26-0329 Kodi Melkizedeki Uyu Ndi Ndani?

Uthenga: 65-0221E Kodi Melkizedeki Uyu Ndi Ndani?

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi wa Moyo Wamuyaya,

Kodi Liwu limene likulankhula nafe pa matepi ndi ndani?

Ife tingathe kudziwa yankho la funso limenelo kudzera ku vumbulutso lochokera kwa Mulungu. Mkwatibwi Wake wokonzedweratu yekha ndiye amene adzakhala ndi Vumbulutso limenelo. Chifukwa chake, tiyenera kufufuza Mawu Ake kuti timvetse amene Iye anati anali ndani: Wotanthawuzira yekha wa Mawu Ake. Ndani angamatule ndi kuwulula Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri? Ndani angawulule zinsinsi zonse zobisika za m’Baibulo? Ndani adzaitana ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake? Ndani adzakhala ndi Liwu losalephera?

Malingana ndi Mawu, si wina koma Melikizedeki, Iyemwini. Munthu wopanda bambo kapena mayi, Amene analibe chiyambi kapena mapeto a masiku. Mulungu, Amene anakhala thupi ndipo anadya nyama ndi mkate wa chimanga, anamwa mkaka wa batala, ndipo analankhula ndi Abrahamu. Iye anali Munthu wokhala ndi umunthu, wokhala ndi thupi la munthu.

Mawu omwewo anati Melikizedeki, Munthu ameneyo, umunthu umenewo, adzakhala ndi moyo ndi kudziulula Yekha kachiwiri mu thupi la munthu monga momwe anachitira kwa Abrahamu, kenako kachiwiri mwa Yesu Khristu; koma lero, mu mthenga wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri wa Chivumbulutso 10:7. Mzimu Wake udzanyeketsa kachisi wapadziko lapansi kuti Iye athe kulankhula ndi kudziulula kwa Mkwatibwi Wake. Mulungu mwiniwake akukhala ndi kulankhula mu thupi la munthu. Mbewu yake yoyamba yobwezeretsedwa kwathunthu inali itacha mokwanira. Dongosolo lathunthu la Mulungu linafika; Mulungu ndi munthu anali Mmodzi. Mulungu anali kulankhula ndi Mkwatibwi Wake pakamwa ndikupita ku khutu monga momwe anachitira kwa Abrahamu.

Iye anadza mkati nakhala mmenemo, mwa Munthu wa Melkezedeki. Ndiye, kenako, ife sitinamvenso za Melkizedeki, chifukwa Iye anadzakhala Yesu Khristu. Melkizedeki anali Wansembe, koma Iye anadzakhala Yesu Khristu. Tsopano, inu munalidutsa ilo. Chifukwa, mmawonekedwe awo, Iye ankadziwa zinthu zonse, ndipo inu simunakhozebe kudziwa izo.

KOMABE…!! Ndiyeno Kodi ifeyo ndife ndani?

Maso athu, thunthu lathu, chilichonse chomwe ife tinali, tinali m’maganizo Ake pachiyambi. Pasanakhalepo Mngelo, nyenyezi, Kerubi, kapena china chilichonse. Iye anaganiza, Iye analankhula, ndipo ndife tili pano.

Uko ndi kusakhala nawo malire. Ife sitingakhoze kumvetsa izo mmaganizo mwathu, koma ndizo Mulungu. Mulungu, wopanda malire!

Pakuti tinali mwa Iye pachiyambi, kodi n’chiyani chomwe chimachitika kwa ife moyo wa padziko lino lapansi utatha?

Pamene mwinjiro wa thupi uwu wavulidwa, pali thupi lachibadwa, fiofane, thupi osati lopangidwa ndi manja, ngakhalenso kuti lobadwa mwa mkazi, limene ife timapitako.

Ndiye thupi ilo limabwereranso ndi kukatenga thupi la ulemerero.

Kodi ndi zinthu zodabwitsa zanji zomwe zili mu nkhokwe za Mkwatibwi Wake. Taonani zomwe zikuchitika pakali pano pamene Iye akuwululira Mawu Ake Kwa ife kuposa kale lonse. Kukamba za kalata yachikondi kwa Mkwatibwi Wake! Ndi tsiku lotani lomwe ife tikukhalamo.

Ife tili ndi Vumbulutso ndipo tikudziwa kuti ndi Melikizedeki, Liwu la Mulungu, likulankhula nafe pa matepi. Ife tili ndi Vumbulutso, ndi njira yoperekedwa ndi yangwiro ya Mulungu ya lero. Kotero, IFE TIMADZIWA YEMWE IYE ALI NDIPO NDIFE MKWATIBWI WAKE.

Vumbulutso limenero likukulirakulirabe tsiku lililonse. Tsiku lililonse likadutsa limatibweretsera chisangalalo chochuluka, vumbulutso lochuluka. Mkwatibwi akudzikonzekeretsa yekha pokhala pamaso pa Liwu Lake, pamene Iye akutiuza kuti Ife ndi ndani, mochuluka momwe Iye amatikondera Ife, momwe Iye sangathe kuyembekezera kukhala nafe!!!

Bwerani, dzikonzekeretseni nokha nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pa chomwe chikukonzekera kuchitika, pamene ife tikumvetsera Liwu la Melikizedeki.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: 65-0221E “Kodi Melikizedeki Uyu Ndi Ndani?”

Malemba Owerenga:
Genesis Chaputala 18
Eksodo 33:12-23
Yohane Woyera 1:1
Aroma 8:1
2 Akorinto 5:1
1 Atesalonika 4:13-18
Timoteo Woyamba 3:16 / 6:15
Ahebri 7:1-3 /13:8
Chivumbulutso 10:1-7 / 21:16