Uthenga: 64-0726M Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake
- 25-1228 Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake
- 24-0324 Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake
- 22-0904 Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake
- 21-0418 Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake
- 19-1110 Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake
- 17-1015 Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake
- 16-0626M Kuzindikira Tsiku Lanu Ndi Uthenga Wake
Wokondedwa Mkwatibwi Wodulidwa,
Lero lino, mpingo wayiwala mneneri wawo. Iwo Samufunanso Iye mpang’ono pomwe kuti azilalikira m’matchalitchi awo. Iwo amanena kuti ali ndi abusa awo kuti aziwalalikira iwo ndi kumatchula mobwereza mawu ndi kumasulira Mawu. Kulalikira n’kofunika kwambiri kuposa kumvetsera liwu la Mulungu pa matepi m’matchalitchi awo.
Koma Mulungu Iye ankadziwa kuti ankayenera kukhala ndi mneneri Wake; mmenemu ndi momwe nthawi zonse Iye amaitanira ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake. Iye anatidula kuchokera m’mitundu yonse ndi Lupanga Lake lakuthwa konsekonse, Mzimu Wake Woyera, Liwu Lake loyankhulidwa ndi mneneri Wake.
Iye watidula ife ndi Liwu limenelo. Ndicho chifukwa chake Iye analijambula ilo ndi kuliyika pa tepi. Mwa Vumbulutso ife timawona momwe Malemba alili angwiro! Mkwatibwi sangache pokhapokha Mwana atamuchetsa iye.
Ziribe kanthu ndi mochuluka bwanji momwe inu mungalalikire, chirichonse chimene inu mungachite, icho sichingakhoze kucha, icho sichingawonetseredwe, icho sichingatsimikiziridwe; kokha ndi Iye Amene anati, “Ine ndine Kuwala kwa dziko lapansi,” Mawu.
Mawu adatiuza ife kuti Mzimu Woyera mwiniwake adzabweranso ndi kudzatichetsa ife, kudzatsimikizira, kudzasonyeza umboni ndi kudzadzipanga Iyemwini kudzadziwonetsera. Kuwala kwamadzulo kwafika. Mulungu akudzionetsera yekha mu thupi kuti ayitane Mkwatibwi Wake.
Iye ndiye amene wakuitanani INU ndi Mzimu Wake Woyera, Mawu Ake, Liwu lake. Iye ndiye amene anakusankhani INU. Iye ndiye amene akukuphunzitsani INU. Iye ndiye amene akutsogolerani INU. Ndi chiyani? Mzimu Wake Woyera, Liwu Lake likuyankhula MWACHINDUNJI KWA INU.
Koma izo ndi zakale kwambiri kwa iwo lero lino. Iwo sangakhoze kusewera matepi m’matchalitchi awo. Iwo Sakuzindikira. Ndicho chifukwa chake ali mu mkhalidwe womwe ali. Koma kwa inu, izo zawululidwa kuti ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu, IZO NDI PAKUTI ATERO AMBUYE KWA INU.
Chotero pakuyenera kubwera a—a—a Mphamvu, Mzimu Woyera Mwiniwake, kuti udzachetse, kapena kutsimikizira, kapena kudzatsimikizira, kapena kudzawonetsera icho chimene Iye ananeneratu kuti chikanadzachitika mu tsiku lino. Kuwala kwa kumadzulo kukupanga zimenezo. Ndi nthawi yotani!
Ife ndife Mkwatibwi wangwiro wa Mawu a Mulungu amene mneneri wake anaona mu masomphenya. Ife ndiwo amene Iye anatumiziridwako mneneri wake kuti awaitane ndi Mawu ake, ndipo iwo tsopano akukhala ndi CHITSITSIMUTSO, chifukwa tsopano ife tikudziwa chimene ife tiri.
Kutsitsimutsa, apo, ndi mawu omwewo amene amagwiritsidwa ntchito kwina kulikonse, ine ndinangowayang’ana iwo, amatanthauza, “chitsitsimutso.” “Iye adzatitsitsimutsa ife akadzatha masiku awiri.” Izo zidzakhala, “Patsiku lachitatu Iye adzatitsitsimutsanso ife, Iye atatibalalitsa ife, ndi kutichititsa khungu, ndi kuting’amba ife.”
Atate anatuma mneneri wake kuti ayang’anire Mkwatibwi wake kuti tisachoke pa mzere. Kumbukirani, awa anali masomphenya!
