Category Archives: Uncategorized

25-0601 Thunthu La Munthu Wangwiro

Uthenga: 62-1014M Thunthu La Munthu Wangwiro

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Zipilala Zamoyo,

Liwu limene tikulimva pa matepi ndi Urimu Tumimu wa Mulungu kwa Mkwatibwi Wake. Iwo tsopano wamulumikiza moyenera Mkwatibwi Wake palimodzi mu mtima umodzi ndi mtima umodzi kuti ukhale mpingo weniweni wodzazidwa-Mzimu, wodzaza ndi mphamvu ya Mulungu, utakhala palimodzi mu malo Ammwambamwamba, ukupereka nsembe zauzimu, matamando a Mulungu, ndi Mzimu Woyera ukuyenda pakati pathu.

Khristu anatitumizira ife Mzimu Wake Woyera kuti ulankhule kupyolera mwa mngelo wake wachisanu ndi chiwiri kutimanga ife aliyense payekha mu msinkhu wa Yesu Khristu, kuti ife tikhale nyumba ya mphamvu ndi malo okhalamo Mzimu Woyera, mwa Mawu Ake.

Ndife olandira a chirichonse. Ndi katundu wathu, NDI WA ife. Ndi mphatso ya Mulungu kwa ife, ndipo palibe amene angatilande iyo. NDI ZATHU.

“Chimene mudzapempha Atate mu Dzina Langa, Ine ndidzachichita.” Ndani angakane kalikonse pamenepo? “Indetu, indetu, Ine ndinena kwa inu, ngati inu munena kwa phiri ili, ‘Sumuka,’ musati mukaikire mu mtima mwanu koma khulupirirani kuti chimene inu mwanena chidzachitika, inu mukhoza kukhala nacho chirichonse chimene inu mwachilankhula.” Ndi malonjezo otani!  Osati kokha ku machiritso, koma chirichonse.

Ulemerero kwa Mulungu… CHILICHONSE CHOMWE IFE TIMAPEMPHA!

Kuyambira pachiyambi, chilengedwe chonse cha Mulungu chikubuwula ndi kuyembekezera tsiku limene ana athunthu a Mulungu adzaonekera. Tsiku limenelo lafika. Lero ndi tsiku limenelo. Iyi ndi nthawi imeneyo. Ndife ana aamuna ndi aakazi owonetseredwa a Mulungu.

Ndife chida chamoyo cha Mulungu chimene Iye akuyendamo, Iye akuwona mkati, Iye akulankhula, Iye akugwira ntchitomo. Ndi Mulungu akuyenda ndi mapazi awiri MWA IFE.

Ndife makalata ake olembedwa owerengedwa ndi anthu onse. Osankhidwa Ake, okonzedweratu, ana aamuna ndi aakazi otengedwa amene Iye akuwapanga kukhala munthu wamoyo, chifaniziro chamoyo, msinkhu wa munthu wangwiro.

koma kudzigwetsera tokha pamaso pa Mulungu Wamoyo, ukoma wamoyo, chidziwitso chamoyo, chipiriro chamoyo, umulungu wamoyo, mphamvu yamoyo, kubwera ndi Mulungu Wamoyo kumapangitsa munthu wamoyo fano lamoyo—thunthu la Mulungu!

Ndi Khristu, mu umunthu wa Mzimu Woyera pa ife, ndi ubatizo woona wa Mzimu Wake Woyera, ndi ukoma Wake wonse wosindikizidwa mwa ife. Mulungu, akukhala mwa ife mu Kachisi wotchedwa Nyumba. Kachisi wamoyo, wa mokhalamo Mulungu wamoyo; Mpingo wangwiro, kuti Mwalawapamutu Wangwiro utiphimbe ife.

Mulungu anatumiza mneneri kuti adzayitane ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake. Anali Adamu Wake woyamba wobwezeretsedwa kwathunthu, msinkhu wa munthu wangwiro mu tsiku lathu, kuti awulule Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake.

Sindingathe kuchoka pamenepo. Palibe chomwe chingandisunthe. Sindisamala zomwe wina akunena; sizimandisuntha ngakhale pang’ono. Ndikhala pomwepo.

Ndidikirira, dikirani, dikirani, dikirani. Musapange kusiyana kulikonse. Iwo amakhala pomwepo. Ndiyeno, tsiku lina, ndidzafuula pamodzi ndi oyera mtima ena onse mogwirizana kuti: “Ife tikupumula ndi chitsimikizo pa Mawu aliwonse! Pa mtengo wa Kalvari.”

Ine ndikulonjeza mmawa uno kwa Iye ndi mtima wanga wonse kuti mwa chithandizo Chake ndipo mwa chisomo Chake, ine ndikupemphera kuti ndifunafuna tsiku ndi tsiku mosalekeza mpaka nditamverera chirichonse cha zofunikira zonsezi zikuyenderera mu kanthunthu kokalamba kangaka. Mpaka nditakhala kuwonekera kwa Khristu Wamoyo,

KWA INE, kumvetsera Mawu a Mulungu pa matepi ndi dongosolo la Mulungu la lero. Ndi Mawu amoyo a Yesu Khristu. Iwo ndiwo Mtheradi wanga molingana ndi Mawu a Mulungu. Ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero.

Chotero, ine ndikufuna kukuitanani inu kuti mudzabwere kulumikizana nane Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ine ndidzamvetsera kwa William Marrion Branham, amene ine ndikukhulupirira kuti ndi Liwu la Mulungu la masiku athu ano, kuphunzitsa Mkwatibwi wa Khristu momwe angakhalire: Thunthu La Munthu Wangwiro 62-1014M.

