Category Archives: Uncategorized

26-0111 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko

Uthenga: 64-0802 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Wanga Kwambiri Wokomamtima.

Ine ndimakukonda iwe kwambiri. Iwe ndiwe mnofu wa mnofu wanga, ndi fupa la fupa langa. Ngakhale ndisanalenge nyenyezi, mwezi, chilengedwe changa chonse, ndinakuona iwe ndipo ndinakukonda iwe kenako. Ndinkadziwa kuti iwe unali gawo la Ine, mmodzi wanga komanso wokomamtima yekhayo. Iwe ndi ine tinali MMODZI.

Tsiku limene ine ndakhala ndikulilakalaka ndi kuliyembekezera kuyambira pamene ndinakuonani inu mapeto ake lafika.Tsopano ine ndikukuitanani inu ndikukugwirizanitsani inu kuchokera kummawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kum’mwera, ndi Liwu Langa. Inu ndinu malingaliro Anga, Mawu Anga, Mkwatibwi Wanga, opangidwa kuwonetseredwa.

Ine ndakhala ndikulakalaka kukuuzani inu chilichonse chomwe chili mumtima mwanga, kotero ine ndinazilemba izo mwa aneneri Anga ndipo ndinasunga Chilichonse kwa zaka zikwizikwi. Ambiri awerenga, ndipo akukhulupirira kwa zaka mazana ambiri, koma ndasunga zinthu zambiri zachinsinsi mpaka INU MUNAFIKA. Ndi inu nokha amene ine ndidzakuuzani.

Iwo ankafunitsitsa kudziwa ndikumva zinthu zodabwitsa zonsezi zomwe ndazisunga mobisa, koma monga momwe ndinakulonjezerani inu, ndakhala ndikuzisunga zachinsinsi mpaka pano, kuti zikhale za INU, MMODZI WANGA KOMANSO YEKHAYO.

Ine ndinakulonjezani inu kuti ine ndikanadzabweranso ndikudziulula ndekha mu thupi la munthu, kuti Ine ndikanakuuzani inu, ndikukuwululirani inu zinthu zonse izi. Ndimafuna kuti inu mumve LIWU LANGA likulankhula kwa inu mwachindunji.

Ine ndadzoza ena ambiri ndi Mzimu Wanga Woyera kuti akuuzeni inu za chikondi Changa, koma monga momwe ine ndakhala ndikuchitira nthawi zonse, ndipo ine sindingakhoze kusinthe, ine ndidasankha munthu m’modzi: Mngelo wanga, mneneri wanga, kuti akhale Liwu Langa kuti Ine ndikhoze kuyankhula Pakuti Atero Ambuye kwa inu.

Ine ndimafuna kukuuzani inu, inu simunapulumutsidwe pa tsiku linalake. Inu Munapulumutsidwa kwa nthawi zonse. Ine ndangobwera kudzakuwombolani inu. Munapulumutsidwa kuchokera pachiyambi chifukwa munali ndi Moyo Wamuyaya kuyambira pachiyambi. Chifukwa chake, m’maso mwanga, machimo anu onse sangawonekereso mpang’ono pomwe kwa ine, chinthu chokhacho chomwe ndimamva ndi liwu lanu. Ndimangoona choyimira chanu.

Momwe Ine ndimafunitsitsa kukuuzani inu zinthu zambiri. Mtima wanga ukudzaza ndi chisangalalo. Momwe Ine Ndikufunitsitsira kukhala ndi Mgonero Wathu wa Ukwati, Zaka Chikwi zathu pamodzi. Kuti ndikuuzeni mwatsatanetsatane zonse zokhudza Kwathu Kwamtsogolo; Momwe ndakukonzerani chilichonse cha inu, ndi chilichonse chokhudza chanu.

Wokomamtima wanga, ngati inu mukuganiza kuti ndi bwino tsopano kumvetsera Liwu Langa likulankhula kwa inu, tangodikirani, uwu ndi mthuzi chabe wa momwe zidzakhalire tikamakakhala mu Mzinda umenewo limodzi. Mneneri wanu adzakhala khomo loyandikira pafupi ndi inu; iye adzakhala wayandikana naye wa inu.

Ife tidzayenda m’misewu yagolide ndikumwa madzi ochokera ku kasupe pamodzi. Tidzayenda kupita ku pamaradaiso a Mulungu ndi Angelo akuzungulira dziko lapansi, kuimba nyimbo za zafuko…Ndi tsiku lotani!

Ine ndikudziwa kuti msewu umaoneka wothyokathyoka, ndipo nthawi zina zimakhala zolimba Kwa inu , koma udzakhala wochepa kwambiri, wochepa kwambiri, pamene tikukhala limodzi wina ndi mzake.

Tsopano, ine kamodzinso ndikusonkhanitsaninso inu ndi kulankhula nanu Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi yaku Jeffersonville, ndikukuuzani zonse za “64-0802 Kwawo Kwamtsogolo kwa Mkwati Wa Kumwamba ndi Mkwatibwi Wapadziko Lapansi”. Ine Sindingathe kudikira kuti ndikhale nanu nthawi imeneyo kenako.

Kumbukirani, ndipo musaiwale, ndimakukondani inu kwambiri.

M’malo mwa Iye,

M’bale Joseph Branham

Malemba:
Mateyu Woyera 19:28
Yohane Woyera 14: 1-3
Aefeso 1:10
2 Petro 2: 5-6 / Mutu Wachitatu
Chivumbulutso 2: 7 / 6: 14 / 21: 1-14
Levitiko 23:36
Yesaya Mutu Wachinayi / 28: 10 / 65: 17-25
Malaki 3: 6

26-0104 Zitsime Zong’aluka

Uthenga: 64-0726E Zitsime Zong’aluka

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Omwa Pa Chitsime Cha Kasupe

Ndi Khirisimasi ndinso Zaka za tsopano zotani zomwe ife takhala tili nazo. Talandira ndikutsegula mphatso za Mulungu zomwe adatumiza kwa Mkwatibwi Wake. Mphatso yathu yoyamba inali Mphatso yayikulu kwambiri ya Khirisimasi yomwe idakulungidwapo. Mulungu Mwiniwake adakulunga Iye mwini mu thupi la munthu ndipo adatumiza phukusi limenelo kudziko lapansi. Inali Mphatso Yake yoyamba yayikulu yobwezeretsa Mkwatibwi Wake.

Kenako Mulungu adatumiza phukusi lina lalikulu kwa Mkwatibwi Wake. Iye Anatikonda ife kwambiri kotero kuti Iye anabwera nadziulula Yekha mu thupi kachiwiri kuti Iye athe kulankhula nafe pakamwa ndi Kupita ku khutu. Anafuna kuti Iye ndi Mkwatibwi Wake akhale Mmodzi.

Ndipo tsopano, abwenzi, musati mundive ine molakwika.Ine nditi ndinene izi ndi ulemu mumtima mwanga, podziwa kuti ndine munthu womangirilidwa ku Kumuyaya amene ndidzayima mu mchiweruzo tsiku lina: Anthu zikwizikwi akuyiphonya mphatso yawo. Mukuona? Iwo sangathe kuyimvetsa iyo. Ndipo iwo akuyiyang’ana, ndipo nanena, “O, iye ndi munthu chabe.” Izo Ndi zoona. Kodi iye anali Mulungu kapena Mose amene anapulumutsa anthu? Iye anali Mulungu mwa Mose. Mukuona? Iwo Analirira kwa mpulumutsi. Ndipo pamene Mulungu anatumiza mpulumutsi kwa iwo, iwo analephera kuchiwona icho, chifukwa icho chinali mwa munthu, koma sanali munthuyo, anali Mulungu mwa munthuyo.

