26-0201 Mafunso ndi Mayankho #2

26-0201 Mafunso ndi Mayankho #2

Uthenga: 64-0823E Mafunso ndi Mayankho #2

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Ana A Mphungu,

Kumene kuli nyama, ndi komwe Mkwatibwi adzasonkhana pamodzi. Ndipo kwa ife, pali malo amodzi okha angwiro omwe ife tingapezeko Manna ya tsopano amenewo: mwa kukanikiza kusewera ndikumva Liwu la Mulungu pa matepi.

Kakamba za Manna YATSOPANO, kodi tingayambe kuganiza zomwe tili nazo ku songa ya Chala chathu? Liwu lenieni la Mulungu likulankhula ndi Mkwatibwi Wake wokondedwa pa tepi, komwe kulibe kuganiza, kulibe kudabwa, kulibe kufunsa kapena kukayikira kuti yemwe tikumva ndi Mulungu, pogwiritsa ntchito liwu la munthu, kulankhula Pakuti Atero Ambuye kwa Mkwatibwi Wake.

Mwa vumbulutso, ife timakhulupirira kuti Ndi malo OKHAWO omwe ife tingapiteko ndi kupumulitsa miyoyo yathu kuti Mawu omwe tikumva si mawu a munthu, komanso sikutanthauzira kwake kapena lingaliro lake kapena wonjezeredwa kwa Iwo, koma iwo Ndi Mawu oyera a Mulungu akulankhula kwa ife ana a Mphungu, akuwulula Mawu Ake.

Ife timasonkhana mozungulira Mawu. Timawerenga Mawu Ake m’Mabaibulo athu. Ife iimamvanso anthu odzonzedwa ndi Mulungu ndinso amuna oyitanidwa odzazidwa ndi Mzimu Wake Woyera, akubwereza ndi kulalikira Mawu a Mulungu, koma mutsiku lathu , Mulungu wapereka malo momwe ife tingamve MAWU Ake ANGWIRO AKULANKHULIDWA, mwa kukanikiza kusewera.

Atate Koteronso amapatsanso Mkwatibwi Wake mwayi wofunsa mafunso omwe anali pamtima pathu kuti tikhale ndi yankho langwiro:

  • Kodi Satana angagwiritse ntchito mphatso ya malilime kapena ulosi mwa munthu amene ali ndi Mzimu Woyera?
  • Kodi Yesu ankatanthauza chiyani mu Mateyu 12, vesi 32?
  • Chonde fotokozani 1 Akorinto 13:8-12.
  • Kodi akazi ndiwololedwa kugwira ntchito mmabwalo awunyinji wa anthu pomwe iwo alinaye mwamuna ndi ana athanzi labwinobwino?
  • Kodi n’kulakwa kuti mkazi azimanga tsitsi lake?

Mulungu wapereka njira zambiri zodalitsira ndi kulimbikitsira Mkwatibwi Wake, koma pali malo amodzi okhawo omwe wapereka komwe Mkwatibwi Wake angakhale ndi chidaliro chama peresenti 100 kuti chomwe iwo akumva ndi MAWU AKE ANGWIRO. Kasupe Mmodzi wa Madzi Amoyo komwe Ana Amphungu amatha kumwa kuchokera ku iye komwe kulibe kuthekera kwa kuipitsidwa kulikonse. KUKANIKIZA KUSEWERA.

Ine ndikukuitanani inu kuti mudzamwe kuchokera ku Kasupe ameneyo Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi ya ku Jeffersonville, komwe ife tidzava 64-0823E “Mafunso ndi Mayankho #2.”

M’bale Joseph Branham