Category Archives: Uncategorized

25-0202 Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele

Uthenga: 61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Osankhidwa,

Ndi nthawi ya dzinja yabwino bwanji yomwe takhala tili nayo tikamaphunzira mibadwo isanu ndi iwiri ya mipingo, kenako Mulungu akuululanso zochuluka kwa ife mu Bukhu la Chibvumbulutso cha Yesu Khristu. Momwe machaputala atatu oyamba a Chibvumbulutso anali mibadwo ya mpingo, kenako momwe Yohane adatengedwera kunka ku mwamba mmutu wa 4 ndi 5 ndikutisonyeza zinthu zomwe zinali mkudza.

Mu mutu wa 6., Iye anaulula momwe Yohane adatsikira dziko lapansi kuti aone zinthu zomwe zikuchitika kuchokera ku mutu wa 6. Kuyambira mutu 19 wa buku la Chivumbulutso.

Mkwatibwi adzakhala wodalitsika bwanji Lamlungu pamene tikumva Liwu la Mulungu likulankhula kudzera mwa mngelo wake Wamphamvu wachisanu ndi chiwiri akutiuza ife chomwe chiti chiwululidwe patsogolo.

Ndine wokondwa kwambiri kunena kuti tsopano tiyamba kuphunzira kwakukulu masabata makumi asanu ndi awiri a Daniel. Mneneri ananena kuti icho chimangilira uthenga wonse tisanapite mu Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri; Malipenga 7; Matsoka atatu; mkazi wovala dzuwa; kutulutsa a m’dierekezi wofiira; handiredi ndi forte-foro sauzande atasindikizidwa apo ; Zonse zikuchitika pakati pa nthawi ino.

Buku la Danieli ndi ndendende kalendala ya m’badwo ndi nthawi yomwe tikukhalamo ino, ndipo chingawoneke chovuta bwanji, Mulungu adzachiswa icho ndikuchipanga icho kukhala chophweka kwa ife.

Ndipo Mulungu akudziwa kuti ndizomwe ndikufuna tsopano, kuti nditonthoze anthu ake ndikuwauza chomwe chili pafupi, Onse a iwo m’mawa uno ndipo kudutsa ku mayiko omwe matepi awa adzapita, Pa dziko lonse lapansi, kuti tili kumapeto a nthawi.

Ndife anthu osankhidwa a Mulungu omwe akukhumba ndi kupempherera tsikulo ndi Ola limenelo. Ndipo maso athu akuyang’anila kumwamba, ndipo tikuyembekezera Iye kudza Kwake.

Tiyeni tonse tikhale ngati Danieli ndikuyang’ana nkhope zathu kumwamba, popemphera ndi mapembedzero, monga tikudziwa pa kuwerenga mawu ndi kumva Liwu lake, Kubwera kwa Ambuye kukuyandikira msanga; Tili kumapeto.

Tithandizeni Atate kuika cholemera chilichonse kumbali, tchimo lililonse, kusakhulupirira kwakung’ono kulikonse komwe kungatibwezere ife mmbuyo. Tsopano tiyeni tikambirane za mayitanidwe apamwamba, podziwa kuti nthawi yathu ndi yochepa.

Uthengawu Wapita kulinkonse. Chilichonse chakonzeka tsopano; Tikuyembekezera ndi kupuma. Mpingo wasindikizidwa. Oipa akuchita zoipa kwambiri. Mipingo ikukhala mpingo wokhuthala, koma oyera anu akubwera pafupi ndi inu.

Tili ndi Liwu likufuula m’chipululu, likuitana anthu kubwerera ku uthenga wa pachiyambi; Kubwerera ku zinthu za Mulungu. Timamvetsetsa mwa vumbulutso izi zinthu zomwe zikuchitika.

Bwerani mudzalumikizane nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00PM nthawi ya ku Jeffersonville , pomwe Mulungu akuwululira Mawu Ake kwa ife, pamene tikuyamba kuphunzira kwakukulu za buku la Danieli.

M’bale. Joseph Branham

61-0730M – Malangizo a Gabriel kwa Daniel

25-0126 Chibvumbulutso, Mutu Faivi Gawo II

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Akupumula,

Ili ndilo Dzinja labwino kwambiri m’miyoyo yathu. Kudza kwa Ambuye kuli pafupi kumene. Ife tasindikizidwa ndi Mzimu Woyera; Chisindikizo cha Mulungu cha chivomerezo chakuti zonse zimene Kristu anafera ndi zathu.

Ife tsopano tiri ndi chikole cha cholowa chathu, Mzimu Woyera. Icho ndi Ndichitsimikizo, malipiro ochepera, kuti talandiridwa mwa Khristu. Ife tikupumula mu malonjezo a Mulungu, tikugona mu kutentha kwa Dzuwa Lake lowala; Mawu Ake otsimikiziridwa, kumvetsera ku Liwu Lake.

