Uthenga: 65-0718E Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake
- 26-0503 Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake
- 24-0728 Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake
- 23-0108 Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake
- 21-0718e Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake
- 20-0329 Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake
- 18-1014 Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake
- 16-1221 Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake
Wokondedwa Mkwatibwi,
Liwu lomwe ife tonse timakonda kumva lidzalankhula Lamlungu lino, ndipo lidzatibweretsera ife Uthenga Wapadera wa Kalata Yachikondi, wa Mkwatibwi wa Yesu Khristu yekha.
Liwu limenelo linangolankhula ku dziko lapansi ndikuwachenjeza iwo kuti, “Musayese kundichitira Ine ntchito mopanda kukhala chifuniro Changa. Ndili ndi njira yangwiro yoperekedwa imene ine ndakupangirani inu, Mkwatibwi Wanga. Kumbukirani Mawu Anga, inu muzingonena zimene Ine ndalankhula pa matepi Anga, chifukwa inu mukulowa mu chiweruzo. Chifundo chakanidwa. Koma kondwerani, ndipo khalani oyamikira, chifukwa ine ndapereka ndi kukupatsani inu Chakudya Chobisika, Chakudya Chauzimu, kuti inu mukhale ndi moyo pa ubwino ndi chifundo cha Vumbulutso la Yesu Khristu.
Tsopano muli chilala m’dzikololi lomvera Liwu Langa . Iwo samakumvetsani inu chifukwa inu mumati ndinu anthu a Tepi, ndipo mukufuna kungomva Liwu Langa pa Matepi; koma ndakuitanani kukutulutsani inu ndipo ndakuwululirani inu njira Yanga yangwiro yoperekedwa ya lero.
Inu simunadziphatikize ndi osakhulupirira panthawi ya chilala. Ine ndakupatsani Liwu Langa kuti likuthandizeni. Mwa kusewera Liwu Langa, mgolo wanu siwudzapita wopanda kanthu, ngakhale mtsuko wanu siwudzauma, mpaka tsiku limene ine ndidzabwera ndikukutengani ngati Mkwatibwi wanga.
Ndicho chifukwa chake Ine ndinali ndi Liwu Langa likujambulidwa, kotero kuti inu muKhale ndi malo angwiro operekedwa oti mupiteko, komwe kulibe cholakwika, palibe chifukwa chofuna kutanthauzira, basi Liwu Loyera la Mulungu. Malo omwe mungapiteko kuti mumve ndendende zomwe Ine ndanena: Pakuti Atero Ambuye.
Ine ndidzalankhula nanu momveka bwino Lamlungu.Ine Ndikufuna kuti inu musadzaiwale zomwe ndidzalankhule nanu. Matepi awa ndicho Chakudya Chanu Chauzimu mu Nyengo Ino. Ndi cholemera kwambiri kwa ena a iwo; sangathe kuchidya icho. Icho sichinawululidwe kwa iwo, koma Ine ndakusankhani INU, ndipo ndakupatsani inu Vumbulutso la njira Yanga Yangwiro yoperekedwa.
Kwa inu, Ndi Chakudya Chobisika, komwe mukukhala ndi ubwino ndi chifundo cha Mawu Amoyo.
Pamene Ine ndinali kukhala m’thupi mwa Mwana wanga wa mamuna, iwo mophweka sanathe kuvomereza yemwe ine ndinali: Mulungu ndi munthu. Kenako ine ndinalonjeza kuti ndidzabweranso m’masiku otsiriza ndikukhalanso m’thupi la munthu monga momwe ndinachitira Abrahamu asanakhalepo, ndipo ine ndidzatsika pansi ndikudziveka ndekha m’thupi la munthu monga momwe ine ndinachitira nthawi imeneyo.
