Wokondedwa Mkwatibwi wa Khristu, tiyeni ife tibwere palimodzi Lamlungu 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, kuti tidzamve 65-1128E Pa Mapiko A Nkhunda Yoyera-mwachipale M’bale. Joseph Branham
Palibe chotupitsa, kapena mawu osadziwika, palibe kutanthauzira kwa munthu kofunika pakati pathu. Timangomvetsera Mawu Oyera Angwiro kuchokera mkamwa mwa Mulungu pamene Iye akulankhula kwa ife milomo ndi khutu.
Tsopano ife tikuwaona Mawu olonjezedwa omwewo, a Luka, a Malaki, malonjezo onse awa kuyambira lero, akupangidwa thupi, akukhala pakati pa ife, amene ife tinawamva ndi makutu athu; tsopano ife tikumuwona Iye (ndi maso athu) akutanthauzira Mawu Ake Omwe, ife sitikusowa kutanthauzira kulikonse kwa munthu.
Mkwatibwi, izo mophweka sizikanakhoza kumveka bwino kuposa izo. Iye ndi Mulungu, atayima pamaso pa Mkwatibwi Wake mu thupi laumunthu, yemwe ife tikhoza kumuwona ndi maso athu omwe, akuyankhula ndi kutanthauzira Mawu Ake Omwe, ndi kuwayika iwo pa tepi. Mawu Angwiro olankhulidwa ndi kulembedwa ndi Mulungu Mwiniwake, motero samasowa kutanthauzira kulikonse kwa munthu.
Mulungu akuyankhula molunjika kwa Mkwatibwi Wake, pa matepi.
Mulungu akutanthauzira Mawu Ake Omwe, pa matepi.
Mulungu akudziwulula Yekha, pa matepi.
Mulungu akumuuza Mkwatibwi Wake, inu simukusowa kutanthauzira kulikonse kwa munthu, Mawu Anga pa matepi ali zonse ZOFUNIKIRA MKWATIBWI WANGA.
Kumbukirani, pamene inu muchoka pano, muyambe kuchokamo mu mankhusu tsopano; inu mukupita mu njere, koma mukakhale mu Kukhalapo kwa Mwana. Musakawonjezere, zimene ine ndanena; musakachotsere, zimene ine ndanena. Chifukwa, ine ndimayankhula Choonadi monga momwe ine ndikudziwira Icho, monga Atate andipatsira ine. Mukuona?
Mulungu wapanga NJIRA YABWINO YOKHAYO kuti Mkwatibwi achite monga momwe anatilamulira ife. Izi sizinachitikepo, mpaka lero. Palibe kungoganiza, popanda kudabwa, palibe funso ngati pali china chowonjezera, chochotsedwa, kapena kutanthauzira. Mkwatibwi wapatsidwa Chibvumbulutso chenicheni: KUSEWERA MATEPI NDI NJIRA YABWINO YA MULUNGU.
Ngati zingachitike, ndiroleni ndinenenso. Vumbulutso langa liri kuti Mkwatibwi wa Yesu Khristu, osati ena, MKWATIBWI, sasowa CHINTHU CHINA CHILICHONSE AYI koma Liwu la Mulungu pa matepi.
Koma pamene Mzimu Woyera uwo kwenikweni Mawu enieni abwera mwa inu (Mawu, Yesu), ndiye, m’bale, Uthenga si chinsinsi kwa inu kenako; inu mukuchidziwa Icho, m’bale, Icho chonse chawala pamaso panu.
Uthenga si chinsinsi kwa ine. Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi kunthawi zonse. Kumwamba ndi dziko lonse lapansi zimatchedwa Yesu. Yesu ndiye Mawu.
Ndipo Dzinalo liri mu Mawu chifukwa Iye ali Mawu. Ameni! Iye ndi chiyani ndiye? Mawu otanthauziridwa ndi mawonetseredwe a Dzina la Mulungu.
Mulungu akulumikiza Mkwatibwi Wake ndi Liwu Lake, limene Iye analilemba ndi kulisungira kwa lero, kotero kuti Iye akhoze kubweretsa Mkwatibwi Wake palimodzi ngati Chigawo Chimodzi. Mkwatibwi aziwona izo ndi kuzizindikira Iyo ngati NJIRA YOKHAYO yomwe Iye angakhoze kubweretsa Mkwatibwi Wake palimodzi.
Iye anachita zimenezi zaka zoposa 60 zapitazo kuti atisonyeze mmene angachitire zimenezi masiku ano. Ndife “m’modzi mwa mipingo yake yomwe ikugwirizana”
Ngati ine sindikhulupirira mu kupita kutchalitchi, nchifukwa chiyani ine ndiri ndi tchalitchi? Ife tinali nawo iwo onse kudutsa m’dzikoli, titalumikizitsana usiku wina, mailosi thuu handiredi aliwonse a mabwalo anali ndi imodzi ya matchalitchi anga.
Magulu ambirimbiri, ali nawo malo awa omwe inu nonse munali nawo kuno kuchokera ku kachisi. Izo zalumikizidwanso ku Phoenix, kuti kulikonse kuli msonkhano, izo zikufika kumene umo…Ndipo iwo akusonkhana mu matchalitchi ndi mmanyumba, ndi zinthu monga choncho, zikudutsa mu mpweya wa mawu wabwino kwambiri.
M’bale Branham akunena momveka bwino kuti anthu mu “nyumba” zawo ndi “zinthu zonga izo” inali imodzi mwa mipingo yake yomwe inali yolumikizana. Motero nyumba, malo opangira mafuta, nyumba, mabanja osonkhanitsidwa pamodzi pa hook up ake anapanga mpingo.
Tiyeni tiwerenge KALATA YA CHIKONDI mwakanthawi kochurukilapo pang’ono
Ife tikupempherera mipingo yonse ndi magulu amene asonkhana pozungulira zo—zo—zoyankhulira zazing’ono kunja kudutsa, kuchokera ku fukoli, njira yonse mpaka ku Gombe la Kumadzulo, kukwera mpaka ku mapiri a Arizona, kutsika mpaka ku zigwa za Texas, njira yonse mpaka ku Gombe la Kummawa, monse kudutsa dziko, Ambuye, kumene iwo asonkhana. Maora ambiri motalikana, ife tiri mu nthawi, koma, Ambuye, ife tiri limodzi usikuuno ngati chimango chimodzi, okhulupirira, tikuyembekezera Kudza kwa Mesiya.