M’bale. Joseph Branham

25-0525 Kukhazikitsidwa #4

Uthenga: 60-0522E Kukhazikitsidwa #4

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Otembenuka,

Mwa Kukanikiza Kusewera, tikumvera Mawu osalephera a Mulungu. Ndi Mawu aliwonse Choonadi, mawu aliwonse a Iwo. Ife tayitanidwa ndi kusungidwa, kudzazidwa ndi kuikidwa pambali; odzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo tsopano ali kale mu Dziko la Kanani. Sitikuwopa kalikonse … PALIBE, timadziwa kuti ndife ndani.

Chifukwa takhala ndi Mawu Ake, monga anatilamulira, adzatiuza kuti anatisiyira cholowa.  Ndi liti pamene Inu munachita izo, Atate? Pamene Ine ndinakusankhani inu ndi kuika maina anu pa Bukhu la Moyo wa Mwanawankhosa asanaikidwe maziko a dziko.

Pamene chidzalo cha nthawi chinadza, Ine ndinatumiza Yesu Mwanawankhosa, Yemwe anaphedwa kuchokera ku maziko a dziko, kuti inu mukhoze kulandira cholowa chanu kuti mukhale ana Anga aamuna ndi aakazi, milungu ing’onoing’ono.

Ndidayenera kukuyang’anirani inu kuti muone ngati mukunjenjemera ndi malo omasuka ndisanakukhazikitseni.

  • “Kodi inu mukukhulupirira kuti kusewera Liwu Langa pa matepi mu mpingo ndi kulakwa?”
  • “Inde, usamasewere matepi kutchalitchi.”
  • “Zitsutseni izo.
  • “Kodi inu mukukhulupirira Mawu Anga pa matepi akusowa kutanthauzira?”
  • “Inde, pakufunika winawake kuti afotokoze Izo.”
  • “Iwe ukuphokosera, zitulutseni kunja izo . Inu Simunakonzekerebe.” 

Pamene mwakonzeka, mudzati, “Ameni” ku Mawu aliwonse. 

  • “Kodi ukukhulupirira kuti Ine ndine yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse?”
  • “Ameni.”
  • “Kodi inu mukukhulupirira Liwu Langa pa matepi ndilo MAWU OFUNIKA KWAMBIRI omwe inu muyenera kuwamva?” 
  • “Ameni.”
  • “Kodi inu mukukhulupirira Liwu Langa pa tepi lidzagwirizanitsa Mkwatibwi?”
  • “Ameni.”
  • “Kodi mukukhulupirira kuti mngelo Wanga wamphamvu adzakuzindikiritsa iwe kwa Ine?”
  • “Ameni.”

Mukukhala olimba tsopano. Ndakuyang’anani kuti muone ngati muli ndi zingwe komanso malo otayirira. Ndakonzeka kutseka chitseko. Ine ndiyika Chisindikizo Changa pa iwe. Mwadutsa pakuwunika kwanga. 

Tsopano ndiroleni ine ndikuuzeni inu chinachake, Okondedwa Anga anthu ofunika mu maiko a tepi; kutsidya kwa nyanja ndi kulikonse komwe muli, musachite mantha. Zonse zili bwino. Ine ndinakudziwani inu asanaikidwe maziko a dziko. Ndinkadziwa zonse zimene zidzachitike. 

Ine ndikudzerani inu posachedwa ndi kukutengerani inu Kumalo kumene kulibe imfa, kopanda chisoni, kopanda nsanje, kopanda kalikonse; ungwiro basi, chikondi changwiro.
    
Kufikira pamenepo, musaiwale konse, Ine ndikupatsani inu Mawu Anga, iwe NDIWE MAWU ANGA opangidwa thupi. Ngati inu mufuna CHINTHU CHILICHONSE, yankhulani Icho, ndiye mukhulupirireni Icho; Ndi cholowa chanu.

Ine ndikutumiza Liwu Langa kwa inu kachiwiri Lamlungu lino ndi kufotokoza Izo zonse kwa inu. Ndikuwuzaninso kuti ndinu ndani, komwe mukupita, ndi momwe zilili kumeneko, pakali pano.

Bwerani mudzajowine Mkwatibwi Wanga pamene Ine ndikuwapangitsa iwo kukhala limodzi mu malo ammwambamwamba Lamlungu lino pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, ndipo mudzandimvere Ine mwakukukhazikani inu pa malo mwa Mawu Anga.   60-0522E  Kukhazikitsidwa Gawo Lachinayi
   

M’bale. Joseph Branham

25-0518 Kukhazikitsidwa #3

Uthenga: 60-0522M Kukhazikitsidwa #3

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Namwali Woyera,

Pamene Ife Tikamasindikiza kusewera, ndi uchi mu m’thanthwe, ndi chimwemwe chosaneneka, ndi chitsimikizo chodala, ndi nangula wa moyo wathu, ndiye chiyembekezo chathu ndi Pokhala, ndi Thanthwe la Mibadwo, ndi chilichonse chomwe chili chabwino, ndi Njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero.

Chifukwa chakuti ife timakanikiza Kusewera, Liwu la Mulungu linatikwatiwitsa Ife; linatitomeretsa ife kwa Khristu, monga Namwali Woyera ku Mawu Ake. Ife tiri naye Mphunzitsi Mmodzi, Liwu limodzi, mneneri Mmodzi, amene akutitsogolera ife mwa Mzimu Woyera.

