All posts by admin5

ISITALA 2026- MWAMBO WA MGONERO WA PADELA NDI KUSAMBITSANA MAPAZI

Okondedwa Azanga Nzika Za Ufumu,

Isitala iyi ikulonjeza kukhala Isitala yayikulu kwambiri yomwe Mkwatibwi adakhalapo nayo. Ife Takhala tikukhala pamaso pa Mwana, tikucha, tikuzindikira kuti ndife ndani. Chidzalo cha Yesu Khristu chikupangidwa kuonetseredwa mwa wina aliyense wa ife pamene Mawu Ake, Liwu Lake, likufuula, kuchokera Kwa Mphungu yaikulu kupita kwa ti ana ta mphungu, kutiitana ife ku Mgonero Wathu wa Ukwati.

Chaka chilichonse nthawi ino Mkwatibwi amakhala pansi pa kuyembekezera kwakukulu kwa Isitala ilimkudza kumapeto kwa sabata. Nthawi yomwe Iye adzatigwirizanitsa kuchokera padziko lonse lapansi kwa masiku anayi mopitiliza, kumulambira Iye, kumuyamika Iye, kumutamanda Iye; chifukwa Iye wauka ndipo akukhala mwa wina aliyense wa ife. Mkwati ndi Mkwatibwi akukhala M’MODZI.

Iye akutipatsa ife nthawi yapaderayi kuti titsekere kunja zinthu zonse za dziko lapansi zomwe zatizungulira ife ndikukhala basi ndi Iye . Palibe zosokoneza za dziko lino, pamene tikupanga dziko lathu ndi Iye. Tsekani zitseko zathu, zimitsani zathu zonse zamagetsi ndi chilichonse chomwe chimatisokoneza kwa Iye.

Chikhumbo chachikulu chomwe wina aliyense wa ife ali nacho ndikukhala pafupi ndi Iye. Ife tikufuna kukhala moyo wodzipereka kwambiri kwa Iye; kukhala nthawi zonse mu chifuniro Chake changwiro. Kukhala okonzeka Kukubwera Kwake. Palibe chilichonse m’dziko lino, kapena m’moyo wathu, chofunika kwambiri kuposa ichi.

Iye watipatsa mwayi wapaderawu kuti tingokhala ndi Iye, kulankhula ndi kusinkhasinkha za Iye. Kukhala pamaso Pake ndikutsegula mitima yathu kwa Iye. IZO ZIDZAKHALA ZOSINTHA MOYO KWA MKWATIBWI WAKE!

Iye akudziwa kuti zingakhale zovuta kwa ena a inu omwe muli ndi ana, banja, ndi maudindo ena omwe tili nawo, koma ngati tigwiritsa ntchito mphindi iliyonse yaulere tiyenera kulankhula ndi Iye, kuyandikira kwa Iye, kutsegula mitima yathu kwa Iye, padzakhala kusintha kwakukulu mu kuyenda kwathu ndi Iye, mpaka sitidzakhalanso chimodzimodzi.

Monga momwe Iye adachitira m’tsiku la Mose pamene Iye adawakhazika ana Ake m’nyumba zawo, magazi anali atapakidwa ndipo anali kudzipangitsa Iwo eni kukonzekera Kutuluka kwawo; momwemonso sabata yapadera iyi ya Isitala yomwe Iye adakonza idzakhala ya aliyense wa ife.

Ulendo wathu udzakhala motere:

LACHINAYI

Unali Lachinayi usiku pamene Ambuye Yesu adadya Mgonero Womaliza ndi ophunzira Ake, pokumbukira Paskha asanatuluke ana a Israeli. Ndi mwayi waukulu bwanji womwe ife tili nawo wolankhulana ndi Ambuye m’nyumba zathu, kumapeto kwa sabata yathu yopatulika, ndikupempha Iye kuti atikhululukire ife machimo athu, ndi kutipatsa zonse zomwe tikufunikira paulendo wathu.

Atate Wakumwamba, tikuyamikira nthawi ino, nthawi inaso yosonkhana pamodzi, mbali ino ya Umuyaya. Ndipo ife tikuyang’anira m’mawa uno kuti mphamvu zatsopano zichokere kwa Inu, kutipatsa kulimba mtima paulendo womwe uli patsogolo. Ife tasonkhana monga momwe ana Achiheberi adachitira m’mawa kwambiri, kuti titenge mana omwe adaperekedwa kwa iwo usiku wonse, kuti awathandize tsiku lotsatira. Ife tasonkhana kuti tidye Mana a uzimu, m’mawa uno, kutipatsa mphamvu paulendo.

Tiyeni tonse tiyambe pa nthawi ya 6:00 PM. pa nthawi yanu yapafupi kuti mumve Mgonero 62-0204, kenako mneneriyo adzatitengera ku Utumiki wathu wapadera wa Mgonero ndi Kutsukana Mapazi ku m’maliziro a tepiyo, yomwe idzaseweredwa pa pulogalamu ya Lifeline (mu Chingerezi), kapena mutha kupanga dawunilodi utumikiwu mu Chingerezi kapena mu zilankhulo zina podina ulalo womwe uli pansipa.

LACHISANU

Tiyeni ife tipite ku pemphero ndi mabanja athu nthawi ya 9:00 AM, ndipo kenako nthawi ya 12:00 PM, kupempha Ambuye kuti akhale nafe ndikudzaza nyumba zathu ndi Mzimu Woyera pamene tikudzipereka ife eni kwa Iye.

Malingaliro athu abwerere m’mbuyo ku tsiku lija ku Kalvari, zaka zoposa 2000 zapitazo, ndikuwona Mpulumutsi wathu atapachikidwa pamtanda. Tiyeni tikumbukire mtengo waukulu umene Iye analipira chifukwa cha ife. Iye anali Mwana wa Mulungu wopanda uchimo, koma anayenera kuvutika monga momwe panalibe munthu wina aliyense akanavutikira, chifukwa machimo athu anaikidwa pa Iye.

Iye anayenera kumutumiza ku gehena wolangidwa (Mukuona?), chifukwa Iye ananyamula machimo athu. Ndipo Khristu anafa, osati wolungama; Khristu anafa wochimwa. Mukuona? Khristu sanachimwepo Iye mwini, koma Iye ananyamula machimo athu pa Iye.