Lero, kachiwiri, anthu zikwizikwi akuyiphonya mphatso yawo ndipo akunena kuti, “Inu simukuyenera kumvera matepi, tsopano pali amuna ena odzozedwa,” zomwe ndi zoona, koma iwo akulephera kuzindikira kuti ilo ndi Liwu LOKHALO lotsimikiziridwa ndi Mulungu , likulankhula Pakuti Atero Ambuye kudzera mwa munthu ameneyo. Liwu limenelo ndi Yurimu Tumimu wa Mulungu, Mtheradi Wake wa lero.

Pamene ife tikumvetsera Liwu Lake pa matepi ife kwenikweni timakhala kuti tikumwa kuchokera ku Chitsime cha Kasupe wa Mulungu, chomwe sichifuna sichifuna kupopa, sichifuna kukoka, sichifuna kujoyina, kapena sichifuna kugwedeza; ife tikungokhulupirira ndi kupumula pa Mawu aliwonse olankhulidwa.

Pa kumvetsera Liwu limenelo pa matepi, malingana ndi Yesu Mwiniwake, ife tili nawo umboni weniweni wa Mzimu Woyera mtsiku lathu.

Kotero pamenepo pali umboni weniweni wa Mzimu Woyera! Iye sanayambe wandiuzapo ine chirichonse cholakwika panobe. Iwo, “Uli umboni wa Mzimu Woyera, ndi iye yemwe angakhoze kukhulupirira Mawu, ngati inu mungakhoze kuwalandira Iwo.

Mulungu wapereka Kasupe amene ife tingamwe kuchokera Kwa iye mphindi iliyonse ya tsiku lililonse. Nthawi zonse amakhala watsopano. Si chinthu chinachake choyima, Iye ndi Kasupe Wake wosaguga, wodzithandizira yekha; inu mukungoyenera Kukanikiza kungosewera.

Kunena za MPHATSO yochokera kwa Mulungu, kodi inu mungaganizire momwe Mphatso iyi kwenikweni ili YAIKULU? Mu mkuphweka pa Kukanikiza kungosewera ndi kumvetsera ku Liwu Lake pa matepi, ndiye lokhalo…LIWU LOKHALO padziko lapansi lomwe inu simukufunaso fyuluta, sefa, kapena china chilichonse.Inu muyenera kungomvetsera, kukhulupirira, ndi kunena ameni ku Mawu onse.

Mulungu mwiniwake wapereka njira iyi, NJIRA YAKE YOKHAYO, yolandililako moyo wosatha, komanso ngakhale chofunika kwambiri, KUKHALA MKWATIBWI WAKE. Tikhoza kungogona pachifuwa Chake ndi kuyamwa mphamvu zathu pomvera Kasupe Wake, Liwu Lake, El Shaddai akulankhula ndi Mkwatibwi Wake.

Chaka chino chikhale chaka chomwe Iye akubwera kwa ife, Mkwatibwi Wake wokondedwa. Ife Tikuyang’anira ndi kuyembekezera ndi chiyembekezo chachikulu. Tsiku lililonse tsopano tidzayang’ana omwe takhala tikulakalaka kuwawona akuwonekera. Ife Tidzazindikira, mu mkutwanima Kwa diso chabe, kuti tidzachoka pano, kuyitanidwa ku Mgonero Wathu wa Ukwati.

Ambuye, pamene ife tidzawona gome lalikulu ilo litayikidwa kunja uko, ku mgonero umenewo, mailosi zikwi utali wake; kuyang’anizana pa gomelo kwa wina ndi mzake, ankhondo akale a zipsyera, misozi ya chimwemwe ikutsikira pansi pa masaya athu. Mfumu kutulukira uko, kukongola Kwake, chiyero, kuyendera pansi motsatira gomelo, ndi kutenga manja Ake Omwe ndi kumaipukuta misonzi kuichotsa pa maso awo, akuti, “Musati muziliranso. Zonse zatha. Lowani mu zisangalalo za Ambuye.” Zovutikira za ulendo sizidzawoneka ngati kanthu pamenepo, Atate, pamene ife tidzafika pa mapeto a ulendo.

Bwerani ndipo mudzamwe, mudzamwe ndipo mudzamwe kuchokera ku Kasupe woperekedwa ndi Mulungu lero ndi ife Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville. Iwo ndi malo okhawo omwe inu mungathe kupumulirako mokwanira ndikunena AMEN ku Mawu aliwonse omwe mukumva. Ndi chitsime chake cha Kasupe choperekedwa kwa Mkwatibwi Wake kuti amwe kuchokera ku icho.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 64-0726E Zitsime Zong’aluka
Malemba oti muwerenge musanamve Uthenga:
Masalmo 36:9
Yeremiya 2:12-13
Yohane Woyera 3:16
Chivumbulutso Mutu 13

25-1228 Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake

Uthenga: 64-0726M Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wodulidwa,

Lero lino, mpingo wayiwala mneneri wawo. Iwo Samufunanso Iye mpang’ono pomwe kuti azilalikira m’matchalitchi awo. Iwo amanena kuti ali ndi abusa awo kuti aziwalalikira iwo ndi kumatchula mobwereza mawu ndi kumasulira Mawu. Kulalikira n’kofunika kwambiri kuposa kumvetsera liwu la Mulungu pa matepi m’matchalitchi awo.

Koma Mulungu Iye ankadziwa kuti ankayenera kukhala ndi mneneri Wake; mmenemu ndi momwe nthawi zonse Iye amaitanira ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake. Iye anatidula kuchokera m’mitundu yonse ndi Lupanga Lake lakuthwa konsekonse, Mzimu Wake Woyera, Liwu Lake loyankhulidwa ndi mneneri Wake.

Iye watidula ife ndi Liwu limenelo. Ndicho chifukwa chake Iye analijambula ilo ndi kuliyika pa tepi. Mwa Vumbulutso ife timawona momwe Malemba alili angwiro! Mkwatibwi sangache pokhapokha Mwana atamuchetsa iye.

Ziribe kanthu ndi mochuluka bwanji momwe inu mungalalikire, chirichonse chimene inu mungachite, icho sichingakhoze kucha, icho sichingawonetseredwe, icho sichingatsimikiziridwe; kokha ndi Iye Amene anati, “Ine ndine Kuwala kwa dziko lapansi,” Mawu.

Mawu adatiuza ife kuti Mzimu Woyera mwiniwake adzabweranso ndi kudzatichetsa ife, kudzatsimikizira, kudzasonyeza umboni ndi kudzadzipanga Iyemwini kudzadziwonetsera. Kuwala kwamadzulo kwafika. Mulungu akudzionetsera yekha mu thupi kuti ayitane Mkwatibwi Wake.

Iye ndiye amene wakuitanani INU ndi Mzimu Wake Woyera, Mawu Ake, Liwu lake. Iye ndiye amene anakusankhani INU. Iye ndiye amene akukuphunzitsani INU. Iye ndiye amene akutsogolerani INU. Ndi chiyani? Mzimu Wake Woyera, Liwu Lake likuyankhula MWACHINDUNJI KWA INU.

Koma izo ndi zakale kwambiri kwa iwo lero lino. Iwo sangakhoze kusewera matepi m’matchalitchi awo. Iwo Sakuzindikira. Ndicho chifukwa chake ali mu mkhalidwe womwe ali. Koma kwa inu, izo zawululidwa kuti ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu, IZO NDI PAKUTI ATERO AMBUYE KWA INU.

Chotero pakuyenera kubwera a—a—a Mphamvu, Mzimu Woyera Mwiniwake, kuti udzachetse, kapena kutsimikizira, kapena kudzatsimikizira, kapena kudzawonetsera icho chimene Iye ananeneratu kuti chikanadzachitika mu tsiku lino. Kuwala kwa kumadzulo kukupanga zimenezo. Ndi nthawi yotani!