Koma ichi ndi tchalitchi, ine ndikukuphunzitsani inu. Izi zikupita pa matepi. Ine ndikufuna anthu omwe amamvetsera matepi, kumbukirani, izi ndi za mpingo wanga.

Ndi chitsimikiziro chotani kwa ife kuti ife tiri mu Chifuniro Chake changwiro. Matepiwo ndi a mpingo wake. Iye akutiphunzitsa Ife. Iye akutiuza ife, mvetserani kwa matepi

Iye Anayamba magawo a mauthenga a za kukhazikitsidwa awa potiuza ife zomwe zidachitika masiku angapo m’mbuyomo. Ndiye, pa Uthenga uliwonse, iye amalankhula za pamene iye anali atasinthidwa. Ziyenera kukhala zofunikira bwanji kuti Mkwatibwi amve zomwe zinachitika ndi zomwe Mkwatibwi ananena kwa iye.

Mneneri wathu adzaweruzidwa ndi Mawu amene iye anawalalikira ndi kuwasiya pa matepi. Mkwatibwi ku tsidya linayo anamuuza iye kuti adzalandiridwa ndi Ambuye wathu. Kenako adzatipereka kwa Iye ngati zikho za utumiki wake, kenako tidzabwerera kudziko lapansi kuti tikakhale ndi moyo kosatha.

Mawu aliwonse omwe timawamva ndi chidutswa. Ife timangopitiriza kuwapukuta Iwo ndi kuwapukuta Iwo pamene Iye akuwulula mochuluka pamene ife tikuwerenga pakati pa mizere.

Momwe ife timakonda kugawana Izo ndi abale athu ndi alongo, “Kodi inu munamva izi?”

“Iye anatisankha ife mwa Iye pasanakhale nkomwe dziko lapansi”? Ndicho cholowa chathu. Mulungu anatisankha ife, ndipo anamulola Yesu kuti abwere ndi kudzalipira mtengo. Motani zimenezo? Kukhetsa Kwake kwa Magazi Ake, kuti pasadzakhale tchimo limene liti lidzawerengedwe kwa ife. Palibe chomwe inu mumachita.

Ndiyeno, zitangochitika izi, kodi inu mwachigwira ichi?

“Woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye.” Inu maso anu akuyang’ana ku Kalvare, ndipo palibe chirichonse chomwe chikuimitseni inu! Kuyenda kumene kwa moyo wanu, inu mukuyenda mu Msewu waukulu wa Mfumu, mutadzozedwa ndi Mafuta wodula, mukukalowa mu malo Oyeretsetsa. Psyi! Ameni.

Tinali ngati ndodo ya Aroni, ndodo yakale youma imene ananyamula kwa zaka 40 m’chipululu. Koma tsopano, chifukwa ife takhala mu Malo Opatulika amenewo pakumva Liwu la Mulungu likuyankhula kwa ife pa matepi, ife taphuka ndipo tachita maluwa, odzaza ndi Mzimu Wake Woyera, ndipo ndife Mkwatibwi Wake akufuula pamwamba pa mapapo athu:

• Woyera, woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, matepi ali oyamba mu mitima yathu.

• Woyera, woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, Iye anatisankha ife asanaikidwe maziko a dziko.

• Woyera, woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, ife ndife mkwatibwi wa Yesu Khristu.

• Woyera, woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, osapanga kusiyanitsa kulikonse ndi zomwe aliyense anena, sitikuloweza zapa matepi, ife tikuwasewera mochuruka.

• Woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, maso athu ayang’ana ku Kalvare, ndipo palibe chimene chikutiletse ife.

Ine ndiri wokondwa kwambiri podzalumikizana mitima ndi ambiri pano amene amadziwa kuti Awa ndi Mawu osalephera a Mulungu. Ndiye Iwo, Iwo ndi Mawu aliwonse Choonadi, Mawu aliwonse a Iwo, gawo lirilonse la Iwo. Ndipo ndi chisomo cha Mulungu, ndakhala nawo mwayi wokaliwona Dzikolo kumene tsiku lina ife tidzapitako.

Bwerani mudzajowine nafe Lamlungu pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene mneneri akutenga Mawu aliwonse ndi kumangowapukuta Iwo. Iye adzachitengera Icho mpaka ku Genesis ndi kuchipukuta Icho, kuchitengera Icho mpaka ku Eksodo ndi kuchipukuta Icho kachiwiri, ndipo ngakhale mpaka ku Chivumbulutso; ndipo Ndi gawo lililonse la Yesu!

M’bale. Joseph Branham

Uthenga:

Kukhazikitsidwa Gawo la Chitatu 60-0522M

Malemba:

Mateyu 28:19
Yohane 17:7-19
Machitidwe 9:1-6, chaputala 18 ndi 19
Aroma 8:14-19
1 Akorinto 12:12-13
Agalatiya 1:8-18
Aefeso Chaputala 1
Ahebri 6:4-6, 9:11-12

25-0511 Kukhazikitsidwa #2

Uthenga: 60-0518 Kukhazikitsidwa #2

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa A Ufumu Wa Unsembe ,

Aliyense alume chala chake, tsina moyo wako, ndikudzutsa mtima wako. Lero, Mkwatibwi wa Yesu Khristu akufuula kuti:

Lero, ulosi umenewu wakwaniritsidwa pamaso pathu pomwe.

Ine ndikukhulupirira, limodzi la masiku aulemerero awa, pamene chitaganya chogwirizana ichi cha mpingo chikupita palimodzi, ndipo papa watsopano akutulutsidwa kuchokera ku United States ndi kuikidwa kumeneko molingana ndi uneneri, ndiye iwo adzapanga fano longa la chirombo.

