Uthenga: 64-0614E Chosamvetseka
- 25-1109 Chosamvetseka
- 24-0225 Chosamvetseka
- 22-0807 Chosamvetseka
- 21-0523 Chosamvetseka
- 16-1130 Chosamvetseka
Wokondedwa Mulungu Wokhala Ndi Chikopa Pa Iye.
Ife Sitili kuseri kwa chophimba tsopano, ana aang’ono, Mulungu wabwera powonekera bwino kwa ife. Mulungu wamphamvu wa Kumwamba ndi dziko lapansi, Amene nthawi zonse wakhala akudziphimba kwa anthu monga Lawi la Moto lomwe linachokera kwa Mulungu ndikukhala m’thupi la padziko lapansi lotchedwa Yesu; kenako anabwerera ku Lawi la Moto ndipo anaonekera kwa Paulo panjira yopita ku Damasiko, tsopano wabweranso powonekera bwino ndipo anakhalanso m’thupi la munthu mwa mngelo wake Mtumiki, William Marrion Branham, akuitana Mkwatibwi Wake kwa Iyemwini.
Mulungu anaika mngelo Wake padziko lapansi kuti adziimire ngati kazembe Wake woyikidwa kuti alowe mu zinthu zazikulu zosadziwika zauzimu. Amazindikira ndi kutulutsa zinthu zomwe malingaliro achithupi sangazindikire. Anatumizidwa kuti abweretse chinsinsi cha Mulungu ndi kulosera zinthu zomwe zilipo, ndi zomwe zakhalapo, ndi zomwe zidzakhalapo. Iye ndi Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi.
Ndi chiyani chimenecho? Mulungu, Mulungu kuseri kwa zikopa, chikopa cha munthu. Kulondola kwenikweni.
Otsutsa ambiri masiku ano sangatimvetse ife okhulupirira enieni. Kwa iwo, takhala ngati nati. Amati ndife okhulupirira milungu ndipo timalambira mneneri…
Wotsutsa, masiku pang’ono apitawo, ananena kwa ine, uko mu Tucson. Iye anati, “Inu mukudziwa, anthu ena amakupangani inu kukhala nati, ndipo ena amakupangani inu kukhala mulungu.”
Ine ndinati, “Chabwino, zimenezo zimayenda bwino.” Ine ndinadziwa kuti iye amayesera kuti anditsutse ine. Mukuona?
Iye anati, “Anthu amaganiza kuti inu ndi mulungu.”
Monga momwe zinalili pamene Yesu anali padziko lapansi, ndi chimodzimodzi lero ndi mneneri Wake. Anthu sali kuseri kwa chophimba; achita khungu ku choonadi. Sitikufuna china chilichonse koma njira yoperekedwa ndi Mulungu lero: Iye mwini wophimbidwa mu thupi, Mawu a Mulungu omwe adalembedwa ndikusungidwa kwa Mkwatibwi.
Pamene Mulungu adawonekera padziko lapansi, Iye anali kubisala kuseri kwa chophimba; kuseri kwa khungu la Munthu wotchedwa Yesu. Anaphimbidwa ndikubisala kuseri kwa khungu la munthu wotchedwa Mose, ndipo iwo anali milungu, osati Milungu; koma iwo anali Mulungu, Mulungu mmodzi, akungosintha chigoba Chake, akuchita zomwezo nthawi iliyonse, kubweretsa Mawu awa. Mulungu adapanga mwanjira imeneyo.
Tangolumikizidwa ku Mawu, Uthenga wa nthawi ino. Tsopano watipanga Mawu ophimbidwa kuseri kwa thupi la munthu. Mkwatibwi ndi Mkwati ndi amodzi. Mulungu ndi mmodzi, ndipo Mawu ndi Mulungu! Talumikizidwa ndi Mawu.
Mwachisoni, kusiyana pakati pa okhulupirira lero ndikuti amamva kuti timayika kwambiri pa mneneri wotsimikiziridwa wa Mulungu. M’malo mwake, akufuna kuyika utsogoleri umenewo kwa abusa awo.
Mulungu sasintha pulogalamu Yake; amatumiza MUNTHU MMODZI kuti atsogolere Mkwatibwi Wake. Ndi Mzimu Wake Woyera mwa aliyense wa ife, kutitsogolera ndi LAWI LA MOTO.