Ife ndife Mkwatibwi wangwiro wa Mawu a Mulungu amene mneneri wake anaona mu masomphenya. Ife ndiwo amene Iye anatumiziridwako mneneri wake kuti awaitane ndi Mawu ake, ndipo iwo tsopano akukhala ndi CHITSITSIMUTSO, chifukwa tsopano ife tikudziwa chimene ife tiri.

Kutsitsimutsa, apo, ndi mawu omwewo amene amagwiritsidwa ntchito kwina kulikonse, ine ndinangowayang’ana iwo, amatanthauza, “chitsitsimutso.” “Iye adzatitsitsimutsa ife akadzatha masiku awiri.” Izo zidzakhala, “Patsiku lachitatu Iye adzatitsitsimutsanso ife, Iye atatibalalitsa ife, ndi kutichititsa khungu, ndi kuting’amba ife.”

Atate anatuma mneneri wake kuti ayang’anire Mkwatibwi wake kuti tisachoke pa mzere. Kumbukirani, awa anali masomphenya!

Mkwatibwi anadutsa malo omwewo amene Iye anali pamene Iye anali pachiyambi. Koma ine ndinali kumuwona Iye akuchoka pa sitepe, ndi kumayesera kumukokera Iye mmbuyo.

Koma kodi “iye” angamukokere m’mbuyo bwanji lero? “Iye”, mwamunayo, sali pano padziko lapansi. NDI MAWU! Kodi Mawu OKHA Otsimikiziridwa a lero ndi ati? Liwu la Mulungu pa matepi.

Atumiki ai oyitanidwa kulalikira Mawu potchula mobwera zomwe mneneriyo ananena. Malinga ndi mneneri mwiniwake, iwo sayenera kunena china chilichonse mochuluka

Zoonadi, aIi oyitanidwa kuphunzitsa ndi kulalikira Mawu amenewo. Koma pali LIWU LIMODZI LOKHA LOMWE NDILOTSIMIKIZIRIDWA NDI MULUNGU IYEMWINI KUTI NDILO PAKUTI ATERO AMBUYE.

Chotero ine ndikunena, mu Dzina la Yesu Khristu! Musati inu muwonjezere kanthu kamodzi. Musati mutenge, kuyika malingaliro anu omwe mwa Iwo. Inu muzingonena chimene chikunenedwa pa matepi awo. Inu muzingochita chimodzimodzi chimene Ambuye Mulungu wakulamulirani kuti muchite. Musati muwonjezere kwa Iwo.

Ngati inu munena kuti “ameni” pa mawu aliwonse amene m’busa wanu kapena mtumiki wanu akunena, inu mwatayika. Koma ngati munena kuti “AMENI” PA MAWU ALIWONSE AMENE MULUNGU ANAYANKHULA KUDZERA MWA MNENERI WAKE PA MATEPI, INU NDINU MKWATIBWI NDIPO MUDZAKHALA NDI MOYO WOSATHA.

Mneneri wa Mulungu anali munthu amene Mulungu anasankha kulankhula kudzera mwa iye. Kunali kusankha Kwa Mulungu kumugwiritsa ntchito iye kulankhula Mawu Ake ndikuwayika pa matepi kuti Mkwatibwi nthawi zonse akhale ndi PAKUTI ATERO AMBUYE WOTI AZIMVERA.

Iye sakufuna kuti Mkwatibwi Wake azidalira zomwe anthu ena akunena, kapena kutanthauzira kwawo Kwa Mawu Ake. Iye akufuna kuti Mkwatibwi Wake azimva kuchokera pakamwa pake kupita m’makutu mwawo. Iye sakufuna kuti Mkwatibwi Wake azidalira wina aliyense koma Iyemwini.

Ife tikadzuka m’mawa, timakonda iye kuti atiuze ife kuti, “Mmawa wabwino abwenzi. Ine Ndilankhula ndi inu lero ndikukuuzani momwe ine ndimakukonderani inu komanso momwe inu ndi ine tili AMODZI. Ndili ndi ambiri omwe ndidzawapatse moyo wosatha, koma INU nokha ndinu Mkwatibwi wanga wogwiridwa pa dzanja. INU nokha ndi amene ine ndapereka Vumbulutso maziko adziko asanakhazikitsidwe .

Ambiri amakonda kundimva, koma ine ndakusankhani inu kuti mukhale Mkwatibwi Wanga. Pakuti mwandizindikira Ine ndipo mwakhala ndi Mawu Anga. Inu Simunanyengerere, simunasewere, koma mwakhalabe okhulupirika ndi Mawu Anga.

Nthawi yayandikira. Ndikubwera kudzakutengani posachedwa. Choyamba, mudzawona omwe ali kale ndi ine tsopano. O, momwe iwo akufunira kukuonani inu ndikukhala nanu. Musadandaule ana aang’ono, chilichonse chili pa nthawi yake, basi pitirizani kumenyera.”

Monga mtumiki wa Uthenga, ine sindingathe kuwona chinthu chimodzi chatsalira koma kupita kwa Mkwatibwi.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 64-0726M “Kulizindikira Tsiku Lanu ndi Uthenga Wake”
Nthawi: 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville

Malemba oti muwerenge musanamve Uthenga:
Hoseya: Chaputala 6
Ezekieli: Chaputala 37
Malaki: 3:1 / 4:5-6
II Timoteo: 3:1-9
Chivumbulutso: Chaputala 11

25-1221 Kupita Kuseri Kwa Msasa

Uthenga: 64-0719E Kupita Kuseri Kwa Msasa

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Wachikondi,

Mulungu samasintha. Mawu Ake samasintha. Pulogalamu yake simasintha. Ndipo Mkwatibwi Wake samasintha, Ife tidzakhala ndi Mawu. Iwo ndi oposa moyo kwa ife; iwo ndi Kasupe wa Madzi amoyo.

Chinthu chokha chomwe ife tapatsidwa ntchito ndikumva Mawu, omwe ndi Mawu a Mulungu otsimikiziridwa omwe adajambulidwa ndikuyikidwa pa matepi. Chinthu chokha chomwe timawona si chikhulupiriro, osati gulu la amuna, sitiwona china chilichonse koma Yesu, ndipo Iye ndiye Mawu opangidwa kukhala thupi mu masiku athu ano.

Mulungu ali mu Msasa wathu ndipo tili panjira yopita ku Ulemerero motsogozedwa ndi Lawi la Moto, lomwe ndi Mulungu Mwiniwake akulankhula kudzera mwa mneneri wake wotsimikiziridwa wa Malaki 4. Tikudya Mana wobisika, Madzi amoyo omwe Mkwatibwi yekha ndi amene angadye.

Mulungu sasintha njira zake, koteroso mdierekezi sasintha njira zake. Zimene adachita zaka 2000 zapitazo, akuchita zomwezo lero, kupatula kuti ali wa mphavu kwambiri.

Tsopano, zitatha zaka foro handiredi, Mulungu anadzayenda kumene pakati pawo tsiku lina. Molingana ndi Lemba, Iye anali woti adzasandulike thupi ndi kudzakhala pakati pawo. “Dzina Lake azidzatchedwa Wauphungu, Kalonga wa Mtendere, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha.”
Ndipo pamene Iye anadzabwera pakati pa anthuwo, iwo anati, “Ife sitimulola kuti Munthu uyu azitilamulira ife!