Kenako pa 12:30 PM, tiyeni tilumikizane pamodzi m’nyumba zathu ndikunva 57- 0419 Ungwiro.

Kenako tiyeni tilumikizane pamodzi m’pemphero mwachangu nthawi yomweyo pambuyo pa utumiki, pokumbukira kupachikidwa kwa Ambuye wathu.

LOWERUKA

Tiyeni tonse tibwere pamodzi mu pemphero nthawi ya 9:00 AM ndi 12:00 PM, ndikukonzekeretsa mitima yathu zinthu zazikulu zomwe Iye adzatichitira pakati pathu.

Ine ndikumva Iye akunena kuti, “Satana, bwera kuno!” Iye ndiye Bwana tsopano. Akufikira, akutenga kiyi ya imfa ndi gehena m’mbali mwake, naipachika pambali Pa Iye Mwini. “Ine ndikufuna nditumikire kukudziwitsani inu. Mwakhala wonyenga kwa nthawi yayitali. Ine ndine Mwana wa Mulungu wamoyo wobadwa kwa namwali. Magazi anga akadali onyowa pamtanda, ndipo ngongole yonse yathunthu yalipidwa! Iwe Siwulinso ndi ufulu mkomwe. Iwe wavulazidwa. Ndipatse ine makiyi amenewo!”

Kenako nthawi ya 12:30 PM, tonse tidzasonkhana pamodzi kuti timve Mawu: 57-0420 Kuikidwa M’manda.

Ndi tsiku la KALATA YOFIWIRA kwambiri bwanji yomwe iyo ili kwa Mkwatibwi Wake padziko lonse lapansi.

Ndiye tiyeni tigwirizanenso pamodzi mu pemphero nthawi yomweyo utatha utumiki.

LAMULUNGU

Tiyeni tidzuke kaye m’mawa monga momwe M’bale Branham adachitira m’mawa pamene bwenzi lake laling’ono, phwiti, adamudzutsa iye nthawi ya 5:00 AM. Tiyeni ife tingoyamika Ambuye chifukwa choukitsa Yesu kwa akufa:

Masiku asanu m’mawa uno, bwenzi langa laling’ono lofiira linaulukira pawindo ndipo linandidzutsa ine. Zikuoneka kuti mtima wake waung’ono unaphulika, ndikunena, “Iye Wauka.”

Nthawi ya 9:00 AM tiyeni tigwirizanenso mu Tcheni chathu cha pemphero, kupemphererana wina ndi mnzake ndikukonzekera kumva Liwu la Mulungu.

Nthawi ya 9:30 AM, Ife tidzasonkhana pamodzi kuti timve Uthenga wathu wa Isitala: 65-0418M Ndi Kutuluka kwa Dzuwa.

Nthawi ya 12:00 PM tidzakweza mawu athu kwa Iye kumuyamika chifukwa cha Mphamvu Yofulumizitsa.

Nthawi ya 3:00 PM, tiyeni tigwirizanenso m’pemphero, kumuyamika chifukwa cha MAPETO A SABATA YODABWISTSA YOMWE IYE WATIPATSA IFE NDI IYE NDI MKWATIBWI WAKE KUZUNGULIRA DZIKO LONSE LA PANSI.

Kwa abale ndi alongo anga akunja, monga chaka chatha, ine ndikufuna kukuitanani kuti mugwirizane nafe pa nthawi ya ku Jeffersonville, nthawi zonse zamapemphero pa ndondomekoyi. Ine ndikuzindikira, komabe, kuti kusewera Matepi Lachinayi, Lachisanu, ndi Loweruka masana pa nthawi ya ku Jeffersonville kungakhale kovuta kwambiri kwa ambiri a inu, choncho chonde musazengereze kusewera Mauthenga amenewo panthawi yomwe ingakhale yoyenera kwa inu. Komabe, ndikufuna kuti tonse tigwirizane Lamlungu nthawi ya 9:30 AM, nthawi ya ku Jeffersonville, kuti timve Uthenga wathu wa Lamlungu pamodzi.

Ndikufunanso kukuitanani inu ndi ana anu kuti mukhale nawo m’mapulojekiti a Creations, kulemba manyuzipepala, ndi maphikidwe, omwe banja lanu lonse lingasangalale nawo limodzi. Tikuganiza kuti mudzawakonda chifukwa onse akuchokera pa MAWU omwe tidzakhala tikuva kumapeto kwa ndondomeko kwa sabata ino.

Zidziwitso pa za kakonzedwe ka mwambo wa mgonero , zinthu zomwe zidzafunike pa mapulojekiti a Creations, ndi zidziwitso zina, onani maulalo omwe ali pansipa.

Tiyeni ife titseke mafoni athu kumapeto kwa sabata ya Isitala kupatula kujambula zithunzi, kumvetsera Zobwereza Za Pa Tsiku, ndikusewera matepi kuchokera ku pulogalamu ya Table, pulogalamu ya Lifeline, kapena ulalo wopangidwa dawunilodi.

Iwo ndi ulemu waukulu kwa ine kukuitanani inu ndi banja lanu kuti mudzabwere pamodzi ndi Mkwatibwi kuzungulira padziko lonse lapansi kumapeto kwa sabata yodzaza ndi KUPEMBEDZA, MATAMANDO NDI MACHIRITSO. Ine ndikukhulupirira kuti ndikwenikweni ndi kumapeto kwa sabata komwe kudzasintha moyo wanu kwamuyaya.

M’bale Joseph Branham

26-0329 Kodi Melkizedeki Uyu Ndi Ndani?

Uthenga: 65-0221E Kodi Melkizedeki Uyu Ndi Ndani?

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi wa Moyo Wamuyaya,

Kodi Liwu limene likulankhula nafe pa matepi ndi ndani?

Ife tingathe kudziwa yankho la funso limenelo kudzera ku vumbulutso lochokera kwa Mulungu. Mkwatibwi Wake wokonzedweratu yekha ndiye amene adzakhala ndi Vumbulutso limenelo. Chifukwa chake, tiyenera kufufuza Mawu Ake kuti timvetse amene Iye anati anali ndani: Wotanthawuzira yekha wa Mawu Ake. Ndani angamatule ndi kuwulula Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri? Ndani angawulule zinsinsi zonse zobisika za m’Baibulo? Ndani adzaitana ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake? Ndani adzakhala ndi Liwu losalephera?

