Category Archives: Uncategorized

24-1201 Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande

Uthenga: 60-1211M Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande

PDF

BranhamTabernacle.org

M’mawa Wabwino Abwenzi

Sizinayambe zachitikapo mu mbiri yakale ya dziko pamene M’kwatibwi wa Khristu wochokera kuzungulira dziko anakhoza kulumikizidwa palimodzi mu mgwirizano umodzi, pamene mkokomo wochokera Kumwamba, Liwu lomwe la Mulungu, likanakhoza kubwera mothamanga mkati. 

Malemba akukwaniritsidwa.  Ndi nthawi yachilumikizano chizindikiro cha Mbewu.  Chilumikizano chosawoneka cha Mkwatibwi wa Khristu chikuchitika pamene ife tikukhala pamaso pa Mwana wamwamuna, kucha, kudzikonzekeretsa Yekha pakumva Liwu lomwelo la Mulungu. 

Ife tikupangidwa angwiro ndi utumiki Wake wofutukuka pasanu.

Ndi angati amakhulupirira kuti mphatso ndi maitanidwe ziri zopanda kulapa?  Baibulo linati pali mphatso zisanu mu mpingo.  Mulungu anaika mu mpingo Atumwi, kapena amishonare, atumwi, aneneri, aphunzitsi, avangeli, abusa. 

  • Mlaliki: Ine ndingapite kumusi  mumsewu uko. Ndiye  winawake akanati, “Kodi ndiwe mlaliki?”  Ine ndikanati, “Inde bwana.  Inde, ndine mlaliki.” 
  • Mphunzitsi: Ndipo tsopano chifukwa chimene ine sindinayambe ndalalikira mmawa uno, chinali chifukwa, ine ndinaganiza, pophunzitsa, ife tikanamvetsa izo bwinoko kuposa kungotenga mutu ndi kuwulumpha iwo.  Ife tikanangophunzitsa izo.
  • Mtumwi: Mawu akuti “mmishonale” amatanthauza “m’modzi wotumizidwa.”  “Mtumwi” amatanthauza “mmodzi wotumidwa.”  Mmishonale ndi mtumwi.  Ine—ine, ndine mmishonare, monga inu mukudziwa, ndimachita uvangeli, ntchito ya umishonare, pafupi kasanu ndi kawiri kutsidya kwa nyanja, kuzungulira dziko. 
  • Mneneri: Kodi mukundikhulupirira kuti ndine mneneri wa Mulungu?  Kenako pita ukachite zimene ndakuuza. 
  • Abusa: Mukudziwa chimene ndakuchitirani inu?  Inu mumanditcha ine m’busa wanu, ndipo inu mukunena bwino, pakuti chotero ine ndiri. 

Ndipo ine ndinawawona mamilioni awo atayima pamenepo, ine ndinati, “Kodi onsewo ndi a Branham?”  Anati, “Ayi.”  Anati, “Iwo ndi otembenuka anu.”  Ndipo ine ndinati, ine—ine ndinati, “Ine ndikufuna kumuwona Yesu.”   Iye anati, “Ayi.  Idzakhala nthawi Iye asanabwerebe.  Koma Iye adzabwera kwa inu poyamba ndipo inu mudzaweruzidwa ndi Mawu amene inu munawalalikira, 

Ndiye tonse tinakweza manja athu ndi kunenabkuti, “Ife tikupumura pa icho!” 

Chinachake chikukonzekera kuti chichitike.  Chikuchitika ndi chiyani?  Akufa mwa Khristu ayamba kuwuka pozungulira ine.  Ndikumva kusintha kwabwera mthupi langa.  Tsitsi langa la Imvi, lapita.  Yang’anani nkhope yanga … makwinya anga onse atha.  Zopsinja zanga ndi zowawa …. ZAPITA. Maganizo anga ankhawa atha nthawi yomweyo.  Ndasinthidwa mu m’kamphindi, mu m’kuphethira kwa diso.