Potengela ndi Malemba, Mwana wa Munthu adzabweranso ndi kukhala ndi moyo ndi kudziulula Yekha mu thupi la munthu, ndipo Iye anachitadi zimenezo, ndipo iwo akunena zomwezo. Inde, iwo amakamba mobwereza ndi kulalikira Uthenga, koma Iwo samalola munthu ameneyo kuwalamulira iwo.

Izi ndizo kwenikweni zomwe zili kuchitika :

Ndipo monga zinaliri kumeneko, chomwechonso izo ziri tsopano! Baibulo linati mpingo wa Laodikaya ukanadzamuika Iye panja, ndipo Iye anali akugogoda, akuyesera kuti alowe mkati. Pali chinachake cholakwika penapake.
Tsopano, bwanji? Iwo anali atapanga msasa wawo wawo.

Munthu anganene kuti, “Ine ndikudziwa ndipo ine ndimakhulupirira kuti M’bale Branham anali mneneri. Iye anali mngelo wachisanu ndi chiwiri. Iye anali Eliya. Timakhulupirira Uthenga uwu. Kenako iye ndikupanga mtundu wina wakunyozela, Iwo angakhale uliwonse womwe ulipo, osasewera Liwu LOKHA LOTSIMIKIZILIDWA la Mulungu mu mpingo wawo… Pamenepo pali chinachake cholakwika penakwake. Tsopano, ndi chifukwa chiyani? Iwo adapanga msasa wawo.

Ine ndikunena zinthu izi kuti osati kuti tilekanitse mpingo iyayi, Mawu a Mulungu ndi emene amachita zimenezo. Ine ndikufuna kuti ife tonse tigwirizane pamodzi, tikhale CHINTHU CHIMODZI wina ndi mnzake komanso ndi Iye, koma pali njira imodzi yokha yochitira zimenezo: mozungulira Liwu la Mulungu pa matepi. Ameneyo ndiye PAKUTI ATERO AMBUYE YEKHA WA MULUNGU.

Mulungu wavumbulutsira njira Yake yangwiro kwa ife. Iyo ili yaulemerero kwambiri ndiposo yosavuta. Uthenga uliwonse umene timamumva Iye akutiuza, kutitsimikizira, kutilimbikitsa, kuti NDIFE MKWATIBWI WAKE. Tili mu chifuniro Chake changwiro. Tadzipanga ife eni kudzikonzekeretsa tokha pa KUMUNVA IYE

Uthenga uwu uli watsopano kwambiri kuposa nyuzipepala ya mawa. Ndife ulosi womwe ukukwaniritsidwa. Ndife Mawu owonetseredwa. Mulungu amatitsimikizira ndi Uthenga uliwonse umene timamva kuti tsiku ili lero , Lemba ili likukwaniritsidwa.

Pakhoza kukhala ena uko kudutsa mafuko, kuzungulira dziko, amene ngakhale tepi iyi idzakawapeza mmakomo mwawo kapena mmatchalitchi mwawo. Ife tikupemphera, Ambuye, kuti pamene msonkhano ukupitirira, pa—pa…kapena tepiyo izikaseweredwa, kapena pamalo amene tingadzakhale tiripo, ka—kapena chikhalidwe, mulole Mulungu wamkulu wa Kumwamba mulemekeze kudzipereka uku kwa mitima yathu mmawa uno, ndipo muchiritse osowa, mupereke kwa iwo zimene iwo akuzisowa.

Dikirani chabe mwa ka mphindi ….Kodi Liwu la Mulungu kwa dziko lapansi linalosela ndi kunena chiyani?….anthu azizasewera matepi m’nyumba zawo kapena m’matchalitchi awo.

Koma ife tikutsutsidwa ndi kudzudzulidwa ponena kuti ife SITINGAKHALE NDI Tchalitchi cha Tepi Cha mnyumba? Kodi M’bale Branham sananenepo kuti muzisewera matepi m’matchalitchi anu?

ULEMERERO KWA MULUNGU, IMVETSENI IYO, WERENGENI IZO, IZO NDI PAKUTI ATERO AMBUYE. Ndipo sikuti Iye anangonena izi zokha, komanso posewera matepi m’nyumba zanu ndi m’matchalitchi, Mulungu wamkulu wa Kumwamba adzalemekeza kukhulupirika kwa mitima yathu ndikuchiritsa osowa ndikutipatsa ife CHILI CHONSE CHOMWE TIKUFUNA!!

Chobwerezedwa ichi chimodzi chokhachi CHIKUTSIMIKIZIRA kuti anthu akumvetsera abusa awo ndipo iwo SAKUMVA MAWU, kapena Iwo angawatsutse ndikuwatsimikizira ndi MAWU kuti ife tili mu CHIFUNIRO CHAKE CHANGWIRO, ndipo ndi CHIFUNIRO CHAKE CHANGWIRO KUSEWERA MATEPI M’MATCHALITCHI AWO.

Sindikusokeretsa kapena kubwereza mawu molakwika Mawu monga momwe ambiri amanenera. Imvereni ndipo muwerenge izo nokha.

Ndipo ndi zophweka komanso zangwiro, INGOKANIKIZANI KUSEWERA ndipo mumve Liwu la Mulungu likulankhula nanu. Nenani “Amen” ku Mawu aliwonse omwe inu mukumva. Inu Simuyenera konse kuwamvetsa, inu muyenera kokha kungokhulupilira izo.

“Ine ndikufuna kuti ndipite opanda msasa. Ziribe kanthu kuti ine ndilipira chiyani, ine nditenga mtanda wanga ndipo ndiziunyamula iwo tsiku ndi tsiku. Ine ndipita mopitirira msasa. Ziribe kanthu kuti anthu azinena chiyani za ine, ine ndikufuna kuti ndizimutsatira Iye kunja kwa msasa. Ine ndakonzeka kuti ndizipita.”

Bwerani ndipo mudzapite mopitilira chotchinga cha mawu kupita ku Mawu a Mulungu Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville. Izo zilibe malire zomwe Mulungu angachite ndiso zomwe adzachita ndi munthu amene ali wokonzeka kupita mopitirira msasa wa anthu.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 64-0719E Kupita Mopitilira Msasa

Malemba Opatulika: Ahebri 13:10-14 / Mateyu 17:4-8

25-1214 Phwando La Malipenga

Uthenga: 64-0719M Phwando La Malipenga

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wangwiro

Izi sizongozipanga, abwenzi. Izi ndi PAKUTI ATERO AMBUYE, Lemba.

Mkristu aliyense amafuna kukhala Mkwatibwi, koma tikudziwa kuti Mkwatibwi Wake adzakhala okhawo osankhidwa ake ochepa . Tikudziwa kuti Iye ali ndi chifuniro chongololera, koma Mkwatibwi Wake ayenera kukhala mu chifuniro chake changwiro. Kotero, ife tiyenera kufunafuna Mulungu mu Mawu Ake, ndipo kenako mwa vumbulutso, ife tidzadziwa chifuniro Cha Iye changwiro momwe ife tingakhalire Mkwatibwi Wake.

Ife tiyenera kufufuza lemba, chifukwa tikudziwa kuti Mulungu SAMASINTHA malingaliro Ake pa Mawu Ake. Mulungu sasintha pologaramu yake.Iye Sasintha CHILICHONSE. Momwe Iye anachitira izo nthawi yoyamba ndi wangwiro. Zimene Iye anachita dzulo Adzachitanso chimodzimodzi lero.

Momwe Iye anapulumutsira munthu kuyambira pachiyambi, Iye ayenera kupulumutsa munthu lero mwanjira yomweyo. Momwe Iye Anachiritsira munthu woyamba, Iye ayenera kuchita chimodzimodzi lero. Momwe Mulungu anasankhira kuyitana ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake, Iye Adzachita chimodzimodzi lero; pakuti Iye ndi Mulungu ndipo sangasinthe. Mawu amatiuza kuti Yesu Khristu ali YEMWEYO dzulo, lero ndi kwanthawi zonse.