Kotero kukhala pa Kulumikizana, kumvetsera kwa M’bale Branham ONSE PA NTHAWI YOFANANA; iwo anali pamodzi ngati gulu limodzi, okhulupirira, kuyembekezera Kudza kwa Mesiya.
Ndiroleni ine ndikufunseni inu funso ndipo inu muwayankhe osonkhana anu. Ngati M’bale Branham akanakhala pano lero, mu thupi, ndipo inu mukanakhoza kukhamukira kapena kulumikizana kuti mumumve iye Lamlungu lirilonse mmawa, Onse pa nthawi imodzi ndi Mkwatibwi kuzungulira dziko, azibusa, kodi inu mungagwirizane ndi kumumva M’bale Branham kapena kodi inu mungalalikire?
M’bale Branham momveka akunena kuti ntchito yanu ndi mpingo wanu. Ngati inu munali kuno zaka makumi asanu ndi chimodzi zapitazo ndipo M’bale Branham anali ndi utumiki, koma mpingo wanu sunapiteko koma kukhala ndi utumiki wawo (umene atumiki ambiri ankachitira kalelo), kodi inu mungapite ku “mpingo wanu”, kapena kodi inu mungapite ku “Branham Tabernacle” kuti mukamve M’bale Branham?
Ndikupatsani yankho langa. Ine ndikanakhala nditaima pakhomo mu mvula, matalala kapena mphepo yamkuntho kuti ndilowe mu Kachisi kuti ndimve mneneri wa Mulungu. Ngati ndikanapita ku mpingo wina uja, ndikanasintha matchalitchi usiku womwewo.
Koma mkazi ameneyo, iye sankadziwa ngati mphamvu inali mu ndodo kapena ayi, koma iye ankadziwa kuti Mulungu anali mwa Eliya. Ndiko kumene Mulungu anali: mwa mneneri Wake. Iye anati, “Monga Ambuye ali wa moyo, ndiye kuti solo yanuso ili moyo, ine sindidzakusiyani inu.”
Ine ndikukuitanani inu kuti mutijowine ife ndi kukhala mmodzi wa mipingo ya M’bale Branham pa nthawi yolumikizirana Lamlungu 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumva Liwu la Mulungu likutibweretsera ife Uthenga: Malo Okhawo Operekedwa Ndi Mulungu Opembedzerapo 65-1128M.
Lero, Mawu awa amene Mulungu analankhula kupyolera mwa Mngelo Wake Wachisanu ndi chiwiri akukwaniritsidwabe kupyolera mwa IFE, MKWATIBWI WA YESU KHRISTU.
Ngati ine sindikhulupirira mu kupita kutchalitchi, nchifukwa chiyani ine ndiri ndi tchalitchi? Ife tinali nawo iwo onse kudutsa m’dzikoli, titalumikizitsana usiku wina, mailosi thuu handiredi aliwonse a mabwalo anali ndi imodzi ya matchalitchi anga.
Ndipo lero, ife tikadali MMODZI WA MIPINGO YAKE. Iye akadali M’BUSA WATHU. Mawu Ake SAMASOWABE KUTANTHAUZIDWA, ndipo ife tikanali osonkhanitsidwa pa dziko lonse, WOl pa MODZI, kumvetsera ku LIWU la Mulungu kumupanga kukhala wa gwiro Mkwatibwi wa Yesu Khristu.
Kapena mwinamwake ena adawuza mipingo yawo, “Tsopano mvetserani, ife timakhulupirira M’bale Branham kuti ndi mneneri wa Mulungu, koma iye sananene kuti ife timayenera kumamvetsera kwa iye mu mipingo yathu. Ine ndikulalikira Lamlungu lino, ndi Lamlungu lirilonse;
Kenako Mkwatibwi , monga Mkwatibwi chabe tsopano, anali ndi Vumbulutso, ndipo ankafuna kumva Liwu la Mulungu mwachinjunji kwa iwo eni. Iwo ankafuna kuti akhale olumikizana ndi Mkwatibwi kuzungulira dziko kuti amve Liwu la Mulungu pamene ilo linali kunveka. Iwo ankafuna kuti azindikiritsidwe ngati umodzi wa mipingo yake, nyumba, kapena kulikonse kumene iwo anali, ndi Uthenga, Liwu, ndipo tsopano matepi.
Lero, Mawu awa akukwaniritsidwabe.
Chifukwa chiyani iwo/ife tinachiwona Icho ndipo ena sanachiwone? Mwa kudziwiratu, ife tinadzozedweratu kuti tiziwone Izi. Koma inu amene simunadzozedwe, simudzaziwona konse Izo. Tirigu akuwawona Iwo ndipo wayamba kuchokapo.
Izi sizikutanthauza kuti muyenera kusiya kupita kutchalitchi chanu. Komanso sizikutanthauza kuti abusa anu asiye kutumikira. Mophweka izi Zikutanthauza kuti mautumiki ambiri ndi azibusa aiwala CHINTHU CHENICHENI, ndiko kusawawuza anthu awo kuti MAWU OFUNIKA KWAMBIRI omwe muyenera kuwamva ndi LIWU la Mulungu pa matepi.
Kupita ku tchalitchi tsiku lililonse sabata iliyonse sikukupanga iwe kukhala Mkwatibwi; chimenecho sichofunikira cha Mulungu. Afarisi ndi Asaduki anali ndi chiphunzitso chimenecho kumusi uko. Iwo ankadziwa chilembo chirichonse cha Mawu aliwonse, koma Mawu Amoyo anali ataima POMWEPO mu thupi la munthu, koma kodi iwo anachita chiyani? Chinthu chomwecho chimene ambiri amachita lerolino.
