26-0510 Tsiku La Anakubala

Uthenga: 59-0510M Tsiku La Anakubala

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi,

Tsopano, ine ndikuganiza kuti palibe kulemekeza kokwanira kumene tikanakhoza kupereka kwa mayi.

Mayi athu ndiye oyamba nafe, ndipo anapatsidwa udindo waukulu wa zomwe ife tidzakhale komanso njira yomwe ife tiyenera kuyendamo. Iye anapatsidwa udindo kuchokera Kwa Mulungu woti atiyike ife panjira yoyenera. Ndicho chifukwa chake mayi ali nako mwapadela , kukhudza kochepa komwe kwapatsidwa kwa iye kuchokera kwa Mulungu.

Ndi dalitso lapadera bwanji lomwe lili mu nkhokwe la ife la Lamlungu lino, pamene ife tikupereka ulemu kwa Amayi onse, pamene ife tidzamva mngelo wachisanu ndi chiwiri wa Mulungu akufotokoza chikondi ndi ulemu womwe amayi athu ali nawo m’mitima mwathu.

Ife tikudziwa kuti tsiku lililonse ndi Tsiku la Anakubala, koma Lamlungu lino tidzapereka ulemu wapadera kwa Amayi onse pamene ife tidzamva mneneri wathu akupereka ulemu kwa iwo monga momwe iye adayankhula zaka 67 zapitazo pa tsiku lomwelo lofanana , pa 10 Meyi , 1959.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: Tsiku la Anakubala 59-0510M

Nthawi: 12:00 P.M. Nthawi ya ku Jeffersonville

Malemba Opatulika: 1 Akorinto 15:1-4