ISITALA 2026- MWAMBO WA MGONERO WA PADELA NDI KUSAMBITSANA MAPAZI

Okondedwa Azanga Nzika Za Ufumu,

Isitala iyi ikulonjeza kukhala Isitala yayikulu kwambiri yomwe Mkwatibwi adakhalapo nayo. Ife Takhala tikukhala pamaso pa Mwana, tikucha, tikuzindikira kuti ndife ndani. Chidzalo cha Yesu Khristu chikupangidwa kuonetseredwa mwa wina aliyense wa ife pamene Mawu Ake, Liwu Lake, likufuula, kuchokera Kwa Mphungu yaikulu kupita kwa ti ana ta mphungu, kutiitana ife ku Mgonero Wathu wa Ukwati.

Chaka chilichonse nthawi ino Mkwatibwi amakhala pansi pa kuyembekezera kwakukulu kwa Isitala ilimkudza kumapeto kwa sabata. Nthawi yomwe Iye adzatigwirizanitsa kuchokera padziko lonse lapansi kwa masiku anayi mopitiliza, kumulambira Iye, kumuyamika Iye, kumutamanda Iye; chifukwa Iye wauka ndipo akukhala mwa wina aliyense wa ife. Mkwati ndi Mkwatibwi akukhala M’MODZI.

Iye akutipatsa ife nthawi yapaderayi kuti titsekere kunja zinthu zonse za dziko lapansi zomwe zatizungulira ife ndikukhala basi ndi Iye . Palibe zosokoneza za dziko lino, pamene tikupanga dziko lathu ndi Iye. Tsekani zitseko zathu, zimitsani zathu zonse zamagetsi ndi chilichonse chomwe chimatisokoneza kwa Iye.

Chikhumbo chachikulu chomwe wina aliyense wa ife ali nacho ndikukhala pafupi ndi Iye. Ife tikufuna kukhala moyo wodzipereka kwambiri kwa Iye; kukhala nthawi zonse mu chifuniro Chake changwiro. Kukhala okonzeka Kukubwera Kwake. Palibe chilichonse m’dziko lino, kapena m’moyo wathu, chofunika kwambiri kuposa ichi.

Iye watipatsa mwayi wapaderawu kuti tingokhala ndi Iye, kulankhula ndi kusinkhasinkha za Iye. Kukhala pamaso Pake ndikutsegula mitima yathu kwa Iye. IZO ZIDZAKHALA ZOSINTHA MOYO KWA MKWATIBWI WAKE!

Iye akudziwa kuti zingakhale zovuta kwa ena a inu omwe muli ndi ana, banja, ndi maudindo ena omwe tili nawo, koma ngati tigwiritsa ntchito mphindi iliyonse yaulere tiyenera kulankhula ndi Iye, kuyandikira kwa Iye, kutsegula mitima yathu kwa Iye, padzakhala kusintha kwakukulu mu kuyenda kwathu ndi Iye, mpaka sitidzakhalanso chimodzimodzi.

Monga momwe Iye adachitira m’tsiku la Mose pamene Iye adawakhazika ana Ake m’nyumba zawo, magazi anali atapakidwa ndipo anali kudzipangitsa Iwo eni kukonzekera Kutuluka kwawo; momwemonso sabata yapadera iyi ya Isitala yomwe Iye adakonza idzakhala ya aliyense wa ife.

Ulendo wathu udzakhala motere:

LACHINAYI

Unali Lachinayi usiku pamene Ambuye Yesu adadya Mgonero Womaliza ndi ophunzira Ake, pokumbukira Paskha asanatuluke ana a Israeli. Ndi mwayi waukulu bwanji womwe ife tili nawo wolankhulana ndi Ambuye m’nyumba zathu, kumapeto kwa sabata yathu yopatulika, ndikupempha Iye kuti atikhululukire ife machimo athu, ndi kutipatsa zonse zomwe tikufunikira paulendo wathu.