Iwo amati, “Izo zinali zipembedzo zimene iye anali kuzikamba.” Iwo samamulola M’bale Branham mu mipingo yawo kuti azilalikira, koma ife timalalikira Mawu ndi kunena mobwereza basi zomwe iye ananena.
Izi ndizodabwitsa. Ambuye alemekezeke. Ndi zomwe muyenera kuchita. Koma Kenako mkumati, lero ndi zosiyana, ndi zolakwika kumasewera matepi a M’bale Branham mu tchalitchi chanu. Inu apo simuli osiyana ndi Afarisi ndi Asaduki, kapena zipembedzo.
Ndiwe wa chinyengo.
Monga zinaliri pamenepo, Ndi Yesu, atayima pakhomo akugogoda, kuyesera kuti alowe kuti ayankhule mwachinjunji kwa Mpingo Wake, ndipo iwo sadzatsegula zitseko zawo, ndipo sadzasewera matepi mu mipingo yawo. “Iye sakubwera mu mpingo wathu ndi kudzalalikira”.
Mdaniyo azipotoza izo ndikuzivunguza mbali zochuruka momwe iye AMADANA ndikuyalutsidwa, komabe, zikuwonekera pamaso pathu pomwe ndipo ambiri akuchoka.
“Pa chiyambi panali” [Osonkhana ati, “Mawu”—Mkonzi.] “ndipo Mawu anali ndi” [“Mulungu,”] “Ndipo Mawu anali” [“Mulungu.”] “Ndipo Mawu anapangidwa thupi ndipo anadzakhala pakati pathu.” Ndi kulondola uko? Tsopano ife tikuwaona Mawu olonjezedwa omwewo, a Luka, a Malaki, malonjezo onse awa kuyambira lero, akupangidwa thupi, akukhala pakati pa ife, amene ife tinawamva ndi makutu athu; tsopano ife tikumuwona Iye (ndi maso athu) akutanthauzira Mawu Ake Omwe, ife sitikusowa kutanthauzira kulikonse kwa munthu. O mpingo wa Mulungu Wamoyo! pano ndi pa lamya! dzukani mwamsanga, nthawi isanathe!
Tsegulani mitima yanu ndi kumva zimene Mulungu wanena kwa inu, mipingo yake yonse. Tsopano ife tikumuwona IYE, ndi maso athu, AKUTANTHAWUZILA MAWU AKE OMWE. Sitikufuna kutanthauzira kulikonse kwa munthu!! DZUKANI NTHAWI ISANATHE!!
Tamva za zinthu izi moyo wathu wonse zimene zikanati zidzachitike mu nthawi yotsiriza. Tsopano tikuwona ndi maso athu zikuchitika.
Iye anatiuza ife, pali NJIRA IMODZI YOKHA, IYO NDI NJIRA YOPEREKEDWA YA MULUNGU IYE ANAPANGIRA MKWATIBWI WAKE. MUYENERA KUKHALA NDI LIWU LA MULUNGU PA TEPI.
Ndikuitana dziko kuti libwere kudzalumikizana nafe Lamlungu pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, ndi kumva Njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero. Ndiye inunso mukhoza kunena kuti, “Ndamva za Inu, koma tsopano ndikukuonani inu”.
M’bale. Joseph Branham
Uthenga: 65-1127E Ine Ndakhala Ndikumva Koma Tsopano Ine Ndawona
Malemba
Genesis 17 Eksodo 14:13-16 Yobu chaputala 14 ndi 42:1-5 Amosi 3:7 Marko 11:22-26 ndi 14:3-9 Luka 17:28-30
Aleluya! Maziko a mitima yathu akonzedwa ndi kumva kwa Mawu ndipo Iwo awululira kwa ife, IFE NDIFE Mkwatibwi waukoma wa Khristu; Mwana wa Mulungu wofunika, waukoma, wopanda tchimo, atayima ndi Mawu a Mkwatibwi angwiro, osaipitsidwa, otsukidwa ndi Madzi a Magazi Ake Omwe.
Ife takhala Mawu owonetseredwa opangidwa thupi, kotero kuti Yesu akhoze kutitengera ife, amene Iye anawakonzeratu asanaikidwe maziko a dziko, kupita ku chifuwa cha Atate.
Dziko likhoza kuwona kuwonetsera kwa Chikhulupiriro chathu pa momwe ife tinali kuchitira, ndi kufotokoza kuti ife tiri nalo Vumbulutso loona lochokera kwa Mulungu la Mawu Ake otsimikiziridwa, ndipo ndife opanda mantha. Sitisamala zomwe dziko lonse likunena kapena kukhulupirira… Sewero la atolankhani ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu kwa Mkwatibwi wa Yesu Khristu.
Alipo ambiri amene amati amakhulupirira Uthenga wa nthawi yotsiriza uwu, amakhulupirira kuti Mulungu anatumiza mneneri, amakhulupirira kuti William Marrion Branham anali mtumiki wa mngelo wachisanu ndi chiwiri, amakhulupirira kuti analankhula PAKUTI ATERO AMBUYE, koma SAKUKHULUPIRIRA kuti Liwu ndilo liwu lofunika kwambiri lomwe inu muyenera kulimva. Iwo samakhulupirira kuti iye analankhula Mawu osalephera. Iwo samakhulupirira kusewera matepi mu mipingo yawo.
Zimatanthauza chiyani? ZIKUTANTHAUZA KUTI SIZINAWULULIDWE KWA IWO!
Ndi vumbulutso. Iye waziwulula izo kwa inu mwa chisomo Chake. Si zimene inu munachita. Inu simunadzigwirire nokha ntchito mu chikhulupiriro. Inu mumakhala nacho chikhulupiriro, icho chimaperekedwa kwa inu mwa chisomo cha Mulungu. Ndipo Mulungu amaziwulula izo kwa inu, choncho chikhulupiriro ndi vumbulutso. Ndipo Mpingo wonse wa Mulungu wamangidwa pa vumbulutso.
Mwa CHIKHULUPIRIRO izo zaululidwa kwa ife kuti Uthenga uwu ndi Liwu la Mulungu pa matepi amene ajambulidwa, ndi kusungidwa, kuti azidyetsa ndi kufikitsa ungwiro Mkwatibwi wa Yesu Khristu.