Malingana ndi Mawu, si wina koma Melikizedeki, Iyemwini. Munthu wopanda bambo kapena mayi, Amene analibe chiyambi kapena mapeto a masiku. Mulungu, Amene anakhala thupi ndipo anadya nyama ndi mkate wa chimanga, anamwa mkaka wa batala, ndipo analankhula ndi Abrahamu. Iye anali Munthu wokhala ndi umunthu, wokhala ndi thupi la munthu.

Mawu omwewo anati Melikizedeki, Munthu ameneyo, umunthu umenewo, adzakhala ndi moyo ndi kudziulula Yekha kachiwiri mu thupi la munthu monga momwe anachitira kwa Abrahamu, kenako kachiwiri mwa Yesu Khristu; koma lero, mu mthenga wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri wa Chivumbulutso 10:7. Mzimu Wake udzanyeketsa kachisi wapadziko lapansi kuti Iye athe kulankhula ndi kudziulula kwa Mkwatibwi Wake. Mulungu mwiniwake akukhala ndi kulankhula mu thupi la munthu. Mbewu yake yoyamba yobwezeretsedwa kwathunthu inali itacha mokwanira. Dongosolo lathunthu la Mulungu linafika; Mulungu ndi munthu anali Mmodzi. Mulungu anali kulankhula ndi Mkwatibwi Wake pakamwa ndikupita ku khutu monga momwe anachitira kwa Abrahamu.

Iye anadza mkati nakhala mmenemo, mwa Munthu wa Melkezedeki. Ndiye, kenako, ife sitinamvenso za Melkizedeki, chifukwa Iye anadzakhala Yesu Khristu. Melkizedeki anali Wansembe, koma Iye anadzakhala Yesu Khristu. Tsopano, inu munalidutsa ilo. Chifukwa, mmawonekedwe awo, Iye ankadziwa zinthu zonse, ndipo inu simunakhozebe kudziwa izo.

KOMABE…!! Ndiyeno Kodi ifeyo ndife ndani?

Maso athu, thunthu lathu, chilichonse chomwe ife tinali, tinali m’maganizo Ake pachiyambi. Pasanakhalepo Mngelo, nyenyezi, Kerubi, kapena china chilichonse. Iye anaganiza, Iye analankhula, ndipo ndife tili pano.

Uko ndi kusakhala nawo malire. Ife sitingakhoze kumvetsa izo mmaganizo mwathu, koma ndizo Mulungu. Mulungu, wopanda malire!

Pakuti tinali mwa Iye pachiyambi, kodi n’chiyani chomwe chimachitika kwa ife moyo wa padziko lino lapansi utatha?

Pamene mwinjiro wa thupi uwu wavulidwa, pali thupi lachibadwa, fiofane, thupi osati lopangidwa ndi manja, ngakhalenso kuti lobadwa mwa mkazi, limene ife timapitako.

Ndiye thupi ilo limabwereranso ndi kukatenga thupi la ulemerero.

Kodi ndi zinthu zodabwitsa zanji zomwe zili mu nkhokwe za Mkwatibwi Wake. Taonani zomwe zikuchitika pakali pano pamene Iye akuwululira Mawu Ake Kwa ife kuposa kale lonse. Kukamba za kalata yachikondi kwa Mkwatibwi Wake! Ndi tsiku lotani lomwe ife tikukhalamo.

Ife tili ndi Vumbulutso ndipo tikudziwa kuti ndi Melikizedeki, Liwu la Mulungu, likulankhula nafe pa matepi. Ife tili ndi Vumbulutso, ndi njira yoperekedwa ndi yangwiro ya Mulungu ya lero. Kotero, IFE TIMADZIWA YEMWE IYE ALI NDIPO NDIFE MKWATIBWI WAKE.

Vumbulutso limenero likukulirakulirabe tsiku lililonse. Tsiku lililonse likadutsa limatibweretsera chisangalalo chochuluka, vumbulutso lochuluka. Mkwatibwi akudzikonzekeretsa yekha pokhala pamaso pa Liwu Lake, pamene Iye akutiuza kuti Ife ndi ndani, mochuluka momwe Iye amatikondera Ife, momwe Iye sangathe kuyembekezera kukhala nafe!!!

Bwerani, dzikonzekeretseni nokha nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pa chomwe chikukonzekera kuchitika, pamene ife tikumvetsera Liwu la Melikizedeki.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 65-0221E “Kodi Melikizedeki Uyu Ndi Ndani?”

Malemba Owerenga:
Genesis Chaputala 18
Eksodo 33:12-23
Yohane Woyera 1:1
Aroma 8:1
2 Akorinto 5:1
1 Atesalonika 4:13-18
Timoteo Woyamba 3:16 / 6:15
Ahebri 7:1-3 /13:8
Chivumbulutso 10:1-7 / 21:16

26-0322 Chikwati Ndi Chilekano

Uthenga: 65-0221M Chikwati Ndi Chilekano

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wotengedwa, Wosankhidwa, ndinso Wokonzedweratu:

Ine ndikukumbukira pomwe ndinali mnyamata wachichepere ndikukula, ndikuyesera kusankha tepi yoti ndimvere. Pamene ndinali kuwerenga mitu yomwe ndimaganiza nthawi zonse, Ine sindinkafuna kumvera Chikwati ndi Chilekano, chifukwa zimenezo zinalibe chochita ndi ine; zinali za anthu okwatira okha.

Kenako tsiku lina, pamene ndimamvetsera Chikwati ndi Chilekano, Atate anandipatsa Vumbulutso la Uthenga umenewo. Kudzoza Kwake kunabwera mumtima mwanga. Iye akulankhula nane. Uthenga uwu NDI wa ine. Iye akundiuza ine kuti Iye anandisankha ine maziko a dziko la pansi asanakhazikitsidwe. Uwu ndi mwambo wa ukwati wanga. Ine Sindikufuna wina koma Iye. Ine ndine woona mtima komanso wokhulupirika kwa Iye, ndi Mawu Ake, ndi Liwu Lake, LOKHALO. Ife ndife M’MODZI.

Zoonadi Uthenga uwu unali kwa abale ndi alongo ambiri omwe anali okwatirana ndipo tsopano analekana, ndipo Iye anali kuwauza iwo chomwe anali kuyenera kuchita; koma panali tanthauzo la patali LOKWANIRA NDI LALIKULU kwambiri, lalikulu kwambiri, lamphamvu kwambiri.