Mawu amadza kwa mmodzi. Mu m’badwo uliwonse, chimodzimodzi, ngakhale mu mibadwo ya mpingo, kuyambira kwa woyamba womwe mpaka kwa wotsiriza. Enawo ali ndi malo awo awo, izo nzoona, zindikirani, koma muzikhala kutali ndi Lawi la Moto ilo. Mukuona?
KOMA TIKUMVA CHIYANI LERO…CHINTHU CHOMWECHO.
Inu mukukumbukira zimene Datani ndi iwo ananena uko? Iwo anati, “Tsopano, Mose, dikira apa miniti chabe! Iwe ukudzitengera wekha kwambiri, mwaona. Tsopano, aliponso anthu ena pano omwe Mulungu wawaitana.”
Sitikutsutsana ndi utumiki; Mulungu wawaitana, koma abale ndi alongo, ngati m’busa wanu sakuika Mawu a Mulungu ngati Mawu ofunikira kwambiri omwe muyenera kumva posewera matepi mu mpingo wanu, sakukutsogolerani ku njira yoperekedwa ndi Mulungu.
Izo ndi zoona. Iwo, mmodzi aliyense, amatsatira mwabwino nthawizonse pamene iwo anali kutsatira, koma pamene wina anayesera kuti adzikweze ndi kutenga malo a Mulungu amene Iye anamupatsa Mose, yemwe anali wokonzedweratu ndi wodzozedweratu ku ntchito imeneyo, kuyesera kuti aitenge iyo, moto unatsika pansi ndipo unadzatsegula nthaka ndi kuwamezera iwo mmenemo. Mukuona? Mukuona? Muzisamala. Mukuona?
Tonsefe tiyenera kulumikizidwa ku Mawu amene analankhulidwa ndi kuikidwa pa matepi. Umenewo ndiye Mtheradi wa Mulungu. Ndiwo Mawu okhawo omwe Mkwatibwi angagwirizane nawo. Utumiki sudzagwirizanitsa Mkwatibwi, koma Mawu a Mulungu okha pa matepi.
Ine sindingachite kalikonse popanda inu; inu simungachite kalikonse popanda ine; komanso sitingachite kalikonse popanda Mulungu. Kotero, pamodzi timapanga thunthu, chilumikizocho. Mulungu ananditumiza ine pa cholinga; inu mukakhulupirira izo, ndipo apo izo zizichitika. Basi ndi zimenezo, Mwaona, kutsimikiziridwa mwangwiro.
Pokhapokha pamodzi zimapanga CHIMODZI, kulumikizana. Mulungu anatumiza William Marrion Branham pa cholinga chimenecho. Ndiye, Pokhapokha ngati mukhulupirira, kodi chidzachitika; zatsimikiziridwa bwino.
Sindine amene ndikunena zimenezo, abale ndi alongo. NDI MULUNGU AKUNENA ZIMENEZO KUDZELA MWA MNENERI WAKE. Musalole munthu aliyense kukuuzani zosiyana kapena kuyesa kukufotokozerani mosiyana. LIWU LA MULUNGU LOKHA PA MATEPI NDILOMWE LINGAGWIRIZANITSE NDI KUMUFIKITSA MKWATIBWI KU UNGWIRO. NDI NJIRA INA ILIYONSE, INU SIMUDZAKHALA MKWATIBWI.
Kotero ine ndikuganiza kuti akuluakulu onse a ife timaganiza chinthu chomwe chomwecho. Mulungu, wokhala ndi khungu pa Iye! [Malo osajambulidwa pa tepi—Mkonzi.] Mulungu, wokhala ndi khungu pa Iye! Izo zikhoza kumveka ngati nati, kwa dziko, koma iyo ikukokera anthu onse kwa Iye.
Kodi mwamva zomwe wangonena kumene? Mulungu wokhala ndi khungu akukoka anthu onse kwa Iye.
Pamene dziko lapansi likulumikizidwa ndi nati, ife tikulumikizidwa ndi Liwu la Mulungu ndipo timatchedwa Mkwatibwi. Likutikoka kuti tituluke mu chisokonezochi, kupita ku Kukhalapo kwa Mulungu. Ife ndife nati ya Mawu a Mulungu.
Bwerani mudzalumikizidwe ndi Mawu a Mulungu limodzi nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ilo likukokela anthu onse kwa Iye.
M’bale Joseph Branham
Uthenga: chosamvetseka. 64-0614E
Malemba: 1 Akorinto 1:18-25. / 2 Akorinto 12:11