Kenako tidzayamba kuyang’ana pozungulira ife ndikuwona okondedwa athu.  O mai, pali Amayi ndi Abambo…Ulemelero, mwana wanga wamamuna…mwana wanga wamkazi.  Agogo amuna, Agogo akazi, oh ndinakusowani nonse.  Hei … pali mzanga wakale.  O TAWONANI, ndi M’bale Branham, mneneri wathu, Aleluya!!  Ndi pano.  Zikuchitika! 

Ndiye palimodzi, zonse mwakamodzi, ife tidzakwatudwira kutali kwinakwake mu mlengalenga kuseri kwa dziko lapansi.  Tidzakomana ndi Ambuye panjira Yake yotsika.  Ife tidzayima pamenepo ndi Iye pa mphete za dziko lapansi ndi kuyimba nyimbo za chiwombolo.  Tidzayimba ndi kumuyamika Iye chifukwa cha chisomo Chake chachiwombolo chimene Iye watipatsa ife.

Zonse zomwe zili munkhokwe ndiza Mkwatibwi Wake. Ndi nthawi yanji yomwe ife titi tidzakhale nayo kunthawi zamuyaya wina ndi mzake, ndi Ambuye wathu Yesu.  Mawu achivundi sangakhoze kufotokoza, Ambuye, momwe ife tikumvera mu mitima yathu. 
Ngati inu mukufuna kuti mumumve Iye akukuitanani inu Mkwatibwi Wake, ndi kukuuzani inu momwe izo ziti zidzakhalire ndi Iye, bwerani muzajoinane  nafe Lamulungu lino pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, ndipo inu mudzadalitsidwa mopitirira muyeso.

M’bale.  Joseph Branham

60-1211M –  Anamwali Khumi, Ndi Ayuda Handirede Ndi Forte-Foro Sauzande

24-1124 M’badwo Wa Mpingo Wa Filadelfia

Uthenga: 60-1210 M’badwo Wa Mpingo Wa Filadelfia

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkazi Wa Yesu Khristu,

Kodi Lamulungu lino ligwirizira chiyani kwa Mkwatibwi wa Yesu Khristu? Kodi mchiyani chomwe Mzimu Woyera adzatiwululira ife? Kuzindikira Kwangwiro. Tsopano tidzamvetsetsa bwino lomwe ndi Chivumbulutso, chophiphiritsira chosiyanitsidwa ndi choyimira ndi chinthu ndi mthunzi. Yesu ndiye Mkate weniweni wa Moyo. Iye ali wothunthu wa Iwo. Iye ndi Mulungu Mmodzi. Iye ndi Aheberi 13:8. Iye ali INE NDINE.

Khristu, pakuwonekera mu thupi ndi kukhetsa Magazi Ake omwe, adachotsa machimo athu kamodzi kokha kwamuyaya mwa nsembe ya Iyemwini; chotero Iye tsopano watipanga ife ANGWIRO. Moyo wake womwe uli mwa ife. Mwazi Wake watiyeretsa ife. Mzimu wake umatidzadza ife. Ndi Mikwingwirima Yake yinatichiritsa KALE.
Mawu ake ali mumtima mwathu ndi m’kamwa mwathu. Ali Khristu m’miyoyo yathu ndipo palibe china chilichonse, popeza chilichonse m’miyoyo yathu chinachokamo ndikukukhala chopanda pake, kupatula Iye ndi Mawu Ake.

Mtima wathu udzadzazidwa ndi chimwemwe pamene Iye akutiuza kuti mwa lamulo lake la uzimu, Iye anadziwa ndendende amene adzakhala Mkwatibwi Wake. Momwe Iye anatisankhira ife. Iye anatiyitana ife. Iye anatifera ife. Iye analipira mtengo wa ife ndipo ife ndife ake, ndipo Iye yekha. Amayankhula, ndipo timamvera, chifukwa ndi chisangalalo chathu. Ndife chuma Chake chokhacho ndipo alibe wina koma IFE. Iye ndi Mfumu yathu ya Mafumu ndipo ife ndife ufumu Wake. Ndife chuma chake chamuyaya.

