26-1025 Kukhazikitsidwa #1

Uthenga: 60-0515E Kukhazikitsidwa #1

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Wokhulupirika mwa Khristu Yesu,

Ndi nthawi ya ulemerero yotani yomwe ife tili nayo. Ife timakhala pansi pa kuyembekezera kwakukulu sabata iliyonse pamene tikulumikizana pamodzi mozungulira Liwu Lake. Maganizo athu auzimu si ali osokonezeka. Ife TIMADZIWA bwino lomwe yemwe Iye ali.Ife timadziwa bwino lomwe chomwe Iye ali.Ife TIMADZIWA bwino lomwe yemwe ife tili; banja limodzi lalikulu NDI IYE! “

“Iye anampatsa munthu kuti adzakhale mulungu wamng’ono.” Chifukwa Iye ndi Mulungu Atate, ndipo Iye anamupanga munthu kukhala mulungu wamng’ono, chotero Iye si wokhalapo yekhanso, Iye akukhala ndi banja Lake. Elah, Elah, Elohim. Tsopano, tsopano Iye ndi Yehova. Yehova, kutanthauza, “Mmodzi Amene akukhala ndi banja Lake.

Banja la Mkwatibwi Wake likupangidwa la mngwiro ndi Liwu la Yehova Mwiniwake.Iye Watiphunzitsa ife momwe tingamenyane ndi mdani aliyense amene amayambana ndi ife; momwe ife tingamupambanire ndikumugonjetsa iye ndi Mawu, chifukwa Mawu Ake ali ndi moyo ndipo amakhala mkati mwa ife.Iye anatitsimikizira ife kuti, “IFE NDIFE MAWU”. Choncho chilichonse chimene ife tipempha m’Dzina Lake, tikhoza kuchilandira icho ngati tikhulupirira… NDIPO IFE TIMAKHULUPIRIRA!

Iye walankhula ndi kutiwululira ife momwe tingakhalire ma thunthu angwiro amuna ndi akazi kuti tikhale malo okhalamo Iye. Iye anafuula ndi kufuula kuti asonkhanitse Mkwatibwi Wake wokondedwa pamodzi kuti atidziwitse ife kuti Iye ndiye Mtsogoleri wathu, ndipo anali kutitsogolera ndi kutilondolera ife kudzera mwa namulondola wake wa mngelo wapadziko lapansi, William Marrion Branham.

Tsopano iye ali ndi phunziro lina lapadera lomwe akufuna kutiphunzitsa ndi kutiwululira ife.Iye akufuna kulengeza kuti ndife ana ake okhazikitsidwa. Dzina lathu ndi labwino monga momwe Dzina lake lilili. Ife tatuluka ku Kanani, kutuluka m’dziko lapansi, ndipo TSOPANO tikukhala pamodzi m’malo amwambamwamba, tikudya Mana wobisika, wosungidwa.

Tsopano Iye atiuza ife zomwe tiyenera kuchita kuti tikhale okonzekera Uthenga Wake wotsatira, ndi zomwe zingachitike ngati ife titatero.

Ife tiyenera kupempheredwa ndi kukonzekera Uthenga; Kudzisonkhanitsa ifeeni pamodzi monga oyera mtima kuti timve Liwu Lake, Kubatizidwa ndi Mzimu Woyera, kudzazidwa ndi madalitso a Mulungu; Popanda malingaliro oipa; Popanda chotsutsana wina ndi mnzake; Kulankhula mu mchikondi ndi mogwirizana; Kukhala mu umodzi, pamalo amodzi pamodzi m’malo amwambamwamba pansi pa mlengalenga wakumwamba; Machimo athu onse pansi pa Magazi, mu mkupembedza kwangwiro; Manja athu ndi mitima yathu zokwezedwa kwa Mulungu, kupembedza pamodzi m’malo amwambamwamba.

Ngati ife tichita zinthu izi, izi ndi zomwe zidzachitike Lamlungu lino:

  • .Machiritso a uzimu
  • .Kudziwa za mtsogolo .
  • .Vumbulutso
  • .Masomphenya .
  • .Mphamvu
  • .Malilime
  • .Kutanthawunzira
  • . Nzeru
  • .Chidziwitso
  • .Madalitso amwambamwamba .
  • Chimwemwe chosaneneka komanso chodzadza ndi Ulemerero

Mtima uliwonse udzadzazidwa ndi Mzimu. Kenako mwadzidzidzi kudzamveka mkokomo wonga mphepo yothamanga mwamphamvu kuchokera Kumwamba ndipo Iye adzatidalitsa ife ndi madalitso onse awuzimu.

Icho ndicho chimene chidzachitike Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, komwe Mulungu wapereka malo apadera komwe Mkwatibwi angasonkhane pamodzi kuti amve Liwu Lake mu mgwirizano umodzi, mu mmalo amodzi, ndi manja ndi mitima yathu zokwezedwa kwa Mulungu, kupembedza pamodzi mu mchikhalidwe chakumwambamwamba.

M’bale Joseph Branham

Uthenga:
Kukhazikitsidwa #1 60-0515E 

Malemba:
Yoweli 2:28
Aefeso 1:1-5 1
Akorinto 12:13 1
Petulo 1:20
Chivumbulutso
17:8
Chivumbulutso 13