Uthenga: 60-0518 Kukhazikitsidwa #2
- 26-1101 Kukhazikitsidwa #2
- 25-0511 Kukhazikitsidwa #2
- 21-0626 Kukhazikitsidwa #2
- 18-0617 Kukhazikitsidwa #2
- 16-0224 Kukhazikitsidwa #2
Wokondedwa Okondendwa
Kodi inu mwakonzeka, ana aamuna ndi aakazi a Mulungu owonetseredwa ndi oleredwa, kukhala pansi pamodzi m’malo amwambamwamba, mogwirizana ndi Mkwatibwi wochokera kuzungulira padziko lonse lapansi, kumva Liwu la Mulungu likulankhula kwa inu pakamwa ndi khutu?
Inde!!! Ife takonzeka kumva Liwu la Mulungu likutiwuza ife bwino lomwe yemwe ife tili.
Ine ndakutchulani inu “okondedwa” chifukwa inu muli. Inu—inu ndi okondedwa anga. Inu mukudziwa chiyani? Mundilole…Apa pakubwera Lemba. Paulo anati, “Ine ndikukuchitirani inu nsanje (Mpingo Wake) ndi nsanje ya umulungu, pakuti ine ndakupalisani inu ubwezi.” Ndi zimenezotu, amene amva izo. Ndi zimenezotu. “Pakuti ine ndakupalisani inu ubwezi, ndakutomeretsani inu kwa Khristu, ngati namwali wangwiro.”
Ulemerero kwa Mulungu, mngelo wake watipalitsa ife ubwezi kwa Iye. Ife ndife namwali oyera mtima ku Mawu Ake, Uthenga uwu, ku Liwu Lake pa matepi. Tsopano ife tatomeredwa kwa Khristu.
Ife tidzakhala okonzeka komanso pansi pa kuyembekezera kwakukulu Lamlungu. Ife tidzaluma chala chathu, tidzatsina miyoyo yathu, ndi kukantha mitima yathu. Ife kamodzinso tidzakhala tikufuulanso, kutamanda Ambuye, kufuula “ameni, haleluya”, monga momwe nyenyezi za m’mawa zinayimbira limodzi ndi ana a Mulungu anafuula ndi chisangalalo; pamene anaona dongosolo la chipulumutso, pamene Mulungu anaika mayina athu m’Buku Lake maziko a dziko asanakhazikitsidwe.
Kodi ife tingamvetse kuti Atate Mulungu wakhala akuyembekezera, kuyambira pachiyambi cha dziko lapansi, mpaka lero, PA IFE? Iye anaona komwe ife tidzawonetseredwe m’masiku otsiriza, ndipo wakhala akuyembekezera ndi kutililira ife kuti tidzuke ndi mphamvu ya Mzimu Woyera kuti atiululire zinthu zachinsisi zomwe zabisika mpaka lero.
M’mibadwo yonse, aneneri akhala akuyembekezera mpaka masiku otsiriza ano kuti zinthu izi ziwonetsedwe. Atate Mulungu anati wakhala akuyembekezera kuti Mpingo Wake ukule kuchokera ku nthawi ya Lutera, nthawi ya Baptisti, nthawi ya Methodisiti, nthawi ya Pentekosite, ndipo tsopano mpaka ku Mwala wapa mutu kuti ukhazikike. Kenako mpaka Chimango titatsilizika.