Iye adzatilimbitsa ndi kutiunikira ndi Liwu lake. Adzafotokoza momveka bwino ndikuulula kuti Iye ndiye Khomo la nkhosa. Iye ali zonse Chiyambi ndi Mapeto. Iye ndi Atate, ndi Mwana wa mwamuna, ndi Mzimu Woyera. Iye ali Mmodzi, ndipo ife tiri amodzi ndi Iye ndi mwa Iye.

Adzatiphunzitsa kuleza mtima, monga anachitira Abrahamu, mwa kufotokoza mmene tiyenera kuyembekezera moleza mtima ndi kupirira ngati tikufuna kulandira lonjezo lililonse.

Adzatiwonetsa momveka bwino tsiku lomwe tikukhalamo. Momwe kusuntha kwa matchalitchi kudzalimba kwambiri pazandale, ndi kukakamiza kwa boma kuti onse alowe nawo mwa kutsatira mfundo zokhazikitsidwa ndi kukhala lamulo, kuti pasapezeke anthu kudziwika ngati mipingo pokhapokha ngati pali ulamuliro wachindunji kapena wosalunjika kwa bungwe lawo.
Iye adzawulula kuti ndi angati amene adzapite nawo, akumaganiza kuti akutumikira Mulungu
mu dongosolo la bungwe. Koma Iye amatiuza ife, “Musawope, pakuti Mkwatibwi sadzanyengedwa, ife tidzakhala ndi Mawu Ake, Liwu Lake.

Zidzakhala zolimbikitsa chotani nanga kumva Iye akutiuza kuti: “Gwirani Mofulumira, limbikirani. Osataya mtima, koma valani zida zankhondo zotetenzera zonse za Mulungu, chida chilichonse, mphatso iliyonse yomwe ndakupatsani ili m’manja mwathu. Usataye mtima konse wokondedwa, ingoyang’ana kutsogolo ndi chisangalalo chifukwa udzavekedwa korona ndi Ine, Mfumu yako ya Mafumu ndi Mbuye wa Ambuye, Mwamuna wako. “

Inu ndinu mpingo Wanga woona; kachisi yemweyo wa Mulungu mwa Mzimu Wanga Woyera amene akukhala mwa inu. mudzakhala mizati m’Kacisi watsopano;
maziko omwewo omwe angagwirizanitse mawonekedwe apamwamba. Ine ndidzakuikani inu ngati wogonjetsa limodzi ndi atumwi ndi aneneri, pakuti Ine ndakupatsani inu Vumbulutso la Mawu Anga, la Inemwini.

Iye adzawulula momveka bwino kwa ife kuti maina athu analembedwa mu Bukhu la Moyo wa Mwana wa nkhosa Wake asanayikidwe maziko a dziko. Chotero tidzakhala pamaso pa mpando wake wachifumu usana ndi usiku kumtumikira Iye m’kachisi wake. Ndife chisamaliro chapadera cha Ambuye; ndife Mkwatibwi Wake.

Tidzakhala ndi dzina latsopano potenga dzina lake. Lidzakhala dzina limene lidzapatsidwa kwa ife pamene atitengera kwa Iyemwini. Ife tidzakhala Mkazi Wake Wa Yesu Khristu.

Yerusalemu watsopano akutsika kuchokera kwa Mulungu kuchokera kumwamba, Mkwatibwi wokongoletsedwera Mwamuna wake. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kapena kulira. ndipo sipadzakhalanso chowawitsa, pakuti zoyambazo zapita; Malonjezo onse odabwitsa a Mulungu adzakwaniritsidwa. Kusintha kudzamalizidwa. Mwana wa nkhosa ndi Mkwatibwi Wake adzakhala kwanthawizonse okhazikika mu ungwiro wonse wa Mulungu.

Wokondedwa Mkazi Wa Yesu Khristu, LOTANI ZA IZO. Zidzakhala zodabwitsa kwambiri kuposa momwe mungaganizire.

