Category Archives: Uncategorized

25-0413 Chisindikizo Chachisanu

Uthenga: 63-0322 Chisindikizo Chachisanu

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Akupumula,

Ife tiri pano. Ife Tafika. Kutsimikizira kwa Mawu kwatsimikizira kuti Vumbulutso lathu la Uthenga uwu likuchokera kwa Mulungu. Ife tiri mu CHIFUNIRO Chake CHANGWIRO pakukhala ndi Liwu la Mulungu pa matepi.

Kodi KUKANIKIZA KUSEWERA ndikofunika bwanji? Mawu omwe tikuwamva pa matepi ndi ofunikira kwambiri, opatulika kwambiri, mwakuti Mulungu Mwiniwake sakanawadalira Iwo ngakhale kwa Mngelo…osati ngakhale kwa mmodzi wa Angelo Ake a Kumwamba. Izo zinkayenera kuti ziwululidwe ndi kubweretsedwa kwa Mkwatibwi Wake ndi mneneri Wake, chifukwa ndi amene Mawu a Mulungu amadzako, mneneri Wake, YEKHA.

Mulungu anadulapo Zisindikizo, analipereka Ilo kwa mtumiki Wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri, ndipo anawulula Bukhu lonse la Chivumbulutso kwa iye. Kenako, Mulungu analankhula kudzera mwa mngelo Wake wapadziko lapansi ndipo anaulula ZONSE kwa Mkwatibwi Wake.

Kanthu kakang’ono kalikonse mwatsatanetsatane kalankhulidwa ndikuwululidwa kwa ife. Mulungu adatisamala ife kwambiri moti sanangotiuza zimene zakhala zikuchitika pano padziko lapansi kuchokera pachiyambi cha nthawi komanso analankhula kudzera mwa mngelo wake ndi kutiuza ife za zimene zikuchitika pano m’malo ngati paradaiso pakali panopa.

Sanafune kuti tizidera nkhawa, kapena kuti tisakayikire zimene zidzatichitikire tikadzachoka m’chihema chimenechi. Kotero, Mulungu Mwiniwake anamutengera mngelo Wake wamphamvu wachisanu ndi chiwiri kudutsa katani la nthawi, kotero kuti iye akakhoze kuchiwona Icho, kuchimverera Icho, ngakhale kuyankhula kwa iwo Kumeneko. Sanali masomphenya, iye anali UKO.

Mulungu anamutengera kumeneko kuti abwerere nadzatiuza kuti: “Ndinali kumeneko, ndinaziwona Izo. Zikuchitika TSOPANO…Amayi athu, atate athu, abale athu, alongo athu, ana aamuna, ana aakazi, akazi, amuna, agogo, Mose, Eliya, WOYERA ONSE amene anatsogola kale ali kumeneko atavala Zovala Zoyera, akupumula ndi kutiyembekezera ife”.

Ife sitidzaliranso, chifukwa Icho chidzakhala chimwemwe chokhachokha. Sitidzakhalanso achisoni, chifukwa Icho chidzakhala chisangalalo chokhachokha. Ife sitidzafa konse, chifukwa Iwo ndi moyo wosatha. Sitingathe kukalamba, chifukwa tonse tidzakhala achichepere kwamuyaya.

Ndi ungwiro…kuphatikizapo ungwiro…kuphatikizaponso ungwiro, ndipo ife tikupita kumeneko!! Ndipo monga Mose, sitisiya ngakhale chiboda,IFE TONSE TIKUPITA… BANJA LATHU LONSE.

Kodi kuli kofunika bwanji KUKONDA m’ngelo wamphamvu wachisanu ndi chiwiriyo?

Ndipo Ilo linafuula, linati, “Zonse zomwe inu munazikondapo…” mphotho ya utumiki wanga. Ine sindikusowa mphotho. Iye anati, “Zonse zimene inu munazikondapo konse, ndi zonse zomwe zinayamba zakukondani inu, Mulungu wazipereka kwa inu.”

Tiyeni tiwerengenso chonde: Kodi Iye anati chiyani?….Mulungu wakupatsani INU!!

Ndipo tidzalowa nawo limodzi ndikukuwa, “Tikupumula

Kodi kopita kwathu kwamuyaya tikupumulira pa chiyani? MAWU ALIWONSE AMENE ANALANKHULIDWA PA MATEPI. Ndine wothokoza kwambiri kwa Ambuye kuti watipatsa Vumbulutso Loona kuti kumakanikiza kusewera ndichinthu CHOFUNIKA KWAMBIRI chomwe Mkwatibwi ayenera kuchita.

Kodi mungafune kupumula nafe? Bwerani mudzalumikizane nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tikumva zonse za tsogolo, komwe tikupita, ndi momwe tingakafikire kumeneko, pamene tikumva Liwu la Mulungu likulankhula ndi kutsegula:  Chisindikizo Chachisanu 63-0322.

M’bale. Joseph Branham

Malemba oti muwerenge musanamve Uthenga:
Danieli 9:20-27 Machitidwe 15:13-14 Aroma 11:25-26 Chivumbulutso 6:9-11 / 11:7-8 / 22:8-9

25-0406 Chisindikizo Chachinai

Uthenga: 63-0321 Chisindikizo Chachinai

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Oyera Obadwira Kumwamba

Atate akutisonkhanitsa ife palimodzi mwa Mawu Ake, ndipo kutsimikizira kwa Vumbulutso limenelo kuli kutipatsa ife kukondoweza. Iye anatisankha ife asanaikidwe maziko a dziko, chifukwa Iye ankadziwa kuti ife tikanakhala okhulupirika ku Mawu Ake mwa kusankha kwathu komwe.

Ndiroleni ine ndinene izo kachiwiri kuti izo zilowerere mwakuya kwenikweni. Iye anayang’ana mu nthawi yonse, mpaka mapeto a nthawi zonse, ndipo ANATIONA IFE…kodi inu mukumva zimenezo? IYE ANAKUONA IWE, IYE ANANDIONA INE, ndipo anatikonda ife, chifukwa mwa kusankha kwathu komwe, ife tikanati TIKHALE NDI MAWU AKE.

Pomwepo, Iye ayenera kuti anasonkhanitsa angelo Ake onse ndi akerubi ndi kutilozera kwa ife ndi kunena kuti: “UYO NDI IYE,” “UYO NDI MKWATIBWI WANGA,” “IWO NDIWO AMENE INE NDAKHALA NDIKUWAYEMBEKEZERA!

Monga Yohane, ndicho chifukwa ife tikuchita kufuula konse uku ndi kukuwa, ndi kutamanda Ambuye, ife takondowezedwa pa Vinyo Watsopano ndipo Ife tikudziwa, MOSAKAYIKILA, IFE NDIFE Mkwatibwi Wake.

Zili ngati mvula yonse ndi mikuntho yomwe takhala nayo muno mu Jeffersonville sabata ino…Ifenso tikutumiza CHENJEZO ku dziko.

Mkwatibwi akukhala ndi Bingu la VUMBULUTSO, NDIPO IZO ZIKUPANGA KUSEFUKURA KWAMPHAVU KWA VUMBULUTSO. MKWATIBWI WADZIKONZEKERETSA YEKHA NDI KUZINDIKIRA YEMWE IWO ALI . PITANI MUM’CHITETEZO MOFULUMIRA. KANIKIZANI SEWERANI KAPENA MUWONONGEDWE.

Ife Sitikukhala mu M’badwo wa Mkango, kapena M’badwo wa Ng’ombe, kapena M’badwo wa Munthu; ife tikukhala mu M’BADWO WA Mphungu, ndipo Mulungu watitumizira ife mphungu yamphamvu, Malaki 4, kuti iitane ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake.

Zidzakhala zoyenera bwanji Lamlungu lino, pamene Ife tidzakhala olumikizana pamodzi kumvetsera Chisindikizo Chachinai. Lidzakhala Tsiku la Kubadwa kwa mphungu ya mphavu mneneri wa Mulungu.