Masiku olonjezedwa amene Ambuye analankhula ndi kuwalakalaka tsopano akuchitika ndipo akukwaniritsidwa pamaso pathu… NDIPONSO MWA IFE. Tsopano ife tili mwa Khristu Yesu, tikukhala mu mtendere wamwambamwamba, madalitso amwambamwamba, Mzimu wamwambamwamba, kumene chilichonse ndi chathu. Ife tili mu Dziko Lolonjezedwa ndipo tili ndi chilichonse mumchikwanekwane. Mbewu Yake yoyamba inafika ku kukhwima kokwanira ndipo inaweyulidwa pamaso pa Mkwatibwi Wake. Mzimu Woyera unabwerera kwa Atate Mulungu ndipo unanena izi za mngelo Wake wamphamvu:
Mngelo wanu akukula mu chisomo! Akuponya zipolopolo m’nkhalango.Iye amatenga nkhosa zanu ndipo amatha kuzigwira monga momwe Inu mumachitira. Iye sadzawapatsanso iwo udzu wa m’nyanja. Iye sadzawapatsanso iwo udzu wachitsulo. Pomwe iwo anabwera mozungulira, nanena, ‘Ife tikufuna kulowa mu mpingo,’ iye anati, ‘Tsekani pakamwa panu, simukusowa zimenezo! Ayi, bwana.Izi ndi zomwe inu mukufunikira, “Lapani, mubatizidwe, aliyense wa inu, mu Dzina la Yesu Khristu, kuti machimo anu akhululukidwe. Inu mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.”‘
“O, kodi Iye akunenadi zimenezo?”
“Inde, Bwana, iye amaterodi.”
“Chabwino, ndi kokha momwe ine ndinazilembera.”
“Ndi momwemo mokha iye amanenera izo.”
“Inu mukudziwa chiyani? Ine ndinaona Arikibishop Wakuti-ndi-wakuti akumuuza kuti iye ‘sakuyenera kubwera mumzinda uno ndikudzachita msonkhano.’ Koma, inu mukudziwa,ine ndinali kumutsogolera iye, ine ndinati, ‘Pita mulimonsemo.’Iwo anamuuza iye kuti kunali bwino awasiye matepi ake onse, ndipo inu musawalole iwo kuti atuluke. Ife tinapita mulimonse!”
“Uyo ndiye mwana wanga woleredwa amene ine ndakhala ndikumuyembekezera. Tsopano nditha kulankhula kudzera mwa iye ndikuulula zinsinsi zanga zonse zobisika kwa nkhosa zanga.”
“Wabwino Atate Mulungu.”
“Tsopano kodi inu mungakonde kuti ine ndikuuzeni inu za ana anu ena?”
“Inde, iwo akuchita motani?”
“Oh Atate…inu kotero mungakhoze kuwanyadira iwo. Iwo ndi otemeredwa ma khoma achikalekale. Mabishopu awo akale aja akuwauzabe iwo chinthu chomwecho, kuti iwo asamapite ku matchalitchi awo a tepi kuti akamve Liwu Lanu. Iwo amati matepi si Liwu lofunikira kwambiri lomwe iwo ayenera kumva; pali maliwu ochuluka ofunikira kwambiri tsopano.”
“Inu mukudziwa zomwe Nkhosa Zanu zimawauza alaliki awo?”
“TSEKANI PA KAMWA PANU,IFE TIKUKHALA NDI MATEPI, TIKUKHALA NDI LIWU LA MULUNGU.”
“Kodi iwo amaterodi?”
“Inde, Bwana, iwo kokha ali ngati Inu.”
“O, izo ndi zopambana bwanji. Zimenezo zimandipanga ine kusangalatsa kwambiri. Ine ndakhala ndikuwayembekezera iwo kwa nthawi yayitali. Tsopano nawonso ali okonzeka KUKHAZIKITSIDWA!!”
“Iwo adzakhala pa mzere wawo wa ntchito Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, kuti adzamve Lawu Lanu. Iwo adzagwirizana ndipo adzasonkhanitsidwa kuchokera padziko lonse lapansi ndi kuitana aliyense kuti agwirizane nawo.”
“Zopambana, INE NDIDZAKHALA PAMODZI NDI IWO.”
M’bale Joseph Branham
Chikumbutso: Musaiwale za Nthawi Yosunga ya Masana
Uthenga: KUKHAZIKITSIDWA #2 60-0518
Malemba Opatulika:
Genesis 1:26
Chaputala Choyamba cha Aefeso
Aroma 8:19
Agalatiya 1:6-9
Chaputala Chachisanu ndi Chimodzi cha Ahebri
Yohane 1:17