Ine ndikuyitana aliyense kuti abwere kudzatijowina ife Lamulungu lino pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene Mwamuna wathu, Yesu Khristu, akuyankhula kupyolera mwa mthenga Wake wamphamvu wa mngelo wachisanu ndi chiwiri ndi kutiuza ife zinthu zonse izi.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga: M’badwo Wa Mpingo Wa Filadelfia 60-1210

24-1117 M’badwo Wa Mpingo Wa Sarde

Uthenga: 60-1209 M’badwo Wa Mpingo Wa Sarde

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Anthu A Tepi,

Ndife onyadira bwanji kutchedwa “Anthu a Tepi”. Mitima yathu imathamanga ndi chisangalalo mlungu uliwonse podziwa kuti tidzakhala osonkhana Pamodzi padziko lonse lapansi pomva Liwu la Mulungu likuyankhula kwa ife.

Tikudziwa, popanda mthunzi wa chikaiko chimodzi, tili mu Chifuniro changwiro cha Mulungu pakukhala ndi Mawu Ake; kumvetsera ku Liwu Lake mwa njira ya mngelo Wake wamphamvu wamthenga wachisanu ndi chiwiri.

Mtumiki yemwe Iye anamusankha wa tsiku lathu ndi William Marrion Branham. Iye ndiye nyali ya Mulungu pa dziko lapansi, ikuunikira kuunika kwa Mulungu. Iye akuyitana mkwatibwi wosankhidwa Wake wa Mawu Oyera mwa mngelo Wake.

Mwa kuphunzira mosamalitsa kwa Mawu Ake, Iye waululira kwa ife mwa Mzimu Wake Woyera kuti William Marrion Branham ndi mngelo yemwe Iye anamusankha kuti apereke Chivumbulutso Chake ndi Utumiki kwa tsiku lathu. Ife tikuona mngelo Wake, NYENYEZI YATHU, mu dzanja Lake lamanja pamene Iye akumupatsa iye mphamvu Yake kuti awulule Mawu Ake ndi kuitana kunja Mkwatibwi Wake.

Iye watipatsa ife Vumbulutso lathunthu la Iyemwini. Mzimu Woyera kudzizindikiritsa Yekha kwa ife kupyolera mu moyo wa mtumiki Wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri; mngelo amene anamusankha kukhala maso ake a m’tsiku lathu lino.

Momwe mitima yathu imatenthera mkati mwathu pamene Iye amatiuza ife ndi Uthenga uliwonse kuti ndi cholinga Chake kutibweretsera ife kwa Iye mwini; kuti ndife Mkwatibwi wa Mawu Ake.

Iye amakonda kutiuza mobwereza bwereza momwe Iye anatisankhira ife asanaikidwe maziko a dziko MWA IYE. Momwe ife tinadziwidwiratu ndi kukondedwa ndi Iye.

Momwe ife timakondera kumumva Iye akuyankhula ndi kutiuza ife kuti tinawomboledwa ndi Magazi Ake ndipo MKOSATHEKA kubwera mu kutsutsidwa. Sitingakhale konse mu mchiweruzo, chifukwa tchimo silingawerengedwe kwa ife.

Momwe ife titi tidzakhale ndi Iye pamene Iye akutenga mpando Wake wachifumu wapadziko lapansi wa Davide, ndipo ife tikulamulira ndi Iye; monga anachitira kumwamba, ndi mphamvu ndi ulamuliro pa dziko lonse lapansi. Mayeso ndi mayesero a moyo uno adzawoneka ngati opanda pake.

Koma watichenjezanso za mmene tiyenera kusamala. Kuti mu mibadwo yonse mipesa iwiriyo inamera mbali ndi mbali. Momwe mdani nthawi zonse wakhala ali pafupi kwambiri; wonyenga kwambiri. Ngakhale Yudasi anasankhidwa ndi Mulungu, ndipo anaphunzitsidwa mu choonadi. Anagawana chidziwitso cha zinsinsi. Iye anali ndi utumiki wa mphamvu wopatsidwa kwa iye ndipo iye anachiritsa odwala ndi kutulutsa ziwanda mu Dzina la Yesu. Koma iye sakanakhoza kupita njira yonse.