Ndicho chikole cha chipulumutso chathu. Ife Sitikudandaula ngati tipita Kumeneko kapena ayi, IFE TIKUPITA! Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Mulungu ananena chomwecho! Mulungu analonjeza ndipo ife tiri nacho chikole. Ife talandira kale Icho ndipo Khristu watilandira ife.

Palibe njira yothawira kwa Izo…m’malo mwake, tiri kumeneko! Zomwe tiyenera kuchita ndikungodikira; Iye ali pansi akuchita Chiwombolo Chachibale pakali pano. Ife tiri nacho chikole chake pakali pano. Ife tikungoyembekezera nthawi imene Iye abwereso Kwa Ife. Kenako, m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso tonse tidzapita ku Phwando la Ukwati.

Kungoganizira zonse zimene zili pa tsogolo pa ife. Malingaliro athu sangatengere zonse mkati. Tsiku ndi tsiku Iye akuwulula zambiri za Mawu Ake, kutsimikizira kuti malonjezo aakulu awa ndi athu.

Dziko likugwa; moto, zivomezi, ndi chipwirikiti kulikonse, koma amakhulupirira kuti ali ndi mpulumutsi watsopano amene adzapulumutsa dziko lapansi, ndikubweretsa m’badwo wawo wagolide. Talandira kale Mpulumutsi wathu ndipo takhala tikukhala mu nyengo yathu ya M’badwo wa Golide.

Tsopano Iye akutikonzekeretsa ife ku Chibvumbulutso chochuluka pamene ife tikulowa mu mutu wa Fayifi wa Chivumbulutso. Iye akukhazikitsa chochitika apa cha kutsegula kwa Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri. Monga momwe iye anachitira mu mutu 1 wa Chivumbulutso, kutsegula njira ya Mibadwo Isanu ndi iwiri ya Mpingo.

Kodi zina zonse za Dzinja zidzakhala bwanji kwa Mkwatibwi? Tiyeni tiwone mwachidule:

Tsopano, ndilibe nthawi. Ine Ndazilemba izo pano. nkhani ina pa izo apa, koma msonkhano wathu wotsatira ife tisanalowe mu izi mwinamwake pamene ine ndidzachoka kutchuthi changa kapena nthawi ina, ine ndikufuna kuti nditenge masabata makumi asanu ndi awiri awa a Daniele ndi kumangiriza izo mkati momwe muno, ndi kuzisonyeza izo pamene izo zitengera izo ku chisangalalo cha Chipentekoste, ndi kuzibweretsa izo m’mbuyo kumene ndi miliri isanu ndi awiri iyo Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri kuti zitsegulidwe pano ife tisanapite, ndi kusonyeza kuti izo ziri pa mapeto, izi…

Ndi nthawi yodabwitsa bwanji yomwe Ambuye wasungira Mkwatibwi Wake. Kudzivumbulutsa Yekha mu Mawu Ake kwa ife kuposa kale. Kutilimbikitsa kuti ndife osankhidwa ake amene Iye akuwadzera. Kutiuza ife kuti tiri mu chifuniro Chake Changwiro pakukhala ndi Liwu Lake, ndi Mawu Ake.

Kodi tikuchita chiyani? Osati chinthu chimodzi, Kungopumula! Kudikirira! Palibenso ntchito zolemetsa, palibenso zokhumudwitsa, TIKUPUMULA PA IZO!

Bwerani mudzapumule nafe Lamlungu lino pa 12:00 p.m., nthawi ya mu Jeffersonville, pamene ife tikumva Liwu la Mulungu LOTSIMIKIZILIDWA likutibweretsera ife Uthenga:
61-0618 – “Chivumbulutso, Mutu Fayifi Gawo II”.

M’bale. Joseph Branham

25-0112 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo III

Uthenga: 61-0108 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo III

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Akumuyaya,

Ndi nthawi yoti tivule chovala chathu chankhondo ndi kuvala kuganiza kwanu kwa uzimu, chifukwa Mulungu akukonzekera kuti amupatse Mkwatibwi Wake Vumbulutso lochuluka la Mawu Ake.

Iye adzakhala akuvumbulutsa kwa ife zinsinsi zonse zakale. Iye adzatiuza zimene zidzachitike m’tsogolo. Zomwe ena onse m’Baibulo adangowona kapena kumva, Iye adzawulula tsatanetsatane wa chilichonse chaching’ono cha Mawu Ake ndi tanthauzo lake kwa ife.

Tidzamva ndi kumvetsa tanthauzo la zizindikiro za m’Baibulo: Zolengedwa Zamoyo, Nyanja Yagalasi, Mkango, Mwana wa Ng’ombe, Munthu, Mphungu, Mpando Wachifundo, Alonda, Akuluakulu, Ma liwu, Chirombo Chakuthengo Chosawetedwa, Zorengedwa za Moyo.