Panali Mwamuna m’modzi, ndipo Iye anali kuyitana ndi kulankhula kwa Ake ambiri, mkwatibwi wosankhidwa. LIWU LA MULUNGU LINALI KUITANA WAKE WOYERA, WOSAWONONGEDWA, NAMWALI MKWATIBWI WA MAWU. Mmodzi amene sanakhudzidwe kapena kuipitsidwa ndi munthu. Mmodzi woona mtima komanso wokhulupirika kwa Iye ndi Mawu Ake okha. Mmodzi amene anakhutitsidwa kwathunthu ndi Iye ndi Mawu Ake.

Mwa Chisomo ndi Chifundo Chake, lero tinganene, popanda mthuzi umodzi wa kukayika, IFE NDIFE NAMWALI WAKE MKWATIBWI WA MAWU. ULEMERERO!!

Iye ankafuna kutsimikiza kuti sipadzakhala malire omasuka pankhani yoitana Mkwatibwi Wake, kotero Iye anabwera yekha ndikukhala m’thupi la munthu kuti awulule Mawu Ake ndikuitana Mkwatibwi Wake kwa Iyemwini. Iye anali Elieza amene akanasankha Mkwatibwi Wa Iyemwini.

Kuti titsimikizire kuti palibe njira yoti tisokonezedwe ndi amene anali kutifunsira ukwati, Iye mwini anatsimikizira chotengera chake chosankhidwa mwa kulankhula naye kuchokera mu mphepo yamkuntho yopachikidwa pamtengo. Kenako Iye analankhula naye moonekera pa Mtsinje wa Ohio pamaso pa anthu zikwizikwi.

Iye ngakhaleso anajambulidwa chithunzi chake pamodzi ndi Iye kotero onetsani ndi kuliwuza dziko lonse lapansi , INE NDINAKUWUZANI INU KUTI INE NDIKANADZABWERANSO NDI KUDZAKHALA NDI MOYO MU THUPI. IYE NDIYE AMENE INE NDINASANKHA KUKHALAMO NDI MOYO, KUTI NDIKUITANENI INU KUTI MUKHALE MKWATIBWI WANGA. SI IYE; NDI INE NDIKULANKHULA KUDUTSIRA MWA IYE. INE NDIKUNGOGWIRITSA NTCHITO LIWU LAKE KUTI LIKHALE LIWU LANGA KWA INU. INE NDIYE AMENE NDAKUYITANANI INU KUTI MUKHALE MKWATIBWI WANGA WANGWIRO.

Vumbulutso la Uthenga Uwu, Mawu Ake, Liwu Lake, ndipo tsopano chomwe amene IFE tili ndizopitirira mawu a munthu kuti ayesere kufotokoza. Ine ndikudziwa kuti inu mukudziwa chenicheni chomwe ine ndikunena. Kukwatulidwa mu Chikhulupiriro kukuchitika. Mkwatibwi akudzikonzekeretsa yekha pokhala mu mkupezeka kwa Mulungu Mwiniwake, kukhala wangwiro.

Ndi mwayi waukulu kwambiri wotani womwe dziko lapansi lili nawo womva Liwu la Mulungu likulankhula ndi iwo; kukhala pansi ndi kumvetsera Mawu pa Mawu pamene Iye akulankhula ndi kuwulula Mawu Ake ndikutiuza amene ife tili. Palibe china choponsa kukhala mumkupezeka Kwake, choncho bwerani mudzalumikizane nafe Lamlungu nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumumva Iye akulankhula ndi Mkwatibwi Wake, Uthenga, “Chikwati Ndi Chilekano” 65-0221M.

M’bale Joseph Branham

Malemba owerenga musanamve Uthenga:

Mateyu Woyera 5:31-32 / 16:18 / 19:1-8 / 28:19
Machitidwe 2:38
Aroma 9:14-23
Timoteo Woyamba 2:9-15
Akorinto Woyamba 7:10-15 / 14:34
Ahebri 11:4
Chivumbulutso 10:7
Genesis mutu 3
Levitiko 21:7
Yobu 14:1-2
Yesaya 53
Ezekieli 44:22

26-0315 Malo Osankhidwa Ndi Mulungu A Kupembedza

Uthenga: 65-0220 Malo Osankhidwa Ndi Mulungu A Kupembedza

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mayi Yesu Khristu,

Tsiku lija ndi Lero. Nthawi ija ndi ino. Mulungu anatumiza mphungu Yake ya mphamvu padziko lapansi kuti idzayitane Mayi Yesu Khristu Wake, kuti alankhule ndi kumuuza kuti, “Inu ndinu AMENE ine ndinasankha. Inu ndinu AMENE ine ndimakukondani.Inu ndinu namwali Mkwatibwi Wanga wa mawu angwiro ,Ife Ndife M’MODZI.”

Kungomva chabe mawu amenewo, mitima yathu imadumphadumpha ndi chisangalalo. Kuganiza, padziko lonse lapansi, ndi ma mamiliyoni ndi mamiliyoni a anthu ake ambirimbiri, pali Mayi Yesu Khristu MMODZI yekha, ndipo INUYO ndinu Iye, amene Iye akubwelera.  

Pali malo AMODZI okha osankhidwa opembedzera. Pali Uthenga UMODZI wokha wosankhidwa wangwiro. Pali MKWATIBWI WANGWIRO MMODZI YEKHA wosankhidwa…NDIPO NDI IFEYO CHIMENECHO!!

Atate ali ndi malo amodzi osankhidwa opembedzera, Ambuye Yesu Khristu; Iye ndiye Mawu. Lero, pali malo amodzi okha omwe imfa ya uzimu siyingakanthe: Mawu. Imfa siyingakanthe Mawu, chifukwa Ndi Mawu Amoyo a Mulungu.

Vumbulutso lonse lathunthu la Mawu Amoyo lavumbulutsidwa kwa Mayi Yesu Khristu okha. Pali malo amodzi okha osankhidwa kumene Mayi Yesu Khristu angapiteko ndikumva Mawu ANGWIRO OLANKHULIDWA. Pali mneneri mmodzi yekha wosankhidwa kukhala Mawu a Mulungu. Pali malo amodzi okha omwe Mayi Yesu angapiteko ndikumva, PAKUTI ATERO AMBUYE: KUKANIKIZA KUSEWERA.