Inu simungakhoze kupita limodzi ndi gawo chabe la Mawu, inu muyenera kutenga Mawu ONSE. Pali anthu amene amaoneka okhudzidwa ndi zinthu za Mulungu pafupifupi zana limodzi pa zana, koma satero.

Iye anati sikunali kokwanira kuti Iye wadziphatikiza Yekha ndi mpingo wonse, kapena ngakhale ndi utumiki usanu wa Aefeso 4. Iye anatichenjeza ife kuti mu m’badwo uliwonse mpingo umasokera, ndipo si anthu wamba okha komaso gulu la atsogoleri achipembedzo — abusa ali olakwa monganso nkhosa.

Chotero mwa uphungu wotsimikizirika wa chifuniro Chake chomwe, Iye anadzibweretsa Yekha powonekera mu m’badwo wathu monga M’busa Wamkulu mu utumiki wa mthenga Wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri kutsogolera anthu Ake kubwerera ku choonadi ndi mphamvu yochuluka ya choonadi chimenecho.

Iye ali mwa Mthenga Wake ndipo amene angakhale ndi chidzalo cha Mulungu adzatsatira Mtumiki monga Mtumikiyo ali wotsatira wa Ambuye mwa Mawu Ake.

Ine ndikufuna kukhala nacho chidzalo cha Mulungu ndi kutsatira mtumiki Wake. Kotero, kwa ife, aku m’pingo wa Branham , njira yokhayo yotsatirira mtumiki pamene iye akutsatira Ambuye mwa Mawu Ake, ndi KUSINDIKIZA KUSEWERA ndi kumva Liwu Loyera la Mulungu likulankhula kwa ife mawu osalephera.

Sitiyenera kuganiza kapena kuyang’ana zomwe tikumva, timangoyenera Kusindikiza kusewera ndikukhulupirira Mawu aliwonse omwe tikumva.

Ine ndinamumva M’bale Branham akunena mawu otsatirawa molawirira mmawa wina pa wailesi ya liwu. Nditamva Izi, zidabwera mu mtima mwanga kuti umu ndi momwe timamvera tikamati:

TIMANGOSINDIKIZA KUSEWERA NDI KUMVETSEMVERA MA TEPI.

Zinamveka ngati mawu a Chikhulupiriro chathu kwa ine.

Ndicho chifukwa ine ndimakhulupirira mu Uthenga uwu, ndi chifukwa Iwo umachokera ku Mawu a Mulungu. Ndipo chirichonse chakunja kwa Mawu a Mulungu, ine sindimakhulupirira izo. Izo zikhoza kukhala chomwecho, komabe ine ndingokhala ndi zomwe Mulungu ananena, ndiyeno ndidzakhala wotsimikiza kuti ine ndikulondola. Tsopano, Mulungu akhoza kuchita chimene Iye akufuna. Iye ndi Mulungu. Koma bola ngati ine ndikhala ndi Mawu Ake, ndiye ine ndimadziwa kuti izo nzabwino. Ndikukhulupirira zimenezo.

Ulemerero, iye anati izo ndi ZANGWIRO KWAMBIRI. Utumiki wina uliwonse ukhoza kukhala, chifukwa Mulungu akhoza kuchita zomwe Iye akufuna, ndi yemwe Iye akufuna kutero, Iye ndi Mulungu. Koma bola ngati ine ndikhala ndi Mawu Ake, Liwu Lake, Matepi, ndiye ine ndimadziwa kuti izo ndizolondola. Ndikukhulupirira zimenezo.