Kotero, Ife tikamawerenga Mawu Ake, timatha kuona bwino lomwe momwe Iye anasankhira kuyitana ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake pa nthawi iliyonse. Adasankha MUNTHU MMODZI. Iye anati iwo anali Mawu a tsiku lawo. Mneneri anatiuza Ife kuti Iye SANALI ndi gulu la amuna; Iwo amakhala ndi njira zosiyanasiyana, malingaliro osiyanasiyana, ndipo chofunika kwambiri, Iye anati, MAWU A MULUNGU SAMAFUNIKA KUTANTHAUZIRA.

Ndiye, zomwe mneneri aliyense adalankhula mu mbadyo uliwonse sizingawonjezeredwepo kapena kuchotseredwapo. Ziyenera kukhala Mawu pa Mawu zomwe IYE ANALANKHULA. Zophweka kwambiri ngati Inu mundifunsa ine kuti nanga njira yoperekedwa ndi Mulungu ndi iti….KHALANI NDI MNENERI.

Tsopano, ife sitikungodziwa kokha kwenikweni yomwe yakhala ili njira yoperekedwa ndi Mulungu kuyambira pachiyambi, Ambuye adzalankhula ngakhale kudzera mwa mngelo wake ndikutiuza zomwe Iye adzachita mtsogolo, kuti basi adzatsimikizire kachiwiri, MULUNGU SAMASINTHA DONGOSOLO LAKE.

Mkwatibwi Wake (ife) titachoka padziko lapansi lino ndikuyitanidwa ku Mgonero wa Ukwati, kodi Mulungu adzaitana bwanji Ayuda osankhidwa 144,000? Gulu la amuna?

Ndipo pa nthawi yomweyo…Tsopano, mwamsanga pamene Mpingo uwu (Mkwatibwi) ukusendezedwa pamodzi, Iwo ukutengedwera mmwamba; ndipo chinsinsi icho cha Chisindikizo cha Chisanu ndi chiwiri, kapena Chisindikizo cha Chisanu ndi chiwiri, chinsinsi cha kupita. Ndipo Ayuda akuitanidwa ndi chinsinsi cha Lipenga la Chisanu ndi chiwiri, chimene chiri aneneri awiri, Eliya ndi Mose, ndipo iwo akubwereranso.

Kotero Mkwatibwi akusendezedwa pamodzi, ife tidzatengedwera mmwamba. Ife Tikudziwa kuti pali chinthu chimodzi chokha chomwe chingamusendeze Mkwatibwi pamodzi, Mzimu Woyera, ndipo Mzimu Woyera ndi Mawu Ake, ndipo Mawu Ake a lero ndi Liwu la Mulungu, ndipo Liwu la Mulungu ndi…

Ngati ine ndidakukhumudwitsani Inu pa kunena zimenezo, mundikhululukire ine, koma, ndinaverera kuti mwina icho chidazembedwa, koma, Ine ndine Liwu la Mulungu kwa inu. Mukuona? Ine Ndikunenanso zimenezo kachiwiri, nthawi imene ija ndidali pansi pa kudzoza, Inu mukuona.

Ndingolankhula ine pomwe pano ndi kunena kuti, CHOBWEREZA CHIMODZI chokha ichi chochokera kwa mthenga wa mngelo wotsimikiziridwa wa Mulungu chiyenera kukhala chokwanira kwa onse odzitcha okhulupirira mu Uthenga wa nthawi yotsiriza uwu kuti apemphe abusa awo kuti azikanikiza kusewera m’matchalitchi awo kapena kuti achoke pa udindo kuti iwo asankhe m’busa wokhala ndi VUMBULUTSO LENI LENI LOCHOKERA KWA MULUNGU.

Choncho, Lipenga linamveka ndipo aneneri awiri awa akuwonekera chifukwa Iye sangakhale ndi mngelo wake wachisanu ndi chiwiri ndi Mkwatibwi wake pano padziko lapansi nthawi yomweyo yomwe akubwera. Ndiye kodi Iye akuwayitani bwanji Ayuda? Mwanjira yofanana momwe Iye anamuyitanila Mkwatibwi wake wa Amitundu.

Ndipo Ayuda akuitanidwa ndi chinsinsi cha Lipenga Lachisanu ndi chiwiri, chomwe ndi aneneri awiri…

Mkwatibwi ayenera kuti achokepo pa njirayo, kuti azipita mmwamba tsopano; kuti antchito awiriwo, antchito awiri awo a Mulungu, mu Chivumbulutso, aneneri awiriwo, akhoza kuwonekera poyera, kuti adzawombe Lipenga la Chisanu ndi chiwiri kwa iwo, kumudzindikiritsa kwa iwo Khristu.

Zomveka bwino kwambiri, Mulungu sasintha dongosolo lake.Iye anatumiza aneneri Ake. Motero, Mkwatibwi Wake adzakhala ndi njira Yake yoperekedwa, mneneri Wake wa angelo, Liwu la Mulungu pa matepi.

Kenako kuti izo zimveke bwino, Mulungu kachiwiri akulankhulanso ndikumuuza Mkwatibwi Wake kuti: Mwakhala okhulupirika kwa Ine ndi njira Yanga yoperekedwa, kotero njira Yanga yoperekedwa ya tsiku lanu idzayankhula kwa inu:

Mngelo wachisanu ndi chiwiri, mtumiki, akuti, “Taonani Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa tchimo la dziko lapansi!”

Kotero lofunikira kwambiri ndi LIWU LIMENELO; LIWU LA MULUNGU akulankhula kudzera mwa mngelo wake wachisanu ndi chiwiri pa matepi. Mulungu adzagwiritsa ntchito MAWU AMENEWO, LIWU LA M’NGELO WAKE WACHISANU NDI CHIWIRI. OSATI GULU…OSATI INE…OSATI M’BUSA WANU…LIWU LA MTUMIKI WAKE WA MNGELO WACHISANU NDI CHIWIRI kuti atidziwitse ife kwa Iye, Ambuye wathu Yesu Khristu.

Motero, ife tikudziwa:

• IFE NDIFE MKWATIBWI WAKE.
• IFE TILI MU CHIFUNIRO CHAKE CHANGWIRO.
• IFE TIKUTSATIRA DONGOSOLO LAKE LA TSIKU LA LERO PAKUKANIKUZA KUSEWERA.

Gawo la Mkwatibwi Wake lidzakhala likusonkhana Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, kumvetsera m’busa wathu, mthenga wa mngelo wa Mulungu, William Marrion Branham, ndipo Iye adzalankhula ndi kutiululira kuti palibe mpingo wina, palibe gulu lina la anthu kuyambira chikhazikitsidwire kwa dziko lapansi, lomwe lakhala ndi mwayi woti ife tigwirizane pamodzi kumvetsera Mulungu akulankhula mwachindunji ndi iwo.

Ndi anthu odala bwanji ife. Ife Ndi okondwa kwambiri. Ife kotero ndi oyamikira kwambiri . Mkwatibwi akukhala MMODZI ndi Mkwati.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: Malipenga A Phwando 64-0719M.