Kudzakhala kuli Kuwala cha mu nthawi ya madzulo, malo okha osankhidwa ndi Mulungu kuti uzipembedzapo. O, kodi Uthenga uwu wafika ku chiyani, kodi Iye achita chiyani? Ndipo mu tsiku lake kudzakhala kuli Kuwala pa nthawi ya madzulo, ndipo (chiyani?) kuti awalandire ana Ake akubwerera kwawo ku Dziko loona lolonjezedwa, ndi chizindikiro chomwe chija cha Lawi la Moto limene linawatsogolera ana a Israeli kudutsa mu chipululu.

Kodi ndimosamala motani momwe Mkwatibwi Wake ayenera kukhalira kuti atsatire ndikumva Liwu la Mwamuna Wake likulankhula naye. Pali malo AMODZI okha omwe ife tingapite ndikukhala otsimikiza handiredi peresenti. Pali Liwu limodzi lokha lomwe ife tayika komwe tikupita Kwamuyaya wathu.

Mayi Yesu Khristu amakhulupirira kuti Mawu omwe iye amamva pa matepi ndi Mawu a Mwamuna Wake.Iye Amakhulupirira kuti Mawu Ake safunikira kutanthauzira. Chifukwa chake, iye amakhulupirira kuti pali malo AMODZI okha operekedwa omwe iye angapite ndi kunena AMENI ku mawu aliwonse.Liwu la Mwamuna Wake pa matepi.

Kamodzinso kena, Mayi Yesu Khristu, ochokera kuzungulira padziko lonse lapansi, akhozanso kunena kuti, “Lero, Mawu awa olankhulidwa, ali kukwaniritsidwa”.

Wokondedwa Mulungu, kutali komwe kuwoloka zipululu uko mu Tucson, kupita mpaka mu California, mpaka mu Nevada ndi Idaho, kupita mpaka cha Kummawa ndi kozungulira, kutsikira mu Texas; pamene kuitanira uku kuli kuperekedwa, anthu atakhala mkati—mu mipingo yaying’ono, malo omwetsera mafuta, mmakomo, akumvetseramo.

Inu muli kuitanidwa kuti mudzamvetsere ndi Branham Tabernacle nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tikumva Mulungu akulankhula ndi Mkwatibwi Wake wosankhidwa, Uthenga: “Malo Osankhidwa Ndi Mulungu Opembedzera” 65-0220.

M’bale Joseph Branham

Malemba Opatulika: Deuteronomo 16:1 mpaka 3

26-0308 Lero Lembo Ili Lakwanitsidwa

Uthenga: 65-0219 Lero Lembo Ili Lakwanitsidwa

PDF

BranhamTabernacle.org

Yokondedwa Mbewu Ya chifumu Yapamwamba,

Nthawi yomwe ife takhala tikuyiyembekezera mwachidwi komanso mofunitsitsa ndi ino. Ife tafika.Ife tikuwona iyo ikutambasulidwa pamaso pathu. Tsiku lililonse ulosi ukukwaniritsidwa, ndipo ife tinganene kuti: LERO LEMBA ILI LAKWANIRITSIDWA PA MASO PATHU.

Ndi kukondoweza Kwa Vumbulutso lotani likuchitika ndi mkwatibwi. Ndi Uthenga uliwonse womwe ife timamva, ife timamvelera mkatikati mwa mitima ndi miyoyo yathu, “Kodi izo zingatheke bwanji kukhala
zazikulu mulimosemo komanso zabwino kwambiri, Ambuye?” Kenako Iye amabwera pakati pathu kachiwiri ndikutidzoza ife pamene ife tikumva Mawu Ake akutiitana ife nati, “Inu ndinu Wokondedwa wanga. Ine ndinakusankhani inu kuti mukhale Mkwatibwi Wanga. Monga Ine ndinakulonjezani inu, Ine ndikubwera chifukwa cha Inu. Ine Ndili pa njira yanga. Posachedwapa Ife tidzakhala limodzi ku muyaya.”

Ife tikufuula kuchokera kuzungulira padziko lonse lapansi, tikukwera Kumwamba ndi ma haleluya athu, ma ulemerero, matamando, ndi kulambira kwa Iye. Satana wagonjetsedwa. Atate wachotsa kukayikira kwathu konse, kusatsimikizika kwathu konse, zonse zoganizira. Ife tikhoza kulengeza ndi mtima wathu wonse ndi moyo wathu wonse, Ife NDIFE Mbewu Yachifumu Yapamwamba ya Abrahamu. Mkwatibwi Wachifumu kwa Mwana wa mwamuna Wachifumu wolonjezedwa.

Kukhalapo kwa Ambuye kwakhala kodabwitsa kwambiri pamene Iye akutivumbulutsira Mawu Ake kuposa kale lonse. Iye wagwirizanitsa Mkwatibwi Wake ndi Mawu Ake, natiyika ife mu Maganizo amodzi ndi mgwirizano umodzi ngati gulu limodzi, kumvetsera Liwu La Mulungu likulankhula ndi kutipanga ife kukhala angwiro ndi Mawu Ake.

Uthenga uliwonse umene ife timava uli ngati chitsime cha kasupe chomwe chikuphulika mkati mwa miyoyo yathu; chikutuluka, chikukankhira, ndi kutumphukira kuchokera ku Mpando wa Chifumu wa Mulungu.Ife Tikumwa ndi kumwa ndi kumwa, kuyipangitsanso miyoyo yathu kukhala yatsopano.

Abale ndi Alongo Anga, Ife ndife kukwaniritsidwa kwa Malemba omwe amati Iye adzakhala ndi namwali Mkwatibwi wa Mawu. Ife ndife: Lero Lemba ili lakwaniritsidwa.

Mulungu Mwiniwake analankhula kuchokera Kumwamba kwa mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri nati, “Monga Yohane Mbatizi anatumizidwa kuti atsogolere Kubwera koyamba kwa Khristu, Uthenga wako udzatsogolera Kubwera kwa Iye kachiwiri, kudziko lonse lapansi.” Mkwatibwi anganene kuti: Lero Lemba ili lakwaniritsidwa.

