23-0115 Iwo Odzozedwawo Pa Nthawi Yotsiriza

Uthenga: 65-0725M Iwo Odzozedwawo Pa Nthawi Yotsiriza

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa nkhosa Osonkhanina Mu khola,

Ndine wokhutitsidwa ndi woyamikira kwambiri kwa Ambuye kusonkhana ndi aliyense wa inu mu Khola la Nkhosa la Mulungu mlungu uliwonse, kumene timabisidwa mobisika, kudya ndi kukhala ndi Chakudya Chobisika chimenecho. Ndi Vumbulutso la Yesu Khristu, kudzitsimikizira ndi kudziulula Yekha kwa ife.

Iye wadzibisa Yekha kuti ena ayang’ana kumene pa Iwo ndipo sachiwona Iwo, koma kwa ife, Mkwati Wake wosankhidwa, ife tikuwona Iwo mwa mbalambanda ndi kukhulupirira Mawu aliwonse. Ife takhala ndi Mawu Ake ndi mneneri Wake monga iwo ali umodzi ndi umodzi.

Ndipo ngati inu muli mwana wa Mulungu, inu muzakhala ndi mneneri wa Baibulo ili. Ndi Mawu.

Aneneri ambiri odzozedwa masiku ano amati “Ndi Mzimu Woyera umene uyenera kukhala nawo, osati mneneri.” Monga aneneri akale, ngati ife tiri ndi funso, payenera kukhala yankho yamunshye. Ife tiyenera kuyenda KU MAWU kuti tikawone zomwe mneneri patsogolo pathu ananena.

Koma pali Mzimu wazohona wa Khristu, ndipo ndiwo Mawu osandulika thupi momwe analonjezera kuchita.

UMODZI weniweni wa Khristu Mzimu umene Iye analonjeza, Malaki 4, Luka 17, Mwana wa Munthu akudziulula Yekha mu thupi la munthu.

Inde, alipo amuna odzozedwa. Inde, ali nako kuitanidwa. Inde, iwo ali ndi Mzimu Woyera weniweni. Inde, ali ndi zolinga ndi zolinga zabwino.

Ndiye tingadziŵe bwanji chabwino ndi choipa?

Zindikirani, iwo akuwoneka chimodzimodzi. Iwo anadzozedwa chimodzimodzi. Koma zindikirani, “Ndi chipatso chawo…”

Ndimasonda kunena zinthu izi koma nthawi lachedwa ndipo nthawi ikuthawa. Izi ndi zimene zikunenedwa ndi kulalikidwa lero ndi mimbulu yolusa ija Paulo anachenjeza mpingo, ndi odzozedwa abodza M’bale Branham anati adzabwera. Iwo ali pano pakati pathu, monga ananenera.

Nayi gawo la kalata yolembedwa kuchokera kwa mtumiki. Chipatso chawo chikuyesa kukayikira mneneri wa Mulungu. Amachenjeza anthu awo kuti ife ndife opembedza potsatira Mneneri ndi Kutyanka Kuliza.

Mvetserani momwe izi ziliri zachinyengo.

Ndi makala wolakwilisidwa kuti chiwanda ichi chalowa muuthenga wathu kotero kuti tsopano timaitana afalitsa za maulaliki a William Branham kuti NDI MAWU A MULUNGU. William Branham sanali liwu lenileni la Mulungu, koma liwu la munthu amene Mulungu anamugwiritsa ntchito. Baibulo silimanena kuti iye anali liwu la Mulungu, koma Baibulo limamutchula iye monga liwu la mngelo wa 7. ( Chiv 3:14; 10:7 ).

Tiyeni tipite ku MAWU ndikulola mneneri wa Mulungu kuvumbulutsa chiphunzitso chonyenga ichi.

Ngati ndakulakwirani ndikunena zimenezo, ndikhululukireni, koma, ndinamva kuti mwina ndakhumudwa, koma, INE NDINE MAWU A MULUNGU KWA INU.

Tsopano kodi inu mukhulupirira ndani, mneneri wodzozedwa wabodza uyu, kapena MTUMIKI WA NGELO WACHISANU NDI CHIWIRI WA MULUNGU? Inu mungakhoze bwanji kukhala pansi pa mtumiki aliyense yemwe angakhulupirire kapena kukuphunzitsani inu zinthu izi? Inu chilibwino mulowe mu Mawu pamene nthawi ikaliko.

Kulakwitsa koyipa kwapangidwa ndi gulu la uthenga pomuyesa William Branham kukhala chishintilizo. William Branham sanali konse chishintilizo! Mawu a Mulungu ndiwo chishintilizo.