Malemba oti muwerenge musanamve Uthenga:

Levitiko 16
Levitiko 23:23-27
Yesaya 18:1-3
Yesaya 27:12-13
Chivumbulutso 10:1-7
Chivumbulutso 9:13-14
Chivumbulutso 17:8

25-1207 Kenako Yesu Anabwera Ndipo Anadzaitana

Uthenga: 64-0213 Kenako Yesu Anabwera Ndipo Anadzaitana

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi wa Mawu,

Tikukhala mu nthawi yamdima kwambiri, koma tilibe MANTHA, Ambuye wabwera. Wabwera kudzakwaniritsa Mawu Ake mu tsiku lomaliza. Chimene Iye anali panthawiyo, Iye ali lero. Chimene kuonekera kwake ndi kudziwika kwake zinali, ndi lero. Iye akadali Mawu a Mulungu, akudziwonetsera Yekha mu thupi la munthu mwa mngelo wake wachisanu ndi chiwiri wamphamvu ndipo watiululila ife, ife ndife Mkwatibwi wake wa Mawu a moyo.

Tilibe nthawi ya mtsutso kapena mkangano; Ife tinadutsa tsiku limenelo; tikupita patsogolo, Ife tikuyenera kukafika kumeneko. Mzimu Woyera wabwera pakati pathu. Ambuye Yesu mu mawonekedwe a Mzimu wadziulula ndi kudziwonetsera Yekha kudzera mwa mneneri Wake kuti Iye ndi Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi Wake.

Iye anati adzabwera. Iye anati adzachita izi. Iye anati adzauka m’masiku otsiriza ndikuchita zinthu izi monga momwe Iye anachitira pamene anabwera m’thupi nthawi yoyamba, ndipo apa akuchita izi. Kodi inu mukuopa chiyani? PALIBE!!!

Tili pa njira ya kwathu yopita ku Ulemerero! Palibe chomwe ife chingatilepheretse. Mulungu adzatsimikizira Mawu Ake. Sindikusamala zomwe zikuchitika. Nthawi yafika yochitapo kanthu. Nthawi yafika yo khulupilira kapena kusakhulupirira. Mzere uja wolekanitsa umene umabwera kwa mwamuna ndi mkazi aliyense wafika.

Inu Munabadwira pa cholinga. Pamene Kuwala kunakukanthani inu, Kunachotsa kudetsedwa konse mkati mwa inu. Pamene munamva Liwu Lake likulankhula ndi inu pa matepi, chinachake chinachitika. Kunalankhula ndi moyo wanu. Kunati, “Ambuye wabwera ndipo akukuitanani inu. Musatope, musaope, Ine ndikukuitanani inu. Ndinu Mkwatibwi Wanga”.

Oh Anthu inu, onetsetsani! Musamangotenga chatheka chilichose pa izo. Mulungu ali ndi pologaramu: Mawu Ake Iye adawajambula pa matepi. Ambuye wabwera ndipo akukuitanani inu. Bwerani ku njira yoperekedwa ndi Mulungu.

Ambuye adzagwirizanitsanso Mkwatibwi Wake padziko lonse lapansi ndi Liwu Lake. Adzatilimbikitsa ife, kutitsimikizira ife, kutichiritsa ife, kutibweretsa mu mKukhalapo Kwake kwamphamvu ndikutiuza ife:

Mbuye wabwera ndipo Iye akuitana iwe. Oh, wochimwa, oh, munthu wodwala, kodi iwe sukuwona Mbuye akuwonetseredwa mwa anthu, pakati pa okhulupirira? Iye wabwera kuti adzaitane ana Ake okhulupirira kuti akhale athanzi. Iye wabwera kuti adzamuitanire wochimwa ku kulapa. Wobwerera mmbuyo, membala wa mpingo, Mbuye wabwera ndipo akukuitanani inu.

Kodi ndikutsanyulila kotani Kwa mzimu woyera komwe mkwatibwi adzakhale nako Lamlungu lino pamene Mulungu akusonkhanitsaso ana ake pamodzi kachiwiri ndi kulowa m’nyumba zathu, m’matchalitchi athu, m’misonkhano yathu, ndikutiyitana ife kunena kuti, “Ambuye wabwera ndipo akuitana. Chilichonse chomwe Inu mukuchifuna, ndi chanu.”

Lolani mawu amenewo alowe mozama m’mitima mwanu, abale ndi alongo. CHILICHONSE CHIMENE INU MUKUFUNA, AMBUYE WABWERA NDIPO APEREKA ICHO KWA INU.

Atate Akumwamba, O Ambuye, mulole izo zichitikenso. Zinthu zonse izi zimene ine ndanena, “Yesu wabwera ndipo akukuitanani inu.” Kodi Iye akuchita chiyani pamene Iye wabwera? Iye akuitana. Ndipo mulole izo zichitikenso, Ambuye. Mulole Mzimu Woyera Wanu ubwere pakati pa anthu usikuuno, Ambuye Yesu mu mmaonekedwe a—a Mzimu. Mulole Iye abwere usikuuno ndipo adzadziulule Yekha, ndipo potero adzadziwonetsere Yekha.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: Kenako Yesu Adabwera Ndipo Adayitana
Nthawi:12:00 PM nthawi ya ku Jeffersonville
Malemba: Yohane Woyera 11:18-28

25-1130 Mbambande

Uthenga: 64-0705 Mbambande

PDF

BranhamTabernacle.org

Yokondedwa Mbambande ya Mulungu,

Moyo wonse weniweni womwe unali mu phesi, ngayaye, ndi mankhusu, tsopano ukusonkhana mwa ife, Mbewu Yachifumu ya Mulungu, Mbambande Zake , ndipo zikupangidwa kukonzekeretsedwa kuuka kwa akufa, kukonzekera kukolola. Alefa wakhala Omega. Woyamba wakhala womaliza, ndipo wotsiriza tsopano ndiye woyamba. Tadutsa mopangidwira ndipo takhala Mbambande za Iye, chidutswa chodulidwa kuchokera kwa Iye.

Mkwatibwi ndi Mkwati ndi Amodzi!

Mulungu adawonetsa mneneri Wake chithunzithunzi cha aliyense wa ife, Mphambande za Iye, mu masomphenya. Pamene Iye adayima pamenepo ndi Ambuye akuyang’ana Mkwatibwi akudutsa pa maso pa Iye,

Iye adationa aliyese wa Ife. Ife tonse maso anthu anali akuyanganira KWAMBIRI PA IYE. Iye anati ife tinali anthu amawonekedwe wokoma kwambiri omwe anali adawawonapo kale m’moyo wake. Panali mpweya chabe mozungulira ife. Ife tinkawoneka okongola kwambiri kwa iye.

Kumbukirani, awa anali MASO MPHENYA a Mkwatibwi; Momwe Iye angadzawonekere, ndipo akutiuza ndendende zomwe Iye anali kuchita. Mvetserani mwatcheru.

Iye adzabwera kuchokera ku mafuko onse, iwo adzapanga Mkwatibwi. Aliyense anali ndi tsitsi lalitali, ndipo analibe zopakapaka, ndipo asungwana okongola kwenikweni. Ndipo iwo anali kundiyang’anitsitsa ine. Icho chinayimira Mkwatibwi kuchokera ku mafuko onse. Mukuona? Iye, aliyense kuyimira fuko, pamene iwo akuguba mwangwiro mu mzere ndi Mawu.

Mkwatibwi, ndiloleni ndinenenso icho kachiwiri kuti, MKWATIBWI, wochokera ku mitundu yonse anali maso awo akuyang’ana pa m’busa wawo, gulu la amuna….AYI, izo si zimene iye ananena. Iwo maso awo Anayang’ana PA MNENERI, kumuyang’anitsitsa iye.

Bola ngati Iwo anali akuyang’ana pa mneneriyo, Iwo anali kuguba mwangwiro. Koma kenako Iye anatichenjeza ife, chinachake chinachitika. Ena anachotsa maso awo pa iye ndikuyamba kuyang’ana china chake chomwe chinangopita mu chisokonezo.