Atate Wakumwamba, tikuyamikira nthawi ino, nthawi inaso yosonkhana pamodzi, mbali ino ya Umuyaya. Ndipo ife tikuyang’anira m’mawa uno kuti mphamvu zatsopano zichokere kwa Inu, kutipatsa kulimba mtima paulendo womwe uli patsogolo. Ife tasonkhana monga momwe ana Achiheberi adachitira m’mawa kwambiri, kuti titenge mana omwe adaperekedwa kwa iwo usiku wonse, kuti awathandize tsiku lotsatira. Ife tasonkhana kuti tidye Mana a uzimu, m’mawa uno, kutipatsa mphamvu paulendo.

Tiyeni tonse tiyambe pa nthawi ya 6:00 PM. pa nthawi yanu yapafupi kuti mumve Mgonero 62-0204, kenako mneneriyo adzatitengera ku Utumiki wathu wapadera wa Mgonero ndi Kutsukana Mapazi ku m’maliziro a tepiyo, yomwe idzaseweredwa pa pulogalamu ya Lifeline (mu Chingerezi), kapena mutha kupanga dawunilodi utumikiwu mu Chingerezi kapena mu zilankhulo zina podina ulalo womwe uli pansipa.

LACHISANU

Tiyeni ife tipite ku pemphero ndi mabanja athu nthawi ya 9:00 AM, ndipo kenako nthawi ya 12:00 PM, kupempha Ambuye kuti akhale nafe ndikudzaza nyumba zathu ndi Mzimu Woyera pamene tikudzipereka ife eni kwa Iye.

Malingaliro athu abwerere m’mbuyo ku tsiku lija ku Kalvari, zaka zoposa 2000 zapitazo, ndikuwona Mpulumutsi wathu atapachikidwa pamtanda. Tiyeni tikumbukire mtengo waukulu umene Iye analipira chifukwa cha ife. Iye anali Mwana wa Mulungu wopanda uchimo, koma anayenera kuvutika monga momwe panalibe munthu wina aliyense akanavutikira, chifukwa machimo athu anaikidwa pa Iye.

Iye anayenera kumutumiza ku gehena wolangidwa (Mukuona?), chifukwa Iye ananyamula machimo athu. Ndipo Khristu anafa, osati wolungama; Khristu anafa wochimwa. Mukuona? Khristu sanachimwepo Iye mwini, koma Iye ananyamula machimo athu pa Iye.

Kenako pa 12:30 PM, tiyeni tilumikizane pamodzi m’nyumba zathu ndikunva 57- 0419 Ungwiro.

Kenako tiyeni tilumikizane pamodzi m’pemphero mwachangu nthawi yomweyo pambuyo pa utumiki, pokumbukira kupachikidwa kwa Ambuye wathu.

LOWERUKA

Tiyeni tonse tibwere pamodzi mu pemphero nthawi ya 9:00 AM ndi 12:00 PM, ndikukonzekeretsa mitima yathu zinthu zazikulu zomwe Iye adzatichitira pakati pathu.

Ine ndikumva Iye akunena kuti, “Satana, bwera kuno!” Iye ndiye Bwana tsopano. Akufikira, akutenga kiyi ya imfa ndi gehena m’mbali mwake, naipachika pambali Pa Iye Mwini. “Ine ndikufuna nditumikire kukudziwitsani inu. Mwakhala wonyenga kwa nthawi yayitali. Ine ndine Mwana wa Mulungu wamoyo wobadwa kwa namwali. Magazi anga akadali onyowa pamtanda, ndipo ngongole yonse yathunthu yalipidwa! Iwe Siwulinso ndi ufulu mkomwe. Iwe wavulazidwa. Ndipatse ine makiyi amenewo!”

Kenako nthawi ya 12:30 PM, tonse tidzasonkhana pamodzi kuti timve Mawu: 57-0420 Kuikidwa M’manda.

Ndi tsiku la KALATA YOFIWIRA kwambiri bwanji yomwe iyo ili kwa Mkwatibwi Wake padziko lonse lapansi.