Izi ndi zomwe iwo adaphonya, nthawi imeneyo ndi tsopano, koma ine sindikufuna kuti inu muiwale. Chakudya chosungidwa chimene ine ndikukudyetsani inu, ndi mthenga wanga, ndi ofanana. Inu Simungathe kuwalekanitsa iwo. Uthenga ndi mthenga ndi ofanana.Ine ndinakuuzani inu m’Mawu Anga zomwe ndikanachita mu tsiku ili. Ndicho chifukwa chake ndi chifuniro changa kuyika Liwu Langa m’matchalitchi anu, m’nyumba zanu, kulikonse komwe inu mupita; chifukwa ndilo Liwu lofunikira kwambiri lomwe inu muyenera kumva. Ndi Liwu LOKHALO lotsimikiziridwa lomwe limalankhula Pakuti Atero Ambuye.
Chifundo chakhala chikukanidwa. Tsopano inu mukukhala pa Mawu Anga.Ine ndakupatsani inu Vumbulutso la yemwe Ine Ndili ndi yemwe INU muli. Sipayenera kukhala mthunzi umodzi wa kukayika m’mitima ndi m’maganizo mwanu. Inu ndinu Mkwatibwi Wanga Wosankhidwa, Wosankhidwiratu, Wokonzedweratu. Ndinu Mawu Anga Olankhulidwa omwe anali mwa Ine pachiyambi.
Inu muli ndi mwayi wopeza Chakudya, Chakudya Chauzimu, chomwe dziko lapansi silikudziwa kalikonse.
Inu muli ndi mwayi wopeza machiritso a matupi athu pamene madokotala alephera; Ndi chimodzi mwa Zakudya zomwe ine ndinalonjeza ndi kukupatsani inu m’masiku otsiriza.
Ine ndinalonjeza kuulula zinsinsi za mitima yanu ndikuchita izi. Ine ndiri mwa inu. Inu ndinu gawo la Ine, ndipo Ine ndine gawo la inu. Zizindikiro izi zidzawatsata iwo amene akhulupirira.
Lamlungu lino Ine ndidzakhala ndikugwirizanitsa Mkwatibwi Wanga kuchokera kuzungulira pa dziko lonse lapansi ndi Liwu Langa. Ine ndidzakuwuzani inu kuti muyike manja anu pa wina ndi mnzake. Musadzadzipempherere nokha, mudzapempherere amene mwamusanjika manja anu pa iye, chifukwa iwo akukupemphererani inu. Ife tidzapemphera limodzi, ndipo sipadzakhala munthu wofooka kulikonse padziko lonse lapansi ngati inu mudzakhulupirira.
Ngati inu mukhulupirira, ndipo mulibe kukayika mumtima mwanu,Ine ndidzalengeza:
Satana, iwe wagonjetsedwa! Yesu Khristu anakugonjetsa iwe! Iye anawuka kwa akufa ndipo akuyima pakati pa ife usikuuno, kutsimikizira Uthenga uwu wa masiku otsiriza. Tuluka mwa anthu awa! Asiye iwo, mu Dzina la Yesu Khristu! “Mu Dzina Langa iwo adzaturutsa adierekezi,” ndipo iwe watulutsidwa. Mu Dzina la Yesu Khristu asiye osonkhana awa!
Padzakhala machiritso akuchitika kuzungulira pa dziko lonse lapansi kuposa kale lonse.
Ife tikanamayembekezera chifukwa chiyani mwa kutalika kwinanso, m’bale wanga wokondedwa, mlongo, pano Iwo uli, Mzimu Woyera, Mulungu, pano pomwe, chinthu chomwecho ife timachikamba.
Ine ndikuyitana dziko lonse lapansi kuti lidzabwere kudzalumikizana nafe Lamlungu lino pa 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, ndikudzamva Uthenga ndi mthenga Wake akutibweretsera ife Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake, Chakudya Chobisika cha Mkwatibwi.
M’bale Joseph Branham
Uthenga: Chakudya Chauzimu Mu Nyengo Yake 65-0718E
Mthenga: M’busa . William Marrion Branham
Malemba Opatulika: 1 Mafumu 17:1-7 / Amosi 3:7 / Yoweli 2:28 / Malaki 4:4 / Luka 17:30 / Yohane Woyera 14:12