Uthenga: 64-0802 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko
- 26-0111 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko
- 24-0414 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko
- 23-0312 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko
- 22-0918 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko
- 21-0502 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko
- 19-1103 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko
- 17-0924 Kwawo Kwa Mtsogolo Kwa Mkwati Wa Kumwamba Ndi Mkwatibwi Wa Padziko
Wokondedwa Wanga Kwambiri Wokomamtima.
Ine ndimakukonda iwe kwambiri. Iwe ndiwe mnofu wa mnofu wanga, ndi fupa la fupa langa. Ngakhale ndisanalenge nyenyezi, mwezi, chilengedwe changa chonse, ndinakuona iwe ndipo ndinakukonda iwe kenako. Ndinkadziwa kuti iwe unali gawo la Ine, mmodzi wanga komanso wokomamtima yekhayo. Iwe ndi ine tinali MMODZI.
Tsiku limene ine ndakhala ndikulilakalaka ndi kuliyembekezera kuyambira pamene ndinakuonani inu mapeto ake lafika.Tsopano ine ndikukuitanani inu ndikukugwirizanitsani inu kuchokera kummawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kum’mwera, ndi Liwu Langa. Inu ndinu malingaliro Anga, Mawu Anga, Mkwatibwi Wanga, opangidwa kuwonetseredwa.
Ine ndakhala ndikulakalaka kukuuzani inu chilichonse chomwe chili mumtima mwanga, kotero ine ndinazilemba izo mwa aneneri Anga ndipo ndinasunga Chilichonse kwa zaka zikwizikwi. Ambiri awerenga, ndipo akukhulupirira kwa zaka mazana ambiri, koma ndasunga zinthu zambiri zachinsinsi mpaka INU MUNAFIKA. Ndi inu nokha amene ine ndidzakuuzani.
Iwo ankafunitsitsa kudziwa ndikumva zinthu zodabwitsa zonsezi zomwe ndazisunga mobisa, koma monga momwe ndinakulonjezerani inu, ndakhala ndikuzisunga zachinsinsi mpaka pano, kuti zikhale za INU, MMODZI WANGA KOMANSO YEKHAYO.
Ine ndinakulonjezani inu kuti ine ndikanadzabweranso ndikudziulula ndekha mu thupi la munthu, kuti Ine ndikanakuuzani inu, ndikukuwululirani inu zinthu zonse izi. Ndimafuna kuti inu mumve LIWU LANGA likulankhula kwa inu mwachindunji.
Ine ndadzoza ena ambiri ndi Mzimu Wanga Woyera kuti akuuzeni inu za chikondi Changa, koma monga momwe ine ndakhala ndikuchitira nthawi zonse, ndipo ine sindingakhoze kusinthe, ine ndidasankha munthu m’modzi: Mngelo wanga, mneneri wanga, kuti akhale Liwu Langa kuti Ine ndikhoze kuyankhula Pakuti Atero Ambuye kwa inu.
Ine ndimafuna kukuuzani inu, inu simunapulumutsidwe pa tsiku linalake. Inu Munapulumutsidwa kwa nthawi zonse. Ine ndangobwera kudzakuwombolani inu. Munapulumutsidwa kuchokera pachiyambi chifukwa munali ndi Moyo Wamuyaya kuyambira pachiyambi. Chifukwa chake, m’maso mwanga, machimo anu onse sangawonekereso mpang’ono pomwe kwa ine, chinthu chokhacho chomwe ndimamva ndi liwu lanu. Ndimangoona choyimira chanu.
Momwe Ine ndimafunitsitsa kukuuzani inu zinthu zambiri. Mtima wanga ukudzaza ndi chisangalalo. Momwe Ine Ndikufunitsitsira kukhala ndi Mgonero Wathu wa Ukwati, Zaka Chikwi zathu pamodzi. Kuti ndikuuzeni mwatsatanetsatane zonse zokhudza Kwathu Kwamtsogolo; Momwe ndakukonzerani chilichonse cha inu, ndi chilichonse chokhudza chanu.
Wokomamtima wanga, ngati inu mukuganiza kuti ndi bwino tsopano kumvetsera Liwu Langa likulankhula kwa inu, tangodikirani, uwu ndi mthuzi chabe wa momwe zidzakhalire tikamakakhala mu Mzinda umenewo limodzi. Mneneri wanu adzakhala khomo loyandikira pafupi ndi inu; iye adzakhala wayandikana naye wa inu.
Ife tidzayenda m’misewu yagolide ndikumwa madzi ochokera ku kasupe pamodzi. Tidzayenda kupita ku pamaradaiso a Mulungu ndi Angelo akuzungulira dziko lapansi, kuimba nyimbo za zafuko…Ndi tsiku lotani!
Ine ndikudziwa kuti msewu umaoneka wothyokathyoka, ndipo nthawi zina zimakhala zolimba Kwa inu , koma udzakhala wochepa kwambiri, wochepa kwambiri, pamene tikukhala limodzi wina ndi mzake.
Tsopano, ine kamodzinso ndikusonkhanitsaninso inu ndi kulankhula nanu Lamlungu lino nthawi ya 12:00 PM, nthawi yaku Jeffersonville, ndikukuuzani zonse za “64-0802 Kwawo Kwamtsogolo kwa Mkwati Wa Kumwamba ndi Mkwatibwi Wapadziko Lapansi”. Ine Sindingathe kudikira kuti ndikhale nanu nthawi imeneyo kenako.
Kumbukirani, ndipo musaiwale, ndimakukondani inu kwambiri.
M’malo mwa Iye,
M’bale Joseph Branham
Malemba:
Mateyu Woyera 19:28
Yohane Woyera 14: 1-3
Aefeso 1:10
2 Petro 2: 5-6 / Mutu Wachitatu
Chivumbulutso 2: 7 / 6: 14 / 21: 1-14
Levitiko 23:36
Yesaya Mutu Wachinayi / 28: 10 / 65: 17-25
Malaki 3: 6