Liwu la mneneri wa Mulungu linalankhula Ilo pa 19 Disembala , 1954, ndipo miyezi 9 pambuyo pake, Robert Prevost, yemwe tsopano akudziwika kuti Papa Leo XIV, anabadwa. Iye tsopano ndi papa watsopano wa Roma. “Pakuti atero Ambuye” wakwanilitsidwa.

Pa 7 Meyi , 1946, MULUNGU anaika mneneri Wake mu Chigayo cha a Green, ku Indiana, kuti amupatse iye utumiki wake ndi kulalikira kwa dziko, uyu ndi wamthenga Wanga wamphamvu wa mngelo wachisanu ndi chiwiri, Liwu Langa kwa dziko. Mverani Inu Iye.

Pamene Mngelo wa Ambuye anakomana ndi ine kunja uko ku Chigayo cha a Green, Indiana, zaka eyiti zapitazo; kuchokera pamene ndinali mwana, wanditsatira ine, wandisonyeza masomphenya. Pamene ine ndinapita kwa Iye. Iye anati, “Ngati iwe uti ukhale woonamtima, nkuwatengera anthu pokukhulupirira iwe, palibe kanthu kati kadzaime patsogolo pa pemphero lako.”

William Marrion Branham ndi Liwu losankhidwa ndi Mulungu ku dziko. Mneneri wamphamvu amene Mawu a Mulungu amafika kwa iye. Molingana ndi Mawu, iye ali wotanthauzira Wauzimu YEKHA wa Mawu a Mulungu.

Iye anatsimikiziridwa ndi Mulungu Mwiniwake, ndi Lawi la Moto.

Pa 7 May , 2025, SATANA anaika gulu lake la Makadinala mu mpingo wa Sisitine ku Roma kuti asankhe Mlowa Mmalo wa Khrisitu, kuti akwaniritse pakuti Atero Ambuye.

Adatsimikiziridwa ndi munthu yemwe ali ndi KUFUFUZA KWA USI WOYERA.

Mkwatibwi wa Khristu kuzungulira dziko lapansi akusangalala, akufuula, akukuwa ndi kutamanda Ambuye pamene ife tikumva, ndi kuona ndi maso athu omwe, uneneri wa mneneri ukukwaniritsidwa.

Zili ngati tikuwona Nyanja Yofiira ikutseguka pamaso pathu. Mana atsopano akugwa kuchokera kumwamba. Mamilioni a zinziri akudyetsa Mkwatibwi. Madzi otuluka mu thanthwe. Moto ukutsika ndi kunyeketsa nsembe limodzi ndi Eliya.

Ulosi ukukwaniritsidwa tsiku lililonse. Mawu olonjezedwa a Mulungu akuwonetseredwa m’miyoyo yathu. Zinthu zikuchitika pozungulira ife. Mkwatibwi wadzikonzekeretsa Yekha pakumva ndi kukhulupirira Mawu. Ndife Mawu opangidwa thupi.

Zoonadi tafika. Nthawi yayandikira. Mkwatibwi akusangalala ndikulumikizana pamodzi padziko lonse lapansi kuposa kale. Mneneri akutsimikizira Mkwatibwi potiuza ife kuti ndife awunsembe achifumu a Mulungu, fuko loyera, anthu achilendo amene aitanidwa, osankhidwa, osankhidwa, ndi oikidwa pambali.

IFE TSOPANO NDIFE Ana amuna ndi Ana Aakazi a Mulungu, otsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu; osati ndi munthu, koma ndi Mzimu. Ife tikudziwa, popanda mthunzi umodzi wa kukaikira, IFE NDIFE MKWATIBWI WAKE. CHIKHULUPIRIRO chathu chikufika patali kwambiri tsiku lililonse. Palibe kutiletsa kapena kutichedwetsa, Mulungu waziululira ndi kuzika Izo mu mtima mwathu ndi mu moyo wathu.

Mkwatibwi akuzindikira kwathunthu chomwe ife tiri. Ife tiri mu Dziko lathu lolonjezedwa lauzimu, mu eni ake onse. Tili ndi mtendere wa Kumwamba, madalitso a Kumwamba, Mzimu wa Kumwamba. ZONSE NDI ZATHU. Ife tikungokonzekera zomwe Iye ali nazo kwa ife lotsatira.

Lipenga la Ambuye lidzawomba, ndipo akufa mwa Khristu adzawuka poyamba.

Matupi akumwamba awa adzatsika ndi kuvala matupi a padziko lapansi, aulemerero ndipo adzasinthidwa m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso. Ife tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo, kukakomana ndi Ambuye mu mlengalenga.

Ndi Tsiku lotani. Ndi Nthawi yotani. Palibe njira yoti ndinene m’mawu aumunthu zomwe tonse tikumva m’miyoyo yathu. Mitima yathu ikuthamanga. Sitikupanga kuti izi zichitike, Mzimu Woyera uli ngati chitsime chotumphukira mkati mwathu. Mkwatibwi wakhala akuyembekezera mphindi iyi kuyambira masiku a Adamu…NDIPO IFE TSOPANO.

Tikukulandirani inu. Tikukuitanani inu. Tikukuchondererani inu. Bwerani mudzalumikizane nafe pa nthawi yodabwitsa kwambiri yomwe ngakhale dziko lakhala likuidziwa, pamene tikumva Liwu la Mulungu likuwululira Mawu Ake kwa ife Lamlungu lino pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, pamene tikumva: 60-0518 kukhazikitsidwa ,Gawo la Chiwiri.

