26-0517 Iwo Odzozedwawo Pa Nthawi Yotsiriza

Uthenga: 65-0725M Iwo Odzozedwawo Pa Nthawi Yotsiriza

PDF

BranhamTabernacle.org

Zokondedwa Mphungu Zosonkhana,

Mutu wokha wa Uthenga wa sabata ino ukuwulula kuzindikira Mzimu Woyera kwa Mkwatibwi. Kuganiza kuti padzakhala amuna odzozedwa enieni omwe adzauka m’masiku ano, ndi kudzoza kwenikweni kwa Mzimu Woyera womwewo womwe unali pa mneneri wathu, koma kukhala abodza.

Mawu amatiuza kuti adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa, kulandira mvula yomweyo, madalitso omwewo monga mneneri weniweni. Anthu adzasiya Mawu enieni otsimikiziridwa a tsikulo kupita ku zilakolako zawo, kudziunjikira aphunzitsi, okhala ndi zoyabwa mmakutu. Zidzakhala pafupi kwambiri ndi Mawu enieni mpaka zidzangokhala pafupifupi kunyenga Osankhidwa.

Kodi kudzoza kumeneko kudzakhala pafupi bwanji? Kodi zidzakhala zosavuta kuzindikira chomwe chili chowonadi ndi chomwe chili chabodza? Mneneri anatiuza kuti Mfumu Davide, munthu wotsatira mtima womwe wa Mulungu, wokhala ndi kudzoza pa iye, adapeza vumbulutso loona; koma ilo linali lolakwika.

CHIYANI!! Lolani chimenecho chilowe mkati mwakanthawi. Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu inali ndi kudzoza kwenikweni ndi vumbulutso loona, koma linali lolakwika! Ana a nkhosa a Mulungu ayenera kukhala maso kwambiri kuti adziwe kuti zomwe akumva ndi kudzoza koona kapena kwabodza; pakuti malo awo amuyaya akupumulira pa zigamulo izi.

Ife tikudziwa kuti Mulungu waika atumiki ambiri odzozedwa kuti athandize kutsogolera ndi kusunga Mkwatibwi Wake m’Mawu. Mawu Ake amanena choncho, ndipo ife tili oyamikira kwambiri Ambuye chifukwa cha aliyense wa iwo. Iwo ayitanidwa kukhala abusa pa nkhosa zawo.Iwo ayenera kuwasunga iwo m’Mawu. Pochita izi, iwo sayenera kulephera kusewera Liwu Lokhalo lotsimikiziridwa la Mulungu kwa nkhosa zawo.

Monga momwe ife tangomvera kumene momwe munthu aliyense angalakwire, ngakhale ali ndi kudzoza koona ndi vumbulutso loona. Koma Mkwatibwi akhoza kukhala otsimikiza konse, chifukwa Mulungu wapereka njira yangwiro yomwe iwo nthawi zonse angakhoze kuti amve KUDZOZA KOWONA, VUMBULUTSO LOWONA, PAKUTI ATERO AMBUYE WOWONA; KOKHA KANIKIZANI KUSEWERA.

“Kumene kuli Nyama,” Manna ali, Mawu ali, “kumeneko mphungu zikakhala zitasonkhana.

Kumene kuli Nyama, kumeneko ndi komwe ife Mphungu tidzasonkhanako. Kumene kuli Nyama yatsopano, Mawu amu nyengo, Uthenga wa ola. Ndipo palibe malo atsopano odyera Manna amenewo kuposa kumva Liwu la Mulungu akulankhula Iyemwini.

Awo ndi Mawu Ake. “Munthu sadzakhala moyo ndi mkate wokha, koma ndi Mawu onse.” Mwaona? Okonzedweratu amadziwa izi. “Mawu achirendo, kapena liwu lachirendo, iwo sadzalitsatira.”

Chifukwa chomwe ife sitidzanyengedwa, ndipo sitinganyengedwe, ndi ndichifukwa chakuti ife ndife Mawu omwe ali ndi vumbulutso ili. Ife sitingakhale china chilichonse. Ife sitingamve china chilichonse. Ife Sitikudziwa china chilichonse.

“INE NDINE!” Osati “Ine ndinali, kapena ndidzakhala ndiri.” INE NDINE,” tensi yapakalipano, Mawu tsopano. Osati Mawu amene analipo, kapena Mawu amene ati adzabwere; Mawu amene alipo tsopano. Mwaona? Inu mwamvetsa zimenezo? “INE NDINE!” “INE NDINE” ali Mawu. “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu.” Ndi kulondola uko? “INE NDINE.” “Mulungu anandituma ine monga mneneri Wake, kuti ndidzatsimikizire izi kuti ziri zoona. Ine ndine yankho kwa Mawu awa, chotero, pamene Iye anabwera pansi pano ndi kuchita izi.”

Ndipo pamene iye anachita izo, Farao anati, “Chabwino, ife tiri nawo anyamata ochuluka mu gulu lathu amene akhoza kuchita zimenezo, nawonso,” osanzira.

Yesu anati, “Tsopano, izo zidzabwereza kachiwiri mu masiku otsiriza,” onani, kumadzitcha chinthu chomwecho.

Ambuye alemekezeke. Kakamba za chitsimikizo cha Mkwatibwi. Pomwe inu mukhala ndi Vumbulutso ili, ndiyeno inu mudzadziwa kuti inu muli wosankhidwa Wake, Okonzedweratu , Mkwatibwi wake wokomamtima.

Mwa kumvetsera Liwu la Mulungu pa matepi, ife tikumvetsera Mwana wa Munthu, amene ndi Khristu. Iye ndiye amene ife tikumudya. Ife sitikudya munthu; munthu, mawu ake adzalephera. Koma ife tikudya Thupi la Mawu a Mwana wa Munthu losalephera.

Ngati inu mukufuna kukhala otsimikiza Wani Handiredi peresenti kuti inu mukumvetsera ku Pakuti Atero Ambuye, bwerani mudzakhale nawo gawo la Mkwatibwi Lamlungu lino pa 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumva Liwu la Mulungu likutiululira zonse zokhudza iwo odzozedwa ps nthawi yotsiriza.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga: Iwo  Odzozedwawo Pa Nthawi Yotsiriza 65-0725M  

Malemba Opatulika:
Mateyu Woyera 5:44-45 / 7:21 / 24:15-28
Luka Woyera 17:30 / 18:1-8
Yohane Woyera 14:12
Aefeso 1:5
2 Timoteo 3:1-8
Ahebri 6:1-8 / 11:4
Chivumbulutso 10:1-7 / 16:13-14
Malaki 4:5
1 Mafumu 22:1-28
Yeremiya: Machaputala 27 ndi 28