Uthenga: 60-0518 Kukhazikitsidwa #2
- 25-0511 Kukhazikitsidwa #2
- 21-0626 Kukhazikitsidwa #2
- 18-0617 Kukhazikitsidwa #2
- 16-0224 Kukhazikitsidwa #2
Okondedwa A Ufumu Wa Unsembe ,
Aliyense alume chala chake, tsina moyo wako, ndikudzutsa mtima wako. Lero, Mkwatibwi wa Yesu Khristu akufuula kuti:
Lero, ulosi umenewu wakwaniritsidwa pamaso pathu pomwe.
Ine ndikukhulupirira, limodzi la masiku aulemerero awa, pamene chitaganya chogwirizana ichi cha mpingo chikupita palimodzi, ndipo papa watsopano akutulutsidwa kuchokera ku United States ndi kuikidwa kumeneko molingana ndi uneneri, ndiye iwo adzapanga fano longa la chirombo.
Liwu la mneneri wa Mulungu linalankhula Ilo pa 19 Disembala , 1954, ndipo miyezi 9 pambuyo pake, Robert Prevost, yemwe tsopano akudziwika kuti Papa Leo XIV, anabadwa. Iye tsopano ndi papa watsopano wa Roma. “Pakuti atero Ambuye” wakwanilitsidwa.
Pa 7 Meyi , 1946, MULUNGU anaika mneneri Wake mu Chigayo cha a Green, ku Indiana, kuti amupatse iye utumiki wake ndi kulalikira kwa dziko, uyu ndi wamthenga Wanga wamphamvu wa mngelo wachisanu ndi chiwiri, Liwu Langa kwa dziko. Mverani Inu Iye.
Pamene Mngelo wa Ambuye anakomana ndi ine kunja uko ku Chigayo cha a Green, Indiana, zaka eyiti zapitazo; kuchokera pamene ndinali mwana, wanditsatira ine, wandisonyeza masomphenya. Pamene ine ndinapita kwa Iye. Iye anati, “Ngati iwe uti ukhale woonamtima, nkuwatengera anthu pokukhulupirira iwe, palibe kanthu kati kadzaime patsogolo pa pemphero lako.”
William Marrion Branham ndi Liwu losankhidwa ndi Mulungu ku dziko. Mneneri wamphamvu amene Mawu a Mulungu amafika kwa iye. Molingana ndi Mawu, iye ali wotanthauzira Wauzimu YEKHA wa Mawu a Mulungu.
Iye anatsimikiziridwa ndi Mulungu Mwiniwake, ndi Lawi la Moto.
Pa 7 May , 2025, SATANA anaika gulu lake la Makadinala mu mpingo wa Sisitine ku Roma kuti asankhe Mlowa Mmalo wa Khrisitu, kuti akwaniritse pakuti Atero Ambuye.
Adatsimikiziridwa ndi munthu yemwe ali ndi KUFUFUZA KWA USI WOYERA.
Mkwatibwi wa Khristu kuzungulira dziko lapansi akusangalala, akufuula, akukuwa ndi kutamanda Ambuye pamene ife tikumva, ndi kuona ndi maso athu omwe, uneneri wa mneneri ukukwaniritsidwa.
Zili ngati tikuwona Nyanja Yofiira ikutseguka pamaso pathu. Mana atsopano akugwa kuchokera kumwamba. Mamilioni a zinziri akudyetsa Mkwatibwi. Madzi otuluka mu thanthwe. Moto ukutsika ndi kunyeketsa nsembe limodzi ndi Eliya.
Ulosi ukukwaniritsidwa tsiku lililonse. Mawu olonjezedwa a Mulungu akuwonetseredwa m’miyoyo yathu. Zinthu zikuchitika pozungulira ife. Mkwatibwi wadzikonzekeretsa Yekha pakumva ndi kukhulupirira Mawu. Ndife Mawu opangidwa thupi.
Zoonadi tafika. Nthawi yayandikira. Mkwatibwi akusangalala ndikulumikizana pamodzi padziko lonse lapansi kuposa kale. Mneneri akutsimikizira Mkwatibwi potiuza ife kuti ndife awunsembe achifumu a Mulungu, fuko loyera, anthu achilendo amene aitanidwa, osankhidwa, osankhidwa, ndi oikidwa pambali.
IFE TSOPANO NDIFE Ana amuna ndi Ana Aakazi a Mulungu, otsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu; osati ndi munthu, koma ndi Mzimu. Ife tikudziwa, popanda mthunzi umodzi wa kukaikira, IFE NDIFE MKWATIBWI WAKE. CHIKHULUPIRIRO chathu chikufika patali kwambiri tsiku lililonse. Palibe kutiletsa kapena kutichedwetsa, Mulungu waziululira ndi kuzika Izo mu mtima mwathu ndi mu moyo wathu.
Mkwatibwi akuzindikira kwathunthu chomwe ife tiri. Ife tiri mu Dziko lathu lolonjezedwa lauzimu, mu eni ake onse. Tili ndi mtendere wa Kumwamba, madalitso a Kumwamba, Mzimu wa Kumwamba. ZONSE NDI ZATHU. Ife tikungokonzekera zomwe Iye ali nazo kwa ife lotsatira.
Lipenga la Ambuye lidzawomba, ndipo akufa mwa Khristu adzawuka poyamba.
Matupi akumwamba awa adzatsika ndi kuvala matupi a padziko lapansi, aulemerero ndipo adzasinthidwa m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso. Ife tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo, kukakomana ndi Ambuye mu mlengalenga.
Ndi Tsiku lotani. Ndi Nthawi yotani. Palibe njira yoti ndinene m’mawu aumunthu zomwe tonse tikumva m’miyoyo yathu. Mitima yathu ikuthamanga. Sitikupanga kuti izi zichitike, Mzimu Woyera uli ngati chitsime chotumphukira mkati mwathu. Mkwatibwi wakhala akuyembekezera mphindi iyi kuyambira masiku a Adamu…NDIPO IFE TSOPANO.
Tikukulandirani inu. Tikukuitanani inu. Tikukuchondererani inu. Bwerani mudzalumikizane nafe pa nthawi yodabwitsa kwambiri yomwe ngakhale dziko lakhala likuidziwa, pamene tikumva Liwu la Mulungu likuwululira Mawu Ake kwa ife Lamlungu lino pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, pamene tikumva: 60-0518 kukhazikitsidwa ,Gawo la Chiwiri.
M’bale. Joseph Branham
Malemba oti muwerenge Uthenga usanayambe:
Genesis 1:26
Aefeso Mutu Woyamba
Aroma 8:19
Agalatiya 1:6-9
Ahebri Chaputala Chachisanu ndi chimodzi
Yohane 1:17