M’bale. Joseph Branham

Malemba oti muwerenge Uthenga usanayambe:

Genesis 1:26
Aefeso Mutu Woyamba
Aroma 8:19
Agalatiya 1:6-9
Ahebri Chaputala Chachisanu ndi chimodzi
Yohane 1:17

25-0504 Kukhazikitsidwa #1

Uthenga: 60-0515E Kukhazikitsidwa #1

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Okhazikitsidwa,

Ife tsopano tikudya zinthu zamphamvu za Mulungu ndi kumvetsa bwino Mawu ake. Mulungu watipatsa ife Vumbulutso loona la Mau ake. Malingaliro athu auzimu onse ndi osasokonezeka.

Ife TIKUDZIWA ndendende Yemwe Iye ali. Ife tikudziwa ndendende chimene Iye ali. Ife TIKUDZIWA ndendende kumene tikupita. Ife TIKUDZIWA ndendende amene ife tili. Ife TIKUDZIWA mwa Yemwe ife tinamukhulupirira ndi kuvomereza kuti Iye ali wokhoza kusunga chimene ife tapereka kwa Iye kufikira tsikulo.

Iye wayankhula ndi kuwulula zinsinsi zonse zomwe zakhala zili zobisika chikhazikitsireni maziko a dziko kwa ife. Iye anatiuza ife momwe ena nthawizonse akhala akukana njira Yake yoperekedwa ndi kukhumba utsogoleri wosiyana, koma Iye akanati akhale ndi kagulu kakang’ono kamene kadzakhala moona ku Mawu Ake.

Kudutsa mdziko, iwo sadzakhala atasonkhana mu malo amodzi kuti akhale ochita zinthu mofanana. Koma magulu aang’ono a iwo adzakhala atamwazikana konse konse padziko lapansi.

Ulemerero, tamwazikana padziko lonse lapansi, koma Ogwirizana monga Mmodzi mwa Kukanikiza kusewera ndikumvetsera ku Liwu la Mulungu likulankhula kwa ife.

Tiyeni tingosuzumira ndi kulawiratu zimene Iye adzatilankhula kudzera mwa mngelo wake wamphamvu pa Lamlungu.

Okondedwa anga osankhidwa, inu tsopano mukukhala pamodzi mu malo a Kumwamba. Osati kokha kulikonse, koma mu malo “Akumwamba”; ndi udindo wanu ngati wokhulupirira. Inu mwapemphereredwa ndi kukonzekera Uthenga. Inu mwadzisonkhanitsa nokha palimodzi monga oyera, wobatizidwa ndi Mzimu Woyera, odzazidwa ndi madalitso a Mulungu. Inu munaitanidwa, osankhidwa, ndipo mzimu wanu wabweretsedwa mu chikhalidwe cha Kumwamba.

Zomwe zingachitike. Mzimu wanga Woyera udzakhala ukusuntha pa mtima uliwonse. Inu Munabadwanso mwatsopano ndipo cholengedwa chatsopano mwa Khristu Yesu. Machimo anu onse ali pansi pa Mwazi. Inu muli mu kupembedza kwangwiro, ndi manja anu ndi mitima yokwezera kwa Ine, mukundipembedza Ine palimodzi mu malo ammwambamwamba.

Inu ndinu wokonzedweratu, Osankhidwa, mu Kudziwiratu Kwanga. Osankhidwa, Oyeretsedwa, Olungamitsidwa mwa Kuikidwiratu. N’zosatheka kuti munyengedwe. Ine ndinakuikani inu asanaikidwe maziko a dziko. Inu ndinu Mulungu wamng’ono, wosindikizidwa ndi Mzimu Woyera wa lonjezano; osati kungobadwira m’banja, Ana Anga aamuna ndi Aakazi.

Ine ndidzakudalitsani inu ndi machiritso Auzimu, kudziwiratu, vumbulutso, masomphenya, mphamvu, malirime, kutanthauzira, nzeru, chidziwitso, ndi madalitso onse a Kumwamba, ndi chisangalalo chosaneneka ndi chodzaza ndi Ulemerero.

Mtima uliwonse udzadzazidwa ndi Mzimu Wanga. Inu mudzakhala mukuyenda limodzi, mutakhala palimodzi, mu malo Ammwambamwamba. Palibe lingaliro limodzi loyipa pakati panu, palibe ndudu imodzi yomwe idzasutidwe, palibe diresi limodzi lalifupi, palibe ichi, icho kapena chimzake, palibe lingaliro limodzi loyipa, palibe yemwe ali ndi kalikonse kotsutsana wina ndi mzake, aliyense akuyankhula mu chikondi ndi chiyanjano, aliyense ndi mtima umodzi mu malo amodzi.

Kenako mwadzidzidzi padzabwera mkokomo wochokera Kumwamba ngati mphepo yothamanga yamphamvu ndipo ndidzakudalitsani inu ndi madalitso onse auzimu. Ndiye inu mudzakhala ngati Davide, kuvina pamaso pa Likasa, kuliwuza dziko kuti simukuchita manyazi, IWE NDIWE MKWATIBWI WANGA WA TEPI! Inu mumakanikiza kusewera ndi kukhulupirira MAWU ALIWONSE amene Ine ndimayankhula. Simudzasunthika, ndipo simungathe kusunthika!

