22-1218 Kodi Mulungu Amasintha Konse Malingaliro Ake Pa Mawu Ake?

Uthenga: 65-0418E Kodi Mulungu Amasintha Konse Malingaliro Ake Pa Mawu Ake?

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa A Mesiya,

Ndife odzozedwa a Mulungu; wodzozedwa ndi Mzimu Wake womwewo, mwa ntchito zomwezo, mwa Mphamvu zomwezo, mwa zizindikiro zomwezo. Zachoka ku mphungu kupita ku mphungu, zachoka kumawu kupita kumawu, Mpaka kuzulisisa kwa Yesu Kristu kwaonetsedwa mu thupi lathu lililonse, zakuthupi, zauzimu, kapena zofuna zilizonse zomwe tifuna. Mphamvu yofulumizitsa imeneyo ikukhala ndi kukhala mkati mwathu. Ndife a Mesiya a Mulungu.

Mlungu uliwonse Vumbulutso la Uthenga uwu; yemwe ife tiri, kumene ife tinachokera, ndi kumene ife tikupita,kunkala kwachikulu na chikulu. Ife tikudabwa ndi chiyembekezero chachikulu, Iwo angakhoze bwanji kukhala nawo ulemerero winanso? Zingakhale zomveka mochuluka bwanji? Koma ndi tepi yatsopano iliyonse imene timva, Mulungu amalankhula kwa ife milomo ndi khutu ndi kuwulula zambiri za Mawu Ake kwa ife, ndi kutitsimikizira ife,BAMENE IFE.

Chifunisiso chachikulu cha mtima wa wokhulupirira aliyense ndi kukhala mu CHIFUNIRO CHABWINO CHA MULUNGU. Sitikufuna kukhala mu chifuniro Chake chololera. Mitima yathu ndi yosweka ndipo timasweka ngati tiona kuti tachita chilichonse chimene sichingamusangalatse. Tikudziwa kuti Mulungu ali ndi Chifuniro Chabwino, ndipo tifuna kukhala mu PULOGALAMU YAKE YOFUNILA YOKWANIRI.

Mu moyo wanga, ndapanga kaimidwe kolimba ponena kuti ndikulupirira chinthu chofunikira kwambiri chomwe membala aliyense Mkwati angachite, onse wokunva ndi atumiki chimodzimodzi, bafunika KUTYANKA KULIZA. Ndikulupirira kuti Ndi Liwu LOKHA lotsimikizidwa la Mulungu la Tsiku lathu limene muyenera kumva ndi kukulupilila Mawu aliwonse.

Ine ndanena kuti ndikukhulupirira kuti atumiki ayenera kuti amuyike M’bale Branham mumbuyo mu maguwa awo ndi kuliza matepi mu mipingo yawo, popeza Ilo liri Liwu lofunika kwambiri lomwe anthu ayenera kumva.

Ndakhala ndikutsutsidwa kwambiri mumoyo wanga chifukwa choyimirira pazomwe ndimakhulupirira kuti ndi Pulogalamu Yake ndi Chifuniro Chanbwino. Zakhala zosamvetsetseka ndipo zinanenedwa kuti ine sindimakhulupirira mu atumiki asanu wa Aefeso 4.

Ndanena zambiri, nthawi zambiri zomwe ndi zabodza. Sindinanenepo, kapena kukhulupirirepo zimenezo. Pali ambiri omwe apidamula mawu anga ndikuuza anthu zinthu zomwe sindinanene kapena kuzikhulupirira, koma izi ziyenera kuziyembekezera.

Payenera kukhala Mawu a Baibulo Choonadi. Ngati inu mumadzinenera kuti inu mukukhulupirira Uthenga uwu, ndiye ife tiyenera kutenga zomwe mneneri ananena, popeza Iwo uli kutanthauzira komwe kwa Mawu a Mulungu. Pakuti iye ali wotanthauzira YEKHA wa Mawu amenewo.

Ngati tinafunsa aliyense wa inu, “Ndani akufuna kukhala m’chifuniro Chabwino cha Mulungu?”
Aliyense wa inu anganene kuti, “INDE, ndicho chofunisisa cha mtima wanga.” Chifukwa chake tiyenera kuyang’ana ku zomwe mneneri ananena kuti ndi Chifuniro Chabwino cha Mulungu.

WONANI: Ngati Uthenga wa pa tepi suli Mtheradi wanu, ndipo simukulupirira Mawu aliwonse, IMANI KUWERENGA KALATA IYI. Kwa ine, sindinu wokhulupirira, chifukwa chake si zanu. Ine ndikhoza kokha kukhala ndi zomwe Mulungu ananena pa tepi.

Ife tikufuna zomwe Iye ananena; osati zomwe mpingo unanena, zomwe Dokotala Jones ananena, zomwe winawake ananena. Ife tikufuna zomwe PAKUTI ATERO AMBUYE ananena, zomwe Mawu ananena.

Tiyenera kudzipereka tokha ku chifuniro Chake ndi Mawu Ake. Ife sitiyenera kufunsa Iwo. Ife tiyenera kukulupirira Izo. Osati muyesere kupeza njira yozungulira Izo. Tengani Iwo momwe Iwo aliri.

Ambiri amafuna kuyendayenda ndi kupita njira ina. Ngati mutero, Mulungu adzakudalitsani, koma mukugwira ntchito mu Chifuniro Chake cholekerera, osati mu chifuniro Chake chabwino, Chaumulungu. Mulungu adzakulekani inu kuti muchite chinachake, ndipo ngakhale akudalitseni inu pochichita icho, koma icho sichinali chifuniro Chake Chabwino.