Kodi ife tingamvetse kuti Liwu lomwelo la Mulungu lankhulidwa m’masiku athu ano kudzera m’milomo ya munthu, kujambulidwa, kusungidwa, ndi kusungidwira kuti iye athe kulankhula ndi aliyense wa ife, Pakuti Atero Ambuye? Iye wazipanga izo kukhala zotheka kuti ife sitimafunikila kuti tisatenge mawu a wina aliyense, osati malingaliro a wina, osati maganizo a wina, basi kungokhala pansi ndikumamvetsera Liwu Lake likuyankhula mwachindunji kwa ife Mawu Ake Oyera.

KODI CHOMWE CHIKUCHITIKA NDI CHIYANI LERO?

Ndipo M-w-a-n-a wa Mulungu yemweyo amene anabwera kummawa ndi kudzadzitsimikizira Yekha ngati Mulungu wowonetseredwa mu thupi, ndi M-w-a-n-a wa Mulungu yemweyo kumadzulo kwa dziko lapansi kuno, amene akudzizindikiritsa Yekha pakati pa mpingo usikuuno, yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Kuwala kwa kumadzulo kwa Mwana kwafika. Lero Lemba ili lakwaniritsidwa pamaso pathu.

KODI IFE TILI MU MCHIFUNIRO CHANGWIRO CHA MULUNGU PAKUNENA NDI KUKHULUPIRIRA: “KUSEWERA MATEPI NDI NJIRA YOPEREKEDWA NDI MULUNGU KWA MKWATIBWI WAKE”?

KODI PALI CHINTHU CHINANSO CHACHIKULU KUPOSA KUMVERA MATEPI?

Nthawizonse mu zitatu, monga ine ndinanenera usiku wathawu, Mulungu amaimiriridwa. Panali anthu Achisodomu, Aloti, ndi a Abrahamu. Izo ziri mmalo omwewo usikuuno, dziko lakhala monga chomwecho.

Zindikirani, Mmodzi amene anatsalira ndi Abrahamu anali Mulungu Mwiniwake. Awiri enawo anali amithenga a Mngelo.

TSONO KODI NDI NDANI YEMWE AKUYANKHULA NDI IFE PA MATEPI?

Ndiroleni ine ndikufunseni inu chinachake. Tayang’anani pa chikhazikitso ichi tsopano. Abrahamu anamutcha Munthu uyu amene ankayankhula ndi iye, “Elohim.” Liwu la Chihebri lakuti Elohim limatanthauza “Wokwanira Zonse Uja, Mmodzi amene ali Wamuyaya,” Elohim, Mulungu Mwiniwake!

KODI NDI KOFUNIKA MOTANI KUKANIKIZA KUSEWERA ?

…“tsiku lina Mzimu Woyera udzabwera ndipo akadzachita chinthu chomwecho, ndipo kudzanena mawu amodzi motsutsa Iwo sadzakhululukidwa nkomwe.” Limenelo ndi tsiku lino, limene Mawu aliwonse ayenera kukhala pamodzi. “Kuyankhula mawu motsutsa Iwo; sichidzakhululukidwa konse mdziko lino kapena dziko likudzalo.”

Ma aleluya athu a sabata yatha ndi kutamanda Ambuye zinali zongokonzekera za zomwe ziti zidzachitike Lamlungu lino, pamene Mkwatibwi akugwirizananso ndikumvetsera MULUNGU akutilimbikitsa ndi kutitsimikizira ife kuti ife ndife osankhidwa Ake, ndipo Iye akubwera posachedwa kuti atitengere ife ku Mgonero Wathu Waukwati waukulu, kenako kwathu kwa mtsogolo.

Ili ndilo tsiku limene AMBUYE adapanga; ife tidzakondwera ndi kusangalala nalo.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 65-0219 – “Lero Lemba Ili Lakwaniritsidwa”

Malemba:
Yohane Woyera Mutu 16
Yesaya 61:1-2
Luka Woyera 4:16

26-0301 Mbewu Sizilowa Ufumu Pamodzi Ndi Makoko

Uthenga: 65-0218 Mbewu Sizilowa Ufumu Pamodzi Ndi Makoko

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Namwali Mkwatibwi Wa Mawu,

Ine ndakhala pano m’mawa uno ndikumva kudzoza kumeneko pamene ndikumvetsera, kuwerenga ndikuphunzira Uthenga uwu umene Mkwatibwi adzamva Lamlungu. Thupi langa lonse ladzozedwa. Mtima wanga ukudzaza ndi chisangalalo chotelocho podziwa kuti, IFE TONSE TIDZASONKHANA PAMODZI KUCHOKERA PA DZIKO LONSE NDI KUDZOZA KOFANANA KOMWEKU. Ife Tidzakondwera, kutamanda Ambuye, nthawi imodzi, pamene IYE akulankhula ndi aliyense wa ife ndikuulula Mawu Ake.

Kudzoza kudzakhala kwakukulu kwambiri kotero kuti padzakhala kufuula ndi kukuwilira, “aleluya, ameni, lilemekezeke Dzina la Ambuye” padziko lonse lapansi nthawi imodzi, pamene tikukwera Kumwamba ndi matamando ndi kupembedza kwathu.

Kodi chidzakhala chikuchitika ndi n’chiyani? Mulungu adzakhala akugwirizanitsa ndi kulankhula ndi Mkwatibwi Wake.Ife tidzakhala Gawo limodzi, mu lingaliro limodzi ndi mgwirizano umodzi pamene Iye akudziulula ndi kudziwonetsera Yekha kwa ife.

Palibe malo akuluakulu omwe inu mungapiteko, palibe Liwu lalikulu lomwe inu mungamve; palibe kudzoza kwakukulu kuposa Liwu la Mulungu likulankhula nanu mwachindunji pa matepi.

Mulungu wakhala akuyang’anira Mawu Ake kuyambira pachiyambi ndipo wapereka malo omwe ana Ake onse angapiteko ndikumva Iye akulankhula ndikutanthawuzira Mawu Ake omwe. Malo omwe palibe kupenekera, chiyembekezo, kapena kudabwa; Iwo ndi malo operekedwa ndi Mulungu kuti mumve PAKUTI ATERO AMBUYE.

Zikakhala kuti izo Zavumbulutsidwa kwa inu, zimakhala ngati kuwala kwakukulu komwe kwayatsidwa mumtima mwanu ndi moyo wanu … Inu mumafuula, “icho ndi ichi. Ine Ndili kuchiwoona icho. Ine ndili MMODZI NDI MAWU. INE NDINE MAWU. INE NDINE MKWATIBWI. INE NDAFIKA.”