Tiyeni tikondwerere tsiku lodabwitsali ndikuthokoza Ambuye chifukwa chotitumizira Ife mthenga wake wa chiwombankhanga, amene anamutuma kuti atiitane Ife ndi kutiululira Ife Mau Ake.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga: Chisindikizo Chachinai 63-0321
Nthawi: 12:00 PM, nthawi yaku Jeffersonville
Malemba oti muwerenge pokonzekera.

Mateyu Woyera 4
Luka Woyera 24:49;
Yohane Woyera 6:63
Machitidwe 2:38
Chivumbulutso 2:18-23, 6:7-8, 10:1-7, 12:13, 13:1-14, 16:12-16, 19:15-17
Genesis 1:1
MaSalimo 16:8-11
2 Samueli 6:14
Yeremiya 32
Yoweli 2:28
Amosi 3:7
Malaki 4

25-0330 Chisindikizo Chachitatu

Uthenga: 63-0320 Chisindikizo Chachitatu

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Eva Wauzimu,

Ndiroleni ine ndiyambe kalata yanga lero ndi bomba la atomiki la Mulungu; osati mfuti ya zipolopolo makumi awiri ndi ziwiri kwa Mkwatibwi wa Yesu Khristu.

Tsopano, ngati inu mukufuna kuzilemba izo; Inde, inu nonse mumawadziwa: Yesu, Yohane 14:12; ndi Yoweli, Yoweli 2:38; Paulo, Timoteo Wachiwiri 3; Malaki, mutu wa 4; ndi Yohane mvumbulutsi , Chivumbulutso 10:17, 1-17 . Mwaona, ndendende zomwe zikanati zidzachitike tsopano!

Chidziwitso ndi chenjezo: Mawu otsatirawa si anu ngati mumakhulupirira.

“Ife timayika kwambiri pa mneneri wa Mulungu.” “Iwe sungakhale Mkwatibwi ngati iwe ungomvetsera kwa mneneri.” “Kusewera matepi mu mpingo ndi kulakwa.” “Tochi yadutsidwa; chofunika kwambiri masiku ano ndikumvetsera ulaliki.” “Kuyikanikiza kusewera zonse pa nthawi imodzi ndi chipembedzo.”

Kwa mpingo, ndi chiyani Icho? Mawu mu thupi anapangidwa thupi pakati pa anthu Ake kachiwiri! Mwaona?

Bumu…Choncho poyikanikiza kusewera, titha kumva Mawu obadwa thupi akusandulika thupi, akulankhula kuchokera ku mlomo kupita ku khutu kwa ife pamene Iye akuwulula Mawu Ake.

Ndipo wina anganene kuti si MAWU OFUNIKA KWAMBIRI KUWAMVA? Gawo ili la mawuwo ndi lanu.

Ndipo iwo sakhulupirira Izo basi.

Pamene vumbulutso lochuluka limene Ambuye amatipatsa ife la Mawu Ake, ndi chimene ife tiri, ndipamenenso aliyense kunja kwa vumbulutso limenero amafikira kutali.

Ndiroleni ine ndinene icho, kwenikweni, kotero inu mudza…icho chidzalowerera mpaka pansi. Ine ndikufuna ichi kuti mumvetse icho. Ndilo liri vuto ndi inu lero, onani, inu simukuwadziwa Mawu! Mwawona?

Mulungu ali ndi amuna odzozedwa kuti azilalikira Uthenga uwu, koma pali Mtheradi umodzi wokha: Mawu. Pamene mumva mtumiki, kapena wina aliyense akulankhula, muyenera kukhala ndi chikhulupiriro kuti mukhulupirire kuti zimene akunena ndi NDENDENDE zomwe Mneneri wa Mulungu ananena kale. Mawu awo, vumbulutso lawo, kutanthauzira kwawo kukhoza kulephera; Liwu la Mulungu pa matepi SILINGALEPHERE KONSE.

Kuyankhula za Mulungu mu kuphweka ndikukanikiza kusewera…Akunenanso izo mobwereza.

Iwo amamuphonya Iye, Mawu amoyo owonetseredwa mu thupi, mwa Mawu amene alonjezedwa. Mawu analonjeza kuchita zinthu izi. Lonjezo linapangidwa, kuti izo zidzakhala monga chonchi mu masiku otsiriza.

Mvetserani ku Bingu Lake. Bingu ndi Liwu la Mulungu. William Marrion Branham ndi Liwu la Mulungu kwa m’badwo uno.

M—Mkwatibwi sanakhalebe nacho chitsitsimutso. Mwawona? Pakhala palibe chitsitsimutso pamenepo, palibe mawonetsedwe a Mulungu kuti amukondoweze Mkwatibwi panobe. Mwawona? Ife tikuyang’anira chimenecho tsopano. Zidzatengera mabingu asanu ndi awiri awo osadziwika kumbuyo uko, kuti amudzutse Iye kachiwiri, onani. Eya. Iye adzachitumiza icho. Iye analonjeza icho. Tsopano yang’anani.

Inu mukhoza kuzipotoza izo ngati mukufuna, koma Mabingu Asanu ndi awiri adzapatsa Mkwatibwi kukondoweza mwa Vumbulutso ndi chikhulupiriro chokwatulitsa, chimene chimadza kokha mwa Mzimu Woyera kuyankhula kupyolera mwa mneneri wa Mulungu. Zikuchitika TSOPANO padziko lonse lapansi. Mulungu ali ndi Mkwatibwi Wake Wokondowezedwa ndi Mawu Ake.

Osati zokhazo, koma Iye wamuwuza kale mdani wathu choti achite.

Iwe uchotse manja ako pa iwo. Iwo akudziwa kumene iwo akupita, pakuti iwo adzozedwa nawo Mafuta Anga. Ndipo pakukhala odzozedwa nawo Mafuta Anga, iwo ali naye vinyo wa chisangalalo, chifukwa iwo akudziwa Mawu Anga a lonjezo, ‘Ine ndidzawawukitsa iwo kachiwiri.’ Usati upweteke Izo! Usati upite kukayesa kuwasokoneza iwo.

Iye Wauza mdani wathu kuti achotse manja ake oipa pa ife. Koma kodi matenda angativutitsebe? Inde. Kodi tidakali ndi mavuto? Inde. Koma Iye anatiuzanso zoyenera kuchita.

Ndi zakuya. Werengani pang’onopang’ono ndi mobwerezabwereza.

Asanakhale Mawu, ali ganizo. Ndipo ganizo liyenera kulengedwa. Chabwino. Kotero, maganizo a Mulungu anakhala chirengedwe pamene iwo analankhulidwa, mwa mawu. Ndipo pamene Iye apereka iwo kwa—kwa inu ngati ganizo, ganizo Lake, ndipo ilo lawululidwa kwa inu. Ndiye, likadali ganizo mpaka inu mutalankhula ilo.

Malingaliro ake anakhala chilengedwa pamene icho chinalankhulidwa. Ndiye, maganizo Ake anaperekedwa ndi kuvumbulutsidwa kwa ife monga Mawu. Tsopano Ilo likadali ganizo ndi ife mpaka ife titayankhula Ilo. CHONCHO IFE TIMALANKHULA… NDIKUZIKHULUPIRIRA IZO.

Ine ndine Mbewu Yachifumu ya Abrahamu. Ine ndine Mkwatibwi wa Khristu. Ine ndinasankhidwa ndi kukonzedweratu asanaikidwe maziko a dziko kuti ndikhale Mkwatibwi Wake, ndipo palibe chimene chingasinthe zimenezo. Lonjezo lirilonse la m’Baibulo ndi langa. Ndi Mawu Ake kwa ine. Ndine wolowa wa Lonjezo lomwelo. Iye ndiye Ambuye Mulungu amene amachiritsa nthenda zanga zonse. Chirichonse chimene ine ndikufuna ndi changa, Mulungu ananena chomwecho.

