23-0129 Mulungu Wa M’badwo Woipa Uno

Uthenga: 65-0801M Mulungu Wa M’badwo Woipa Uno

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Namwali wamung’ono wa Khristu, Mawu, Nkhosa,

Sitingakhale chinanso. Sitingamve china chilichonse. Sitikudziwa china chilichonse. Sitikufuna china chilichonse. Kumene kuli Nyama yatsopano, KUTYAKA KULIZA, amene ali Mawu a nyengo, kumeneko mphungu zidzasonkhana. Mawu obwera kumoyo mwa ife.

Sitili ndi wina aliyense! Inu ndinu anthu opatulidwa, oyera kwa Ambuye, odzipereka kwa Mawu ndi Mzimu wa Mulungu, kuti mubale chipatso cha lonjezo Lake la tsiku lino. Timakula nthawi zonse ndi kukhwima pomva Mau a Mulungu.

Mneneri anatiuza ife kuti tiloze mmbuyo ku matepi awa. Ngati muli ndi makina a tepi, sonkhanitsani gulu la anthu ndi kutyaka iyo, ndipo mvetserani mwatchifupi. Mvetserani ku Liwu Lake, zomwe Iye akutiuza ife. Mawu a Mulungu safuna kutanthauzira; Iye amachita kutanthauzira Kwake Kwake. “Ine ndine Liwu la Mulungu kwa inu.”

Ndipo ili ndi Ilo, Baibulo, palibe mawu amodzi oti awonjezedwe kwa Ilo kapena kuchotsedwa kwa Ilo. Ingokhalani kumene ndi Liwu limenelo. “Mlendo sangamutsatire,”

Kodi zingatheke bwanji kuti munthu asaone Njira yoperekedwa ndi Mulungu masiku ano? Koma ulemerero kwa Mulungu, ife tikhoza kuchiwona Icho, chifukwa ndife osankhidwa kuti tiziwone Izo. Ife sitinga, ndipo ife sitingakhoze kunyengedwa, chifukwa ife ndife Mawu Ake owonetseredwa.

Abale ndi alongo, lakani izi zilowetsedwa mphindi imodzi chabe, NDIFE MAWU AKUONETSEDWA!! Mulungu Mwiniwake, akuyankhula kupitira mu milomo ya munthu, akutiuza ife IFE NDIFE MAWU. Sitiyenera kuopa chilichonse. Zonse zomwe tikufuna ndi zathu.

Mlungu uliwonse timayembekezera kuti Yehova adzatichezera. Ife tiribe malo pano oti tikhazikike aliyense, ngakhalenso aliyense sangakhoze kubwera ku Jeffersonville, kodi ife timaba tumizira iwo Mawu kupitira mu njira ya intaneti.

Ife tiri mumanyumba zathu, mu mipingo yathu, m’magalimoto athu, tasonkhana mozungulira maikolofoni athu ku chokera dziko lonse, kuyembekezera Kubwela kwa Ambuye.

Iwo asonkhana pamodzi nafe ku Africa, kuyembekezera Kubwela kwa Ambuye. Iwo asonkhana pamodzi nafe ku Mexico, kuyembekezera Kubwela kwa Ambuye. Ku Ulaya, Scandinavia, Australia, Middle East, South America, kuchokera konse mu dziko lapansi, kuyembekezera Kubwela kwa Ambuye.

Ndipo ife tasonkhana kuno ku mpingo wakwathu, Kachisi, tikuyembekezera Kubwela kwa Ambuye. Ife tiri maningi ochuluka mu nthawi, koma ife tiri pamodzi monga chigawo chimodzi, okhulupirira, kumvetsera ku Liwu la Mulungu, kuyembekezera Kubwea kwa Mesiya.

Ndife anthu oyitanidwa ndi osankhidwa a Mulungu kuchokera mu m’badwo woyipa uno chifukwa cha Dzina Lake. Ife tikuyesedwa ndi kutsimikiziridwa kwa Satana kuti ndife Mawu. Ndife gawo la Mtengo wa Mkwati Wapachiyambi uwo. Ife tikuwona moyo wathu ukuwonetseredwa ndi Mawu amenewo.

