthawizonse ndimalozera kwa iwo, ngati iwo ali membala wa mpingo wina, “Kawoneni abusa anu.”

Muyenera kuchita monga momwe abusa anu akunenera.

Kenako mneneri amauza abusa anu, kuti atsimikize kuti amvetsetse.

Tsopano, abusa, ine ndikufuna inu mudziwe izo, kuti, izi ndi kwa osonkhana anga okha omwe ine ndimalankhula zinthu izi. Ndipo ine ndiri nawo ufulo wochita zimenezo, chifukwa ine ndinaikidwa ndi Mzimu Woyera kuti ndiziyang’anira nkhosa izi.

Watumidwa kuti aziyang’anira ife, nkhosa zake; amene Mulungu wawaika mu zisamaliro AKE. Mzimu Woyera ndi m’busa wathu pamene Iye akulankhula kwa ife ndi kutitsogolera ife tsiku lirilonse ndi Liwu Lake lotsimikiziridwa.

Izi ndi zimene Yehova akutitsogolera kuchita. Ife sitikutsutsa inu kapena abusa anu, kapena momwe inu mukumverera kutsogozedwa ndi Ambuye kuti muchite. Munthu aliyense ayenera kuchita zimene akuona kuti Yehova akumutsogolera kuchita mogwirizana ndi Mawu.

Tili ndi chosefela chimodzi, UTHENGA UWU. Chirichonse chimene timamva chiyenera kupita mu sefa imeneyo. Liwu limene timamva pa matepi ndilo Liwu lokha lomwe tili nalo 100% kukutila kuti NDI KULANKULA KWA AMBUYE.

Kodi inu mukhulupirira kuti kudzoza kumeneko pa anthu amenewo kutanthauza kuti ndi kudzoza kwa Mzimu Woyera?” Inde, bwana, Mzimu Woyera weniweni wa Mulungu pa munthu, koma iwo ndi abodza.

Kopita kwathu Kwamuyaya zimatengera zomwe IYE ANENA PATEPI, osati zomwe munthu wina aliyense kapena gulu la anthu likunena. Choncho, sitingathe, ndipo sitidzamva wina aliyense. Kodi munthu angachite bwanji mwayi?

Bwerani mudzasonkhane pamodzi ndi ife mochulukira, popeza muona kuti tsiku lilikuyandikira.

Anthu akhoza kukhala mnyumba zawo momwemo kapena mwawo…kusonkhana m’malo awo, matchalitchi awo, ndi zina zotero, ndi kumvetsera misonkhano.

Kuti, abwenzi anga, molingana ndi mneneri wa Mulungu, osati kutanthauzira kwa munthu wina pa zomwe Baibulo limanena, tikudzisonkhanitsa tokha pamodzi mozungulira Mawu mochuluka kwambiri momwe ife tikuwonera tsiku likuyandikira.

Kodi chingalawa popanda Mulungu n’chabwino bwanji? Ndi bokosi yankuni chabe, magome angapo amiyala.

Bwerani mudzasonkhane nafe pamene tikumvera chosefela choperekedwa ndi Mulungu, pamene akutibweretsera Uthenga: Chosefela Cha Munthu Woganiza 65-0822E.

M’bale. Joseph Branham

Onani zomwe mukumenyera. Onani zomwe mulili pano. Yang’anani zomwe mumapitira kutchalitchi. Zomwe zimakupangitsani inu…Ndi zabwino kupita ku tchalitchi, koma osanpita ku tchalitchi kokha; izo sizingakupulumutseni inu.