Mulungu mu Kuphweka: Chikhulupiriro chimadza pakumva, kumvera Mawu. Mawu amadza kwa mneneri.

Aliyense akufuna kugwiritsa ntchito “ZOBWEREZA” kutsimikizira malingaliro awo, maganizo awo, uthenga wawo. Ndipo iwo akulondola, chomwechonso ine, ndi chifukwa chake zonse zomwe ine ndikukupatsani inu ndi mawu obwereza kuti ndikuuzeni inu: Khalani nawo Matepi. Mvetserani kwa Liwu limenelo. Liwu limenelo ndi Liwu la Mulungu. Inu muyenera kukhulupirira Mawu aliwonse pa Matepi, osati zomwe wina aliyense anena. Liwu Limenelo NDI MAWU OFUNIKA KWAMBIRI OMWE MUYENERA KUMVA.

Ena amagwiritsa ntchito mawu obwereza kuti akubweretseni inu ku utumiki wawo, ku mpingo wawo, kutanthauzira kwawo, vumbulutso lawo. “Khalani ndi abusa anu.” (Chabwino, ine ndimazikonda izo nanenso, chifukwa ife timachitaso izo, abusa osiyana basi.) “Iye si nsangalabwi yokhayo pa gombelo.” “Iye sananene ku kusewera matepi mu tchalitchi.”

Musati muyike kumasulira kwamtseri kulikonse kwa Iwo. Iye akufuna angwiro, osakhudzidwa, osati ngakhale kudzivula. Ine sindingafune mkazi wanga kumavulira amuna ena. Ndipo pamene inu mupita kukamvera ku malingaliro ena aliwonse, opyola Iwo, inu mukumvetsera, inu mukumuvulira Satana. Ameni! Kodi izo sizikukupangani inu kumverera mwachipembedzo? Mulungu akufuna inu mukhale osakhudzidwa. Mukhale pomwepo nawo Mawu amenewo. Mukhale pomwepo nawo Iwo. Chabwino.

Koma ine ndi nyumba yanga, Ife tidzakhala okanikiza kusewera ndi kutsatira Mawu Obadwa M’thupi a Mulungu akulankhula kudzera mwa mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri. Ife sitidzawonjezera kutanthauzira kwathu kwamseri kwa Iwo; sitidzavulira kapena kumvera malingaliro aliwonse. Ife TIDZAKHALA NDI MAWU AMENEWO MONGA MOMWE ANALANKHULIDWILA PA MATEPI. Iwo Ndi Mulungu mu Kuphweka.

Ndi nthawi yaulemerero bwanji yomwe ife titi tidzakhale nayo Lamlungu lino pa 12:00 p.m., nthawi yaku Jeffersonville, pomwe ife tikumva: Chisindikizo Chachitatu 63-0320. Ndikufuna kukuitanani Inu kuti mubwere kuzalumikizana ndi ife pamene ife tikulumikizana mozungulira pa Mawu a tsiku la lero.

M’bale. Joseph Branham

Malemba oti Muwerenge musanayambe kumvera Uthenga:
Mateyu woyera 25:3-4
Yohane woyera 1:1, 1:14, 14:12, 17:17
Machitidwe Mutu Wachiwiri
Timoteyo woyamba 3:16
Ahebri 4:12, 13:8
Yohane woyamba 5:7
Levitiko 8:12
Yeremiya mutu wa 32
Yoweli 2:28
Zekariya 4:12

Ndiloleni nditengere mwayi uwu kuti ndifotokozenso ichi momveka bwino mobwereza. Ine sindikutsutsana ndi utumiki wofutukuka usanu. Ine ndimakhulupirira mu utumiki wofutukuka usanu. Sindikuona kuti n’kulakwa kumvera mtumiki. Ndikukhulupirira kuti muyenera kumvera abusa anu kumene Mulungu wakuyikani. Mfundo yanga ndi iyi yakuti, ndikukhulupirira kuti Mulungu anatumiza mneneri m’tsiku lathu. Mulungu anaulula Mawu Ake kwa mneneri Wake. Ine ndikhoza kulakwitsa, abusa anu akhoza kulakwitsa, koma ife TIYENERA kuvomereza (ngati ife timanena kuti ife tikukhulupirira UTHENGA UWU kuti ndi Choonadi ndipo M’bale Branham ndi mneneri wa Mulungu) zimene zikunenedwa pa matepi ndi PAKUTI ATERO AMBUYE. Ngati inu simukukhulupirira izo, ndiye inu simukukhulupirira Uthenga uwu. Chifukwa chake, ndikukhulupirira kuti ndi MAWU OFUNIKA KWAMBIRI AMENE MUYENERA KUMVA. Inu simukusowa kuti muzindimva ine, inu simusowa kuti mumve wina aliyense, koma INU MUYENERA KUMVA MAWU AMENE ALI PA TEPI.

25-0323 Chisindikizo Chachiwiri

Uthenga: 63-0319 Chisindikizo Chachiwiri

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Omvetsera tepi,

Funso: Kodi tili mu Chifuniro Chake changwiro posewera Matepi?
Yankho: INDE.

Funso: Kodi Mkwatibwi akusowa zambiri kuposa zomwe zanenedwa pa Matepi?
Yankho: AYI.

Funso: Kodi tikuphonya kena kake pomvetsera Matepi OKHA?
Yankho: AYI.

Funso: Kodi tingakhale Mkwatibwi pongomvetsera Matepi OKHA?
Yankho: MOTSINDIKA KWAMBIRI, INDE!

Tsopano kumbukirani, “Palibe choti chiwululidwe; Mulungu sadzachita kanthu, nkonse, mpaka poyamba Iye atawulula icho kwa antchito Ake, aneneri.”

Kotero, ZONSE zomwe Ife tikufuna zinalankhulidwa ndipo ziri pa matepi; kapena, pamene mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri adzabwerera kudziko lapansi, IYE adzatiuza ife pamenepo.

O Mkwatibwi, tiyeni tiwone mwamasomphenya zomwe zikuchitika ndi Mkwatibwi wa Khristu padziko lonse lapansi. Atate akusonkhanitsa Mkwatibwi Wake palimodzi ndi Liwu Lake ndipo likubangula, “Pakuti Atero Ambuye.”

Kumbukirani, iye anatiuza chimene Mabingu anali: “Phokoso lowomba lalikulu la Bingu ndi Liwu la Mulungu”. Ndipo kodi Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi ndi chiyani? Mthenga wa mngelo wachisanu ndi chiwiri wa Mulungu, William Marrion Branham.

Iye anati pakubwera Mabingu asanu ndi awiri achinsinsi amene sanalembedwe nkomwe. Ndipo kuti kupyolera mu Mabingu Asanu ndi awiri awo, izo zidzabweretsa Mkwatibwi palimodzi kwa chikhulupiriro chokwatulitsa.

Mawu a Ambuye amadza kwa aneneri Ake. Ngati Iye akanakhala ndi kachitidwe kabwinoko, Iye akadagwiritsa ntchito iko. Iye anasankha dongosolo labwino kwambiri pachiyambi ndipo Iye sangasinthe, ndipo sadzasintha.

Chotero, Liwu la Mulungu, likuyankhula kupyolera mwa mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri, likubweretsa Mkwatibwi Wake palimodzi ndi kutipatsa ife Chikhulupiriro Chokwatulitsa.

Mpingo sunadabwepo kuchokera 1933, kumusi ku mtsinje tsiku lija, kuti William Marrion Branham ndi Liwu la Mulungu, Likubangula, “Pakuti Atero Ambuye,” ndipo anatumizidwa kuyitana, kusonkhanitsa, ndi kutsogolera Mkwatibwi.

Ine ndikufuna kuti ndikuyitaneni inu kuti mubwere kudzamvetsera nafe Lamlungu pa 12:00 p.m., nthawi yaku Jeffersonville, pamene Ambuye wathu Yesu akutsegula Bukhu, akumatula Chisindikizo, ndi kuchitumiza Icho ku dziko lapansi, kwa mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri, kuti adzawululire Icho kwa Ife!