Mkwatibwi anadutsa malo omwewo amene Iye anali pamene Iye anali pachiyambi. Koma ine ndinali kumuwona Iye akuchoka pa sitepe, ndi kumayesera kumukokera Iye mmbuyo.
Koma kodi “iye” angamukokere m’mbuyo bwanji lero? “Iye”, mwamunayo, sali pano padziko lapansi. NDI MAWU! Kodi Mawu OKHA Otsimikiziridwa a lero ndi ati? Liwu la Mulungu pa matepi.
Atumiki ai oyitanidwa kulalikira Mawu potchula mobwera zomwe mneneriyo ananena. Malinga ndi mneneri mwiniwake, iwo sayenera kunena china chilichonse mochuluka
Zoonadi, aIi oyitanidwa kuphunzitsa ndi kulalikira Mawu amenewo. Koma pali LIWU LIMODZI LOKHA LOMWE NDILOTSIMIKIZIRIDWA NDI MULUNGU IYEMWINI KUTI NDILO PAKUTI ATERO AMBUYE.
Chotero ine ndikunena, mu Dzina la Yesu Khristu! Musati inu muwonjezere kanthu kamodzi. Musati mutenge, kuyika malingaliro anu omwe mwa Iwo. Inu muzingonena chimene chikunenedwa pa matepi awo. Inu muzingochita chimodzimodzi chimene Ambuye Mulungu wakulamulirani kuti muchite. Musati muwonjezere kwa Iwo.
Ngati inu munena kuti “ameni” pa mawu aliwonse amene m’busa wanu kapena mtumiki wanu akunena, inu mwatayika. Koma ngati munena kuti “AMENI” PA MAWU ALIWONSE AMENE MULUNGU ANAYANKHULA KUDZERA MWA MNENERI WAKE PA MATEPI, INU NDINU MKWATIBWI NDIPO MUDZAKHALA NDI MOYO WOSATHA.
Mneneri wa Mulungu anali munthu amene Mulungu anasankha kulankhula kudzera mwa iye. Kunali kusankha Kwa Mulungu kumugwiritsa ntchito iye kulankhula Mawu Ake ndikuwayika pa matepi kuti Mkwatibwi nthawi zonse akhale ndi PAKUTI ATERO AMBUYE WOTI AZIMVERA.
Iye sakufuna kuti Mkwatibwi Wake azidalira zomwe anthu ena akunena, kapena kutanthauzira kwawo Kwa Mawu Ake. Iye akufuna kuti Mkwatibwi Wake azimva kuchokera pakamwa pake kupita m’makutu mwawo. Iye sakufuna kuti Mkwatibwi Wake azidalira wina aliyense koma Iyemwini.
Ife tikadzuka m’mawa, timakonda iye kuti atiuze ife kuti, “Mmawa wabwino abwenzi. Ine Ndilankhula ndi inu lero ndikukuuzani momwe ine ndimakukonderani inu komanso momwe inu ndi ine tili AMODZI. Ndili ndi ambiri omwe ndidzawapatse moyo wosatha, koma INU nokha ndinu Mkwatibwi wanga wogwiridwa pa dzanja. INU nokha ndi amene ine ndapereka Vumbulutso maziko adziko asanakhazikitsidwe .
Ambiri amakonda kundimva, koma ine ndakusankhani inu kuti mukhale Mkwatibwi Wanga. Pakuti mwandizindikira Ine ndipo mwakhala ndi Mawu Anga. Inu Simunanyengerere, simunasewere, koma mwakhalabe okhulupirika ndi Mawu Anga.
Nthawi yayandikira. Ndikubwera kudzakutengani posachedwa. Choyamba, mudzawona omwe ali kale ndi ine tsopano. O, momwe iwo akufunira kukuonani inu ndikukhala nanu. Musadandaule ana aang’ono, chilichonse chili pa nthawi yake, basi pitirizani kumenyera.”
Monga mtumiki wa Uthenga, ine sindingathe kuwona chinthu chimodzi chatsalira koma kupita kwa Mkwatibwi.
M’bale Joseph Branham
Uthenga: 64-0726M “Kulizindikira Tsiku Lanu ndi Uthenga Wake”
Nthawi: 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville
Malemba oti muwerenge musanamve Uthenga:
Hoseya: Chaputala 6
Ezekieli: Chaputala 37
Malaki: 3:1 / 4:5-6
II Timoteo: 3:1-9
Chivumbulutso: Chaputala 11