Icho Chikuchitika ndipo iwo sakudziwa. Ndi choncho. Mukuona? Inde bwana! Pakuti kumene kwafa nyama ndi kumene mphungu zidzasonkhana…?…Ndi zimene linanena. Kodi nyama yakufa kumene ndi chiyani? Mawu. Iye ndi Mawu, nyama yakufa, Khristu, Khristu mwa inu, yemweyo dzulo, lero ndi nthawi zonse. Izo zili zolondola bwanji!

Pamene ife tisonkhana kuti timve Mawu, zosamalira zathu zonse, nkhawa zathu zonse, mavuto athu onse, zimangotha momphweka. Ife timakondwera pamene tikuzindikira kuti ife tilibe chodela nkhawa nacho; ife ndife Mkwatibwi Wake. Iye siali nafe kokha, KOMA ALI MWA IFE. NDIFE MKWATIBWI WA MBEWU YA MAWU. Chilichonse ndi changwiro. Nthawi yake ndi yangwiro. Ife ndife angwiro.

Ife tili okhutira kwambiri ndi oyamikira kwambiri kunena kuti ife ndife Mawu Ake obadwa kwa namwali opangidwa kuwonetseredwa; Yesu Khristu yemweyo dzulo, lero, ndi kwa nthawi zonse, wokhala ndi moyo ndi kupezeka mkati mwathu. Aleluya!

Ife sitingathe kunyengelera pa MAWU AMODZI. Ife tiyenera kumva Mawu a Mulungu pa matepi.

Kodi inu munamuona mphungu akuvomerezera zosayenera? Ayi, bwana! Palibe zonyengerera mwa iye. Ndi momwenso Mkhristu weni weni amachitira. Iye siwolobodoka ayi. Amasaka mpakana atachipeza. Ameni. Inde, bwana! Iye mpakana atapeza chakudya chake. Iye amafuna manna atsopano. Adzafika pamenepo nakumba mpaka atachipeza Amauluka chokwera m’mwamba. Ngati sichiri m’chigwa chino, iye amakweranso m’mwamba pang’ono. Ukapita m’mwamba kwambiri, umaonanso kwambiri. Kotero ndi nthawi ya mphungu za tsiku lino kuti ziyambe kuuluka m’mwamba zedi, kukumba mu malonjezo a Mulungu, osati kumakhala moyo ndi chakudya cha akhwangwala chimene chinaphedwa zaka zapitazo. Tulukanimo m’menemo.

Khala okonzeka Mkwatibwi, ife tidzakhala tikudya Manna watsopano aja, titakhala pansi pa kudzoza kwakukulu komwe kulipo, Lamlungu lino nthawi ya 12:00 P.M, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tikumva: 65-0218 Mbewu Si ili Yolandira Cholowa Pamodzi Ndi Makoko.

Ife tikuitana Mkwatibwi kuchokera kuzungulira padziko lonse lapansi kuti adzalumikizane nafe kudya pa Njira Yangwiro Yoperekedwa ndi Mulungu ya lero. Malo okhawo kumene MKWATIBWI anganene kuti ameni ku Mawu aliwonse. Kumene kudzoza kwakukulu kwa Mzimu Woyera kumalankhula ndi kupangitsa Mkwatibwi Wake kukhala wangwiro mwa Kukanikiza Kusewera ndi kumva ndi kulandira Mawu Ake.

M’bale Joseph Branham

Malemba:
Mateyu Woyera 24:24
Luka Woyera 17:30
Yohane Woyera 5:24 / 14:12
Aroma 8:1
Agalatiya 4: 27-31
Ahebri 13:8
1 Yohane 5:7
Chivumbulutso 10
Malaki 4

26-0222 Munthu Kuthawa Pamaso Pa Ambuye

Uthenga: 65-0217 Munthu Kuthawa Pamaso Pa Ambuye

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Ana A Nkhosa,

Ndi ulemu waukulu komanso mwayi waukulu wotani kunena kuti, “Ndife ana a nkhosa a Mulungu, amene Iye anawatumizira mthenga wake wachisanu ndi chiwiri kuti adzaitane ndikudyetsa Manna Ake osungidwa ndi obisika.”

Ife tikukhutitsidwa ndipo tikukhulupirira kuti Uthenga uwu ndi Liwu la Mulungu lomwe latumizidwa kuti lifikilitse ku ungwiro Mkwatibwi Wake. Ife tikukhulupirira kuti mankhusu akuchoka ku tirigu, ndipo tsopano Mkwatibwi Wake akukhala munkupezeka kwa Mwana, KUKANIKIZA KUSEWERA kuti ache.

Ndipo ndi chimene ife tadzera pano, mzanga, kudzakhala Pamaso pa Mwana kufikira gulu lathu lapang’ono la anthu pano, kufikira litachera kwa Khristu, ilo nkusandulika mkate pa gome Lake. Ndi chimene ine ndikufuna kuti iwo achite.

Aliyense amene sakhulupirira kuti KUKANIKIZA KUSEWERA ndi kumva Liwu la Mulungu lotsimikiziridwa likulankhula kuti ndiye Mawu ofunikira kwambiri omwe muyenera kumva, ndi munthu amene akuthawa pamaso pa Ambuye.

Iwe uyenera kuti ukomane nacho icho, kapena kuchitapo chinachake cha izo. Inu muli nawo udindo, wina aliyense ali nawo, ndipo inu muyenera kukomanizana nazo zinthu izi.

Kodi chobwereza ichi ndi chowona komanso chofunikira bwanji masiku ano. Pali magawano ochuluka pakati pa oitanidwa ake a Mulungu. Kodi ndikofunikira kwambiri kusewera matepi mu tchalitchi kuti mumve Liwu la Mulungu, kapena kodi tsopano ndikofunikira kwambiri kuti utumiki ulalikire Mawu?