Tidzamva ndikumvetsetsa zonse za alonda a Chipangano Chakale. Yuda: Mlonda wa Kum’maŵa; Efraimu: Mlonda Wa Kumadzulo; Rueben: Mlonda waku Mmwela; ndi Dani: Mlonda wa Kumpoto.

Palibe chimene chikanakhoza kubwera paliponse mozungulira mpando wachifundo umenewo popanda kuwoloka mafuko amenewo. Mkango, luntha la munthu; Ng’ombe: kavalo wantchito; Mphungu: Kuthamanga kwake.

Momwe Kumwamba, dziko lapansi, pakati, ndi pozungulira, iwo anali alonda. Ndipo pamwamba pake panali Lawi la Moto. Palibe chinakhudza mpando wachifundo uwo popanda kudutsa mafuko amenewo.

Tsopano pali alonda a Chipangano Chatsopano: Mateyu, Marko, Luka ndi Yohane, kupita molunjika patsogolo. Chipata chakum’maŵa chimayang’aniridwa ndi mkango, chipata chakumpoto chimayang’aniridwa ndi chiwombankhanga chowuluka, Yohane, m’vangeri. Ndiye sing’anga wa mbali iyi, Luka, munthuyo.

Mauthenga anai a Uthenga Wabwino amateteza Madalitso a Chipentekoste ndi Lemba lirilonse kukhalira khonde ndendende zomwe iwo ananena. Ndipo tsopano Machitidwe a atumwi akuwonetsera lero ndi Mauthenga anai kuti Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi nthawizonse.

Pamene wodzozedwa woona wa Mulungu ayankhula, Ilo ndi Liwu la Mulungu! Ife tikungofuna kufuula, “Woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye!”

Palibe basi njira yopitira kutali kwa Icho. Ndipotu, ife sitingathe kuchoka kwa Icho, chifukwa Icho sichingatichokere kwa ife. Ndife odindidwa chisindikizo mpaka tsiku la chiombolo chathu. Palibe mtsogolo, palibe kalikonse, zowopsa, njala, ludzu, imfa, kapena CHINTHU, chimene chingatilekanitse ife ku chikondi cha Mulungu chimene chiri mwa Khristu Yesu.

Asanaikidwe maziko a dziko maina athu anayikidwa pa Bukhu la Moyo wa Mwanawankhosa kuti tiwone Kuwala UKU, kulandira Liwu Ili, kukhulupirira Uthenga Uwu, kulandira Mzimu Woyera wa tsiku lathu ndi kuyenda mwa Iwo. Pamene Mwanawankhosa anaphedwa, MAYINA ATHU anayikidwa pa Bukhu pa nthawi yomweyo Dzina la Mwanawankhosa linayikidwa pamenepo. ULEMERERO!!

Kotero, palibe chimene chingatilekanitse ife ku Uthenga uwu. Palibe chimene chingatilekanitse ife ku Liwu limenelo. Palibe chimene chingatenge Vumbulutso la Mawu Awa kwa ife. Ndi zathu. Mulungu anatiyitana ife ndipo anatisankha ife ndipo anatikonzeratu ife. Zonse ndi za Ife, Ndi zathu.

Pali njira imodzi yokha yopezera zonsezi. Inu Mukuyenera kutsukidwa ndi madzi a Mau. Inu mukuyenera kumva Mawu inu musanalowe mmenemo. Ndipo pali njira imodzi yokha imene inu mungafikire kwa Mulungu, ndiyo mwa Chikhulupiriro. Ndipo Chikhulupiriro chimadza pakumva, kumva Mawu a Mulungu, amene akunyezimiritsidwa kuchokera ku Malo Opatulikitsa kupita kwa mthenga wa m’badwowo.

Kotero, apa, mngelo wa m’badwo wa mpingo akunyezimira m’madzi awo Yemwe Munthu uyu ali muno, akunyezimiritsa chifundo Chake, Mawu Ake, chiweruzo Chake, Dzina Lake. Zonse zikuwonetseredwa muno pamene inu mumalekanitsidwa ndi kuzikhulupirira Izo. Kodi mukumvetsa?

Musati musiye kumvetsera kwa matepi, ingokhalani nawo Iwo. Fufuzani Izo ndi Mawu ndi kuwona ngati Izo ziri zolondola. Ndiyo Njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero.

Bwerani mudzakhale nafe Dzinja ili pamene tikulumikizana pamodzi kuchokera ku dziko lonse lapansi ndikumva Liwu la Mulungu likuwululira Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake kuposa kale. Palibe kudzoza kwakukulu kuposa kukanikiza kusewera ndi kumvetsera ku Liwu Lake.

