25-0824 Mgonero

Uthenga: 65-1212 Mgonero

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mawu Otsimikiziridwa Mkwatibwi Yekha,

Ndife othokoza bwanji kwa Mzimu Woyera chifukwa cha Vumbulutso loona la Mawu Ake otsimikiziridwa a lero. Ambiri amadzinenera kuti amakhulupirira M’bale Branham kuti ndi mneneri wa Mulungu amene amakwaniritsa Malemba olonjezedwa a iyemwini, koma Vumbulutso loona la Mawu ndi dongosolo la Mulungu labisika kwa iwo.

Ndi kalata yachikondi iliyonse yomwe Mkwatibwi amamva, Mulungu amatsimikizira kwa ife kuti tili mu Chifuniro Chake changwiro pomvera Njira Yake yoperekedwa ya lero, Liwu la Mulungu pa Matepi.

Ndipo ife tikuyenera kumutsatira Iye, ndiyo njira yokhayo yokhalira nawo Moyo Wamuyaya. Chotero utsogoleri wa Mulungu ndi: kutsatira Mawu otsimikiziridwa a ora mwa Mzimu Woyera.

NJIRA YOKHA yopita ku Moyo Wamuyaya ndi: Mzimu Woyera ukukutsogolerani kuti muzitsatira Mawu otsimikiziridwa. Ndani ali nawo Mawu otsimikiziridwa a lero? Kodi Mulungu anamusankha ndani kuti azitanthauzira Mawu Ake? Kodi Mulungu ananena kuti linali liwu lake la ndani lero? Kodi Mulungu Mwiniwake anati ndani anali mtsogoleri wotsimikiziridwa kuti atsogolere Mkwatibwi Wake lero? Utumiki?

Chimodzimodzi monga ine ndinanena, mphungu yaing’ono pamene iyo inamva Liwu la Mkwati, iyo inapita kwa ilo, odzozedwa, Mawu otsimikiziridwa a Mulungu a tsiku lotsirizali.
Nowa anali Mawu otsimikiziridwa a tsiku lake.
Mose anali Mawu otsimikiziridwa a tsiku lake.
Yohane anali Mawu otsimikiziridwa

Iwo akhoza kupotoza chirichonse kapena kutanthauzira kulikonse kwa Iwo akufuna, koma:
WILLIAM MARRION BRANHAM NDI MAWU OTSIMIKIZIRIDWA A MULUNGU A LERO!!

Chotero utsogoleri wa Mulungu ndi: kutsatira Mawu otsimikiziridwa a ora mwa Mzimu Woyera.

Ndipo kusewera Liwu lotsimikiziridwa la Mulungu mu mpingo wanu si chinthu chofunika kwambiri chimene Mkwatibwi angachite? Ndikofunikira kwambiri kumva liwu losiyana?

Kodi ndi gulu la amuna ndi utumiki wawo umene udzalumikizana ndi kutsogolera Mkwatibwi? Kodi Mkwatibwi adzalumikizidwa ndi zomwe utumiki ukunena? Onse akunena zosiyana, ndiye titsatire ndani?

Kodi kutanthauzira kwawo kwa Uthenga uwu ndi kumene ife tidzaweruzidwa nako? Kodi iwo ali nalo Lawi la Moto likutsimikizira utumiki wawo? Kodi ndiko kutanthauzira kwawo kwa Mawu Mtheradi wanu?

Mneneri anati Mkwatibwi adzakhala WOLUMIKIZANA. Dzifunseni nokha, ndi chiyani chiti chidzachititse uneneri uwu kuti ukwanilitsidwe kuti Ambuye abwere ndi kudzamukwatula Mkwatibwi Wake?

Ndiyeno, pamene anthu a Mulungu ayamba kusonkhananso palimodzi, pamakhala chiyanjano, pamakhala mphamvu. Mukuona? Ndipo paliponse pamene anthu a Mulungu abwera palimodzi kwathunthu, ine ndikukhulupirira chiukitsiro chidzachitika apo ndiye. Padzakhala nthawi ya mkwatulo pamene Mzimu Woyera udzayamba kuwasonkhanitsa iwo. I—iwo adzakhala apang’ono, ndithudi, koma kudzakhala kuli kusonkhana kwakukulu.

Kodi padzakhala kusonkhana kwakukulu kuzungulira utumiki wa munthu wina, kupatulapo mneneri wotsimikiziridwa wa Mulungu? Kodi lidzakhala GULU la atumiki chifukwa ena mwa awutumiki wofutukuka pasanu amanena kuti MUSAMASEWERE LIWU la Mulungu mu tchalitchi mwanu, ndi zolakwika. Kodi iwo adzatsogolera Mkwatibwi ndiye?