Ndi CHIKHULUPIRIRO chenicheni, chosaipitsidwa mu zomwe Mulungu ananena kuti ndi Choonadi. Ndipo Izo zazikika mu mtima mwathu ndi solo ndipo palibe kanthu koti zisunthe Izo. Icho chikhala pomwepo mpaka mneneri Wake atidziwitse ife kwa Ambuye wathu.
Sitingathe kudzithandiza tokha. Iye anatikonzekeretsa ife kuti tilandire ndi kukhulupirira Izo asanaikidwe maziko a dziko. Iye ankadziwa kuti ife tikanalandira Liwu Lake mu m’badwo uno. Iye anatidziwiratu ndipo anatikonzeratu kuti tilandire.
Ndiye, ntchito zomwe Mzimu Woyera ukuchita lero, mwa masomphenya awa osalephera konse, malonjezo osalephera konse, zizindikiro zonse zautumwi zolonjezedwa mu Baibulo, za Malaki 4, ndi, o, Chivumbulutso 10:7, zonse za izo zikukwaniritsidwa; ndi kutsimikiziridwa mwasayansi, njira ina iliyonseyo. Ndipo ngati ine sindinakuwuzeni inu Choonadi, zinthu izi sizikanati zichitike. Koma ngati ine ndakuwuzani inu Choonadi, izo zimachitira umboni kuti ine ndakuwuzani inu Choonadi. Iye akadali yemweyo, dzulo, lero, ndi kwanthawizonse, ndipo mawonetseredwe a Mzimu Wake akumutengera Mkwatibwi kutali. Lolani chikhulupiriro chimenecho, vumbulutso ligwere mu mtima mwanu, kuti, “Ili ndilo oralo.”
Ili ndilo oralo. Uwu ndi Uthenga. Ili ndi Liwu la Mulungu loyitana Mkwatibwi wa Yesu Khristu. O Mpingo, mulole Ambuye akonzere malo ogona a mtima wanu kuti mukhale nacho Chikhulupiriro ndi kuwulula kwa inu kuti kumva Liwu ili, pa matepi, ndi kumene kudzakhala kungwiro ndi kumugwirizanitsa Mkwatibwi wa Yesu Khristu.
Ine kamodzinso ndikukuitanani inu kuti mubwere kudzatijowina ife Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, kuti mudzatengere CHIKHULUPIRIRO Chanu ku malo apamwamba, ndi kukhala limodzi nafe mu malo akumwamba pamene ife tikumva Liwu la Mulungu likutipanga ife kukonzekera kudza Kwake kwaposachedwapa.
M’bale. Joseph Branham
Chonde khalani mu pemphero kwa ife sabata yamawa pamene tikuyamba kampu yathu yoyamba ya Still Waters.
Uthenga: Ntchito Ndi Chikhulupiriro Chofotokozedwa 65-1126
Palibe njira yozungulira izo, inu ndinu Jini Lauzimu la Mulungu, chiwonetsero cha zikhumbo za maganizo Ake, ndipo munali mwa Iye asanaikidwe maziko a dziko.
Ife sitingapitirirenso, ndife ofanana ndendende ndi njere yomwe idapita munthaka. Ndife Yesu yemweyo, mu mawonekedwe a Mkwatibwi, ndi mphamvu yomweyo, Mpingo womwewo, Mawu omwewo amoyo ndi akukhala mwa ife kupanga mutu, KUKONZEKERA MKWATULO.
Anatiuza ife kuti talekanitsidwa ku mgwirizano wathu woyamba, ndi imfa yauzimu, ndipo tsopano tabadwanso, kapena takwatiwanso, ku mgwirizano wathu watsopano wauzimu. Osatinso moyo wathu wakale wachithupi ndi zinthu za mdziko, koma wa Moyo Wamuyaya. Nyongolosi yomwe inali mwa ife pachiyambi, yatipeza ife!
Zimatanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti bukhu lathu lakale lapita ndi mgwirizano wathu wakale, lasamutsidwa. TSOPANO ili mu “Bukhu Latsopano” la Mulungu; osati bukhu la moyo… ayi, ayi, ayi… koma mu Bukhu la Moyo wa Mwanawankhosa. Chimene Mwanawankhosa anachiombola. Ndi chiphaso chathu chaukwati chimene nyongilodzi yathu yaoyo osatha imagwirizirako.
Mwakonzeka? Apa izo zikubwera. Inu kulibwino mudzitsine nokha ndi kukonzekera kukuwa ndi kufuula ulemerero, aleluya, mulemekezeke Ambuye, ndi migolo iwiri ndi katundu wakumwamba.
“Kodi mukutanthauza kundiuza ine kuti buku langa lakale ndi zolakwa zanga zonse, zolephera zanga zonse …”
Mulungu anachiyika icho mu Nyanja ya Kuyiwala Kwake, ndipo inu simunakhululukidwe kokha, koma inu mwalungamitsidwa…Ulemerero! “Kulungamitsidwa.”
Ndipo izi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti inu simunachite m’komwe ngakhale pa maso pa Mulungu. Iwe umayima mwangwiro pamaso pa Mulungu. ULEMERERO! Yesu, Mawu, anatenga malo anu. Iye anakhala inu, kuti inu, wochimwa wonyansa, mukhoze kukhala Iye, MAWU. Ife ndife MAWU.
Izo zimatipanga ife nyongolodzi Yake yaing’ono yomwe inakonzedweratu kuchokera pachiyambi. Ndife Mawu akubwera pa Mawu, pa Mawu, pa Mawu, pa Mawu, ndipo ife tikubwera mu thunthu lokwanila la Khristu kotero kuti Iye akhoze kubwera kudzatitenga ife kuti tikhale Mkwatibwi Wake.
Kodi chikuchitika ndi chiyani TSOPANO?
Ndi Chilumikizano Chosaoneka Cha Mkwatibwi Wa Khristu kusonkhana mozungulira Mawu, kuchokera kuzungulira dziko.