Kuchokera pansi pamtima, nditha kunena kuti: Ndine wokondwa kunena kuti ndine Mmodzi wa Iwo ndi aliyense wa inu.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga: 61-0108 – “Chivumbulutso, Mutu Foro Gawo III”
Nthawi: 12:00 PM. Jeffersonville nthawi

24-1229 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo I

Uthenga: 60-1231 Chibvumbulutso, Mutu Foro Gawo I

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Oyera Ovala Mwinjiro Woyera,

Tikamamva Liwu la Mulungu likuyankhula nafe, chinachake chimachitika mkati mwa moyo wathu.  Thupi lathu lonse limasinthidwa ndipo dziko lotizungulira likuwoneka kuti likutha. 

Kodi munthu angakhoze bwanji kufotokoza zomwe zikuchitika mu mitima yathu, malingaliro athu, ndi moyo wathu, pamene Liwu la Mulungu livundukula Mawu Ake ndi Uthenga uliwonse umene timamva?

Monga mneneri wathu, timamva kuti takwatulidwira kumwamba kwachitatu ndipo mzimu wathu ukuwoneka kuti ukuchoka mu thupi lachivundi ili. Palibe mawu ofotokozera zomwe timamva pamene Mulungu akutiululira Mawu ake kuposa kale. 

Yohane anaikidwa pa chisumbu cha Patmo ndipo anapemphedwa kuti alembe zimene anaona ndi kuziika mu bukhu lotchedwa Chivumbulutso, kotero izo zikanadzapita kupyola mu mibadwo. Zinsinsi zimenezo zakhala zobisika mpaka zidaululidwa kwa ife kupyolera mwa mthenga Wake wosankhidwa wa 7.  

Ndiye Yohane anamva Liwu lomwelo pamwamba pa iye ndipo anakwatulidwira kumwamba kwachitatu. Liwu lija linamuwonetsa iye mibadwo ya mpingo, kudza kwa Ayuda, kutsanulidwa kwa miliri, Mkwatulo, Kudza kachiwiri, Zakachikwi, ndi Kwawo Kwamuyaya kwa opulumutsidwa Ake. Iye anamutengera iye mmwamba ndipo anabwereza chinthu chonsecho kwa Yohane monga Iye anati Iye akanadzachita. 

Koma kodi Yohane anaona ndani pamene anaona kubwerezako? Palibe amene amadziwa mpaka lero.  

Chinthu choyamba chimene anaona pakubwera chinali Mose. Iye anaimira oyera mtima akufa amene adzaukitsidwa; mibadwo isanu ndi umodzi yonse yomwe inagona.
Koma si Mose yekha amene anaima pamenepo, komanso Eliya anali pamenepo. 

Kodi Eliya amene anali kuyima anali ndani? 

Koma Eliya anali kumeneko; m’thenga wa tsiku lotsiriza, ndi gulu lake, la osandulika, okwatulidwa.

ULEMELERO…HALELUYA…Kodi Yohane adamuwona atayimapo ndani? 

Osati wina koma mthenga wa mngelo wa 7 wa Mulungu, William Marrion Branham, ndi GULU LAKE LA OSANDULIKA, OKWATULIDWA… ALIYENSE WA IFE!!

Eliya ankayimira oyeramtima akufa…Ine ndikutanthauza Mose, ndi kuwukitsidwa. Eliya ankayimira gulu losandulika. Kumbukirani, Mose anali woyamba, ndipo kenako Eliya. Eliya anali woti adzakhale mthenga wa tsiku lotsiriza, kuti ndi iye ndi gulu lake kukanadzabwera chiwukitsiro…kukanadzabwera…chabwino, ukanadzabwera Mkwatulo, ine ndikutanthauza. Mose anabweretsa chiwukitsiro ndipo Eliya anabweretsa gulu Lokwatulidwa. Ndipo, pamenepo, onse a iwo anayimiriridwa pomwepo.

Lankhulani za kuvundukula, kuwulula, ndi Chivumbulutso. 

Apa Iwo uli! Ife tiri nawo Iwo kumene ndi ife tsopano, Mzimu Woyera, Yesu Khristu, yemweyo dzulo, lero, ndi nthawizonse. Ndinu…Iwo ukulalikira kwa inu, Iwo ukukuphunzitsani inu, Iwo ukuyesera kuti ukufikitseni inu kuti muwone chimene chiri cholondola ndi cholakwika. Ndi Mzimu Woyera Mwiniwake ukuyankhula kupyolera mu milomo ya munthu, ukugwira ntchito pakati pa anthu, kuyesa kusonyeza chifundo ndi chisomo.

Ndife Oyera Ovala Mwinjiro Woyera amene mngelo wake anawaona akuchokera ku dziko lonse lapansi kudzadya Mkate wa Moyo. Tili pa kutomeledwa ndipo wokwatitsidwa ndi Iye ndipo tamva kupsompsona kwa Iye kwa chikwati mu mtima mwathu. Ife tinadzilonjeza tokha kwa Iye, ndi ku Liwu Lake lokha. Tilibe, ndipo sitidzadzidetsa ndi mawu ena aliwonse.