M’bale. Joseph Branham

Tsiku: Lamlungu, pa 23 Marichi , 2025
Uthenga: Chisindikizo Chachiwiri 63-0319
Nthawi: 12:00 PM, nthawi yaku Jeffersonville

Malemba oti muwerenge musayambe kumvera Uthenga:
Mateyu woyera 4:8 / 11:25-26 / 24:6
Marko woyera 16:16
Yohane woyera 14:12
2 Atesalonika 2:3
Ahebri 4:12
Chibvumbulutso 2:6/6:3-4/17/19:11-16
Yoweli 2:25
Amosi 3:6-7

25-0316 Chisindikizo Choyamba

Uthenga: 63-0318 Chisindikizo Choyamba

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Wanga Mfumukazi ya Kumwamba,

Ine Ndili nazo zochuruka za inu munkhokwe Lamlungu lino. Choyamba, mudzamva kugunda kwa Bingu.  Ilo lidzakhala Liwu Langa, Liwu la Mulungu kuyankhula kwa inu, Mkwatibwi Wanga. Ndidzakhala ndikuwululira Mawu Anga kwa inu kuposa kale. Inu mudzandiwona Ine, Mwanawankhosa wamagazi amene anaphedwa kuchokera ku maziko a dziko, akutenga ndi kutsegula Bukhu, kumatula Zisindikizo, ndi kulitumiza Ilo kumusi uko ku dziko lapansi, kwa m’thenga Wanga wa mngelo wachisanu ndi chiwiri, William Marrion Branham, kuti adzawululire kwa INU zinsinsi zimene zakhala ziri zobisika kuchokera ku maziko a dziko!

Kudzakhala kukuwa, kufuula, ndi ma aleluya ochokera kuzungulira dziko lonse pamene ine ndikuyankhula kwa inu. Mkango udzakhala ukubangula; odzozedwa, mphamvu, ulemerero, mawonetseredwe adzakhala oposera mawu. Inu, Mfumukazi Yanga, mudzakhala pamodzi m’malo amwambamwamba pamene Ine ndikulankhula ndi inu ndi kukupatsani inu mphavu ya Chikhulupiriro yokwatulitsa. Ife

Kumbukirani, inu muyenera kukhala nacho Chikhulupiriro chija chimene chinaperekedwa kamodzi kwa oyera. Ndinakuuzani kuti, Muzimvera mngelo wanga amene ndinamutuma kwa inu.

Iye ali woti “abwezeretse Chikhulupiriro cha ana kubwerera kwa atate.” Chikhulupiriro choyambirira cha Baibulo ndi chakuti chibwezeretsedwe ndi mngelo wachisanu ndi chiwiri.

Mawu Anga amakuuzani inu, mu masiku a Liwu la mngelo wachisanu ndi chiwiri, kuwomba kwake, kuwomba lipenga la Uthenga; ayenera kutsiriza zinsinsi zonse za Mulungu. Sipangakhoze kukhala chinthu chimodzi chowonjezedwako ndipo palibe chochotsedwapo kwa chimene ine ndinanena pa matepi; muzingonena zomwe ndidalankhula kudzera mwa m’thenga Wanga wa m’ngelo. Ichi ndichifukwa chake ndinali nalo ilo lidajambulidwa, kuti mophweka muzingotha ​​KUSINDIKIZA KULISEWERA ndikumva ndendende zomwe ndinanena, ndi momwe Ine ndinazinenera. Idzakupatsani Inu mphavu ya Chikhulupiriro chokwatulitsa.

Mfumukazi yanga yokondedwa, m’maso mwanga inu muli wangwiro, mtheradi, wopanda uchimo pamaso panga. Osadandaula, Inu SIMUDZAPITA mu chisautso; pakuti mwalandira Magazi Anga, Mawu Anga, mngelo Wanga, Liwu Langa, kotero inu kwenikweni mulibe uchimo pamaso panga.

Ine Ndilinazo Izo zainu zazikulu munkhokwe. Inu mukuwona Mawu Anga akufutukuka pamaso panu tsiku lililonse. Ndakhala ndikuyika zizindikiro kumwamba kuti ndikuuzeni kuti chinachake chikukonzekera kuchitika. Ine Ndikubwera, khalani okonzekera. Ikani Mawu Anga, Liwu Langa, choyamba m’moyo wanu.

Ikani chirichonse pambali, palibe chinthu chofunika kwambiri kuposa Mawu Anga. Ndikudziwa kuti m’dani akufuna kukugwetsani, koma ndinakulonjezani kuti ndidzakukwezani. Ine ndiri ndi inu, ngakhale MWA INU. Inu ndi Ine tikukhala Amodzi pamene Ine ndikuwululira Mawu Anga kwa inu.
Inu mukudziwa mu mtima mwanu, NDINU Mfumukazi Mkwatibwi wanga. Inu mukudziwa ine ndinakukonzeranitu inu. MUkudziwa kuti ndimakukondani. Mukudziwa kuti ndimakhala nanu mphindi iliyonse ya tsiku lililonse. Inu mukudziwa kuti Ine SINDIDZAKUSIYANI INU.

Tizikhala ndi nthawi yodabwitsa yotere pamene ndikukuwululirani zambiri Lamlungu lililonse, tsiku lililonse, pamene mukundimva Ine ndikulankhula kudzera mwa mngelo Wanga kwa inu. Ena mwina sangamvetse kapena kuwona zomwe inu mukuwona, koma Izo zazikika mu mtima mwanu kuti iyi ndi Njira Yanga yoperekedwa.

Ndi pothawirapo bwanji ndakupatsani inu. Inu mophweka Mutha Kungosindikiza kuSewera nthawi ina iliyonse, masana kapena usiku, ndikundimva ine Ndikulankhula nanu. Ndidzabweretsa chitonthozo ku moyo wanu pamene ndikuwululira Mawu Anga ndikukuuzani inu yemwe inu muli. Uthenga uliwonse ndi wa Inu, ndipo wa inu nokha. Tikhoza kuyanjana ndi kupembedza limodzi nthawi iliyonse yomwe inu mukufuna.

Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, gawo la Mkwatibwi lidzasonkhanitsidwa kuchokera kuzungulira dziko kuti adzamve zinsinsi zazikulu izi zikuwululidwa. Ine Ndikukuitanani inu kuti mubwere kulumikizana nafe pomwe tikumvera, 63-0318 – “Chisindikizo Choyamba”.

M’bale. Joseph

Malemba oti muwerenge pokonzekera kumva Uthenga:
Mateyu 10:1 / 11:1-14 / 24:6 / 28:19
Yohane 12:23-28
Machitidwe 2:38
2 Atesalonika 2:3-12
Ahebri 4:12
Chivumbulutso 6:1-2 / 10:1-7 / 12:7-9 / 13:16 / 19:11-16
Malaki chaputala chachitatu ndi chaputala cha folo
Daniele 8:23-25/11:21/9:25-27

25-0309 Cholekanitsa Pakati Pa Mibadwo Isanu Ndi Iwiri Ya Mpingo Ndi Zisindikizo Zisanu Ndi Ziwiri

Uthenga: 63-0317E Cholekanitsa Pakati Pa Mibadwo Isanu Ndi Iwiri Ya Mpingo Ndi Zisindikizo Zisanu Ndi Ziwiri

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Obwezeretsedwa,

Ine Sinditopa kumva Liwu la Mulungu likutiuza kuti ndife ndani, komwe timachokera, komwe tikupita, zomwe tili.
wolandira cholowa, ndi momwe amatikondera ife.

unsembe wauzimu, fuko lachifumu, kupereka nsembe zauzimu kwa Mulungu, zipatso za milomo yawo, kupereka mayamiko kwa Dzina Lake.” Ndi a—ndi anthu otani! Iye ali nawo iwo.

