26-1004 Nkhondo Yaikulu Imene Yakhala Ikumenyedwa

Uthenga: 62-0311 Nkhondo Yaikulu Imene Yakhala Ikumenyedwa

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa AMikaya,

Nkhondo yaikulu kwambiri imene idamenyedwapo tsopano yakonzeka kuyamba kuchitika. Mulungu wakhala akusankha asilikali Ake apamwamba kwa zaka zoposa sikisi sawuzande, ndipo inu munakonzedweratu ndi kusankhidwa kuti mukhale mu Gulu Lankhondo Lake Lalikulu.

Iye wakhala akukuvekani inu, ndi kukuphunzitsani inu, ndipo tsopano mzere wa nkhondo wakhazikitsidwa, kukozekela kuti iyambe. Osati kokha kuti Iye wakusankhani inu kuti mukhale mu Gulu Lankhondo Lake Lalikulu, koma wakusankhani inu kuti mukhale Mikaya mneneri mu gulu lankhondo Lake.

Nthawi yafika, tsiku lafika; Inu mudzalandira maphunziro molunjika kuchokera ku Lawi la Moto Iyemwini kuti mugonjetse mdani aliyense.Inu Mudzalandira malangizo apadera, Mawu pa Mawu, pa zomwe inu muyenera kuchita kuti muwononge mizimu yonse yoipa. Idzachotsa matenda aliwonse ndi mdierekezi aliyense amene abwera pamaso panu. Palibe chimene chingathe kuyima pa njira yanu.

Pambuyo pa maphunziro apaderawa, mudzalimbikitsidwa ndi Mawu Ake kotero kuti mudzatulutsa zoipa zonse. Mudzachotsa kulingalira. Mudzachotsa zikhulupiriro zachabe. Mudzachotsa nkhawa. Mudzachotsa matenda. Mudzachotsa tchimo.Inu mudzamvetsetsa kuti muli pamwamba pa izo, mwaukitsidwa mwa Khristu Yesu, mukukhala m’malo amwambamwamba, ndi mdierekezi aliyense pansi pa phazi lanu.

Inu mudzamvetsetsa kwathunthu ndi KUKHULUPIRIRA kuti ndinu Mawu.

Iye adzakhala akukuphunzitsani inu zomwe muyenera kukhala nazo a tcheru.Iye adzakulangizani inu kuti ngati mdani wanu angakuchititseni kukhulupirira kuti Chida chanu sichili champhamvu mokwanira,iye adzakulandani chida chanu.

Koma ife tidzakumbukira maphunziro athu, asilikali, ndi kumuwuza mdierekezi uja kuti: Si ife, ife sindife kanthu. Chida chathu ndi Mawu a Mulungu ndipo adzagonjetsa MDIEREKEZI ALIYENSE, nthawi iliyonse, malo aliwonse, chifukwa ndi MAWU AKE, NDIPO IYE WATIPHUNZITSA IFE NDI KUTIULULIRA IFE KUTI TSOPANO NDIFE MAWU AKE OPANGIDWA THUPI. CHONCHO,ife sitingagonjetsedwe, ndife gulu lankhondo losagonjetseka la MULUNGU.

Limodzi mwa masiku aakulu kwambiri mu mbiri ya dziko lapansi lichitika Lamlungu lino. A Mikaya Ake adzagwirizana pamodzi kuchokera kuzungulira dziko lonse lapansi pansi pa Liwu la wa Wankhondo wawo wamkulu, pamene tidzalumikizidwa pamodzi mu mtima umodzi, popanda mthunzi umodzi wa kukayika kulikonse.

Ndiye, ngati ife tingokhulupirira kokha, NDIPO IFE TIMAKHULUPIRIRA, sipadzakhala munthu wofooka kuzungulira padziko lonse lapansi. Ngati ife tingakhoze kutenga chinthu icho china chake kukonzedwa, sipakanakhala munthu wina aliyense wofuna Mzimu Woyera koma akanawulandira iwo, ndipo pakanakhala kuchiritsidwa kwadzidzidzi kwa moyo ndi thupi, ngati ife tidzasunga malo athu. Tsopano nthawi ndi ino.Ife ndife anthu. Mzimu wa Mulungu wadzutsa muyeso woyenera kutsutsana ndi mdierekezi aliyense; ife ndife MMODZI MWA IWO ndipo palibe chotiletsa ife!!