Ndipo, kenako, ine ndinayenera kumuyang’anitsitsa Iye. Iye adzachoka pa malo a Mawu ngati ine sindimuyang’ana iye, pamene iye akudutsa, ngati iye ati apyolepo. Mwina idzakhala nthawi yanga, pamene ine ndatha, mukuona, pamene ine ndatsiriza, kapena chirichonse chimene chiri.

Iye ayenera kumuyang’anira iye, kapena adzachoka pa malo pamene Iye akudutsa. Koma kenako iye akunena kuti mwina ikhoza kukhala nthawi yanga, ndikamaliza, pamene ine sindili pano, Angachoke pamalo posayang’ana maso awo pa iye.

Iye anali kuchenjeza MKWATIBWI momveka bwino, Inu muyenera kuyang’ana maso anu pa Liwu la Mulungu pa matepi. Imeneyo ndiyo njira yoperekedwa ndi Mulungu lero. Limelo ndilo Liwu lomwe lidzalumikizitsa ndi kupangitsa Mkwatibwi kukhala wangwiro. Ngati Inu mutachotsa maso anu ndi makutu anu pa Liwu, Inu mudzachoka mzere ndi kulowa mu chisokonezo.

Uthenga uliwonse umakhala womveka bwino kwambiri ndipo kwambiri zedi. Ndi Mulungu wamphamvu amene akuvundukulidwa pamaso pathu, akudyetsa Mkwatibwi wake ndi Mana yobisika yomwe ife tingadye kokha basi. Ndi wolemera kwambiri kwa ena onse, koma ndi Chakudya Chobisika kwa Mkwatibwi.

Ndi Chiyamiko chotani chomwe Mkwatibwi akukhala nacho, kudyerera pa Mawu, kukhala Mbambande ya Mkwatibwi Wake wa Mawu.

Akuyima yekha, monga Mkwati, “wokanidwa ndi anthu, wonyozedwa ndi kukanidwa ndi mipingo.” Mkwatibwi akuyima motero. Ndi chiani icho? Ndiyo Mbambande Yake, onani, ndiwo Mawu amene Iye angakhoze kugwiritsamo ntchito, kupangidwa kuwonekera. Kukana!

Bwerani mudzalumikizane ndi ife Lamlungu nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene Mulungu akulankhula kudzera mwa mngelo wake wamphamvu, ndikutidula ndi kutipukuta ife kuti tikhale Mbambande ya Mulungu.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 64-0705 Mbambande

Malemba oti muwerenge Chiyanjano chisanayambe:

Yesaya 53:1-12
Malaki 3:6
Mateyu Woyera 24:24
Marko Woyera 9:7
Yohane Woyera 12:24 / 14:19

25-1123 Mulungu Wamphamvu Kuvundukulidwa Pamaso Pathu

Uthenga: 64-0629 Mulungu Wamphamvu Kuvundukulidwa Pamaso Pathu

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Branham Tabernacle,

NDI nthawi za ulemerero bwanji zomwe tikukhala nazo. Mawu ndi Mkwatibwi ndi amodzi ndipo ndi ofanana. Tikukhala kuseri kwa chophimba mum’kupezeka Kwa Ulemerero wa Shekinah. Ife tikuwona Mulungu akudzibisa yekha kuseri kwa khungu mwa m’thenga wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri . Mulungu, kachiwiri, akudzibisa yekha kuseri kwa khungu la munthu mwa aliyense wa ife. Palibe funso lina. Palibe kukayika kwina, Ife NDIFE osankhidwa Ake, okonzedweratu, Mawu opangidwa thupi, Mkwatibwi wangwiro wa Mawu

Pamene Ife tikulumikizana pamodzi kuchokera padziko lonse lapansi, ife tikumvetsera Mawu Ake akulankhula ndi kuwulula kwathunthu Mawu Ake kwa ife Vumbulutso lathunthu kuti Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero ndi kwa nthawi zonse. Kuwonekera kwa Mawu, Elohim, Mulungu m’thupi akulankhula ndi Mkwatibwi Wake. Mulungu m’thupi alindi moyo ndi kukhala mwa aliyense wa ife. Pulogalamu yomaliza ya Mulungu tsopano ikuwonetseredwa mwathunthu ndikuwonetsedwa mwa aliyense wa ife.

Ife tili okondwa kwambiri komanso othokoza Ambuye kutchedwa achilendo ndi ma nati okhala ndi zolumikizidwako zowoneka mwachilendo. Koma tikudziwa Amene ife tikulumikizidwako naye, ndi omwe tili: Mkwatibwi Wa Mulungu Wolumikizidwa ku Tepi; Ndipo ikutikokera kwa Iyemwini, kukhala yomangililidwako molimba ndi molimba kwambiri pamene ife tikukhala MMODZI NDI IYE, Yesu Khristu yemweyo dzulo, lero, ndi kwa nthawi zonse.

Ife Tatsegula chophimba ndipo talowa mu Lawi la Moto ndipo tikupezamo madalitso a Mulungu! Anthu sangathe kuwona. Sangathe kumvetsa. Koma kwa ife, zili powonekera kwambiri, chifukwa tili mu mzimu womwewo monga Wolemba wathu ndi Mtsogoleri wathu. Ndi Liwu la Mulungu pa Matepi likutsogolera Mkwatibwi Wake.

Tikukhala pa M’kate Wowonetsera, Manna omwe amaperekedwa kwa anthu olekanitsidwa okha. Ndi Chinthu chokhacho chomwe tingadye. Ndi chinthu chokhacho chomwe timaloledwa kudya. Ndipo ndi cha anthu okha omwe aloledwa, okonzedweratu ndipo akudziwa chomwe icho chiri.

Ine ndimangokonda kumumva Iye akutiuza kuti NDIFE NDANI:

Mmodzi yemweyo amene anabwera pansi pa Tsiku la Pentekoste, ndi Mzimu Woyera womwewo umene ukuwonetseredwa lero, kuchokera ku Ulemelero kupita ku Ulemelero, kupita ku Ulemelero. Ndipo wabwerera ku Mbewu Yake yapachiyambi, ndi ubatizo wa Mzimu Woyera; ndi zizindikiro zomwezo, zodabwitsa zomwezo, ubatizo womwewo; mtundu womwewo wa anthu, kumachita mwanjira yomweyo, ndi mphamvu yomweyo, zomverera zomwezo. Izo zikuchokera ku Ulemelero kupita ku Ulemelero.

Ife tabwerera ku Mbewu yopachiyambi ndi ubatizo wa Mzimu Woyera. Zizindikiro zomwezo, zodabwitsa zomwezo, ubatizo womwewo, anthu amtundu womwewo, tikuchita chimodzimodzi, ndi mphamvu yomweyo, kumverera komweko.

IFE NDIFE ANGWIRO, OBWEZERETSEDWA MWATHUNTHU, MKWATIBWI WA MAWU WA TEPI!

Ife tikugonjetsa. Tikukhala. Tikuima. Tikukhala pa Mawu Ake oyera omwe anasungidwira Mkwatibwi Wake. Iye akutipanga ife kukhala angwiro tsiku ndi tsiku. CHIKHULUPIRIRO chathu chafika pamlingo watsopano podziwa kuti NDIFE NDANI, ndipo ndi:

Chosakanidwa, Chosakambirana ndipo koposa zonse, sichili ndi MANGAWA.

Kodi mukufuna kukhala osangalala kuposa momwe mudakhalirapo?
Kodi mukufuna kukhutira 1000% kuti zomwe mukumva ndi pakuti Atero Ambuye? Kodi mukufuna kupangidwa kukhala angwiro ndi Mawu a Mulungu?