Ena akhoza kuwakana Iwo, kapena osawamvetsa Iwo, koma kwa inu, Ndi Chizindikikiro chanu chaulemu. Monga Davide adanena kwa mkazi wake; “Inu mukuganiza kuti ichi chinali chinachake, ingodikirani mpaka mawa, ife tidzakhala tikumvetsera kwa matepi ngakhale ochuluka, kutamanda Ambuye, odzazidwa ndi Mzimu Wake; pakuti ife tikukhala mu Kenani, kupita ku dziko lolonjezedwa.”

Kenako ndidzayang’ana pansi kuchokera Kumwamba ndikukuuzani:

“Ndiwe Mkwatibwi wa pamtima Wanga Womwe.”

Madalitso amenewa angakhale anunso. Bwerani, kulumikizana nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, ndi kuona kukhalapo kwa Ambuye kuposa kale lonse pamene tikumvetsera Liwu la Mulungu la lero likulankhula kwa ife ndi kutibweretsera Uthenga: Kukhazikitsidwa #1 60-0515E.

Kumbukirani, izi ndi za kwa mpingo, osati kwa wakunja. Icho ndi chinsinsi mmafanizo kwa iye, samatha konse kuti amvetse, zimapita pamwamba pa mutu wake, iye samadziwa konse za icho kuposa kalikonse. Koma, kwa mpingo, icho ndi uchi mu thanthwe, icho ndi chimwemwe chosaneneka, icho ndi chitsimikizo chodala, icho ndi nangula ya solo, icho ndi chiyembekezo chathu ndi pokhalapo, icho ndi Thanthe la Mibadwo, oh, icho ndi chirichonse chimene chiri chabwino.Pakuti miyamba ndi dziko lapansi zidzapita, koma Mawu a Mulungu sadzapita.

Pakuti kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka, koma Mawu a Mulungu sadzachoka.

M’bale. Joseph Branham

Malemba oti muwerenge Uthenga usanayambe:
Yoweli 2:28
Aefeso 1:1-5
1 Akorinto 12:13
1 Peturo 1:20
Chivumbulutso 17:8
Chivumbulutso 13

25-0427 Mfumu Yokanidwa

Okondedwa Abwezi Ofunika,

Okondedwa anga, okondedwa anga a Uthenga, ana anga obadwa kwa Mulungu.

Ndi Mathero asabata osangalatsa otani yomwe tinali nayo ndi Ambuye wathu. Zinali ngati chinthu china chilichonse, kungocheza ndi Iye, kulankhula naye, kumva Mawu Ake, kumulambira, kumuthokoza komanso kumuuza ndimochuruka bwanji mmene ife timamukondera.

Ndi zopambana bwanji kukhala mu tsiku lino ndi kukhala gawo la Malemba akukwaniritsidwa. Kodi mawu aumunthu angafotokoze bwanji zonse zomwe zili mu mtima mwathu? Monga mneneri ananena, Si ine, pali Chinachake basi mkati mkati, chikukankhira ndi kutumphukira mwa ine; chitsime cha Mzimu Woyera. Ndi Mkwatibwi kudzikonzekeretsa Yekha kwa Mkwati.

Ndi mosangalatsa bwanji Mkwatibwi kukhala molondola kwambiri isanafike nthawi ya ukwati wake. Mtima wake umayamba kugunda kwambiri pamene masekondi angapo apita….akudziwa kuti nthawi yafika. “Ndadzikonzekeretsa ndekha. Iye akudza kwa ine. Tsopano tidzakhala AMODZI.”

Ife kwenikweni Tikukhaladi m’mnyengo zomalizira za nthaŵi. Mkwatibwi posachedwapa adzakwatulidwa ndi kuitanidwa ku Mgonero wathu wa chikwati. Iye akutitengera ife kumtunda kwatsopano. Palibenso funso; osadabwanso; NDIFE MKWATIBWI.

Ndipo Iye sanamalize panobe. Iye amafunabe kudalitsa ndi kulimbikitsa Mkwatibwi wake wokondedwa. Momwe amakondera kumulimbikitsa ndi kumuuza momwe amamukondera. Iye Ndi wonyadira bwanji ndi Iye!

Iye alinso ndi Vumbulutso lina lapadera kwambiri loti amupatse Iye. Pamene pali ma liwu ochuluka padziko lapansi akukana kusewera matepi, Iye amafunanso kutsimikizira Mkwatibwi kuti ali mu Chifuniro Chake changwiro ndi Njira Yake yoperekedwa.

Dongosolo lake nthawi zonse limakanidwa. Mkwatibwi Wake nthawizonse wakhala akuzunzidwa. Anthu nthawi zonse amafuna njira yawoyawo, malingaliro awo. Iwo akufuna mtsogoleri wina kuti awatsogolere. Koma Mulungu anatumiza mtsogoleri MMODZI kuti adzatsogolere Mkwatibwi Wake, Iyemwini, Mzimu Woyera, ndi Mzimu Woyera wa tsiku lino, monga mu MASIKU ENA ONSE, ALI MNENERI WA MULUNGU.

Iwo akhala akufuna kuti amuna aziwatsogolera. M’masiku a Samueli, Mulungu ananena kuti iwo akumukana posafuna kuti Samueli aziwatsogolera. Zinaoneka zachilendo popeza Samueli nayenso anali mwamuna, koma kusiyana kwake kunali kuti Samueli ndi munthu amene Mulungu anamusankha kuti awatsogolere iwo. Sanali Samueli, Anali Mulungu akumugwiritsa ntchito Samueli. Iye anali MAWU osankhidwa ndi Mulungu NDI MAMUNA KUTI AWATSOGOLERE IWO, koma iwo ankafuna mawu ena.