Ndikudziwa kuti ambiri amawerenga makalata anga ndipo samamvetsetsa zomwe ndikunena komanso zomwe ndimakhulupirira kuti ndi Chifuniro cha Ambuye kwa mpingo wathu. Ndiloleni ndinenenso modzichepetsa monga momwe mneneri ananenera kuti: “Makalata amenewa analembedwera mpingo wanga wokha. Iwo amene akukhumba kuti azitchula kuti Branham Tabernacle ndi mpingo wawo. Omwe AMAFUNA KUDZIWIKA NDI KUTCHEDWA ANTHU A TEPI”.

Ngati simukugwirizana ndi zomwe ndikunena komanso kukhulupirira, zili bwino abale ndi alongo anga. Makalata anga sanalembedwe kwa inu kapena motsutsana ndi inu kapena mipingo yanu. Mpingo wanu ndi woyima pawokha ndipo muyenera kuchita monga momwe mukumverera kuti mukutsogozedwa kuti muchite, koma molingana ndi Mawu, momwemonso kotero Uli wathu, ndipo izi ndi zomwe tikukhulupirira kuti ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu kwa ife.

Nonse ndi olandiridwa nthawi zonse kusonkhana nafe Lamlungu lililonse pa 12:00 P.M., nthawi ya Jeffersonville. Sabata ino, Nyenyezi ya Mulungu ya m’badwo wathu, William Marrion Branham, adzakhala kutibweretsera ife Uthenga, 60-1209 M’badwo wa Mpingo wa Sardean.

M’bale. Joseph Branham

24-1110 M’badwo Wa Mpingo Wa Tiyatira

Uthenga: 60-1208 M’badwo Wa Mpingo Wa Tiyatira

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wowunikiridwa,

Momwe Ambuye akuwululira kwa ife kuti mu mibadwo yonse pakhala pali gulu laling’ono lomwe limakhala ndi Mawu Ake. Iwo sanagwere mu msampha wonyenga wa mdani, koma anakhala owona ndi okhulupirika ku Mawu a tsiku lawo.

Koma sipanakhalepo nthawi, kapena gulu la anthu, limene Ambuye wakhala wonyada nalo, kapena anali ndi chidaliro chochuluka kuposa ife. Ife ndife Mkwatibwi Wake Wachikazi Wosankhidwa yemwe sadzanyengedwa, ndipo ngakhalenso chofunika kwambiri, NDIZOSATHEKA, kunyengedwa; pakuti ife timamva Liwu la M’busa ndi kumutsatira Iye.

Iye akutiwonetsa ife kuti mu mibadwo yonse pakhala pali magulu awiri a anthu, onse akulengeza vumbulutso lawo kuchokera kwa Mulungu ndi ubale wawo ndi Mulungu. Koma Iye anatiuza ife, Ambuye akuwadziwa iwo amene ali Ake. Amalondola maganizo athu. Iye amadziwa zimene zili m’mitima mwathu. Iye amawona ntchito zathu pakukhala ndi mneneri ndi Mawu Ake, omwe ali chiwonetsero chotsimikizika cha zomwe zili mkati mwathu. Maganizo athu, zolinga zathu zimadziwika kwa Iye pamene Iye amayang’anira zochita zathu zonse.

Amatiuza kuti malonjezano onse amene anapereka ku m’badwo uliwonse, ndi ATHU. Iye amationa ife amene tikupitiriza kuchita ntchito zake mokhulupirika mpaka mapeto. WATIPATSA mphamvu pa mafuko. Amatiuza kuti ndife olamulira amphamvu, okhoza, osasunthika amene angathe kupirira mwamphamvu vuto lililonse. Ngakhale mdani wothedwa nzeru adzasweka ngati pangafunike kutero. Chisonyezero chathu cha ulamuliro ndi mphamvu Yake chidzakhala ngati cha Mwana wa mamuna yemweyo. ULEMERERO!!

Taona kuzama kwa Mulungu m’moyo wathu. Ndizochitika zaumwini za Mzimu wa Mulungu kukhala mwa ife. Malingaliro athu amawalitsidwa ndi nzeru ndi chidziwitso cha Mulungu kudzera m’Mawu ake.