Mkwatibwi akukonzekera kukwera mmwamba monga Yohane anachitira; mu Kukhalapo kwa Mulungu. Tidzakwatulidwa pa Mkwatulo wa Mpingo. Momwe izo zimangozungulira moyo wathu! 

Kodi Iye atiululira chiyani motsatira? 

Ziweruzo; mwala wa sardine, ndi chimene umaimira; idachita gawo lotani. Yaspi, ndi miyala yonse yosiyana. Iye adzazitenga zonse izi mmusi kupyola mu Ezekieli, kubwerera ku Genesis, kubwerera ku Chivumbulutso, kubwera mmusi pakati pa Baibulo, kuzimangiriza izo palimodzi; miyala yonseyi ndi mitundu yosiyanasiyana.

Ndi Mzimu Woyera womwewo, Mulungu yemweyo, kusonyeza zizindikiro zomwezo, zodabwitsa zomwezo, kuchita chinthu chomwecho basi monga Iye analonjezera. Ndi Mkwatibwi wa Yesu Khristu akudzikonzekeretsa Yekha pakumva Liwu Lake.

Ife tikukulandirani inu kuti mulumikizane nafe pamene ife tikulowa mu malo ammwambamwamba pa 12:00 p.M., nthawi ya Jeffersonville, kuti tidzamve Eliya, mthenga wa Mulungu mu m’badwo wotsiriza uno, akuwulula zinsinsi zimene zakhala zobisika mu mibadwo yonse.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga:  60-1231 Chivumbulutso,Mutu Foro Gawo I 

Chonde kumbukirani Uthenga wathu wa Chaka Chatsopano, Lachiwiri usiku: Mpikisano 62-1231. Palibe njira yabwinoko yoyambira Chaka Chatsopano.

24-1222 Mphatso Yokulungidwa ya Mulungu

Uthenga: 60-1225 Mphatso Yokulungidwa ya Mulungu

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkazi Wa JEZU,

O Mwanawankhosa wa Mulungu, Inu ndinu Mphatso yayikulu yokulungidwa ya Mulungu ku dziko. Inu mwatipatsa ife Mphatso yaikulu kwambiri imene inayamba yaperekedwapo, Inu eni. Inu musanalenge nyenyezi yoyamba, Inu musanalenge dziko lapansi, mwezi, mphavu ya dzuwa, Inu munatidziwa ife ndi kutisankha ife kukhala mkwatibwi wanu

Pamene Inu munatiwona ife pamenepo, Inu munatikonda ife. Ife tinali mnofu wa mnofu Wanu, fupa la fupa Lanu; ife tinali gawo la Inu. Momwe Inu munatikondera ife ndi kufuna kuyanjana nafe. Munafuna kugawana nafe Moyo Wanu Wamuyaya. Kenako Tidadziwa pamenepo, tidzakhala Anu m’kazi wa JEZU.

Inu munawona kuti ife tidzalephera, kotero Inu munayenera kutipatsa njira yotibwezeretsa ife . Tinali otayika komanso opanda chiyembekezo. Panali njira imodzi yokha, Munayenera kukhala “Chilengedwe Chatsopano”. Mulungu ndi munthu anayenera kukhala Mmodzi. Inu munayenera kuti mukhale ife, kuti ife tikhoze kukhala Inu. Chotero, Inu munaika dongosolo lanu lalikulu zaka zikwi zapitazo m’munda wa Edeni.

Inu mwakhala olakalaka kwambiri kukhala nafe, Mkwatibwi Wanu wangwiro wa Mawu, koma Inu munadziwa poyamba kuti Inu munayenera kutibwezeretsa ife ku zonse zomwe zinatayika pachiyambi. Munadikirira ndikudikirira ndi kudikirira mpaka kufikila tsiku lino kuti mumalize dongosolo Lanu.

Tsiku lafika. Kagulu kakang’ono kamene mudakawona pachiyambi kali pano. Wokondedwa wanu yemwe amakukondani Inu ndi Mawu Anu kuposa china chilichonse.

Inali nthawi yoti Inu mubwere ndi kudziulula Nokha mu thupi la umunthu monga Inu munachitira ndi Abrahamu, ndipo monga Inu munachitira pamene Inu munakhala Chirengedwe chatsopano. Momwe Inu munali kufunitsitsa za tsiku lino kotero kuti Inu mukhoze kuwulula kwa ife zinsinsi Zanu zonse zazikulu zimene zinali zobisika kuchokera ku maziko a dziko.

