22-1211 Uku Ndi Kutuluka Kwa Dzuwa

Uthenga: 65-0418M Uku Ndi Kutuluka Kwa Dzuwa

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Tempele ya mphamvu,

Munthu wakhala ofunisisa mu mtima mwake kukhala ngati Abrahamu pamene anakhala kunyumba kwake cha m’ma 11:00. Atakweza maso anaona amuna atatu akubwera kwa iye anali nadoti ku zovala zawo. Iye anathamangira kwa iwo mwamsanga, ndipo anati, “Ambuye wanga.” Anayima pamenepo pamaso pake, mu thupi laumunthu akuyankhula, anali Melkizedeki Wamkulu.

Lamlungu lino, kufunisisa mu mitima yathu kudzachitika kwa aliyense wa ife. Ife tonse tidzasonkhana pamodzi kuchokera kuzungulira dziko, kumvetsera kwa Melkizedeki wamkulu yemweyo akuyankhula kwa ISE. Munthu wamene analibe bambo, wopanda mayi, wopanda chiyambi cha masiku kapena mathero a moyo, Mulungu, en morphe, amalankhula nafe kupitila mu milomo ya munthu, momwe Iye anachitira tsiku limenelo kwa Abrahamu.

Palibe njira ina yomvera Liwi pokhapokha kuchila KUTYANKA KULIZA. Sipanayambe pakhala nthawi mu mbiriyakale imene Mkwatibwi wakhala akulumikizidwa kuchokera kuzungulira dziko kuti amve Liwu la Melkizedeki likuyankhula pa nthawi yeniyeni yomweyi. Mulungu akugwirizanitsa Mkwatibwi Wake ndi Liwu limenelo.

Ife takhala nawo, kwa zaka, Mawu a Mulungu. Tsopano ife tiri naye Mulungu wa Mawu, mwaona, ndipo pomwe pano akukhala Mawu Ake. Kodi ndi zoona, chimodzi cha zizindikiro zazikulu zotsiriza zimene zalonjezedwa kwa Mpingo Kudza kwa Ambuye kusanachitike.

Lamlungu lino, Mkwatibwi adzakhala ndi Uthenga wa Isita mu Disemba; ndi Uthenga wake womwe ife titi tiumve.

Zimango. Mphamvu. Mphamvu yofulumizitsa. Khristu woukitsidwa. Anawonetseredwa Ana a Mulungu. Mzimu womwewo umene unakhala mwa Khristu ukhala mwa ife. Moyo womwewo, mphamvu zomwezo, opindula omwewo, omwe Iye anali nawo, ife tiri nawo. Ndemanga yachidule. Mbewu yoyamba imene inafika pa kukhwima ikuweyulidwa pamaso pa anthu. Ife tiri tsopano mnofu wa mnofu Wake, fupa la fupa Lake; Moyo wa Moyo Wake, Mphamvu ya Mphamvu Yake! Ndife Iye!

Yesu Kristu woukitsidwayo; Melkizedeki Mwiniwake, adzafuula ndi kutiuza ife, “Ine ndinali ndi Liwu langa litajambulidwa ndipo linaikidwa pa tepi ya maginito kotero kuti ine ndikhoze kukukokerani inu kwa ine, ndipo ine ndikanakhoza kuyankhula kwa inu monga momwe ine ndinachitira Abrahamu. Ndikufuna kuti mumve kuchokera kwa Ine mwachindunji.”

Inu ndinu Mpingo wanga wokonzedweratu, wokonzedweratu! Matupi anu ndiwo kachisi wa Mphamvu, chifukwa kuyambira pachiyambi inu munali gawo la Zimango.

Ndilo vumbulutso Lauzimu lija la Mawu opangidwa thupi. Ngati Iwo unali thupi mu tsiku limenelo mwa Mwana, Mkwati, Iwo ndi thupi lero mwa Mkwatibwi. Mwaona?

Mphamvu yofulumizitsa imeneyo ikukhala mwa ife. Sitiyenera kuopa kalikonse. Mzimu womwewo umene unali mwa Iye, tsopano uli mwa ife ndipo Iwo ukufulumizitsa thupi lathu lachivundi. Sitikuyembekeza choncho, TIKUDZIWA CHONCHO. Ife tinazipanga izo kale, Iye anatipangira izo.

Ndiye, kutsiriza masanawa, Melkizedeki adzayankhula kachiwiri ndi kunena;

Anthu awa, omwe ali mbadwa anzawo a Ufumu, eni ake a Mphamvu yofulumizitsa, afulumizitseni Izo kwa iwo, Ambuye, pakali pano. Ndipo mulole Mzimu upite kuchokera ku mphungu kupita kwa mphungu, kuchokera ku Mawu kupita ku Mawu, mpaka chidzalo cha Yesu Khristu chiwonetseredwe mu thupi lirilonse, kwa thupi, lauzimu, kapena chosowa chirichonse chimene iwo akuchifuna, pamene ife tikuyika manja athu pa modzi. wina. Mu Dzina la Yesu Khristu.

Kuchokera mphungu kupita kwa mphungu, Mawu kupita ku Mawu, chidzalo cha Yesu Khristu chidzawonetseredwa mu lirilonse la matupi athu. ULEMERERO!!

Izi zikhoza kuchitika kokha ndi KUDINISA KULIZA, kodi bwerani mudzajowine nafe ndi kudzatenga nawo gawo mu chisangalalo chazakudya pa Stored Up Food, pamene tikumva Liwu Lija, Lamlungu pa 12:00 p.m., nthawi ya Jeffersonville, kutibweretsera ife Uthenga, Ndiko Kutuluka Kwake. Dzuba 65-0418M.

Bro. Joseph Branham

Malemba

Levitiko 23:9-11
Mateyu 27:51; 28:18
Marko 16:1-2
Luka 17:30; 24:49
Yohane 5:24; 14:12
Machitidwe 10:49; 19:2
Aroma 8:11
1 Atesalonika 4:16
Ahebri 13:8
Chivumbulutso 1:17-18