Timapita kulikonse kumene Mkwati ali. Sitidzasiyidwa ndi Iye. Sitidzachoka kumbali Yake. Tidzagawana naye mpando wachifumu. Tidzavekedwa korona wa ulemerero ndi ulemu Wake.

Iye watiululira ife momwe mdani wakhala akunyenga mu m’badwo uliwonse ndi momwe kuliri kofunika KUKHALA NDI MAWU AKE OYAMBIRIRA. Palibe Mawu amodzi omwe angasinthidwe. M’badwo uliwonse unawonjezedwapo ndi kuchotsedwapo, kuyika kutanthauzira kwawo kwawo ku Mawu apachiyambi; ndipo amatayika kosatha potero.

Mu M’badwo wa Mpingo wa Tiyatira, mzimu wachinyengo uwo unayankhula kupyolera mwa papa waku Roma ndi kusintha Mawu Ake. Analipanga kukhala “mkhalapakati mmodzi pakati pa Mulungu ndi munthu (osati anthu).” Chotero tsopano iye akuyimira pakati pa mkhalapakati ndi anthu. Chotero, dongosolo lonse la Mulungu linasinthidwa; osati pakusintha liwu, koma pakusintha LEMBO IMODZI. Satana anali atasintha “E” kukhala “A”.

Mawu aliwonse adzaweruzidwa ndi Mawu Ake Apachiyambi oyankhulidwa pa matepi. Chotero, Mkwatibwi Wake AYENERA kukhala ndi matepi. Pamene mdani akuyesera kuwafooketsa anthu powapatsa iwo dongosolo losiyana, lingaliro losiyana, chilembo chosiyana, Mkwatibwi AKHALA NDI MAWU OYAMBIRIRA.

Mu m’badwo uliwonse Yesu akudzizindikiritsa Yekha ndi mtumiki wa m’badwo umenewo. Iwo amalandira kuchokera kwa Iye vumbulutso pa Mawu a m’badwo wawo. Vumbulutso la Mawu ili likubweretsa osankhidwa a Mulungu kuchokera mdziko ndi kulowa mu chiyanjano chathunthu ndi Yesu Khristu.

Iye waitana ndi kudzoza amuna ambiri kuti akhale mdalitso kwa mpingo, koma Iye YEKHA ali ndi MTUMIKI MMODZI yekha amene Iye anamuitana kuti ATSOGOLELE Mpingo Wake mwa Mzimu Wake Woyera. Pali LIWU LIMODZI ndilo PAKUTI ATERO AMBUYE. Pali LIWU LIMODZI limene anena kuti adzatiweruza nalo. Pali LIWU LIMODZI lomwe Mkwatibwi Wake akuyika popita kwawo Kwamuyaya. LIWU LIMENERO NDI LIWU LA MULUNGU PA MATEPI.

Mkwatibwi, chifuniro cha Mulungu kwa ife ndi Ungwiro, ndipo pamaso pake, ndife Angwiro. Ndipo ungwiro umenewo ndi chipiriro, kuyembekezera pa Mulungu…ndi kuyembekezera Mulungu. Amatiuza kuti ndi njira ya makhalidwe athu.

Tikhoza kukhala ndi mayesero, mayesero ndi masautso ambiri, koma kukhulupirika kwanu ku Mau ake kukugwira ntchito chipiriro mwa ife kuti tikhale angwiro ndi amphumphu, osasowa kanthu.

Ife sitidzaiwala konse CHIKHULUPIRIRO chimadza pakumva, kumva Mawu, ndipo Mawu amadza kwa mneneri.

Bwerani ndi kudzawona chisangalalo chachikulu cha moyo wanu pamene mukukhala limodzi nafe mu malo ammwambamwamba pamene tikumva Liwu la Mulungu likutibweretsera ife Mawu pa: M’badwo wa Mpingo wa Tiyatira 60-1208, pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville.

M’bale. Joseph Branham