Kenako Ine ndikukuitanani kuti mudzalumikizane ndi ife , aku Branham Tabernacle, Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tikumva Mawu a Mulungu akulankhula nafe Mawu a Moyo Wamuyaya: Mulungu Wamphamvu Kuvundukulidwa Pamaso Pathu 64-0629. 

M’bale Joseph Branham

25-1116 Khristu Wozindikiritsidwa Wa Mibadwo Yonse

Uthenga: 64-0617 Khristu Wozindikiritsidwa Wa Mibadwo Yonse

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mawu Amoyo a Mulungu,

Zaka zonsezi ine ndakhala ndikuzibisa izo mu mtima mwanga, kumuphimba Khristu, Lawi la Moto lomwe lija likutanthauzira Mawu, monga zinalonjezedwa.

Ndikudziwa kuti izi zimveka mopanda nzeru kwa anthu ambiri, koma ngati mungopirira ndi mthenga wa mngelo wa Mulungu kwa mphindi zochepa, ndikupempha Mulungu kuti akupatseni vumbulutso lowonjezera, ndikukhulupirira kuti iye, mothandizidwa ndi Mulungu komanso ndi Mawu Ake, komanso molingana ndi Mawu Ake, adzamubweretsa Iye pano pamaso panu. Mulungu, akuulula ndi kudziwonetsera Yekha, kutanthauzira ndi kuulula Mawu Ake.

Ndi chitsitsimutso chotani chomwe chakhala chikuchitika mwezi watha uno mkati mwa Mkwatibwi wa Yesu Khristu. Mulungu, akuulula Yekha kuposa kale lonse, akulankhula ndi Wokondedwa Wake, kupanga chikondi ndi Iye, kumutsimikizira, Ndife Amodzi ndi Iye.

Palibe kukayikira, palibe kusatsimikizika, palibe kukayikira, ngakhale mthunzi wa kukayikira; Mulungu watiululila kwa ife: Liwu la Mulungu likulankhula pa matepi ndi NJIRA YOPEREKEDWA NDIPOSO NJIRA YANGWIRO KWA MKWATIBWI WAKE LERO.

Anapereka njira iyi kuti tisadzafunikire iyo kuisefa, kuifotokoza, kapena kuigwiritsa ntchito mwa umunthu mwanjira iliyonse; zingomverani kokha basi Liwu Loyera la Mulungu likulankhula kuchokera ku mulomo kupita ku khutu kwa aliyense wa ife.

Iye adadziwa kuti tsiku lino likubwera. Iye adadziwa kuti Mkwatibwi Wake angadzadye Manna Obisika okha, Chakudya Chake cha Nkhosa. Sitikufuna kumva china chilichonse kupatula Mawu a Mulungu ochokera kwa Mulungu Mwiniwake.

Ife tadutsa chophimba chimenecho kulowa mu Ulemerero wa Shekinah. Dziko lapansi silingathe kuwona. Mneneri wathu sangatchule mawu ake moyenera. Sangavale bwino. Sangavale zovala za ubusa. Koma kuseri kwa chikopa cha munthu, mkati mwake muli Ulemerero wa Shekinah. Mkati mwake muli mphamvu. Mkati mwake muli Mawu. Mkati mwake muli Mkate Wowonetsera. Mkati mwake muli Ulemerero wa Shekinah, womwe ndi Kuwala komwe kumakhwimitsa Mkwatibwi.

Ndipo kufikira inu mutabwera kuseri kwa chikopa cha katumbu chimenecho, kufikira inu mutatuluka mu chikopa chanu chakale, maganizo anu akale, tizikhulupiriro tanu takale, ndi kubwera mu Kukhalapo kwa Mulungu; pamenepo Mawu amadzakhala chenicheni chamoyo kwa inu, pamenepo inu mumadzutsidwira ku Ulemelero wa Shekinah, zikatero Baibulo limadzakhala Bukhu latsopano, pamenepo Yesu Khristu amakhala yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Inu mukukhala mu Kukhalapo Kwake, mukudya mkate wopanda chotupitsa umene wangoperekedwa tsiku limenelo kwa okhulupirira, ansembe okha. “Ndipo ife tiri ansembe, unsembe wachifumu, fuko loyera, anthu achilendo, akupereka nsembe zauzimu kwa Mulungu.” Koma inu mukuyenera kulowa mkati, kuseri kwa chophimba, kuti mukamuwone Mulungu wovundukulidwa. Ndipo Mulungu wavundukulidwa, ndiwo Mawu Ake akuwonetseredwa.

Ndife anthu osamvetseka ku dziko lapansi, koma ife ndi ukhutitsidwa kudziwa kuti Bauti wathu ndi ndani ndiposo onyadira kukhala nati ya matepi Ake, olumikizidwa ku Mawu Ake, chifukwa amatikokera kwa Iye.

Ngati simulumikizidwa ku matepi, siyinu chinthu china koma mulu wa chiphakasa!!!

Tsopano, zindikirani tsopano, Mulungu! Yesu ananena kuti, “Iwo amene Mawu amabwerako, ankatchedwa ‘milungu,’” amenewo anali aneneri. Tsopano, osati munthuyo iyemwini anali Mulungu, osatinso kuti thupi la Yesu Khristu linali Mulungu. Iye anali munthu, ndipo Mulungu amaphimbidwa kuseri kwa Iye.

Mulungu, tsiku lina adaphimbidwa kuseri kwa chikopa cha katumbu. Mulungu, tsiku lina ataphimbidwa ndi thupi la munthu wotchedwa Melkizedeki. Mulungu, adaphimbidwa ndi thupi la munthu wotchedwa Yesu. Mulungu, adaphimbidwa ndi thupi la munthu wotchedwa William Marrion Branham. Mulungu, adaphimbidwa ndi thupi la munthu wotchedwa MKWATIBWI WAKE.

Izo kotero ndikofunikira kukumbukira, koma ambiri akulephera ndipo iwo akuyang’ana china chake basi. Chinthu chomaliza chimene Abrahamu anaona, chinthu chomaliza kuchitika moto usanagwe ndi kuweruza dziko la Amitundu, mwana wolonjezedwa asanabwere, chinthu chomaliza chimene mpingo wachikhristu udzawona mpaka kuwonekera kwa Yesu Khristu ndi Melkizedeki, Mulungu woonekera mu m’thupi, akuulula Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake.

Palibe china chilichonse chomwe chikubwera. Palibe china chilichonse chomwe chinalonjezedwa m’Mawu Ake. Palibe munthu, kapena gulu la anthu lomwe lidzabwere kudzamupanga wangwiro Mkwatibwi.

Ayi! Iwo akufuna kuti azibwera kuno ku mpingo kuti akhale angwiro. Mukuona? Kuti i—ife timapeza chiyanjano wina ndi mzake kuno ku mpingo, koma ungwiro umabwera mwa pakati pa ife ndi Mulungu. Magazi a Khristu ndi amene amatipanga ife angwiro mwa Mzimu Woyera.

Uthenga uwu, Liwu ili, Mawu otsimikiziridwa a Mulungu, akumupanga kukhala wangwiro Mkwatibwi wa Yesu Khristu.

Ndikukupemphani aliyense wa inu kuti abwere kudzamvetsera nafe Liwu la Mulungu pamene likumupanga kukhala wangwiro Mkwatibwi Wake Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tikumva: 64-0617 “Khristu Wozindikiritsidwa Wa Mibadwo Yonse”.

M’bale Joseph Branham

Malemba oti muwerenge Uthenga usanaperekedwe:

Deuteronomo 18:15
Zakariya 14:6
Malaki 3: 1-6
Luka Woyera 17: 28-30
Yohane Woyera 1: 1 / 4: 1-30 / 8: 57-58 / 10: 32-39
Ahebri 1: 1 / 4: 12 / 13: 8
Chivumbulutso 22: 19