26-0524 Ndi Chiani Chokopa Pa Phiri?

Uthenga: 65-0725E Ndi Chiani Chokopa Pa Phiri?

PDF

BranhamTabernacle.org

Zokondedwa Mphungu Zosonkhana,

Kodi chokopa chachikulu ichi chomwe chikuchitika padziko lonse lapansi ndi chiyani? Anthu ochokera padziko lonse lapansi akusonkhana nthawi ya 12:00 PM nthawi ya ku Jeffersonville, atakhala m’nyumba zawo ndi m’matchalitchi awo ndi chiyembekezo chachikulu, akuyembekezera kumva Liwu la Mulungu likulankhula nawo.

Ndi zachilendo komanso zopanda nzeru kwa dziko lapansi kungomvetsera matepi. Iwo amati ife tikhoza kumva matepi nthawi iliyonse. Palibe chifukwa chomvera nthawi imodzi. Inu Muyenera kumvetsera utumiki wamoyo, mlaliki, osati matepi okha.Iwo akodwa mu miyambo yawo.

Palibe chonga ichi chomwe chinachitikapo mu m’mbiri ya dziko lapansi. Nchiyani chomwe chakopa anthu awa kuti agwirizane onse nthawi imodzi kuti amve Liwu limenelo lakuyitana lomutulutsa kwa Mkwatibwi Wake? Ndi Mulungu akukwaniritsa Luka 17:30. Ndi Mulungu akukwaniritsa Chivumbulutso 10:7. Ndi Mulungu akuwulula Ahebri 13:8, Melkizedeki mu thupi la munthu, monga momwe Iye adachitira kwa Abrahamu.

Iwo akudikira ndi kudabwa, Kodi Iye adzalankhula chiyani? Kodi Chidzachitika nchiyani Iye akadzayamba kulankhula? Iwo amafuna kukhalapo pa kulumikizana Kwa pa telefoni kuti apeze chilichonse chimene Iye akunena. Iwo amafuna icho. Iwo amafuna kuchimva icho chonse nthawi imodzi ndi Mkwatibwi padziko lonse lapansi. Pakuti iwo amakhulupirira kuti iye ndiye liwu limene Mulungu anasankha kukhala Liwu Lke kuti liyitane kumutulutsa ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake.

Ngakhale kuti ali kutali kosiyana kwa maola ambiri mu nthawi, koma onse ali pamodzi ngati CHIMODZI, akumvetsera, akumvetsera Liwu limenelo likulankhula nawo kuchokera ku Tchalitchi chawo cha panyumba. Akukhala munkupezekapo kwa Mwana wamamuna, akucha ndikuyembekezera Kubwera kwa Mesiya.

Mitima yawo ikuthamanga. Mzimu Woyera ukuwaulula zomwe zikuchitika. Mulungu wakhala akuyembekezera kufikira mpaka lero kuti awonetse Mawu Ake ndikusonkhanitsa Mkwatibwi Wake. Izo Zikuchitika, ndipo iwo ndi gawo la Izo. Chowonadi cha zomwe zikuchitika chikugwera m’mitima yawo. Iwo awerenga za izo m’Malemba kwa zaka mazana ambiri, koma tsopano ndi zenizeni. Vumbulutso la Mawu likuonekera kudzera mwa iwo. Maulosi a mneneri akukwaniritsidwa.

Pamene iwo akukhala pansi pa kudzoza kwakukulu kwa Liwu Lake lamphamvu, Iye amalengeza kwa iwo kuti akonzekere; pakuti usikuuno Iye apempherera aliyense wa iwo. Iye amatiuza kuti akayamba kupemphera, muyike manja pa odwala, chifukwa Mulungu alipo paliponse, kulikonse komwe ali: ku Texas, ku California, ku Arizona, South America, ngakhale m’nyumba za m’nkhalango mbali ina ya dziko lapansi. Kulikonse kumene iwo akulumikizidwa pa intaneti, ikani manja pa wina ndi mnzake tikayamba kupemphera ndipo Mulungu adzachiritsa aliyense wa iwo, ngati akhulupirira, pakuti Ndi Pakuti Atero Ambuye.