Ponena izi tsopano, izi zikupita mu fuko lonseli. Mu New York, tsopano ili twente-faifi minitsi pasiti leveni. Kutali uko mu Philadelphia ndi kuzungulira kumeneko, oyera okondedwa awo akhala ali uko akumvetsera, pakali pano, mu mipingo konse kozungulira. Kutali uko, kutali komwe kuzungulira Mexico, kutali uko mu Canada ndi konse kozungulira, kudutsa. Mailosi thuu handiredi, kulikonse mkati mwa dera la North America kuno, pafupifupi, anthu ali kumeneko, akumvetsera pakali pano. Zikwi kuchulukitsa ka zikwi, akumvetsera.
Ndiwo Uthenga wanga kwa inu, Mpingo, inu omwe muli mchilumikizano, chilumikizano chauzimu mwa Mawu,
Iye anati Icho chinali chilumikizano chauzimu cha Khristu ndi Mpingo Wake, ndipo Izo ZIKUCHITIKA PALI PANO. Thupi likukhala Mawu, ndipo Mawu akukhala thupi. Ife tawonetseredwa, ndi kutsimikiziridwa; zomwe Baibulo linanena kuti zidzachitika mu tsiku lino, ndipo Izo zikuchitika tsopano, tsiku ndi tsiku mwa aliyense wa ife.
Mulungu adzakhala ndi Mpingo waukoma. Mkwatibwi Wake woona, wokhulupirika wa Mawu. NDIFE AMAYI WOSANKHIDWA wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Ndi Nthawi Yanji Yino, Bwana?
Ife tiri nalo vumbulutso mu masiku otsiriza ano, la Uthenga wa Ambuye Mulungu kuti usonkhanitse Mkwatibwi Wake palimodzi. Palibe m’badwo wina umene iwo unalonjezedwapo. Izo zinalonjezedwa mu m’badwo uno: Malaki 4, Luka 17:30, Yohane Woyera 14:12, Yoweli 2:38. Malonjezo amenewo ali chimodzimodzi basi monga Yohane M’batizi anadzizindikiritsa yekha mu Lemba.
Ndani anakwaniritsa malemba amenewa?
Mngelo wake wamphamvu wachisanu ndi chiwiri, William Marrion Branham. Iye nthawizonse ankazichita izo mwa dongosolo. Iye ankazichita izo nthawi iliyonse mwa dongosolo. Iye akuchita izo kachiwiri mu tsiku lathu, kuitana ndi kusonkhanitsa Mkwatibwi Wake waukoma mu tsiku lotsiriza mwa mneneri Wake.
Bwerani mudzajowinane nafe pamene tikumva Mawu olonjezedwa a tsiku lathu akuyankhula, ndi kutiuza ife chomwe ife tiri ndi zomwe zikuchitika mu tsiku lathu. Chilumikizano Chosaoneka Cha Mkwatibwi Wa Khristu 65-1125.
Ndipo tsopano Mulungu nthawizonse wakhala akutumiza anamulondola Ake, Iye nthawizonse sanayambe wakhalapo wopanda namulondola, nthawizonse kudutsa mmibadwo. Mulungu nthawizonse amakhala naye wina amene amamuimirira Iye pa dziko lapansi ili, mu mibadwo yonse.
Mulungu safuna kuti tizidalira kumvetsa kwathu kapena maganizo opangidwa ndi anthu. Ndi chifukwa chake amatumiza Mkwatibwi Wake Mtsogoleri; pakuti ali ndi kunvetsa, pomuka ndi choti achite. Mulungu SANAYAMBE WASINTHAPO dongosolo Lake. Iye sanalepherepo kutumiza Namulondola kwa anthu Ake, koma inu muyenera kumuvomereza Namulondola ameneyo.
Inu muyenera kukhulupirira Mawu aliwonse amene Iye amanena kupyolera mwa Namulondola Wake. Iwe uyenera kupita momwe Namulondola Wake akuti uzipita. Ngati muyamba kumvetsera ndi kukhulupirira mawu ena monga kalozera wanu,inu mudzangotayika.
Yohane Woyera 16 akuti Iye anali ndi zinthu zambiri zoti atiuze ife ndi kutiululira kwa ife, potero Iye amatumiza Mzimu Wake Woyera kuti Utitsogolere ndi kutiuza ife. Iye anati Mzimu Woyera ndiye mneneri wotsogolera wa m’badwo uliwonse. Choncho, aneneri ake anatumidwa kuimira Mzimu Woyera kuti atsogolere Mkwatibwi Wake.
Si munthuyo, koma Mzimu Woyera MWA munthu ameneyo. Munthu amene anamusankha kuti adziyimire yekha ndi kukhala mtsogoleri wathu wapadziko lapansi amene amatsogoleredwa ndi Mtsogoleri wathu wa Kumwamba. Mawu amatiuza ife kuti tiyenera kumutsatira Namulondola ameneyo. Ziribe kanthu zomwe timaganiza, zomwe zikuwoneka ngati zomveka, kapena zomwe munthu wina anganene, sitiyenera kugawa izi, wotsogolera ndi mmodzi yekha.
Mulungu amatumiza Namulondola, ndipo Mulungu amafuna kuti inu muzikumbukira kuti ameneyo ndi Namulondola Wake woikidwapo.
Mtsogoleri wathu mneneri wasankhidwa ndi Mulungu kuti alankhule Mawu Ake. Mawu ake NDI MAWU A MULUNGU. Mtsogoleri wa mneneri, ndipo iye yekha, ali nako kutanthauzira Kwauzimu kwa Mawu. Mulungu analankhula Mawu Ake kwa iye mulomo kwa khutu. Chifukwa chake, simungathe kutsutsa, kusintha, kapena kulingalira Mawu a Mtsogoleri wanu.
Inu muyenera kumutsatira Iye, ndipo Iye yekha. Ngati simutero, mudzatayika. Kumbukirani, pamene musiya Iye, Wotsogolera wosankhidwa ndi Mulungu, mumakhala nokha, kotero ife tikufuna kukhala pafupi ndi namulondola yemwe Iye anamusankha, ndi kumva ndi kumvera Mawu aliwonse amene Iye amanena kupyolera mwa iye.