Chitonthozo chathu chokha ndi mtendere zimadza pakumva Liwu la Mulungu likulankhula kwa ife, ndiye kulankhula mobwezera kwa Atate mwa kupereka nsembe zauzimu mwa zipatso za milomo yathu, kupereka matamando ku Dzina Lake.

Dziko lonseli likubuula. Chirengedwe chikubuula. Ife tikubuula ndi kuyembekezera kudza kwa Ambuye. Dzikoli lilibe kanthu kwa ife. Ife tiri okonzeka kuti tichoke ndi kupita ku Mgonero wathu wa Chikwati ndi Kwathu Kwamtsogolo limodzi ndi Iye ndi onse amene ali Kumeneko, basi kupyola katani ya nthawi, akutiyembekezera ife.

Tiyeni tidzuke tidzigwedeze tokha! Tsinani chikumbumtima chathu, tidzidzutse tokha ku zomwe zikuchitika pakali pano ndi zomwe zidzachitike mu mphindi ya kuphethira kwa diso.

Palibe mu mbiriyakale ya dziko zomwe zakhala zotheka kuti Mkwatibwi wa Khristu akhale wolumikizana kuchokera kuzungulira dziko, onse pa nthawi yofanana yomweyo, kuti amve Liwu la Mulungu likuyankhula ndi kuwulula Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake.

Okhulupirira, dzifunseni nokha, ndi liwu liti, mtumiki wuti, munthu uti, angalumikizitse ndi kubweretsa Mkwatibwi wa Khristu pamodzi? Ngati inu muli Mkwatibwi wa Khristu, inu mukudziwa kuti palibenso Liwu lina koma Liwu la Mulungu pa matepi.

Inde, Mzimu Woyera uli mwa aliyense wa ife, mu udindo uliwonse wa mpingo, koma Mulungu Mwiniwake anatiuza ife kuti Iye adzaweruza dziko ndi Mawu Ake. Mkwatibwi amadziwa kuti Mawu Ake amabwera kwa mneneri Wake. Mneneri wake ndi YEKHAYO wotanthauzira Wauzimu wa Mawu Ake. Zimene Iye analankhula sizingawonjezedwepo kapena kuchotsedwapo. Ndi Mawu,a pa matepi, amene ife tonse tidzaweruzidwa nawo, ndipo palibe mawu ena kapena kutanthauzira kwa Mawu amenewo.

Sizingatheke kuti liwu lina lirilonse ligwirizanitse Mkwatibwi. Ndi Liwu la Mulungu lokha pa matepi lingakhoze kugwirizanitsa Mkwatibwi Wake. Ndi Mawu okhawo omwe Mkwatibwi angagwirizane nawo. Ndi Liwu lokhalo limene Mulungu Mwiniwake anatsimikizira kukhala Liwu Lake kwa Mkwatibwi Wake. Mkwatibwi Wake ayenera kukhala mu Malingaliro Amodzi ndi Chigwirizano Chimodzi kuti akhale ndi Iye.

Ma tumiki akhoza kutumikira, aphunzitsi akhoza kuphunzitsa, azibusa akhoza kuchitira ubusa, koma Liwu la Mulungu pa matepi liyenera kukhala Liwu lofunika kwambiri lomwe iwo ayenera kuliyika pamaso pa anthu. Iwo ndiwo Mtheradi wa Mkwatibwi.

Ngati muli ndi Vumbulutso la izo, ndiye ichi ndi chimene chiti chichitike.

Mawu amatiuza ife kuti Adamu anataya cholowa chake, dziko lapansi. Tsopano, ilo linachoka mdzanja lake kupita kwa iye amene anamugulitsa, Satana. Iye anagulitsa chikhulupiriro chake mwa Mulungu, kwa malingaliro a Satana. ndipo iye analanditsa chidutswa chirichonse kwa manja a Satana. Iye anachipereka icho kuchokera mdzanja lake kupita kwa Satana.

Mulungu ndi Mulungu wa chilengedwe chonse, kulikonse, koma Mwana Wake, Adamu, anali ndi dziko lapansi ili pansi pa ulamuliro wake. Iye amakhoza kuyankhula, iye amakhoza kutcha dzina, iye amakhoza kunena, iye amakhoza kuimitsa chirengedwe, iye ankakhoza kuchita chirichonse chimene iye ankafuna kutero. Iye anali ndi ulamuliro wathunthu, wapamwamba kwambiri padziko lapansi.

Adamu anataya zonse, koma ulemerero kwa Mulungu, zonse zomwe iye anataya ndi kulandidwa zidawomboledwa ndi Muomboli wathu Wachibale, palibe wina koma Mulungu Wamphamvuzonse, amene anakhala Emanuele, mmodzi wa ife. TSOPANO, NDI ZATHU.

Ndife ana Ake aamuna ndi aakazi amene ati adzalamulire ndi kukhala mafumu ndi ansembe limodzi ndi Iye. Tili ndi moyo wosatha ndi Iye ndi onse amene timawakonda. Sipadzakhalanso matenda, sipadzakhalanso chisoni, sipadzakhalanso imfa, umuyaya basi zonse palimodzi.

Tikaganizira zimenezi, tingalole bwanji kuti mdierekezi atigwetse pansi? Ndi ATHU, ndikomwe tikupita posachedwa. Iye watipatsa ife chinthu chachikulu kwambiri chimene angatipatse ife. Masiku ochepa awa a mayeso ndi mayesero padziko lapansi amizidwa mwachangu ndi KUGONJETSA KWATHU KWAKUKULU MASIKU CHABE OMWE ALI PA TSOGOLO PATHU.

CHIKHULUPIRIRO chathu sichinakhale chokulirapo. Chisangalalo chathu sichinakhalepo chachikulu. Timadziwa kuti ndife ndani komanso komwe tikupita. Tikudziwa kuti tili mu chifuniro Chake changwiro pa kukhala ndi Mawu Ake. Chomwe ife tikusowa kuti tichite ndi kukhala nawo matepi ndi kukhulupirira Mawu aliwonse; osati kuvetsa zonse, KOMA KUKHULUPILIRA MAWU ONSE…ndipo TIMAWACHITA!

Chikhulupiriro chimadza pakumva, kumva Mawu. Mawu amadza kwa mneneri. Mulungu analankhula Izo. Mulungu anazijambula Izo. Mulungu anaulula Izo. Ife tikuzimva Izo. Ife timakhulupirira IZO.

Inu mukhoza kupeza Vumbulutso ili kokha pa kumva Liwu la Mulungu pa matepi.

Zonse izo zimene Khristu ati adzachite pa matsiriziro zidzaululidwa kwa ife sabata ino, mu Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri, ngati Mulungu angatilole ife. Mwaona? Chabwino. Izo zidzaululidwa. Ndi kuululidwa, pamene Zisindikizo zikutsegulidwa ndi kuperekedwa kwa ife, ndiye ife tikhoza kuona chimene dongosolo lopambana la chiombolo ili liri, ndipo liti ndi momwe chiti chidzachitike. Zonsezo ndi zobisika mu Bukhu ili la chinsinsi pano. Ndi losindikizidwa, liri ndi Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri, ndipo kotero Mwanawankhosa ndi yekhayo Mmodzi Amene angamatule izo.

Lamlungu lino pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, gawo la Mkwatibwi kuchokera kuzungulira dziko lapansi adzakhala akumvetsera ku Liwu la Mulungu onse pa nthawi imodzi. Tidzakhala tikugunda mwamphavu kumwamba ndi mapemphero athu ndi kumulambira IYE. Ndikukuitanani Inu kuti mubwere kulumikizana nafe pamene tikumva: Cholekanitsa Pakati Pa Mibadwo Isanu Ndi lwiri Ya Mpingo Ndi Zisindikizo Zisanu Ndi Ziwiri 63-0317E.

Chonde musaiwale za kusintha kwa nthawi yaku Jeffersonville kumapeto a sabata ino.

