26-0412 Kodi Mulungu Amasintha Konse Malingaliro Ake Pa Mawu Ake?

Uthenga: 65-0418E Kodi Mulungu Amasintha Konse Malingaliro Ake Pa Mawu Ake?

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Ofulumizitsidwa,

Momwe mitima yathu inakondwera monga Mphungu kumapeto kwa sabata ino ya Isitala. Tsiku ndi tsiku, kudzoza kwake kunali kukukulirakulirabe kwambiri. Mgonero, Kuikidwa m’manda, Ungwiro, kenako chimake chachikulu chomwe Iye anatiwumbirako: Ndikutuluka kwa Dzuwa…ULEMERERO, IYE WAUKA ndipo ali ndi moyo mwa aliyense wa ife. Iye anali kuulula Mawu Ake kwa aliyense wa ife monga momwe sitinamvepo kale. Kudzoza kunadzaza mitima yathu, kukhalapo kwake kunadzaza mlengalenga; zinkaoneka ngati Kukwatulidwa kunali pafupi.

Iye anatiuza zomwe zinachitika zaka 2000 zapitazo, kenako zomwe zinali kuchitika mu 2026. Yesu anali Mbewu yoyamba ya Tirigu wa Mulungu yomwe inaukitsidwa kwa akufa. Iye anaukitsidwa ndi Mphamvu ya Mulungu yofulumizitsa. Mulungu anafulumizitsa moyo Wake, anamuukitsa Iye kwa akufa, ndipo Iye anali zipatso zoyamba za iwo omwe anagona. Anali woyamba kufika kukucha, Mtolo wa Mulungu womwe unaweyulidwa ngati chikumbutso cha kuyamika Mulungu, kukhulupirira kuti enafe tidzabwera. Icho chinali chizindikiro.

KENAKO IYE ANATIWULULIRA ZIMENE ZILI KUCHITIKA LERO. Monga momwe Iye anaweyulidwa pa Tsiku la Pentekoste pamene kunamveka mkokomo wochokera Kumwamba ngati kuweyula, mphepo yamphamvu yothamanga ikuweyulira pa anthu. Inaweyulidwiranso pamwamba pa anthu monga momwe Iye analonjezera mu Luka 17:30 ndi Malaki 4, pamene M-w-a-n wa munthu adzawululidwa ndi kuweyulidwanso pa anthu.

Tsopano, Mwana wa munthu ndi Ndani? “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu. Ndipo Mawu anasandulika thupi, ndipo anadzakhala pakati pathu.” Ndipo ngati kuphunzitsa konse kumene ife tiri nako, ndi kutsimikizira kwa Mawu a Mulungu; mwa Mawu a Mulungu, mwa zizindikiro, ndi zodabwitsa, ife tikuziwona lero, kuti mu Bukhu la—la Luka apa, kuti monga ife tangobwereza kumene, kapena—Luka mutu wa 17 ndi ndime ya 30; ndi Malaki 4, ndi Malemba osiyanasiyana amene ife tikuwadziwa, kuti Mawu amenewo akuweyulidwanso pa anthu, kuti miyambo yakufa ya anthu yafa, ndipo Mwana wa Mulungu ali moyo kachiwiri ndi ubatizo wa Mzimu Woyera pakati pathu pomwe, ndipo akutipatsa ife Moyo.

Mzimu Woyera unapitirizabe kuweyulira ndi kuweyulirabe, kuulula ndi kuulula Mawu Ake… Mphamvu, machitidwe, Mphamvu yofulumizitsa…

Kenako, pamene zinaoneka ngati sizingakule kwambiri, Iye anatiuza kuti:

Iye anandilola ine kuyang’ana kudutsa katani, ndipo ine ndinakuonani inu nonse kumeneko. “Onse amene iwe unawakonda, ndi onse amene anakukonda iwe, iwo aperekedwa kwa iwe.” Mukuona? Ine ndinawawona iwo paliponse kumeneko monga choncho. Chinali chiyani chimenecho? Mphamvu Yofulumizitsa.

IYE ANATIONA IFE KUMENEKO!! Kupitirira katani ya nthawi….ife tinali KUMENEKO ndi iye; okondedwa athu onse omwe adatsogola…abambo, amayi, ana. Ife tidali nawo pamodzi ndi onse omwe sitinakumanenawopo: Mose, Eliya, Petro, Paulo….tinali tonse pamodzi.

Kenako, monga momwe basi wokondedwa Mzimu Woyera Iye ali wokongola, Iye sankafuna kutiiwala ife odwala, ovutika maganizo komanso omenyedwa, choncho Iye anadziweyula iyemwini pa ife kuti aliyense achiritsidwe ku chilichonse chomwe tinkachifuna.

Anthu awa, amene ali nzika zimzathu za Ufumu, eni a Mphamvu zofulumizitsa, fulumizitsani Iyo kwa iwo, Ambuye, pakali pano. Ndipo mulole Mzimu upite kuchokera kwa mphungu kupita kwa mphungu, kuchokera ku Mawu kupita ku Mawu, mpaka chidzalo cha Yesu Khristu chitawonetseredwa mu thupi lirilonse, ku zakuthupi, zauzimu, kapena chosowa chirichonse chimene iwo akuchisowa, pamene ife tikuyikana manja athu pa wina ndi mzake. Mu Dzina la Yesu Khristu.

Mawu amenewo. Liwu limenelo. CHILICHONSE chimene ife tikufuna chili pa matepi, Mkwatibwi. Mulungu sasintha malingaliro ake pa Mawu Ake. Palibe dontho limodzi kapena Mutu umodzi omwe ungasinthidwe, kotero Iye anapanga njira kuti Mkwatibwi Wake amve NDENDENDE ndi makutu awo chimene Iye amafuna alankhule Kwa iwo.

Mulungu walankhula ndi Mkwatibwi Wake ndipo wawulula CHILICHONSE. Izo zili zojambulidwa. Mkwatibwi ayenera kubwera kwa Mkwati; Iyo ndiyo njira Yake yangwiro yoperekedwa yomwe yapangidwira lero.Izo ndi PAKUTI ATERO AMBUYE.

Kodi Mulungu amasintha konse malingaliro Ake pa Mawu Ake? AYI. Iye ali ndi CHIFUNIRO CHANGWIRO NDI CHIFUNIRO CHONGOLOLERA. Mkwatibwi ayenera kukhala mu CHIFUNIRO Chake CHANGWIRO. Palibe Chifuniro changwiro china, kapena malo angwiro, kuposa kumva Liwu la Mulungu mwachindunji kuchokera kwa Mulungu Mwiniwake.

Kuitana kwanga kwa wina aliyense wa inu ndikuti mudzalumikizane nafe Lamlungu pa 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, kudzanva Liwu la Mulungu likutibweretsera Mawu Oyera. Palibe kufunikira koganizira, kungokhala kumbuyo basi ndi kumanena AMEN KU MAWU ALIWONSE….palibe malo ena omwe zingachitikire, ndi kokha mwa KUKANIKIZA KUSEWERA.

M’bale Joseph Branham.

Uthenga: 65-0418E — Kodi Mulungu Amasintha Konse Malingaliro Ake pa Mawu Ake?

Tiyamba ndi ndime 61.

Malemba Oti muwerenge musanamve Uthenga:
Eksodo mutu wa 19
Numeri 22:31
Mateyu Woyera 28:19
Luka 17:30
Chivumbulutso mutu wa 17