Pamene Aisrayeli anachoka ku Igupto kupita ku dziko lolonjezedwa, pa Eksodo 13:21 , Mulungu anadziŵa kuti iwo anali asanayendepo mwanjira imeneyo. Anali ma mailosi makumi anayi okha, komabe iwo ankasowa chinachake choti apite nawo. Iwo anataya njira yawo. Kotero Iye, Mulungu, anawatumizira iwo Mtsogoleri. Eksodo 13:21, chinachake chonga chonchi, “Ine ndikutumiza Mngelo Wanga patsogolo panu, Lawi la Moto, kuti likusungeni inu panjira,” kuti likawalondolere iwo ku dziko lolonjezedwa ili. Ndipo ana a Israeli ankatsatira Namulondola uja, Lawi la Moto (usiku), Mtambo usana. Pamene Iwo anaima, iwo anaima. Pamene Iwo adayenda, adayenda. Ndipo pamene Iye anawafikitsa iwo kufupi ndi dziko, ndipo iwo sanali oyenera kuti awoloke, Iye anawatsogolera iwo kubwerera ku chipululu kachiwiri.
Iye anati umenewo ndi mpingo lero. Ife tikanapita kale tikadangodzikonza tokha ndi kukhala mu dongosolo, koma Iye anachita kutitsogolera ife kuzungulira ndi kuzungulira ndi kuzungulira.
Iwo anali oti angotsatira wotsogolera wawo pamene IYE AMATSATIRA ndi kumva kuchokera ku Lawi la Moto. Iye anawauza iwo zimene Mulungu ananena ndipo iwo anayenera kumvera Mawu aliwonse amene iye ananena. Iye anali Liwu la Namulondola. Koma anafunsa ndi kukangana ndi wotsogolera woikidwa ndi Mulungu, motero anayendayenda m’chipululu kwa zaka makumi anayi.
Pamene Mulungu anamuchotsa Mose pamalopo, Yoswa anadzozedwa kuti azitsogolera anthu, zomwe zikuimira Mzimu Woyera lero. Yoswa sanalalikire china chatsopano, komanso sanayese kutenga malo a Mose, komanso sanayese kutanthauzira zomwe wotsogolera ananena; iye anangowerenga zimene Mose ananena ndi kuwauza anthu, “Khalani ndi Mawu. Anangowerenga zimene Mose ananena.
Ndi mtundu wangwiro bwanji wa lero. Mulungu anamutsimikizira Mose ndi Lawi la Moto. Mneneri wathu anatsimikiziridwa ndi Lawi la Moto lomwelo. Mawu amene Mose analankhula anali Mawu a Mulungu ndipo anaikidwa mu Likasa.
Pamene Mose anachotsedwapo, Yoswa anadzozedwa kutsogolera anthu mwa kusunga Mawu amene Mose analankhula pamaso pawo. Iye anawauza iwo kuti akhulupirire ndi kukhala ndi Mawu aliwonse amene kalozera wa Mulungu analankhula.
Yoswa nthaŵi zonse ankaŵerenga zimene Mose analemba Mawu ndi Mawu m’mipukutu. Iye anayika Mawu pamaso pawo nthawizonse. Mawu a tsiku lathu sanalembedwe, koma Iwo anajambulidwa kotero kuti Mzimu Woyera ukhoze kukhala ndi Mkwatibwi Wake kumva Mawu pa Mawu chimene Iye analankhula, mwa Kukanikiza kusewera.
Mulungu sasintha dongosolo Lake. Iye ndi Namulondola wathu. Liwu Lake ndi lomwe likutsogolera ndi kugwirizanitsa Mkwatibwi Wake lero. Ife timangofuna kumva Liwu la Namulondola wathu pamene Ilo limatitsogolera ife ndi Lawi la Moto. Ndi chilumikizano chosaoneka ndi maso cha Mkwatibwi wa Khristu. Ife timalidziwa Liwu Lake.
Pamene namulondola wathu abwera pa guwa, Mzimu Woyera umamukhudza iye ndipo Iwo sulinso iye, koma Namulondola wathu. Iye akukweza mutu wake m’mwamba ndi kufuula, “Atero Ambuye, Atero Ambuye, Atero Ambuye! Ndipo membala aliyense wa Mkwatibwi wa Khristu kuzungulira dziko amabwera kumene kwa iye. Chifukwa chiyani? IFE TIMAMUDZIWA MTSOGOLERI WATHU MMENE IYE AMAYANKHULIRA.
Mtsogoleri Wathu = Mawu Mawu = Amadza kwa mneneri Mneneri = Mulungu womasulira yekha waumulungu; Mtsogoleri wake wapadziko lapansi.
58 Muzikhala kumbuyo kwa Mawu! O, inde, bwana! Muzikhala ndi Namulondola ameneyo. Muzikhala kumbuyo komwe kwa Iye. Musamapite kutsogolo kwa Iye, inu muzikhala kumbuyo kwa Iye. Muzimulola Iye kuti azikutsogolerani inu, osati inu muzimutsogolera Iye. Inu muzimulola Iye kuti azipita.
Ngati inu simukufuna kuti mutayike, bwerani mudzamvetsere kwa Namulondola wathu pamene Iye akuyankhula kupyolera mu kalozera Wake woikidwa pa dziko Lamlungu lino pa 12:00 p.M., nthawi ya ku Jeffersonville.
Liwu limene tikulimva pa matepi ndi Urimu Tumimu wa Mulungu kwa Mkwatibwi Wake. Iwo tsopano wamulumikiza moyenera Mkwatibwi Wake palimodzi mu mtima umodzi ndi mtima umodzi kuti ukhale mpingo weniweni wodzazidwa-Mzimu, wodzaza ndi mphamvu ya Mulungu, utakhala palimodzi mu malo Ammwambamwamba, ukupereka nsembe zauzimu, matamando a Mulungu, ndi Mzimu Woyera ukuyenda pakati pathu.