Ndishosavuta kuti aliyense akhulupirire kuti Yesu anali yankho lachindunji ku ulosi uliwonse womwe uyenera kukwaniritsidwa mwa Iye, chifukwa akuyang’ana mmbuyo kuti awone zikuchitika. Koma mu m’badwo woipa wamakono uno, iwo akuchita chinthu chomwecho chimene iwo ankachichita apo, pochitanthauzira Icho mwanjira ina, ndipo awapangitsa anthu kupita mu zosokeretsa zamphamvu kuti akhulupirire bodza. Ngati iwo akanakhoza kokha kuzindikira Iwo ali Mawu omwewo a m’badwo uno akuwonetseredwa.

Pali chinthu chimodzi chokha chimene chingakhoze kubweretsa Mkwati pamodzi, Uthenga uwu. Pali chinthu chimodzi chokha chimene ife tonse tingagwirizane nacho, Uthenga uwu. Pali Liwu limodzi lokha limene latsimikiziridwa kuti liri KULANKULA AMBUYE, Liwu la Mulungu pa tepi.

Tsopano, mipingo yozizira basi, yofunda, yokhuthala, ndi zina zotero, za fioloje zopangidwa ndi anthu, zomwe sizikana; Osankhidwa sakanapereka tcheru kwa izo. Koma zili pamwamba apo pafupifupi ngati zenizeni. Kungosiya Mawu amodzi ndi zonse zomwe muyenera kuchita. Lonjezedwa za m’badwo; nthawi yabwino kwambiri! Akhristu, kulikonse, samalani ku nthawi limene tikukhalamo! Lembani pansi, ndi kuwerenga, ndi kumvetsera pafupi.

Mulungu wa m’badwo woipa uwu akuchita zonse zomwe angathe kuti anyenge anthu powasunga Mawu Ake otsimikiziridwa kwa iwo. Iye akuyesera kuti awapangitse iwo kusakhulupirira Mawu amodzi okha, monga iye anachitira kwa Eva pachiyambi.

Koma Mkwati wa Mawu wa Khristu akubwera ku Mutu. Timabwereranso kwa Mnzathu komwe tinayambira. Nthawi yotuluka yayandikira. Mulungu Abwela ku Mkwati Wake yemwe amakhala ndi Mawu Ake.

Mzimu Woyera uli pano ukuitana Mkwati wa Khristu. Iye akuchita izo mwa kutsimikizira Mawu Ake a lonjezo kwa Iye, a m’badwo uno, kusonyeza kuti Iwo ndi Khristu.

Palibe chachikulu kuchila kukhala olumikizana ndi Mkwati kuzungulira dziko, kumvetsera ku Liwu la Mulungu likuyankhula molunjika kwa inu. Palibe chifukwa choyembekezera, kudabwa kapena kupemphera zomwe mukumva ndi zoona. Pakuti Iwo ali OWLIKIRIKA YEKHA, KULANKULA MAWU YA AMBUYE.

Bwerani mudzatimvetsere:

Ndipo zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika Kumwamba, wakukhala nao mphamvu yaikuru; ndipo dziko lapansi linawalitsidwa ndi ulemerero wake.

Pa 12:00 P.M., nthawi ya Jeffersonville, monga ife tikumva: MULUNGU WANTHAWI YOIPA INO 65-0801M.

Bro. Joseph Branham

Malemba yo werenge pamene mukalibe kuvelera Uthenga:

Mateyu 24 mutu 27:15-23
Luka 17:30 St
Yohane 1:1/14:12
Machitidwe 10:47-48
1 Akorinto 4:1-5; chaputala 14
2 Akorinto 4:1-6
Agalatiya 1:1-4
Aefeso 2:1-2/4:30
2 Atesalonika 2:2-4 / 2:11
Ahebri mutu 7
1 Yohane chaputala 1 / 3:10 / 4:4-5
Chibvumbulutso 3:14/13:4/Mitu 6-8 ndi 11-12/18:1-5
Miyambo 3:5
Yesaya 14:12-14