23-0305 Edeni Wa Satana

Uthenga: 65-0829 Edeni Wa Satana

PDF

BranhamTabernacle.org

Ana Anga Okondedwa,

Inu ndimwe chikhumbo cha Ine, Atate anu a Kumwamba. Inu munali mwa Ine kuyambira pachiyambi. Simukukumbukira chabe, koma munali ndi Ine. Ndinafunisisisa kwambiri kukudziwani chifukwa ndimafuna kuti ndikugwireni, kukamba nanu, kumikondani inu, ndi kumiposhani mumanja anu.

Monga mwana wanga, ndiwe gawo la Ine, wopangidwa thupi, monga ine ndinapangidwa thupi, kodi ife tikhoze kukhala ndi chiyanjano wina ndi mzake monga banja la Mulungu pa dziko lapansi. Chimenecho chinali chofuna Changa ndi zomwe ninalikufuna kuchokera pachiyambi.

Ndinakupangirani Munda wa Edeni kuti tiyanjane, koma mdani Wanga anazembera ndi chinyengo, anatenga dziko lapansi ndikutanthauzira molakwika pulogalamu kwa inu.

Iyi ndi nthawi lachinyengo limene mukukhalamo, koma ilinso nthawi yaulemerero kwambiri ya mibadwo yonse, chifukwa tsopano mukuyang’anizana ndi Zakachikwi zazikulu kachiwiri; mukuyang’anizana ndi Edeni kachiwiri.

Mzimu wanga si chinachake chimene chimaphunzitsidwa mwa inu. Ndi chinthu chomwe ine ninakonzedweratu mwa kudziwiratu Kwanga mwa inu ndi kwanja Langa lamphamvu. Tsopano kuitana Kwanga kotsiriza kuli kuti ndimugwire Mkwati Wanga; “chokani pakati pawo, patukani”.

Lero iwo sakuyesera kukhazikitsa Mawu Anga mu mitima ya anthu, iwo ali kuyesera kudzikhazikitsa okha. Mipingo ikuyesera kukhazikitsa chiphunzitso cha mpingo mu mtima wa munthu. Munthu aliyense amati, “Ndachita izi. Ine, ine, changa, chipembedzo changa, ine, ichi.” Akudzikhazikitsa okha, osati Anga Mawu amene analankhulidwa kupitila mwa mneneri wanga.

Inu simukufunika kuti mumvetse chirichonse chimene ine ndikunena, inu muyenera kungokhulupirira Izo chifukwa ine ndinanena chomwecho, ndipo izo zikukhazikitsa icho kwanthawizonse.

Mzimu wanga Woyera ukugwira ntchito mwa inu. Ndi Moyo mwa inu, osati kutengeka; ayi mtundu wina wa umboni wathupi, koma Iwo ndi Munthu, INE, Yesu Khristu, Mawu a Mulungu, okhazikitsidwa mu mtima mwanu, ndipo amafulumizitsa Mawu aliwonse a m’badwo uno. Ndi Mzimu Wanga Woyera ukugwira ntchito mwa inu molingana ndi Mawu.

Mkwati wanga woyamba analephera pakumvetsera kumakanizo ya Satana, koma Ine ndakuwombola iwe mwa Inemwini, amene ali Mawu opangidwa thupi. SIMUDZANDIKANGIWA INU. Inu ndinu Mkwati Wanga wa Mawu namwali amene simudzamvera kumaganizilo ya Satana. Inu mudzakhala ndi Mawu Anga.

Zakachikwi zikadzatha, ndiye padzakhala Edeni wokhazikitsidwa kachiwiri; Ufumu wanga waukulu udzachotsedwa. Ndinalimbana nazo ndi satana m’menemo m’munda wa Getsemane, ndipo ninaiwinaso Edeni Wanga. Tsopano ndapita kuka konza Edeni wanu Watsopano Kumwamba. Ndibweranso kwa inu posachedwa, mitima yanu osati isavutike.

Sipadzakhalanso mumana, pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidzapita. ne ndidzayikonzanso iyo ndi ubatizo wa Moto umene uti udzaphe nyongolosi iliyonse, iliyonse matenda, matenda aliwonse, ndi chonyansa chirichonse chimene chinayamba chakhalapo pa dziko lapansi.

Iye adzaphulika, ndipo padzabwera Dziko Latsopano. Kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zidzapita. Padzakhala Yerusalemu Watsopano akugwa kuchokera kwa Ine kuchokera Kumwamba. Kumeneko ndidzakhala ndi inu, makhalidwe Anga azoona, Ana Anga ndi
ana aakazi. Tidzayanjana mu choyera, ndi maso anu kuvalika ku tchimo lililonse.

Ndabweranso kwa inu monga mwamene ndi nakulailani kuti ndidzachita. Ndasunga Yanga Mawu kwa inu. Ine ndakhala nawo Mawu Anga atalembedwa pa tepi ya maginito kuti pasakhale kusamvetsetsana, popanda funso, Mawu anga abwino okha kwa inu; pakuti Iwo uli
Kukamba kwa M’buye.

Khalani ndi mumtima yanu choyera. Sungani mitima yanu yobisika. Yang’anani maso anu ophimbidwa ku zinthu za mdziko kuti akhale winawake wamkulu.

Osayiwala konse, ndidzatembenukira kumadzulo ndikupitamo anso, limodzi la masiku awa. Kufikira pamenepo, tenga Dzina Langa ndi iwe; Izo zidzakusangalatsani ndi kukupatsani inu chitonthozo, zitengeni izo, kulikonse inu komuyenda, pa kutyanka kuliza.

Osanyengerera pa Mawu amodzi. Mawu Anga pa tepi safunika kutanthauzira. Inu ndinu gawo la Ine, chikhumbo Changa. Dzikoli ndi Edeni wa Satana, koma ndakupangani kukhala Edeni Watsopano kumene tidzakhala pamodzi kwamuyaya. Kufikira pamenepo, gwirizanani pa Mawu Anga. Kondanani wina ndi mzake.

Bwerani mujoinane nawo ku Branham Tabernacle Lamlungu lino pa 12:00 P.M., nthawi ya Jeffersonville, ndi kumva Ine ndikuyankhula kupitila mwa mneneri Wanga wosankhidwa ndi kuwulula Mawu Anga pamene inu mukumva; Edeni wa Satana 65-0829. M’malo mwake,

M’bale . Joseph Branham

Malemba oti muwerenge:

2 Timoteyo 3:1-9
Chivumbulutso 3:14
2 Atesalonika 2:1-4
Yesaya 14:12-14
Mateyu 24:24