M’bale. Joseph Branham

25-0302 Mulungu Kudzibisa Yekha Mu Kuphweka, Ndiye Nkudziwulula Yekha Momwemo

Uthenga: 63-0317M Mulungu Kudzibisa Yekha Mu Kuphweka, Ndiye Nkudziwulula Yekha Momwemo

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Akakombo Apadziwe

Pa February 28, 1963, Kunagunda. Whii-Whii, Angelo Asanu ndi awiri anabwera kuchokera ku Umuyaya ndipo anawonekera kwa Mngelo Wachisanu ndi chiwiri wa Mngelo Mthenga wa Mulungu. Iye anakwatulidwira mmwamba mu piramidi ya kuwundana. Kenako, mtambo wauzimu unawonekera mu mlengalenga ku Arizona. Icho chinali chizindikiro, Mulungu anali kutumiza mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri kubwerera ku Jeffersonville kuti adzatsegule Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri.

February 28, 2025, mapulaneti asanu ndi awiri amayenda mlengalenga. Mkwatibwi akudzikonzekeretsa Yekha kuti kudzasonkhana ndi kumva Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri.

Inu mukuitanidwa, ndi Ambuye Mwiniwake, kuti mudzasonkhane ndi Mkwatibwi kuchokera kuzungulira dziko, kuti mudzamve Liwu la Mulungu likuwulura Chivumbulutso cha Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri.

Tsiku limene aneneri ndi anzeru ankalilakalaka ndi kuliyembekezera kuyambira pa chiyambi cha nthawi, likuchitika. Mngelo wamphamvu amene Mulungu ananena kuti adzatumiza padziko lapansi m’masiku otsiriza wabwera kudzatsegula ndi kuwulula zinsinsi zobisika za Mulungu, kuti Ambuye wathu Yesu abwere chifukwa cha Mkwatibwi wake wokhulupirika ndi kutitengera Ife ku Mgonero wathu wa Ukwati.

Ntchito yanga yoyamba, mmene ine ndimalowa mkachisi watsopano, ine ndimakwatitsa mnyamata ndi msungwana atayima mu ofesi. Icho chikhale choyimira, kuti ine ndidzakhala mtumiki wokhulupirika kwa Khristu, kuti ndipeze Mkwatibwi wokonzekera mwambo wa Tsiku limenelo.

Lero , Mawu awa akukwaniritsidwa. Mulungu akuyankhula kupyolera mwa mngelo Wake, kukonzekeretsa Mkwatibwi Wake ku mwambo wa Tsiku limenelo. Tikutsatira malangizo kudzera mu kalata. Mkwatibwi wadzikonzekeretsa Yekha pa KUKHALA NDI MAWU A MULUNGU PA MATEPI.

Kodi tangomva zotani m’maloto ndi masomphenya? Chakudya, NDI ICHI APA, awa ndi malo. Liwu linati kwa iye, “Liwu linanena kwa ine, “Liwu linanena kwa ine, “Bweretsa mkati Chakudya. Uchisunge Icho mkati. Iyo ndi njira yokha yowasungira iwo pano, ndi kuwapatsa iwo Chakudya.”

Ambiri amakhulupirira kuti iye akungotanthauza, “ingokhalani ndi Mawu,” ndipo izo nzowonadi, iye akunena kuti; koma Mkwatibwi adzawerenganso pakati pa mizere pamene Mkwati akuyankhula kwa Mkwatibwi Wake.

Ngakhale masomphenya amene Mulungu amapereka pa malo ano, iwo ali osamvetsedwa kwambiri. Ndicho chifukwa inu mukundimva ine pa matepi, kuti, “Nenani zimene matepi akunena. Nenani zimene masomphenya akunena.” Tsopano, ngati inu muli maso kwambiri, inu muona chinthu china. Mwaona? Ine ndikuyembekeza kuti ine sindikusowa kuchigwira icho mdzanja langa ndi kukuonetsani inu.

Ngakhale masomphenyawo sanamvetsetsedwe, ngakhale kuti anali atatha kale kupereka matanthauzo kwa iwo. Ndi zomwe amatiuza, ngati simukufuna kusokonezedwa, kapena kusamvetsetsa, Dinani Sewerani kuti mumve ndendende zomwe Liwu la Mulungu likunena.

Ine ndikudziwa kuti Mawu ali ndi matanthauzo apawiri, koma uku ndi kumasulira kwanga: Maloto ndi masomphenya onse ananena chinthu chomwecho; khalani nawo matepi. Ngati inu muli ndi funso, pitani ku matepi. Matepiwo ndi Chakudya chosungidwa-cha Mulungu. Ingonenani zomwe zili pa matepi; musati muwonjezere kalikonse kwa Iwo. Matepi ali PAKUTI ATERO AMBUYE kwa Mkwatibwi. Mawu amadza kwa mneneri, yekha. Mneneri ndi YEKHA wotanthauzira Wauzimu wa Mawu. Mneneri anali woti ayitane ndi kutsogolera Mkwatibwi. Ine ndidzaweruzidwa ndi zomwe zinanenedwa pa MATEPI.

Chilichonse chimandilozera ine ku MATEPI.

Okondedwa anga Akakombo apadziwe, kwa ine, KUSINDIKIZA KUSEWERA NDI MULUNGU MU KUPEKWA KWA LERO.

Mlungu uliwonse ndimakhala osangalala kwambiri; ndi chiyani chiti chidzaululidwe lero pamene Mkwatibwi Wake adzasonkhana kuti amve Uthenga? Ine Ndikudziwa kuti Mzimu Woyera adzakhala akudzoza aliyense wa ife pamene akuwululira Mawu Ake kuposa kale. Ine ndikumverera, pa mphindi iliyonse, Iye adzabwera ndi kudzatitengera ife ku Mgonero wathu wa Chikwati.

Ife tiri, ana aamuna ndi aakazi a Mulungu. Ife Tili, mphukira zochokera kwa Mulungu. Ife ndicholowa cha dziko lapansi. Ife tikhoza kulamulira chilengedwe. Ife tikhoza kulankhula nkukhalapo. Ndife Mkwatibwi!

Tiyeni tidzipereke tokha mwatsopano ku ntchito, ndi kudzipatulira tokha kwa Khristu.

M’bale. Joseph Branham

Tsiku: Lamlungu, Marichi 2, 2025
Uthenga: Mulungu Kudzibisa Yekha Mu Kuphweka, Ndiye Nkudziwulula Yekha Momwemo
63-0317M
Nthawi: 12:00 PM, nthawi yaku Jeffersonville.

25-0223 Kodi Ichi Ndi Chizindikiro Cha Mapeto, Bwana?

Uthenga: 62-1230E Kodi Ichi Ndi Chizindikiro Cha Mapeto, Bwana?

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Mabwana,

Ichi ndi Chizindikiro. Iyi ndi nthawi. Uwu ndi, Uthenga. Awa ndi Mawu. Ili ndilo, Liwu la Mulungu. Uyu ndi Mwana wa Munthu. Iyi ndiyo, njira yoperekedwa ndi Mulungu. Awa ndiwo mapeto a nthawi.

Palibe m’neneri, palibe mtumwi, palibe, mu nthawi iliyonse, anayamba wakhalapo mu nthawi yotero yomwe ife tikukhalamo tsopano. Zalembedwa m’miyamba. Zalembedwa pa nkhope ya dziko lapansi. Zalembedwa m’nyuzipepala iliyonse. Awa ndiwo mapeto, ngati mungathe kuwerenga zolembedwa.

Iye amene ali nalo khutu, muloleni iye amve zomwe Mulungu anayankhula, ndi kuchita rekodi, kotero iwo sakanakhala mawu anga, maganizo anga, lingaliro langa, koma Liwu lomwe la Mulungu likulangiza Mkwatibwi Wake chimene chiri njira Yake YOKHA yangwiro yoperekedwa kwa lero.