CHONDE NDITHANDIZENI! KODI NDI MTUMIKI UTI YEMWE NDIYENERA KUMUTSATIRA POMWE NDIKUFUNA KUKHALA WOLUMIKIDWA NAWO PA PAMSONKHANO WAWUKULU UWO.

Ena amati utumiki wofutukuka pasanu a Mabingu Asanu ndi awiri adzafikitsa Mkwatibwi ku ungwiro . Atumiki ena awutumiki wofutukuka pasanu amati masiku a utumiki wa Munthu Mmodzi atha. Atumiki ena a utumiki wofutukuka pasanu amati ife tiyenera kubwerera ku Pentekosite. Ena amati Uthenga SULI M’theradi. Ena amati ukamasewera matepi ndiwe wokhulupirira milungu. Onse amanena chinachake chosiyana, ndipo ONSE ali ndi matanthauziridwe osiyana, malingaliro osiyana, koma aliyese wa iwo amanena kuti IWO akutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.

KODI NDI MTUMIKI WUTI WA UTUMIKI WOFUTUKUKA PASANU YEMWE NDIYENERA KUMUTSATIRA? Bola ngati ine nditsatila abusa “ANGA” awutumiki wofutukuka pasanu, ine ndidzakhala Mkwatibwi? Pali “Magulu” osiyanasiyana a atumiki wofutukuka pasanu. Atumiki 20 awa amasonkhana pamodzi ndi kuchititsa misonkhano yawo, koma 20 amatsutsana kwathunthu ndi azitumiki ena amene akukhala ndi misonkhano yosiyana…ndi misonkhano iti yomwe ine ndipite kuti ndikakhale wangwiro ndi wolumikizana…ena a iwo…onse a iwo?

Ndipo anthu amakhulupilira kuti CHISOKONEZO CHIMENECHI CHILUMIKIZITSA NDIKUMUFIKITSA KU UNGWIRO MKWATIBWI? Onse amati iwo ali Atumiki WOONA AWUTUMIKI WOFUTUKUKA PASANU WOITANIDWA NDI MULUNGU. Koma iwo sakukutsogolerani inu ku UTSOGOLERI WOONA WA MZIMU WOYERA, AKUKUKUTSOGOLERANI INU KWA IWO ENI NDIKU UTUMIKI WAWO.

Kwa ine, simukusowa ngakhale vumbulutso kuti mudziwe zomwe sizingagwirizane kapena kutsogolera Mkwatibwi yense. MAWU OKHA ati adzayanjanitse Mkwatibwi, mwa LIWU LA MULUNGU YEKHA PA MATEPI.

Abale ndi alongo, kulibwino kuti mudzuke ngati mukutsatira m’busa amene akungolalikira ndi kubwereza mawu Mawu, omwe ali odabwitsa ndipo ALI NDENDENDE chimene ayenera kuchita, koma osakuuzani, ndipo chofunika kwambiri, KUCHITA, posewera LIWU LA MULUNGU PA MATEPI MU MPINGO WANU.

M’bale Branham anatiuza kuti:

Tsopano, ife tiri ndi madongosolo Auzimu atatu okha omwe atsalira kwa ife: amodzi a iwo ndi—ndi mgonero, kutsukana-mapazi, ubatizo wa madzi. Ndi zinthu zitatu zokhazo. Ndiwo ungwiro, wa zitatuzo, mwaona.

Ine ndikufuna kuti ife tikhale ndi Chiyanjano cha Mgonero ndi kutsukana Mapazi Lamlungu lino, ngati Ambuye alola. Monga tinachitirapo m’mbuyomu, ndikukulimbikitsani inu kuti muyambe nthawi ya 5:00 PM. Mu nthawi ya m’dera lanu . Ngakhale kuti M’bale Branham ananena kuti atumwi amadya Mgonero nthawi iliyonse imene iwo ankasonkhana, iye ankakonda kuti azidya iwo nthawi yamadzulo, ndipo ankawutchula kuti Mgonero wa Ambuye.

Utumiki wa Uthenga ndi Mgonero udzakhala pa Wailesi ya Liwu, ndipo padzakhalanso ulalo wa fayilo yomwe mungatsitse, kwa iwo omwe sangathe kupeza Wilesi ya Liwu Lamlungu madzulo.

M’bale Joseph Branham