Mulungu waitana ndi kuyika utumiki pano kuti usunge Mawu pamaso pa anthu. Iwo ndi Abusa. Mawu amaphunzitsa izi. Iwo ayenera kulemekezedwa ndi kupatsidwa ulemu monga anthu omwe Mulungu wawaitana ndi kuwaika. Ife Sitingathe, ndipo sitiyenera, kunena kuti Iwo si Mkwatibwi. Zimenezo ndi ZOLAKWIKA ndipo sizikugwirizana ndi zomwe mneneri anatiphunzitsa ife. Ine Ndamvapo anthu akunena kuti: “Ngati iwo sakusewera matepi m’matchalitchi awo, iwo ndi otsutsa Mawu.” Inu simukuyenera kunena chinthu monga chimenecho. Zimenezo zikundiwonetsa ine kuti inu muli ndi mzimu wolakwika.

Ndamva ena akunena kuti, “Onse ayenera kumalumikizidwa ndi BT kapena Iwo sali mu chifuniro cha Mulungu”. Inu simukuyenera kunena chinthu monga chimenecho. Mulungu yekha ndiye amadziwa amene ali ndi amene siali Mkwatibwi. Umenewo si mzimu wa Mkwatibwi kunena zinthu monga zimenezo.

Ngakhale ena mwa anthu omwe akulumikizidwa ndi ku BT akunena kuti, “ngati inu mupita kutchalitchi kukamvera matepi ndi kusamavera mu m’nyumba mwanu inu mukulakwitsa!” Zimenezo si zoona abale ndi alongo. Ngati inu mukunena zimenezo, SIYANI, mukulakwitsa. Aliyense ayenera kuchita monga momwe IYE AKUMVELELA KUTSOGOZEDWA NDI AMBUYE MOMWE ACHITIRE.

Atumiki ambiri amaona kuti kulalikira ndiyo njira yoperekedwa ndi Mulungu lero. Ife timangowona zinthu mosiyana, ndiko kulondola. Kodi M’bale Branham ndimochuluka motani anapanga kufanizila uku pa zimenezi? Tamumva pa mafunso ndi mayankho, pamene anthu ankalankhula za M’bale Jackson kuti akulakwitsa, anawadzudzula ponena chilichonse chotsutsana naye ndi mpingo wake.

Ine ndikungolalikira mwa njira ya kalata iyi zomwe ine ndimakhulupirira kuti ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu ya Branham Tabernacle. Iwo ndi abale ndi alongo athu. Iwo amakonda Ambuye ndi Uthenga uwu. Umu ndi momwe amamvera kuti Ambuye akuwatsogolera. Ambuye alemekezeke.

Iwo amaziona izo mwanjira ina ndipo ife timazionaso mwa ina, Izo zilibwino. Ine sindingathe kuziona mwanjira yawo ndipo iwo sangaone yanga. Kwa ine, pali njira zambiri zomwe Mulungu wapereka, koma pali NJIRA IMODZI YANGWIRO, NDIPO KWA INE, NDIYO KUMAKANIKIZA KUSEWERA.

Ine ndikupemphera kuti musandive molakwika apa. Kusanjika manja ndi kupempherera anthu ndi zolondola ma peresenti handiredi molingana ndi Mawu. Kudzoza ndi mafuta ndi kupempherera odwala ndi Mawu a Mulungu molingana ndi Malemba. M’bale Branham analalikira ndi kutiphunzitsa ife tonse kukhala Mawu. Koma ine ndikufuna NJIRA YANGWIRO YA MULUNGU YOMWE IYE ANAYIPERELA …. INGOKHULUPIRIRANI CHIFUKWA MULUNGU ANANENA CHONCHO. Ndicho chimene ine ndikuyesetsa kuchita.

Koma tsopano pa machiritso, ndi chifundo cha Mulungu kuti IYE, “Ndi mikwingwirima Yake munachiritsidwa.” Tsopano, choyamba Mawu amanena choncho, zimenezo ziyenera kukhala zokwanira, koma ngati simukukhulupirira mu Mawu, ndiye kuti pali mphatso mu Mpingo, monga amuna omwe ali wodzonzedwa kudziwa momwe angaphunzitsire zimenezo, zomwe zidzapangitsa kuti zikhale zomveka kwa inu, ndiko kuti, ndi chikhulupiriro kukhulupirira.

Ine ndimakhulupirira mu utumiki wofutukuka pasanu. Ndimakhulupirira Mulungu anaitana anthu kuti azilalikira ndi kuphunzitsa Mawu. Koma, ine ndimakhulupirira kuti kumva Liwu la Mulungu pa matepi ndi NJIRA YANGWIRO KWA INE.

Pakumva matepi, ine sindiyenera kumvetsetsa, KUNGOKHULUPIRIRA MAWU ONSE AMENE INE NDIMAMVA. Palibe munthu, palibe mtumiki, palibe malo ena omwe ine ndingapiteko komwe ine ndimakhulupirira MAWU ONSE ndikuyika komwe ndikupita Kwamuyaya, koma matepi.

Kuyambira pachiyambi cha nthawi Mulungu sanapatse anthu ake mwayi ndi luso lodzimvera okha Mawu ake akulankhula milomo ndi khutu. Chinsinsi chilichonse chimawululidwa m’matepi. Funso lililonse limayankhidwa pa matepi. Chilichonse chomwe Mkwatibwi amafunika kuti akhale wangwiro chili pa matepi.

Mawu aliwonse olankhulidwa pa matepi ndi Mawu a Mulungu. Ine sindingamvetse kapena kufotokoza chilichonse, koma ine sindiyenera kutero. Amangofuna kuti ine ndinene AMEN KU MAWU ONSE, ndipo MATEPI ndi malo okhawo omwe ine ndingachite zimenezo.

Koma pamene—pamene iwe uyenera kuchita chinachake chosiyana, pamene iwe uyenera kuti uyime mmene iwe ukumverera kwa chimene iwe ukudziwa kuti ndicho Choonadi, apo ndi pamene pali gawo lovuta, apo ndi pamene kukhula kumabwera, pomwe apo.

Ine ndikukhulupirira kuti ndi zonse zomwe zili mwa ine, tili mu Chifuniro changwiro cha Mulungu ndipo ife tili m’chombo chopita ku Nineve. Ine ndikufuna kuti dziko lapansi libwere kudzayenda nafe pa chombo chathu ndi ife Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumva Mulungu akulankhula ndi Ana a nkhosa ake.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 65-0217 “Munthu Kuthawa Pamaso Pa Ambuye”

Malemba oti muwerenge:
Yona 1:1-3
Malaki 4
Yohane Woyera 14:12
Luka 17:30