Khristu anatitumizira ife Mzimu Wake Woyera kuti ulankhule kupyolera mwa mngelo wake wachisanu ndi chiwiri kutimanga ife aliyense payekha mu msinkhu wa Yesu Khristu, kuti ife tikhale nyumba ya mphamvu ndi malo okhalamo Mzimu Woyera, mwa Mawu Ake.
Ndife olandira a chirichonse. Ndi katundu wathu, NDI WA ife. Ndi mphatso ya Mulungu kwa ife, ndipo palibe amene angatilande iyo. NDI ZATHU.
“Chimene mudzapempha Atate mu Dzina Langa, Ine ndidzachichita.” Ndani angakane kalikonse pamenepo? “Indetu, indetu, Ine ndinena kwa inu, ngati inu munena kwa phiri ili, ‘Sumuka,’ musati mukaikire mu mtima mwanu koma khulupirirani kuti chimene inu mwanena chidzachitika, inu mukhoza kukhala nacho chirichonse chimene inu mwachilankhula.” Ndi malonjezo otani! Osati kokha ku machiritso, koma chirichonse.
Ulemerero kwa Mulungu… CHILICHONSE CHOMWE IFE TIMAPEMPHA!
Kuyambira pachiyambi, chilengedwe chonse cha Mulungu chikubuwula ndi kuyembekezera tsiku limene ana athunthu a Mulungu adzaonekera. Tsiku limenelo lafika. Lero ndi tsiku limenelo. Iyi ndi nthawi imeneyo. Ndife ana aamuna ndi aakazi owonetseredwa a Mulungu.
Ndife chida chamoyo cha Mulungu chimene Iye akuyendamo, Iye akuwona mkati, Iye akulankhula, Iye akugwira ntchitomo. Ndi Mulungu akuyenda ndi mapazi awiri MWA IFE.
Ndife makalata ake olembedwa owerengedwa ndi anthu onse. Osankhidwa Ake, okonzedweratu, ana aamuna ndi aakazi otengedwa amene Iye akuwapanga kukhala munthu wamoyo, chifaniziro chamoyo, msinkhu wa munthu wangwiro.
koma kudzigwetsera tokha pamaso pa Mulungu Wamoyo, ukoma wamoyo, chidziwitso chamoyo, chipiriro chamoyo, umulungu wamoyo, mphamvu yamoyo, kubwera ndi Mulungu Wamoyo kumapangitsa munthu wamoyo fano lamoyo—thunthu la Mulungu!
Ndi Khristu, mu umunthu wa Mzimu Woyera pa ife, ndi ubatizo woona wa Mzimu Wake Woyera, ndi ukoma Wake wonse wosindikizidwa mwa ife. Mulungu, akukhala mwa ife mu Kachisi wotchedwa Nyumba. Kachisi wamoyo, wa mokhalamo Mulungu wamoyo; Mpingo wangwiro, kuti Mwalawapamutu Wangwiro utiphimbe ife.
Mulungu anatumiza mneneri kuti adzayitane ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake. Anali Adamu Wake woyamba wobwezeretsedwa kwathunthu, msinkhu wa munthu wangwiro mu tsiku lathu, kuti awulule Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake.
Ndidikirira, dikirani, dikirani, dikirani. Musapange kusiyana kulikonse. Iwo amakhala pomwepo. Ndiyeno, tsiku lina, ndidzafuula pamodzi ndi oyera mtima ena onse mogwirizana kuti: “Ife tikupumula ndi chitsimikizo pa Mawu aliwonse! Pa mtengo wa Kalvari.”
Ine ndikulonjeza mmawa uno kwa Iye ndi mtima wanga wonse kuti mwa chithandizo Chake ndipo mwa chisomo Chake, ine ndikupemphera kuti ndifunafuna tsiku ndi tsiku mosalekeza mpaka nditamverera chirichonse cha zofunikira zonsezi zikuyenderera mu kanthunthu kokalamba kangaka. Mpaka nditakhala kuwonekera kwa Khristu Wamoyo,
KWA INE, kumvetsera Mawu a Mulungu pa matepi ndi dongosolo la Mulungu la lero. Ndi Mawu amoyo a Yesu Khristu. Iwo ndiwo Mtheradi wanga molingana ndi Mawu a Mulungu. Ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero.
Chotero, ine ndikufuna kukuitanani inu kuti mudzabwere kulumikizana nane Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ine ndidzamvetsera kwa William Marrion Branham, amene ine ndikukhulupirira kuti ndi Liwu la Mulungu la masiku athu ano, kuphunzitsa Mkwatibwi wa Khristu momwe angakhalire: Thunthu La Munthu Wangwiro 62-1014M.
Mwa Kukanikiza Kusewera, tikumvera Mawu osalephera a Mulungu. Ndi Mawu aliwonse Choonadi, mawu aliwonse a Iwo. Ife tayitanidwa ndi kusungidwa, kudzazidwa ndi kuikidwa pambali; odzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo tsopano ali kale mu Dziko la Kanani. Sitikuwopa kalikonse … PALIBE, timadziwa kuti ndife ndani.
Chifukwa takhala ndi Mawu Ake, monga anatilamulira, adzatiuza kuti anatisiyira cholowa. Ndi liti pamene Inu munachita izo, Atate? Pamene Ine ndinakusankhani inu ndi kuika maina anu pa Bukhu la Moyo wa Mwanawankhosa asanaikidwe maziko a dziko.
Pamene chidzalo cha nthawi chinadza, Ine ndinatumiza Yesu Mwanawankhosa, Yemwe anaphedwa kuchokera ku maziko a dziko, kuti inu mukhoze kulandira cholowa chanu kuti mukhale ana Anga aamuna ndi aakazi, milungu ing’onoing’ono.
Ndidayenera kukuyang’anirani inu kuti muone ngati mukunjenjemera ndi malo omasuka ndisanakukhazikitseni.
“Kodi inu mukukhulupirira kuti kusewera Liwu Langa pa matepi mu mpingo ndi kulakwa?”
“Inde, usamasewere matepi kutchalitchi.”
“Zitsutseni izo.
“Kodi inu mukukhulupirira Mawu Anga pa matepi akusowa kutanthauzira?”