Ife Tafa ku zokhudzira zathu, tafa ku kulingalira kwathu, tafa ku zinthu izo zonse. Moyo wathu wabisika ndipo taikidwa m’manda mu Dzina la Yesu Khristu, ndi kuukitsidwa pamodzi ndi Iye. Ndipo kumene Iye ali, komweko ife tilinso.

Ife tatulukila panja panthu, mdierekezi, pa kukuphulitsa ndi, “PAKUTI ATERO AMBUYE. PAKUTI ATERO AMBUYE. PAKUTI ATERO AMBUYE.” Ife Potsiriza tikununkhiza m’pweya wabwino. “PAKUTI ATERO AMBUYE.” pano ife Tikubwera mdierekezi, tatulutsa mitu yathu panja. “PAKUTI ATERO AMBUYE, IWE WAGONJETSEDWA.”

Kodi ife timagonjetsa mdierekezi ndi chiyani?

Mawu!
Tiyeni ife tinene izo; Mawu! Mawu! MAWU!!

MALANGIZO ENA OCHURUKA OPHUNZITSIRA

Tsopano m’dani akamalimbana ndi kuyesa kunena kuti iwe uyenera kuchita izi, iwe uyenera kuchita izo, iwe ndiwe wopanda pake, suyenera, sunachiritsidwe, iwe ukanalinso ndi mavuto ako ofanana omwewo. Kodi iwe uchite chiyani?

Choka kwa ine.” Phwaa! Inu mumudule iye ndi Mawu. Kaya icho ndi chiwanda, kaya iye ndi mdani, kaya awo ndi matenda, kaya iyo ndi nthenda, chirichonse chimene icho chiri, muwatenge Mawu amenewo ndipo muwakoke Iwo ndi Lupanga. Ndipo ngati inu muchimenya icho nthawi yoyamba, icho nkusamawoneka kuti chikusuntha, muchimenyenso icho kachiwiri, ndi kuchimenyanso icho, ndi kuchimenyanso icho.

Ife Timangovomereza Mawu pa maziko akuti, “Mulungu adanena choncho,” ndipo izo zimakhazikitsa chilumikizano pakati pa ife ndi Iye. Njira iliyonse yakhala yotseguka pakati pathu.Ife timanena kuti, “Ine Sindikudziwa kuti ndidzazipeza liti izo, koma ine ndidzazipeza izo. MULUNGU ANENANA CHONCHO. Kukayika kulikonse KWAPITA…ife tikukayikiranso ngakhale kukayika kwathu.”

Ife timakaniza mdierekezi ndi kutenga Mawu a Mulungu. Ngati ndimva kutentheka, kapena kusamva kutentheka, ziribe kanthu zomwe zichitika, Mulungu ananena choncho. Izo zimakhazikitsa izo.

Tsatirani malangizo awa, asilikali, ku kalata. Bwerezani Mawu awa pamene mdani akulimbana nanu. Si Mawu anu, iwo ali MAWU AKE, NDIPO MAWU AKE SANGAKHOZE KULEPHERA. Iye watipatsa ife mphamvu kuti tigwiritse ntchito Mawu Ake potipanga ife kukhala Mawu Ake. Pamene Satana akulimbana nanu, muwerengereni iye malamulo anu.

MALANGIZO A MKULU WATHU WANKHONDO

Apa pali ndendende zomwe ine ndikufuna kuti inu muzichita.

Bwerezani lumbiro ili ndi kukhulupirira Mawu aliwonse pa chiwombolo chathunthu.

Satana, pita kutali! Ine ndikutulukamo muno.” Ndi zimenezotu. “Ine sindikhala muno, panonso. Ine sindikhalanso muno, panonso. Ine sindiri pa bwalo la Mdierekezi wakale uyu panonso. Ine ndikukonkhomola njira yanga kuti ndituluke, mmawa uno. Ameni. Ndine mphungu.” Ameni! Aleluya!

Kenako ine ndikufuna kuti inu muzichita izi:

Kuphulitsa izo ndi, “PAKUTI ATERO AMBUYE. PAKUTI ATERO AMBUYE. PAKUTI ATERO AMBUYE.”

Tsegulani maganizo anu, nenani, “Mawu Anu ndi oona.”