Ndiye tiyeni tigwirizanenso pamodzi mu pemphero nthawi yomweyo utatha utumiki.

LAMULUNGU

Tiyeni tidzuke kaye m’mawa monga momwe M’bale Branham adachitira m’mawa pamene bwenzi lake laling’ono, phwiti, adamudzutsa iye nthawi ya 5:00 AM. Tiyeni ife tingoyamika Ambuye chifukwa choukitsa Yesu kwa akufa:

Masiku asanu m’mawa uno, bwenzi langa laling’ono lofiira linaulukira pawindo ndipo linandidzutsa ine. Zikuoneka kuti mtima wake waung’ono unaphulika, ndikunena, “Iye Wauka.”

Nthawi ya 9:00 AM tiyeni tigwirizanenso mu Tcheni chathu cha pemphero, kupemphererana wina ndi mnzake ndikukonzekera kumva Liwu la Mulungu.

Nthawi ya 9:30 AM, Ife tidzasonkhana pamodzi kuti timve Uthenga wathu wa Isitala: 65-0418M Ndi Kutuluka kwa Dzuwa.

Nthawi ya 12:00 PM tidzakweza mawu athu kwa Iye kumuyamika chifukwa cha Mphamvu Yofulumizitsa.

Nthawi ya 3:00 PM, tiyeni tigwirizanenso m’pemphero, kumuyamika chifukwa cha MAPETO A SABATA YODABWISTSA YOMWE IYE WATIPATSA IFE NDI IYE NDI MKWATIBWI WAKE KUZUNGULIRA DZIKO LONSE LA PANSI.

Kwa abale ndi alongo anga akunja, monga chaka chatha, ine ndikufuna kukuitanani kuti mugwirizane nafe pa nthawi ya ku Jeffersonville, nthawi zonse zamapemphero pa ndondomekoyi. Ine ndikuzindikira, komabe, kuti kusewera Matepi Lachinayi, Lachisanu, ndi Loweruka masana pa nthawi ya ku Jeffersonville kungakhale kovuta kwambiri kwa ambiri a inu, choncho chonde musazengereze kusewera Mauthenga amenewo panthawi yomwe ingakhale yoyenera kwa inu. Komabe, ndikufuna kuti tonse tigwirizane Lamlungu nthawi ya 9:30 AM, nthawi ya ku Jeffersonville, kuti timve Uthenga wathu wa Lamlungu pamodzi.

Ndikufunanso kukuitanani inu ndi ana anu kuti mukhale nawo m’mapulojekiti a Creations, kulemba manyuzipepala, ndi maphikidwe, omwe banja lanu lonse lingasangalale nawo limodzi. Tikuganiza kuti mudzawakonda chifukwa onse akuchokera pa MAWU omwe tidzakhala tikuva kumapeto kwa ndondomeko kwa sabata ino.

Zidziwitso pa za kakonzedwe ka mwambo wa mgonero , zinthu zomwe zidzafunike pa mapulojekiti a Creations, ndi zidziwitso zina, onani maulalo omwe ali pansipa.

Tiyeni ife titseke mafoni athu kumapeto kwa sabata ya Isitala kupatula kujambula zithunzi, kumvetsera Zobwereza Za Pa Tsiku, ndikusewera matepi kuchokera ku pulogalamu ya Table, pulogalamu ya Lifeline, kapena ulalo wopangidwa dawunilodi.

Iwo ndi ulemu waukulu kwa ine kukuitanani inu ndi banja lanu kuti mudzabwere pamodzi ndi Mkwatibwi kuzungulira padziko lonse lapansi kumapeto kwa sabata yodzaza ndi KUPEMBEDZA, MATAMANDO NDI MACHIRITSO. Ine ndikukhulupirira kuti ndikwenikweni ndi kumapeto kwa sabata komwe kudzasintha moyo wanu kwamuyaya.

M’bale Joseph Branham