Sauli anadziwa kuti anthu amaopa Samueli, choncho anayenera kulengeza kuti, “Sauli NDI Samueli”. Iye ankayenera kuwaopseza anthu kuti amutsatire Iye. Ndithudi, iye anaitanidwa. Zoonadi, iye anali atadzozedwa ndi Samueli kuti akhale mfumu yawo, koma Mulungu ANALI nayo Njira yoperekedwa, ndipo mneneri Iye anamusankha kuti awatsogolere iwo, ngakhale kumutsogolera Sauli. Mulungu analankhula ndi mneneri Wake ndipo anamuuza Sauli choti achite. Pamene Sauli anaganiza kuti nayenso wadzozedwa, ndipo sanafune kumva mneneri yekha, Mulungu anachotsa ufumu wake.

Ndiyeno kenako pamene iwo anachita izo, pamene kugonjetsedwa kwakukulu kunabwera, ndiye Sauli anadula ng’ombe ziwiri zazikulu ndi kuzitumiza izo kwa anthu onse. Ndipo ine ndikukhumba inu mukanazindikira apa, pamene Sauli anatumiza zidutswa za ng’ombe kwa Israeli yense, ndipo anati, “Mulole munthu aliyense amene sadzatsatira Samueli ndi Sauli, msiyeni iye, ng’ombe iyi, akhale monga choncho.” Kodi mukuona mmene iye anayesera mwachinyengo kudziimira yekha ndi munthu wa Mulungu? Zinali zosemphana bwanji ndi Chikristu! Kuopa anthu kunali chifukwa cha Samueli. Koma Sauli anawachititsa kuti onse azimutsatira chifukwa chakuti anthu ankaopa Samueli. “Muwalole iwo kuwatsatira Samueli ndi Sauli.”     

Tsiku lina Sauli anavutika kwambiri. Sanathe kupeza yankho kuchokera kwa Mulungu. Sanathe kupeza chitonthozo. Anafuna mayankho. Iye ankadziwa kumene ankayenera kupita kuti akapeze yankho limene ankafuna; panali malo amodzi okha, MNENERI WA MULUNGU, SAMUELI. Iye anali atapita, koma iye anali akadali LIWU LA MULUNGU, NGAKHALE MU PARADISO.

Atate ankafuna kuti Mkwatibwi wawo adziwe amene anamusankha kuti atsogolere mkwatibwi wake m’tsiku lomaliza lino, choncho anatenga mngelo Wake wamphamvu kupyola katani la nthawi kuti atiuzenso, kutitonthoza, ndi kutilimbikitsa kuti tili mu chifuniro Chake changwiro ndi chifuniro chake choperekedwa.

Mvetserani mosamala kwambiri kwa ZONSE zimene mneneri akunena.

Tsopano, ine sindikanafuna kuti inu mubwereze izi. Izi ziri pamaso pa mpingo wanga, kapena nkhosa zanga zimene ine ndikuzitumikila.    

 Iye asanatiuze kanthu kalikonse, choyamba amafuna kuti ife tidziwe kuti izi ndi za IFE, MPINGO WAKE, NKHOSA ZAKE, ZIMENE IYE AKUZITUMIKILA. Chotero, ngati inu simungakhoze kunena kuti, “M’bale Branham ndi m’busa WANGA,” ine ndinanenapo izo kale, koma palibe chifukwa chokhalira kuwerenga mopitirira apo, izi si zanu, kuphatikizanso iye sanafune kuti ife tibwereze izo kwa wina aliyense koma kwa iwo amene amakhulupirira ndi kunena, “M’bale Branham ndi m’busa wanga”.

Pomwepo pali yankho lathu ku funso lomwe timapeza kutsutsidwa kochuluka ponena kuti: “M’bale Branham ndi m’busa wathu.” (Awo ndi anthu awo a tepi .) Iwo akulondola, iye ali, ndipo ife tiri.

Chonde musakwiyitsidwe ndi ine, sindikunena zinthu izi kuti ndikhumudwitse aliyense, zomwe zingakhale zolakwika, koma ndi zomwe Iye akunena kwa Mkwatibwi. Ine sindikuyika kutanthauzira kwanga kwa izo, Iye akunena izo momveka…Mawu a Mulungu sasowa kutanthauzira.

Kaya izo zinali, ine ndinali mu thupi ili kapena kunja, kaya kunali kumasulira, izo sizinali ngati masomphenya aliwonse amene ine ndinayamba ndakhalapo nawo.

Tsopano Iye akutiuza ife kuti izi sizinali ngati masomphenya enawonse omwe adawonapo. Anapita kwinakwake komwe anali asanakhaleko. Zinali zazikulu kuposa masomphenya aliwonse omwe adawonapo. Iye sanali kulota, anawona thupi lake pa kama; IYE ANALI KUMENEKO.

Mkwatibwi wa Yesu Khristu, mulole izo zimire mkati mwabwino kwenikweni. Uyo anali Mkwatibwi wa Yesu Khristu ku mbali inayo, nthawi yapano, yemwe anabwera akuthamanga kwa iye, akufuula ndi kumugwira iye, akuponya mikono yawo momukumbatira iye ndi kunena, “O, m’bale wathu wofunika!”

Iye anali kumeneko; iye amakhoza kuchimverera icho; iye amakhoza kuwamva iwo. Iwo anali kuyankhula kwa iye. Iye anayima, ndipo anayang’ana, iye anali wamng’ono. Iye anayang’ana mmbuyo pa thupi lake lokalamba lomwe linali litagona ndi manja ake kumbuyo kwa mutu wake.