Ambuye, ine sindilabadira chirichonse cha momwe ine ndikumverera, chimene aliyense, akudzinenera yekha. Ine ndasiya, ine ndikupemerera uliwonse wa mpita wanga, kukhumudwitsidwa kulikonse, ndi kukaikira, ndi kusakhulupirira kumene ine ndinayamba ndakhalapo nako. Kumverera kulikonse kumene ine ndinayamba ndakhalapo nako, matenda onse amene ine ndinayamba ndakhalapo nawo, chirichonse chimene ine ndinayamba ndakhalapo nacho, ine ndikuzipemerera izo zonse. Ine ndikuzilambalala zonse izo. Ine ndikubwera molunjika kwa mzimu wanga.

CHIKHULUPIRIRO chanu chidzayamba kukwera m’mwamba ndi m’mwamba. Kenako nenani kwa Iye, O Ambuye, tsikani. Inu munati munandipanga ine kukhala wakhalidwe mwaufulu.

“Iwe ndiwe, mwana Wanga wamamuna.”

Chabwino, ine ndatsegula mtima wanga ndi maganizo anga.

“Lowani mkati, Ambuye Yesu.”

Ndipo mugwire Chikhulupirirocho, Lupanga ilo la Mzimu, PAKUTI ATERO AMBUYE.

Mufuule, “Aleluya!” Ameni.

Ndiye mudulire pansi mdani aliyense pamaso panu. Ameni. Ndi zimenezotu. Kumudula mdani aliyense. Ngati—mzimu wakale wa chipukwani ukukupangani inu kumadzimverera…Muchidulepo chinthu chimenecho, ndi Mawu a Ambuye.

MALANGIZO ANU OTSIRIZA MSILIKALI.
UZANI MDANI:

Choka kwa ine.” Phwaa!

Inu mumudule iye ndi Mawu. Kaya icho ndi chiwanda, kaya iye ndi mdani, kaya awo ndi matenda, kaya iyo ndi nthenda, chirichonse chimene icho chiri, muwatenge Mawu amenewo ndipo muwakoke Iwo ndi Lupanga. Ndipo ngati inu muchimenya icho nthawi yoyamba, icho nkusamawoneka kuti chikusuntha, muchimenyenso icho kachiwiri, ndi kuchimenyanso icho, ndi kuchimenyanso icho. Ndipo muchimenye icho mpaka inu mutabowola dzenje pamenepo, monga ngati kamwanapiye kakang’ono kakamasuzumira panja; kapena mphungu, chimene inu muli. Kusuzumira nokha kudutsa chikhokhombe chakale icho cha matenda. Mudzidulire njira yanu, ndi kuti, “Aleluya! Kodi china chiri kuti?” Ameni. Nkhondoyo ndi imeneyo. Ameneyo ndiye msilikari. Ameneyo ndiye msilikari wa mtanda. Inde, bwana. Kumugwetsera panja mdani aliyense. Bwanji? Bwanji?

Ife, Mbewu yokonzedweratu, yachifumu ya Abrahamu.

Ulemerero, mdani aliyense wagonjetsedwa. PALIBE chimene chingaime pamaso pa Mawu a Mulungu, ndipo ife ndife Mawu a Mulungu. Ife ndife Mbewu Yake Yachifumu ndipo lonjezo lililonse NDI LATHU.

Tsiku lafika, Mkwatibwi amakhulupirira Mawu aliwonse ndipo akuchita pa Iwo. Ife tadzikonzekeretsa tokha mwa kumva ndi kukhulupirira Mawu Ake.

Ngati inu mukusowa chilichonse, ngati mukufuna kudzazidwa ndi Mzimu Woyera, ngati mukufuna kuchiritsidwa, ngati mukufuna kuti mdierekezi aliyense atulutsidwire kunja, ngati inu mukufuna kukhala Mkwatibwi wa Khristu, tsopano nthawi ndi yino, kumva ndi kukhulupirira Liwu Lake ndiye malo.

Ngati inu mukulakalaka zinthu izi ndipo inu mukufuna kukhala pamaso pa Ambuye, pafupi kuposa momwe munakhalapo kale lonse, bwerani mudzalumikizane nafe Lamlungu nthawi ya 12:00PM, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene Mkulu wathu Wankhondo wa nyenyezi zinayi akulangiza Mkwatibwi Wake wamphamvu Mikaya momwe angagonjetsere mdierekezi aliyense, mdani aliyense, kuti amasulidwe, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera Wake, ndi kukonzekera Kudza Kwake posachedwa.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: Nkhondo Yaikulu Kwambiri Imene Idamenyedwapo. 62-0311

Mawu:
1 Petro 5:8-10
Aefeso 6:10-17
Danieli 12:1-7