Kufikira pamenepo, musaiwale konse, Ine ndikupatsani inu Mawu Anga, iwe NDIWE MAWU ANGA opangidwa thupi. Ngati inu mufuna CHINTHU CHILICHONSE, yankhulani Icho, ndiye mukhulupirireni Icho; Ndi cholowa chanu.
Ine ndikutumiza Liwu Langa kwa inu kachiwiri Lamlungu lino ndi kufotokoza Izo zonse kwa inu. Ndikuwuzaninso kuti ndinu ndani, komwe mukupita, ndi momwe zilili kumeneko, pakali pano.
Bwerani mudzajowine Mkwatibwi Wanga pamene Ine ndikuwapangitsa iwo kukhala limodzi mu malo ammwambamwamba Lamlungu lino pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, ndipo mudzandimvere Ine mwakukukhazikani inu pa malo mwa Mawu Anga. 60-0522E Kukhazikitsidwa Gawo Lachinayi
Pamene Ife Tikamasindikiza kusewera, ndi uchi mu m’thanthwe, ndi chimwemwe chosaneneka, ndi chitsimikizo chodala, ndi nangula wa moyo wathu, ndiye chiyembekezo chathu ndi Pokhala, ndi Thanthwe la Mibadwo, ndi chilichonse chomwe chili chabwino, ndi Njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero.
Chifukwa chakuti ife timakanikiza Kusewera, Liwu la Mulungu linatikwatiwitsa Ife; linatitomeretsa ife kwa Khristu, monga Namwali Woyera ku Mawu Ake. Ife tiri naye Mphunzitsi Mmodzi, Liwu limodzi, mneneri Mmodzi, amene akutitsogolera ife mwa Mzimu Woyera.
Koma ichi ndi tchalitchi, ine ndikukuphunzitsani inu. Izi zikupita pa matepi. Ine ndikufuna anthu omwe amamvetsera matepi, kumbukirani, izi ndi za mpingo wanga.
Ndi chitsimikiziro chotani kwa ife kuti ife tiri mu Chifuniro Chake changwiro. Matepiwo ndi a mpingo wake. Iye akutiphunzitsa Ife. Iye akutiuza ife, mvetserani kwa matepi
Iye Anayamba magawo a mauthenga a za kukhazikitsidwa awa potiuza ife zomwe zidachitika masiku angapo m’mbuyomo. Ndiye, pa Uthenga uliwonse, iye amalankhula za pamene iye anali atasinthidwa. Ziyenera kukhala zofunikira bwanji kuti Mkwatibwi amve zomwe zinachitika ndi zomwe Mkwatibwi ananena kwa iye.
Mneneri wathu adzaweruzidwa ndi Mawu amene iye anawalalikira ndi kuwasiya pa matepi. Mkwatibwi ku tsidya linayo anamuuza iye kuti adzalandiridwa ndi Ambuye wathu. Kenako adzatipereka kwa Iye ngati zikho za utumiki wake, kenako tidzabwerera kudziko lapansi kuti tikakhale ndi moyo kosatha.
Mawu aliwonse omwe timawamva ndi chidutswa. Ife timangopitiriza kuwapukuta Iwo ndi kuwapukuta Iwo pamene Iye akuwulula mochuluka pamene ife tikuwerenga pakati pa mizere.
Momwe ife timakonda kugawana Izo ndi abale athu ndi alongo, “Kodi inu munamva izi?”
“Iye anatisankha ife mwa Iye pasanakhale nkomwe dziko lapansi”? Ndicho cholowa chathu. Mulungu anatisankha ife, ndipo anamulola Yesu kuti abwere ndi kudzalipira mtengo. Motani zimenezo? Kukhetsa Kwake kwa Magazi Ake, kuti pasadzakhale tchimo limene liti lidzawerengedwe kwa ife. Palibe chomwe inu mumachita.
“Woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye.” Inu maso anu akuyang’ana ku Kalvare, ndipo palibe chirichonse chomwe chikuimitseni inu! Kuyenda kumene kwa moyo wanu, inu mukuyenda mu Msewu waukulu wa Mfumu, mutadzozedwa ndi Mafuta wodula, mukukalowa mu malo Oyeretsetsa. Psyi! Ameni.
Tinali ngati ndodo ya Aroni, ndodo yakale youma imene ananyamula kwa zaka 40 m’chipululu. Koma tsopano, chifukwa ife takhala mu Malo Opatulika amenewo pakumva Liwu la Mulungu likuyankhula kwa ife pa matepi, ife taphuka ndipo tachita maluwa, odzaza ndi Mzimu Wake Woyera, ndipo ndife Mkwatibwi Wake akufuula pamwamba pa mapapo athu:
• Woyera, woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, matepi ali oyamba mu mitima yathu.
• Woyera, woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, Iye anatisankha ife asanaikidwe maziko a dziko.
• Woyera, woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, ife ndife mkwatibwi wa Yesu Khristu.
• Woyera, woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, osapanga kusiyanitsa kulikonse ndi zomwe aliyense anena, sitikuloweza zapa matepi, ife tikuwasewera mochuruka.
• Woyera, woyera, woyera, kwa Ambuye, maso athu ayang’ana ku Kalvare, ndipo palibe chimene chikutiletse ife.
Ine ndiri wokondwa kwambiri podzalumikizana mitima ndi ambiri pano amene amadziwa kuti Awa ndi Mawu osalephera a Mulungu. Ndiye Iwo, Iwo ndi Mawu aliwonse Choonadi, Mawu aliwonse a Iwo, gawo lirilonse la Iwo. Ndipo ndi chisomo cha Mulungu, ndakhala nawo mwayi wokaliwona Dzikolo kumene tsiku lina ife tidzapitako.
Bwerani mudzajowine nafe Lamlungu pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene mneneri akutenga Mawu aliwonse ndi kumangowapukuta Iwo. Iye adzachitengera Icho mpaka ku Genesis ndi kuchipukuta Icho, kuchitengera Icho mpaka ku Eksodo ndi kuchipukuta Icho kachiwiri, ndipo ngakhale mpaka ku Chivumbulutso; ndipo Ndi gawo lililonse la Yesu!