Inu mumanyadira kwambiri Mkwatibwi Wanu. Momwe Inu mumakondera kumuwonetsera Iye ndi kumuuza Satana, “Ziribe kanthu zomwe iwe ungayese kuchita kwa iwo, iwo sadzasuntha; iwo sadzanyengerera pa Mawu Anga, Liwu Langa. Iwo ali MKWATIBWI WANGA WA MAWU Angwiro.” Iwo ndi okongola kwambiri kwa Ine. Tangoyang’anani pa iwo! Kupyolera mu mayeso awo onse ndi mayesero, iwo amakhala okhulupirika ku Mawu Anga. ndidzawapatsa mphatso yosatha. Zonse zomwe ndili, ndipereka kwa iwo. TIDZAKHALA AMODZI.

Zonse Zomwe tinganene n’zakuti: “JEZU, TIMAKUKONDANI. Tiloleni ife tikulandireni Inu munyumba mwathu. Tiloleni ife tikudzozeni Inu ndi kusambitsani mapazi anu ndi misozi yathu ndi kuwapsyopsyona iwo. Tifuna Tikuuzeni momwe timakukonderani Inu.”

Zonse zomwe ife tili, tikupereka kwa Inu JEZU. Imeneyo ndiyo mphatso yathu kwa Inu JEZU. Timakukondani. Timakukondani Inu. Ife tikukupembedzani Inu.

Ine ndikukuitanani aliyense wa inu kuti adzakhale nafe Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, ndi kumulandira JEZU munyumba mwanu, mu mpingo wanu, mu galimoto yanu, kulikonse kumene inu mungakhale, ndi kulandira Mphatso yaikulu kwambiri imene inayamba yapatsidwapo kwa munthu; Mulungu Mwiniwake akuyankhula ndi kuyanjana ndi inu.

M’bale. Joseph Branham

60-1225 Mphatso Yokulungidwa ya Mulungu

CHIDZIWITSO CHAPADERA

Wokondedwa Mkwatibwi,

Ambuye wayika pamtima wanga kukhala ndi Uthenga Wapadera ndi Utumiki wa Mgonero pa Madzulo a Chaka Chatsopano kachiwiri chaka chino. Ndi chinthu chachikulu chiti chimene tingachite, abwenzi, kuposa kumva Liwu la Mulungu likulankhula kwa ife, kutenga nawo mbali pa Mgonero wa Ambuye, ndi kuperekanso miyoyo yathu ku utumiki Wake pa kulowa mu m’Chaka Chatsopano. Idzakhala nthawi yopatulika bwanji kutsekera dziko kunja, ndi kulumikizana ndi Mkwatibwi pa kusonkhana kwapadera kumeneku mu Mawu, pamene tikunena kuchokera mu mitima yathu, “Ambuye, tikhululukireni ife zolakwa zathu zonse zomwe takhala tikuchita chaka chonse; tsopano tikuyandikira kwa Inu, ndikufunsani ngati mudzatigwira dzanja ndi kutitsogolera chaka chomwe chikubwerachi. Mulole ife tikutumikireni Inu kuposa kale lonse, ndipo ngati icho chiri mu Chifuniro Chanu Chaumulungu, mulole icho chikhale chaka cha Mkwatulo waukulu umene uti uchitike. Ambuye, ife tikungofuna kuti tipite Kwathu kukakhala ndi Inu mu Muyaya.” Ine Sindili onyalanyaza kudikira kusonkhana mozungulira Mpando wachifumu Wake ku msonkhano wapadera wodziperekanso uwu, alemekezeke Yehova.

Kwa okhulupilira okhala mu dera la Jeffersonville, Ine ndikufuna kudzayamba tepi nthawi ya 7:00 pm pa nthawi ya kwathu kuno. Uthenga wonse ndi Mgonero udzakhala pa Wailesi ya Liwu panthawiyo, monga tinachitira m’mbuyomu. Tidzakhala ndi mapaketi a vinyo a Mgonero omwe adzapezeke Lachitatu, pa Disembala 18, kuyambira 1:00 – 5:00 pm, kuti mudzawatengere ku nyumba ya YFYC.

Kwa inu amene mumakhala kunja kwa dera la Jeffersonville, chonde khalani ndi chiyanjano chapadera chimenechi panthawi yomwe ndi yabwino kwa inu kwanuko. Tidzakhala nayo linki yotengera Uthenga ndi Chiyanjano cha Mgonero posachedwapa.

Pamene tikuyandikira Tchuthi cha Khrisimasi, ndikufuna ndikufunireni inu ndi banja lanu Nyengo ya Tchuthi YABWINO NDI YOTETEZEKA, ndi Khrisimasi yabwino, yodzaza ndi chisangalalo cha Ambuye Yesu woukitsidwayo… LIWU.