Bwerani ndi kumvetsera pamene Iye akutiuza ndi kuwulula kwa ife mwa malembo, mwa masomphenya, mwa kutanthauzira kwa maloto, kuti tikhale ndi Uthenga, kuti tikhale ndi matepi. Muzinena ZOKHAZO zomwe zili pa matepi.

Palibe njira yabwino, kapena njira yotsimikizika, yoposa kumva Liwu la Mulungu kuchokera kwa Mulungu Mwiniwake. Mulungu analamulira Mkwatibwi Wake polankhula kupyolera mwa mneneri Wake ndi kutiuza ife, KUSINDIKIZA KUSEWERA, munyengo.

Lankhulani Ilo, lilalikireni ilo, chitirani umboni za ilo, ndi kuliwuza dziko lapansi za ilo, koma Iye amatiuza ife kuti pali njira imodzi yokha yangwiro yoperekedwa kuti afikitse Mkwatibwi ungwiro: kumvetsera kwa Liwu la Mulungu pa matepi. Ngati chinachake chikukudodometsani inu, sewerani tepiyo. Iyenera kukhala YOYAMBA, ndipo ndilo Liwu lofunika kwambiri lomwe muyenera kulimva. Ndi Mawu Ake angwiro amene anawayika pa tepi.

Tsopano fanizirani ngakhale ilo ndi enawo, maloto. Awa anali masomphenya. Chakudya, ndi Ichi apa. Awa ndiwo malowo.

Mvetserani, mwa maloto ndi masomphenya, Chakudya cha Mkwatibwi chiri kuti? Malowo ali kuti? Uthenga wa Mkwatibwi uli pa matepi.

Ndipo pano ndimamverera ngati kwathu, kwa ine. Malo ake ndi ano. Ndipo ngati inu mungazindikire, maloto anayankhula chinthu chomwecho, onani, kumene Chakudya.

Kuti atsimikizire kuti ife tiri nacho Icho, iye akutiuza ife kamodzinso, matepiwo ali Chakudya cha Mkwatibwi.

“Palibenso nthawi.” Ngati iyo ili, tiyeni tidzikonzekere tokha, abwenzi, kukakomana naye Mulungu wathu.

Inde, Ambuye, ndicho chokhumba cha mtima wathu, kukonzekera kukumana nanu, kuti ife tikhale Mkwatibwi Wanu. Tichite chiyani Ife Ambuye? Njira Yanu yoperekedwa ndi yotani? Dongolo lanu ndilotani? Njira Yanu yangwiro ndi iti? Inu munatitumizira ife mneneri yemwe Inu mudakhoza kuyankhula naye kuti atiuze ife. Chonde tilangizeni.

Pakhala pali Chakudya chochuluka chimene chayikidwa muno tsopano. Tiyeni tichigwiritse ntchito Icho. Tiyeni tichigwiritse ntchito Icho tsopano.

Kodi munthu angakhale wakhungu bwanji? Iye Amatiuza choti tichite: pa matepi pali chakudya chambiri chosungidwa; chigwiritseni ntchito TSOPANO. Ili ndi langizo la Mulungu kwa Mkwatibwi Wake.

Ngati inu mukuti inu mumakhulupirira Uthenga uwu, khulupirirani William Marrion Branham ndi mneneri wamthenga wa Mulungu wotumidwa kudzayitana Mkwatibwi; moyo wake umakwaniritsa malembo Onse omwe ananena za iye; khulupirirani ilo kuti ndi Liwu la Mulungu la tsiku lino, Kotero IYE; Mulungu, akuyankhula kupyolera mwa mneneri Wake, amamuuza Mkwatibwi mu Chichewa chomveka bwino choti achite.

Ngakhale kuti ife timasekedwa, kuzunzidwa, ndi kunyozedwa chifukwa choti ife timangomvetsera ku matepi, ife tikuchita ndendende zomwe Iye anatiuza ife kuti tichite. Zikomo Ambuye chifukwa cha Vumbulutso.

Ndikufuna kuitana dziko kuti mulumikizane nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, monga tikumva: 62-1230e, “Kodi Ichi Ndi Chizindikiro Cha Mapeto, Bwana?” Tidzakhala tikumva zonse za izo :

Mabingu, Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri, Thanthwe la Piramidi, Chakudya Chauzimu, Muyaya, Kuwundana kwa Angelo, Likulu Langa, Masomphenya, Maloto, Uneneri, Zinsinsi Zobisika, Lemba pambuyo pa Lemba.

Palibe chinthu china chachikulu m’moyo uno kuposa kumva ndi kumvera Liwu la Mulungu.

M’bale. Joseph Branham

Malemba:
Malaki Chaputala 4
— Mateyu 13:3-50
Aroma 9:33; 11:25; 16:25
1 Akorinto 14:8/15 Mutu
Agalatiya 2:20
Aefeso 3:1-11 / 6:19/ 5:28-32
Akolose 4:3
1 Atesalonika 4:14-17
1 Timoteo 3:16
Ahebri 13:8
2 Petulo 2:6
Chivumbulutso 1:20 / 3:14 / 5:1 / 6:1 / 10:1-7 / 17th Chapter

25-0216 Sabata La Makumi Asanu Ndi Chiwiri La Daniele

Uthenga: 61-0806 Sabata La Makumi Asanu Ndi Chiwiri La Daniele

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Akuyang’anira Ndinso Akuyembekenzera,

Pali chisangalalo pakati pa Mkwatibwi kuposa kale. Tili pa kuyembekezera kwakukulu; Chaka chathu chachisangalalo chikukonzekera kuti chichitike. Mkwatibwi wayembekezera motalika kwambiri kuti tsiku ili lifike. Mapeto a nyengo ya m’badwo wa Amitundu yafika ndipo chiyambi cha muyaya ndi Ambuye wathu chiyamba posachedwapa.

Ife tikumvetsa nthawi yomwe tikukhalamo pa kumva Mawu. Nthawi yatha. Nthawi ya Mkwatulo yayandikira. Tafika. Mzimu Woyera wabwera ndi kuwulula kwa Mkwatibwi Wake zinthu zonse zazikulu, zakuya, zinthu za zinsisi.

Ife tiri mu kusimidwa, kufunafuna Mulungu; kudzikonzekeretsa tokha. Tataya zinthu zonse za dziko lino. Zosamalira za moyo uno sizitanthauza kanthu kwa ife. Chikhulupiriro chathu chafika patali kwambiri kuposa kale lonse. Mzimu Woyera ukumupatsa Dona Wake wosankhidwa Chikhulupiriro chokwatulitsa, kotero Iye akhoze kubwera ndi kumuchotsa Iye.

191 Masabata sikisite naini awa analondolera mwangwiro; kupita kwina kwa Ayuda kumalondolera mwangwiro; m’badwo wa mpingo umalondolera mwangwiro. Ife tiri pa mapeto a nthawi, nthawi yotsiriza, m’badwo wa mpingo wa Laodikaya, kutha kwa iwo. Atumiki nyenyezi onse alalikira uthenga wawo. Iwo wapita kunja. Ife tikungogubuduka.

Ndi nthawi yodabwitsa bwanji yomwe Ife tikukhalamo. Ndi nthawi yovuta kwambiri pamene m’dani akulimbana ndi aliyense kuposa kale. Iye akuponya zonse zimene ali nazo kwa ife. Iye ali mu kusimidwa, chifukwa akudziwa kuti nthawi yake yafika kumapeto.

Koma panthawi yomweyomweyo, Ife sitinakhalepo osangalala kwambiri mmiyoyo yathu.

• Sitinakhalepo pafupi ndi Ambuye.
• Mzimu Woyera amadzaza mum’tsempha uliwonse wa thupi lathu.
• Chikondi chathu pa Mau ake sichinakhale chokulirapo.
• Vumbulutso lathu la Mau ake limadzaza moyo wathu.
• Tikugonjetsa mdani aliyense ndi Mau.