Tsopano ife takhazikitsa IYE ANALI UKO, ndipo Uyo anali Mkwatibwi wa Yesu Khristu yemwe iye anali kumuwona. Ndiyeno Tsopano tiyeni timve zomwe liwu lochokera kumwamba linanena kwa iye.

Ndiyeno Liwu lija limene linali kuyankhula, kuchokera pamwamba pa ine, linati, “Inu mukudziwa, zinalembedwa mu Baibulo kuti aneneri anasonkhanitsidwa ndi anthu awo.”

Mulungu sanali kumuwonetsa kokha ndi kumulimbikitsa mneneri Wake, koma panali zochulukira kwa Izo. Akanadzabweranso ndi kutiuza osati kokha kumene tikupita ndi momwe zingakhalire, koma kutiuza ife tiri mu Chifuniro Chake changwiro pa Kukanikiza kuyisewera ndipo ndi momwe inu mumafikira kumene Mkwatibwi ali.

M’bale Branham ananena kuti adafunitsitsa kumuona Yesu mochuruka kwambiri. Koma adati kwa iye:

“Tsopano, Iye ali pamwamba pang’ono, mmwamba momwemo.” Anati, “Tsiku lina Iye adzabwera kwa inu.”

Iwo anapitiriza kumuuza IYE CHOMWE IYE ANALI.

“Inu munatumizidwa, ngati mtsogoleri.” Ndipo Mulungu adzabwera.Ndipo Iye atachita izo, Iye adzaweruza inu molingana ndizomwe inu munawaphunzitsa iwo. Choyamba ngati iwo adzalowe mkatimo Kapena ai. Ife tidzalowa mkati mmenemo molingana ndi chiphunzitso chanu

Kodi Ndani anatumidwa monga mtsogoleri? Tidzaweruzidwa molingana ndi zomwe watiphunzitsa? Tidzalowa Kumwamba molingana ndi chiphunzitso cha ndani?

Wina akhoza kunena, ine ndimawaphunzitsa anthu anga zomwe M’bale Branham ananena…

Tiyeni tiwerenge monga momwe Iye akufuna POWONETSETSA kuti Ife timvetsetse molondola bwinobwino.

Ndipo anthu amenewo anakuwa, ndipo anati, “Ife tikudziwa zimenezo, ndipo ife tikudziwa kuti ife tikupita nawe, tsiku lina, kubwerera ku dziko lapansi.” Anati, “Yesu adzabwera, ndipo inu mudzaweruzidwa molingana ndi Mawu amene inu munatilalikira ife.

Tidzaweruzidwa ndi Mawu amene IYE analalikira kwa ife. Chotero, chiweruzo chimabwera kuchokera ku zomwe Liwu la Mulungu linanena pa matepi. Kodi Wina angakhoze bwanji kunena kuti Liwu la pa matepi sali MAWU OFUNIKA KWAMBIRI omwe inu mungawamve?

“Ndiyeno ngati inu mudzalandiridwa nthawi imeneyo, yomwe inu mudzakhalako,”

Kodi Inu Mwakonzeka. Izi zidzakhomerera msomali pa chimene chiri Chifuniro changwiro cha Ambuye kwa Mkwatibwi wa Yesu Khristu. Mkwatibwi akumuuza mneneri zomwe IYE ADZACHITA. Palibe wina aliyense. Osati gulu. Osati m’busa wina, mneneri wa Mulungu, WILLIAM MARRION BRANHAM.

“ndiye mudzatipereka kwa Iye ngati zikho za utumiki wanu.”

Kodi Ndani amene atipereke kwa Ambuye Yesu?
Kodi Masiku ongomvera mneneriyo atha?
Kodi M’bale Branham sananene konse zosewera matepi?

Mkwatibwi akukuwa ndikunena kuti ngati mukufuna kukhala Mkwatibwi kulibwino Kumakanikiza kusewera.

Kodi Simunakhutitsidwebe? Chabwino, pali ngakhale zochuruka.

Anati, “Inu mudzatilondolera kwa Iye, ndipo, tonse palimodzi,kenako ife tidzabwerera ku dziko lapansi, kukakhala moyo kwanthawizonse.”

Kodi Ndani atitsogolere kwa Iye? Ndani akutsogolera Mkwatibwi? Mkwatibwi akumuuza iye kuti IYE ADZATSOGOLERA MKWATIBWI KWA IYE, kenako ife tidzabwerera ku dziko lapansi kudzakhala kwamuyaya.

Ngati pali Vumbulutso LILILONSE mwa inu nkomwe. Ngati inu mukuti inu mukukhulupirira Uthenga uwu, ine ndikupemphera kuti Mulungu awulule kwa inu kuti inu MUYENERA kuika Liwu Lake, matepi, POYAMBA.
Abusa, ikaninso mneneri mu maguwa anu. Matepi ndi Mau ofunikira kwambiri omwe muyenera kuwamva pamene mudzaweruzidwa ndi LIWU LIMENERO.

Malinga ndi Mawu, ife tili mu Chifuniro Chake changwiro ndi choperekedwa kwa tsiku lathu pomvetsera Liwu la Mulungu pa matepi.

Ngati Mulungu watsegula maso anu ku Chivumbulutso choona ku Mawu Ake, ine ndikukuitanani inu kuti mudzalumikizane nafe Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, pamene ife tikumva 60-0515M Mfumu Yokanidwa.

M’bale. Joseph Branham