Mulungu akudalitseni,

M’bale Joseph

Gwero: https://branhamtabernacle.org/en/bt/F6/110067

24-1218 Mau Osazindikirika

Wokondedwa Mkwatibwi Wa Mpingo Wa Pakhomo,

Tiyeni tonse tisonkhane pamodzi ndikunvetsera uthenga 60-1218-Mau Osazindikirika, Lamlungu lino pa 12:00PM,
Nthawi ya ku Jeffersonville.

M’bale. Joseph Branham.

24-1208 M’badwo Wa Mpingo Wa Laodikaya

Uthenga: 60-1211E M’badwo Wa Mpingo Wa Laodikaya

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Osankhidwa,

Taonani, ndaima pakhomo, ndi kugogoda: ngati wina amva mau Anga, ndikutsegula pakhomo, ndidzalowa mwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.

Utumiki, tsegulani makomo anu kwa mngelo wa Mulungu nthawi isanathe. Ikani Liwu la Mulungu libweleleso mu maguwa anu posewera matepi. Ndi Liwu lokhalo lotsimikiziridwa la Mulungu la tsiku lathu ndi Mawu osalephera. Ndi Mau okhawo omwe ali ndi PAKUTI ATERO AMBUYE. Ndi Liwu lokhalo Mkwatibwi aliyense angakhoze kunena AMEN kwa iye.

Ndi m’badwo waukulu kuposa nthawi zonse. Yesu akutipatsa kufotokoza kwa Iye mwini pamene masiku a chisomo chake akutha. Nthawi yafika kumapeto. Iye waulula makhalidwe Ake omwe kwa ife mu m’badwo wotsiriza uno. Watipatsa kuyang’ana komaliza pa Umulungu Wake Wachisomo ndi wapamwamba. M’badwo uwu uli vumbulutso la mwala wa pamutu la Iye mwini.

Mulungu anabwera mu m’badwo wa Laodikaya uwu ndipo anayankhula kupyolera mu thupi la munthu. Liwu Lake linalembedwa ndi kusungidwa kuti litsogolere ndi kupangitsa ungwiro Mkwatibwi wa Mawu Ake. Palibenso Liwu lina limene lingakhoze kupangitsa Mkwatibwi Wake kukhala wangwiro koma Liwu Lake Lomwe.

Mu m’badwo wotsiriza uno, Liwu Lake pa matepi layikidwa pambali; latulutsidwa kunja kwa mipingo. Iwo sasewera matepi. Chotero Mulungu akuti, “Ine ndikutsutsana nanu nonse. Ine ndidzakulavula iwe mkamwa Mwanga. Awa ndi mathero.

“Pa mibadwo isanu ndi iwiri mwa mibadwo isanu ndi iwiri, sindinawone kalikonse koma anthu olemekeza mawu awo omwe kuposa Anga. Chotero pa mapeto a m’badwo uwu Ine ndikulavula inu kutuluka mkamwa Mwanga. Zonse zatha. Ndilankhula inde cha bwino. Inde, ndili pano pakati pa Mpingo. Ameni wa Mulungu, wokhulupirika ndi woona adzadziulula Yekha ndipo izo zikhala NDI MNENERI WANGA.”

Monga mmene zinalili poyamba, iwo akuyenda moona mtima n’kukhala mmene anachitira makolo awo akale m’masiku a Ahabu. Anali mazana anai a iwo, ndipo onsewo anali mu m’gwirizano; ndipo mwa iwo onse kunena chinthu chomwecho, iwo anapusitsa anthu. Koma mneneri MMODZI, MMODZI YEKHA, anali wolondola ndipo ena onse olakwa chifukwa Mulungu anali atapereka vumbulutso kwa MMODZI YEKHA.

Izi sizikunena kuti mautumiki onse ndi abodza ndi kupusitsa anthu. Komanso sindikunena kuti munthu amene ali ndi mayitanidwe otumikira sangathe kulalikira kapena kuphunzitsa. Ine ndikunena kuti Utumiki wofutukuka usanu WOWONA udzayika MATEPI, Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi, ngati Liwu lofunika kwambiri lomwe inu MUYENERA KUMVA. Liwu la pa matepi liri Liwu LOKHALA limene latsimikiziridwa ndi Mulungu Mwiniwake kuti liri PAKUTI ATERO AMBUYE.

Chenjerani ndi aneneri onyenga, pakuti iwo ndi mimbulu yolusa.

Kodi mungadziwe bwanji njira yolondola ya lero? Pali kusiyana koteroko pakati pa okhulupirira. Gulu limodzi la anthu limati utumiki wofutukuka usanu udzachititsa Mkwatibwi kukhala wangwiro, pamene ena amati Kusewera matepi basi. Sitiyenera kugawanika; ife tiyenera kuti tigwirizane ngati MKWATIBWI MMODZI. Yankho lolondola ndi liti?