Iwo akumvetsa tsopano kuti m’mibadwo yonse ndi mneneri aliyense amene anakhalapo kapena amene adzakhalapo, padzakhala anthu enaake omwe adakonzedweratu kuti amve Uthenga umenewo, ndipo amenewo adzautsatira iwo. Iwo Sadzavomera gulu. Iwo Sadzavomera ndi kutsutsidwa kwa wosakhulupirira amene amati ndi njira yolakwika kapena si njira yoperekedwa ndi Mulungu. Iwo alibe mkangano ndi iwo.Iwo ali ndi chinthu chimodzi chomwe AYENERA KUCHITA, ndicho kukhulupirira ndipo kuti apeze gawo lililonse la Iwo momwe iwo angathere, kuulowetsamo monga Mariya amene anakhala pa Mapazi a Yesu. Iwo Sachita manyazi, iwo amanyadira kwambiri kunena kuti iwo ndi mnyamata wa tepi kapena kuti mtsikana wa tepi amene amakanikiza kusewera.

Liwu limenelo lawachenjeza kale kuti padzakhala odzozedwa pa nthawi yotsiriza omwe adzakhala ndi kudzoza kwakukulu, Mzimu Woyera. Adzatchula mobwereza mneneri ndi Uthenga wa nthawiyo; akunena kuti ndi okhulupirira, koma ali odzozedwa abodza.

Iwo adzakhala pafupi kwambiri ndi kudzoza kwenikweni komwe kukadati kunyenge osankhidwa omwe ngati n’kotheka, koma Iwo akudziwa kuti iwo sanganyengedwe, chifukwa iwo NDI MAWU. Iwo ndi Mkwatibwi weniweni amene anakhala ndi Mawu a Mulungu.

Liwu limenelo likulengeza kwa iwo kuti mu tsiku lino ilo Silidzakhala ndimu, kapena mphesa. Zimenezo zingakhale zosavuta kuzindikira kusiyana. Koma lidzakhala tangelo, theka la ndimu, theka la lalanje, mtundu wosakanikirana. Lidzawoneka ngati lalanje, koma silidzakhala lili ilo, chifukwa nthambi yatsopanoyo idzakhala handiredi peresenti ngati yapachiyambi. Iwo ADZAKHALA ndi Liwu Mawu apachiyambi. Iwo sadzatenga mlowammalo. Iwo Adzakhala ndi iye amene, Mulungu mwini wake adalengeza kuti ndi LIWU LAKE, MAWU AKE, otsimikiziridwa ndi Lawi la Moto.

Kodi chikuchitika nchiyani?

Mbewu ya Mulungu yokonzedweratu singachite china chilichonse koma kutsatira ndi kumvetsera Liwu limenelo, chifukwa limatanthauza zambiri kuposa moyo kwa iwo. Inu mukhoza kutenga miyoyo yawo, koma inu simungathe kutenga Liwu limenelo.

Kodi chokopa ndi chiyani?

Mulungu, monga mwanthawi zonse, akukwaniritsa Mawu Ake.

Bwerani mudzalumikizane nafe ndikukhala gawo la ulosi wa mneneri womwe ukukwaniritsidwa Lamlungu lino pa 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tikumva Malemba akuwonetseredwa.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 65-0725E “Kodi Ndi Chiyani Chokopa Pa Phiri?”

Malemba:
Mateyu Woyera 21:1-4
Zekariya 9:9 / 14:4-9
Yesaya 29:6
Chivumbulutso 16:9
Malaki 3:1 / Mutu wa 4
Yohane Woyera 14:12 / 15:1-8
Luka Woyera 17:22-30