NDIPO, sitinakhalepo otsimikiza kwambiri kuti ndife ndani:

• OKONZEDWERATU
• OSANKHIDWA
• OSANKHIDWA
• Mbewu Yachifumu
• OKOMA APA MTIMA
• AMUYAYA, IWO OVALA MWINJIRO WOYERA, MAYI JÉZU, OMVETSERA KU MATEPI, OWUNIKILIKIDWA, NAMWALI WOLANGIDWA, WODZAZIDWA NDI MZIMU, WOSAGONJETSEDWA, WOKHAZIKITSIDWA KWAUZIMU, WOSAIPITSIDWA, MKWATIBWI WA MAWU NAMWALI.

Mchiyani Chikubwera chotsatira ? Mwala ukubwera. Tikuyang’ana, kuyembekenzera ndi kupemphera mphindi iliyonse tsiku lililonse. Palibenso china chilichonse chovuta koma kudzikonzekeretsa tokha pa kubwera kwake.

Sikuti, “Tikuyembekeza choncho”, TIKUDZIWA. Kulibenso zokaikitsa zochuruka zina zilizonse. Mu M’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso kudzakhala kuti kwatha, ndipo tidzakhala kuti tili kumbali inayo ndi okondedwa athu onse ndi IYE pa Mgonero wathu wa Ukwati.

NDIPO ICHO NDI CHIYAMBI CHABE …NDIPO KULIBE MAPETO!!

Bwerani mudzakonzekere Mgonero wa Chikwati uwu nafe Lamlungu lino pa 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene Mulungu akuyankhula kupyolera mwa mngelo Wake wamphamvu, yemwe Iye anamutuma kuti adzatsogolere Mkwatibwi Wake, monga iye akuuzira, ndi kuwulula, zinsinsi zonse za Mulungu.

M’bale. Joseph Branham

Uthenga: 61-0806 – Sabata La Makumi Asanu Ndi Awiri La Daniele

25-0209 Cholinga Chofutukuka Pasanu Ndi Kamodzi Cha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele

Uthenga: 61-0730E Cholinga Chofutukuka Pasanu Ndi Kamodzi Cha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wa kukondwera,

Tayang’ana nkhope zathu Kumwamba m’mapemphero ndi mapembedzero kuti tipeze tsiku ndi ola lomwe tikukhalamo.

Monga sizinachitikepo kale lonse, ife tikukhala pamodzi mu malo amwambamwamba, kuchokera kuzungulira dziko, kumva Mulungu akulankhula ndi kuwulula Mawu Ake kwa ife kupyolera mwa mngelo Wake wamphamvu wamthenga. Mngelo wapadziko lapansi wamthenga yemwe Atate anamutumiza kwa Mkwatibwi Wake mu tsiku lotsiriza ili kuti awulule Mawu Ake.

Gabrieli ndi mngelo wa anthu osankhidwa a Mulungu, Ayuda. Koma kwa Mkwatibwi Wake wa Amitundu, Melkizedeki Iyemwini anabwera ndipo anayankhula kupyolera mu thupi la munthu mwa mngelo wapadziko lapansi wotchedwa William Marrion Branham, kotero kuti Iye akhoze kulankhula ndi kuwulula Mawu Ake ONSE kwa Mkwatibwi Wake wokondedwa wapamtima.

Iye anali nalo ilo likujambulidwa, kusungidwa, ndi kusamaliridwa, kotero kuti Mkwatibwi akakhale ndi Chakudya Chake chauzimu, Manna obisika, mmanja mwawo miniti iliyonse ya tsiku lirilonse mpaka mapeto a nthawi.

Mkati mwathu ndimodzazidwa ndi kudzoza komweko pomwe tikunva Liwu la Mulungu kuwulula Mawu Ake kwa ife. Momwe Iye amavumbulutsira Mawu Ake kuti tithe kuwona bwino bwino ndi kumvetsetsa tanthauzo lake. Ilo likuwulula ola lomwe tikukhalamo, Limatiuza ife amene tiri ndi chimene chiti chichitike posachedwapa; Mkwatulo wathu ukubwera posachedwa.

Iye akuwululira kwa Mkwatibwi Wake zomwe ziti zichitike pano pa dziko lapansi pamene ife tiri naye Iye pa Mgonero wa Chikwati. Momwe Iye adzatsegula maso akhungu a osankhika ake; iwo amene Iye anawachititsa khungu chifukwa cha Mkwatibwi Wake wa Amitundu.

Abwenzi anga, ndikudziwa mmene tatopela ndi dziko lino ndipo tikulakalaka za kudza kwake kudzatichotsa, koma tiyeni tisangalale ndi kuyamikira zimene zikuchitika pakali pano pamaso pathu.

Tiyeni tikweze manja athu mmwamba, mitima yathu, mawu athu, ndi kukondwera. Osati kokha kuti tikuyembekezera zimene Iye ati atichitire posachedwapa, koma tiyeni tikondwere ndi zimene Iye akutiululira ndi kutichitira ife TSOPANO.

Iye akutiuza ife kuti ndife Mkwatibwi Wake wokonzedweratu akulumikizana limodzi ndi Iye ndi Mawu Ake. Iye akutitsimikizira mobwereza bwereza, ife tiri mu Chifuniro Chake changwiro pokhala ndi Liwu Lake, Mawu Ake, mngelo Wake. Iye Watipatsa ife CHIKHULUPIRIRO chodziwa ndi kuzindikira cha chomwe Ife tiri:
MAWU AKE OKHALA MTHUPI.

Tilibe kanthu koti tizikawopa; tilibe kanthu koti tizidandaula nako; tilibe kanthu koti kazitikwiyitsa. Kodi ndikudziwa bwanji zimenezo? MULUNGU ANANENA CHOMWECHO! CHONCHO TIYENI TIKONDWERE, KHALANI OSANGALALA, KHALANI OYAMIKILA; MAWU AMOYO AMAKHAKHALA NDI KUKHALA PAKATI PATHU. NDIFE MBEWU YAKE YAPAMWAMBA YAUFUMU.

Ine Zoonadi Ndikukhulupirira kuti Ambuye akuyeneranso kukhala wokondwa kudziwa kuti nthawi yafika ndipo tadzikonzekeretsa tokha pokhala wowona ndi mokhulupirika ku Mawu Ake.

Monga mnyamata wamng’ono yemwe anayang’ana pa kalilole kwa nthawi yake yoyamba, ife tikuyang’ana mu Mawu Ake, kuwona yemwe ife TILI. Ambuye…NDI INE. Ine ndine Mkwatibwi wa Mawu Anu amoyo. Ine Ndine amene munasankha. Ine ndiri mwa Inu, Inu muli mwa ine, ndife amodzi.

Kodi Ife sutingakondwerere bwanji ndi kukhala anthu osangalala kwambiri amene anakhalapo padziko lapansi? Oyera ndi aneneri onse tisanakhalepo ife ankafuna kukhala mu tsiku lino ndi kuwona malonjezo awa akukwanilitsidwa. Koma mwa CHISOMO cha Mulungu, Iye anatiika IFE kuno.

Sitingadikire:

Uuu, mai! [M’bale Branham akuwombetsa manja ake—Mkonzi.] Psyuu! Mwa kuyankhula kwina, pamene mdani akhala atachotsedwa, mapeto a tchimo abwera, kubweretsamo kwa chilungamo chosatha kutabwera, Satana akusindikizidwira mu dzenje lopandamalire, ndipo chidziwitso cha Ambuye chidzaphimba dziko lapansi monga madzi aphimbira nyanja. Ameni! Ulemerero kwa Mulungu! Izo zikubwera, m’bale, izo zikubwera!

Kodi ndi Kudzoza kotani kumene kudzakhala kukuchitika Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, pamene ife tidzasonkhana palimodzi kuchokera kuzungulira dziko kuti tidzamve mngelo wa Mulungu, Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi, kutibweretsera ife Uthenga: Cholinga Chofutukuka Pasanu ndi Kamodzi Cha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele 61-0730E.

M’bale. Joseph Branham