Tiyeni titsegule mitima yathu palimodzi ndi kumva zomwe Mulungu akunena kudzera mwa mneneri Wake kwa Mkwatibwi. Pakuti ife tonse tikuvomereza, kuti M’bale Branham ndi mngelo mthenga Wake wa wachisanu ndi chiwiri.

Pamaziko a khalidwe laumunthu lokha, aliyense amadziwa kuti pamene pali anthu ambiri pali ngakhale malingaliro ogawanika pa mfundo zazing’ono za chiphunzitso chachikulu chimene onse amagwirizira pamodzi. Ndani ndiye amene adzakhala nayo mphamvu ya kusalephera yomwe iti ibwezeretsedwe mu m’badwo wotsiriza uno, pakuti m’badwo wotsiriza uwu ubwereranso ku kuwonetsera Mkwatibwi wa Mawu Oyera? Izo zikutanthauza kuti ife tidzakhala nawo Mawu kamodzinso monga iwo anaperekedwa mwangwiro, ndi kumveka mwangwiro mu masiku a Paulo. Ndikuuzani amene adzakhala nayo. Iye adzakhala mneneri monga wotsimikiziridwa mwathunthu, kapena ngakhale wotsimikiziridwa mwathunthu kuposa momwe analiri mneneri aliyense mu mibadwo yonse kuchokera kwa Enoki mpaka tsiku lino, chifukwa munthu uyu mofunikila adzakhala nawo utumiki wa uneneri wa mwala wapamwamba, ndipo Mulungu adzamuwonetsa iye apo. Iye sadzasowa kuti aziyankhulire yekha, Mulungu adzayankhula mmalo mwa iye ndi liwu la chizindikiro. Ameni.

Chotero, Uthenga uwu wolankhulidwa ndi mthenga Wake unaperekedwa mwangwiro, ndipo umamveka mwangwiro.

Kodi Mulungu ananenanso chiyani china za mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri wamthenga ndi Uthenga wake?

  • Adzamvera kwa Mulungu yekha.
  • Adzakhala ndi pakuti “atero Ambuye” ndi kuyankhula m’malo mwa Mulungu.
  • Iye adzakhala kamwa ya Mulungu.
  • IYE, MONGA KUNALEMBEDWA PA Malaki 4:6, ADZABWEZERETSA MITIMA YA ANA KUBWELERA KWA ATATE.
  • Iye adzabwezeretsanso osankhidwa a tsiku lomaliza ndipo adzamva mneneri wotsimikiziridwa akupereka choonadi chenicheni monga momwe zinalili ndi Paulo.
  • Adzabwezeretsa chowonadi monga adali nacho.

Ndiyeno kodi Iye ananena chiyani za ife?

Ndipo iwo osankhidwa pamodzi ndi iye mu tsiku limenelo adzakhala iwo amene moona adzawonetsera Ambuye ndi kukhala Thupi Lake ndi kukhala liwu Lake ndi kuchita ntchito Zake. Aleluya! Kodi inu mukuziwona izo?

Ngati mukadali mu kukaikira kulikonse, funsani Mulungu mwa Mzimu Wake kuti akudzazeni inu ndi kukutsogolerani inu, pakuti Mawu amati, “ OSANKHIDWA KUMENE KOKHA SADZAPUSITSIDWA”. Palibe mwamuna aliyense amene angakunyengeni inu ngati ndinu Mkwatibwi.

Pamene Amethodisti analephera, Mulungu anadzutsa ena ndipo kotero izo zapitirira kupyola mu zaka mpaka mu tsiku lotsiriza ili palinso anthu ena mu dziko, amene pansi pa mthenga wawo adzakhala liwu lotsiriza ku m’badwo wotsiriza.

Inde bwana. Mpingo sulinso “choyankhulira” cha Mulungu. Iyemwini ali kamwa payekha. Chotero Mulungu akutembenukira pa iye. Iye adzaphatikizana ndi iye kupyolera mwa mneneri ndi mkwatibwi, pakuti liwu la Mulungu lidzakhala mwa iye. Inde, chifukwa anena m’mutu wotsiriza wa Chivumbulutso vesi 17, “Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani.” Kamodzinso dziko lidzamva molunjika kuchokera kwa Mulungu monga pa zinalili pa Pentekosite; koma ndithudi Mkwatibwi wa Mawu uyo ​​adzakanidwa monga zinalili mu m’badwo woyamba.

Mkwatibwi ali nalo liwu, koma ilo lidzangonena zomwe ziri pa matepi. Pakuti Liwu limenelo ndi LOLUNJIKA KUCHOKERA KWA MULUNGU, motero silikusowa kutanthauzira monga linaperekedwa mwangwiro ndipo limamveka mwangwiro.

Bwerani mudzajowine nafe Lamulungu lino pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, pamene ife tikumva Liwu lija likuwululira kwa ife: M’badwo wa Mpingo wa Laodikaya 60-1211E. 

Mbale. Joseph Branham