Mulungu anatumiza mngelo wake wachisanu ndi chiwiri ku dziko lapansi kuti aitane Mkwati Wake. Ife tikuupirira kuti Uyo anali Mwana wa Munthu akudziulula Yekha mu thupi la munthu. Ndi Liwu lomwe la Mulungu limene lalembedwa ndi kusungidwa kwa Mkwati Wake.

Mulungu Mwiniwake anamuuza mneneri wake, ngati iwe upangitsa anthu kuti akukhulupirire INU, palibe chimene chidzakuimitseni. Iye anali amene anasankhidwa ndi Mulungu kuti atsogolere Mkwati Wake. Palibe amene angatenge malo ake. Ziribe kanthu kuti AKora angati auke bwanji, kapena a Datani angati, anali William Marrion Branham amene Mulungu anamuitana kuti atsogolere Mkwati Wake. Iyi ndi Pulogalamu la Mulungu ndi CHIFUNIRO Chake CHABWINO.

Ngati anthu sangayende mu chifuniro Chake Chabwino, Iye ali nako chifuniro chongololera Iye akulekani inu kuti muyendemo.

Tsopano, Mulungu ndi wabwino…Iye amatumiza Mawu Ake. Ngati inu simudzawakhulupirira Mawu Ake, ndiye Iye amaika mu Mpingo maudindo asanu osiyana: Choyamba, atumwi, aneneri, aphunzitsi, abusa, alaliki. Iwo ali akukwaniritsa Mpingo.

Motero, utumiki unakwezedwa chifukwa chakuti anthu m’mibadwo yonse sanavomereza PULOGALAMU YA CHIFUNIRO CHABWINO CHA MULUNGU; Mawu Ake olankhulidwa ndi mneneri Wake. Ife tiyenera kukhulupirira Mawu amene mneneri wa Mulungu analankhula. Sitifunikira wina aliyense kapena china chilichonse.

Ndiye ntchito ya atumiki ndi kubweretsa anthu kubwerera ku Pulogalamu la Chifuniro Chake Chabwino, lomwe ndi: KHALANI NDI MATEPI, CHIFUKWA CHILI CHIFUNIRO CHABWINO MULUNGU. Kenako sungani CHIFUNIRO CHABWINO PULOGALAMY patsogolo pawo nthawi zonse ndi: KUTYANKA KULIZA.

Inu muyenera kuti mubwerere ndi kuyamba pamene inu munayambira, kapena pamene inu munasiyira, ndi kutenga Mawu wonse a Mulungu.

Ndiye muyenera kuchita chiyani kuti mukhale mu CHIFUNIRO CHAKE CHABWINO: TYAKANI KULIZA.
Kodi abusa ayenera kuchita chiyani kuti akhale mu CHIFUNIRO CHABWINO CHAKE: TYAKANI KULIZA.

Kodi mneneri wa Mulungu anachita chiyani pamene anapita kumisonkhano? Kupempherera odwala, ndi zinthu monga izo? Iye amakhoza kunena zinthu mozungulira kuti nkhosa zimve izo, chifukwa ife tikudziwa chimene Iye akulankhula. Apo ayi, inali nyambo chabe pa mbedza. Iye anawasonyeza iwo zizindikiro monga kuzindikira za mumtima, ndipo ankadziwa zinsinsi za mitima yawo, kuti azingowakoka anthu. Koma kenako ananena kuti chofunika kwambiri chinali:

Chinthu choyamba chimene mukudziwa, tepi imalowa m’nyumba mwawo. Ndi zimenezo, ndiye. Ngati iye ali nkhosa, iye amabwera nayo pomwepo. Ngati iye ndi mbuzi, amathamangitsa tepiyo.

Ndiwe nkhosa kapena mbuzi? Gulu laling’ono la Mulungu lakhazikika pa Mawu amenewo. Tili mu Chifuniro Chake Chanbwino momwe Tikutyanka kuliza monga izo zinali, ndipo ziri, Pulogalamu Lake loyambirira.

Khalani bwino ndi Mawu Ake, chifukwa ndi zomwe ziti zidzatuluke pamapeto pake, Mawu, Mawu ndi Mawu. “Aliyense amene adzachotse Mawu amodzi kwa Iwo, kapena kuwonjezera liwu limodzi kwa Iwo!” Izo ziyenera kukhala, Mawu amenewo.

Ndine wothokoza kwambiri kwa Ambuye kudziwa, mwa Vumbulutso lauzimu, kuti ine ndiri mu Chifuniro Chake Chabwino molingana ndi Mawu Ake. Ine sindikuwonjezera kutanthauzira kwanga kwa Iwo, kapena kumvetsa kwanga kwa Iwo, koma kumva ndi makutu anga omwe chimene chiri PAKUTI ATERO AMBUYE ndi Chifuniro Chake Chabwino.

Ine ndikukuitanani inu kuti mubwere ndi kudzayendera nafe Lamlungu lino pa 2:00 p.m., nthawi ya Jeffersonville, pamene ife tikumva: Kodi Mulungu Amachinja Maganizo Ake Pa Mawu Ake? 65-0418E. Pali zabwino zambiri mu Uthenga uwu, inu mukhala ACHUMA mu Mzimu Wake Woyera tikamaliza.

Bro. Joseph Branham

Eksodo chaputala 19
Numeri 22:31
Mateyu 28:19
Luka 17:30
Chivumbulutso mutu wa 17