Amen, Mawu a Mulungu NDI chishintilizo chathu. Kodi Mawu anabwela kwa ndani, inu kapena IYE? Kodi wotanthauzira mwaumulungu wa MAWU A MULUNGU ndi ndani, inu kapena IYE? Ndi ndani yemwe Lawi la Moto linamutsimikizira kuti ali NDI MAWU AMBUYE, inu kapena IYE?

Chifukwa iwe umapeza amuna awiri, iwe uli nawo maganizo awiri.

Ife sitikufuna amuna awiri kapena maganizo awo, ife tifuna zomwe mneneri wa Mulungu ananena pa tepi.

Ndipo uyenera kufika ku chishintilizo chimodzi, ndipo chishintilizo changa ndi Mawu, Baibulo.

Ndi zimenezo, monga momwe munanenera, Baibulo ndi lake ndi chishintilizo lathu, koma kenako akuti:

Ndikudziwa kuti inu, abale athu, mumayang’ana kwa ine kuti ndine chishintilizo chanu.

Kotero yembekezani kamphindi, izo zikumveka zosiyana ndi zomwe MUNANENA. Iye anati ife timayang’ana kwa iye kukhala Chishintilizo chathu.

Molingana ngati ndimatsatira Mulungu, monga Paulo ananenera m’Malemba, “Inu munditsate ine, monga ine ndimatsatira Khristu.”

Kodi ameneyo si wodzozedwa? Kodi iye sankadziwa zimene ankanena?

Kodi mneneri wa Mulungu anatiuza chiyani sabata yatha?

Ife tikupeza kuti pamene munthu abwera, wotumizidwa kuchokera kwa Mulungu, wodzozedwa ndi Mulungu, ndi MAWU AMBUYE owona, uthenga ndi mthenga zimakhala mmodzi ndi mmodzi.

Anati simungawalekanitse, ali chinthu chimodzimodzi, koma inu mukuti tiyenera?

William Branham sali wosiyana ndi munthu aliyense wachivundi, pakuti iye anali munthu wa zikhumbo, monga analiri Eliya.

Ameni, iye anali munthu motsimikiza, koma iye anali MUNTHU amene Mulungu anamusankha kuti amuululireko Mawu Ake onse, ndi kutitsogolera ife ku Dziko Lolonjezedwa. Iye anali mmodzi yemwe Mulungu anati, apangitseni anthu kuti akukhulupirireni INU.

Chinthu chomwecho, odzozedwa, kulalikira Uthenga wa pentekoste, koma kukana lonjezo la tsiku-lino la Mawu kukhala likutsimikiziridwa, “Yesu Khristu yemweyo dzulo, lero, ndi nthawizonse.”

Kodi ife tingadziwe bwanji kusiyana kwake ngati iwo ali odzozedwa owona a Mzimu Woyera? Anatipatsa zitsanzo kuti tidziwe aneneri onyenga kuchokera kwa mneneri woona.

Balamu ndi Mose. Mikaya ndi Zedekiya. Yeremiya ndi
Hananiya. Muzochitika zonse onse awiri anali aneneri odzozedwa a Mulungu, koma kodi iye anatiuza kuti tichite chiyani, KHALANI NDI MNENERI WA MULUNGU WOYENZEKEZEKA. Imeneyi ndi njira YOKHALA yotsimikizira kuti mukutsatira Njira yoperekedwa ndi Mulungu, ndipo muli mu chifuniro Chake chanbwino.

Ine ndine mmodzi yekha amene ali pafupi pamene Iye azichita izo. Ine ndinali liwu lokha limene Iye ankagwiritsa ntchito, kuti azinene Izo. Sizinali zomwe ndimadziwa; ndi chimene ine ndinangodzipereka kwa icho ndekha, chimene Iye anachiyankhula nacho.

Ndizo zonse Mkwati akufuna ndi zosowa. Liwu Limodzi. Mneneri umodzi. Uthenga umodzi. Mtumiki umodzi.

O Atate, ndife othokoza bwanji chifukwa cha chisomo Chanu ndi chifundo kwa ife. Munatiuza kuti palibe chovuta ndi Inu. Palibe chovuta ndi ife. Pakuti zinthu zonse ndi zotheka kwa iwo amene akhulupirira, ndipo ife TIKHULUPIRIRA.

Bwerani mudzabwere nafe Lamlungu nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya Jeffersonville, pamene tili ndi Liwu losankhidwa ndi Mulungu limatiuza zonse za Odzozedwa Pa Nthawi Yotsiriza 65-0725M.

Bro. Joseph Branham