25-0601 Thunthu La Munthu Wangwiro

Uthenga: 62-1014M Thunthu La Munthu Wangwiro

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Zipilala Zamoyo,

Liwu limene tikulimva pa matepi ndi Urimu Tumimu wa Mulungu kwa Mkwatibwi Wake. Iwo tsopano wamulumikiza moyenera Mkwatibwi Wake palimodzi mu mtima umodzi ndi mtima umodzi kuti ukhale mpingo weniweni wodzazidwa-Mzimu, wodzaza ndi mphamvu ya Mulungu, utakhala palimodzi mu malo Ammwambamwamba, ukupereka nsembe zauzimu, matamando a Mulungu, ndi Mzimu Woyera ukuyenda pakati pathu.

Khristu anatitumizira ife Mzimu Wake Woyera kuti ulankhule kupyolera mwa mngelo wake wachisanu ndi chiwiri kutimanga ife aliyense payekha mu msinkhu wa Yesu Khristu, kuti ife tikhale nyumba ya mphamvu ndi malo okhalamo Mzimu Woyera, mwa Mawu Ake.

Ndife olandira a chirichonse. Ndi katundu wathu, NDI WA ife. Ndi mphatso ya Mulungu kwa ife, ndipo palibe amene angatilande iyo. NDI ZATHU.

“Chimene mudzapempha Atate mu Dzina Langa, Ine ndidzachichita.” Ndani angakane kalikonse pamenepo? “Indetu, indetu, Ine ndinena kwa inu, ngati inu munena kwa phiri ili, ‘Sumuka,’ musati mukaikire mu mtima mwanu koma khulupirirani kuti chimene inu mwanena chidzachitika, inu mukhoza kukhala nacho chirichonse chimene inu mwachilankhula.” Ndi malonjezo otani!  Osati kokha ku machiritso, koma chirichonse.

Ulemerero kwa Mulungu… CHILICHONSE CHOMWE IFE TIMAPEMPHA!

Kuyambira pachiyambi, chilengedwe chonse cha Mulungu chikubuwula ndi kuyembekezera tsiku limene ana athunthu a Mulungu adzaonekera. Tsiku limenelo lafika. Lero ndi tsiku limenelo. Iyi ndi nthawi imeneyo. Ndife ana aamuna ndi aakazi owonetseredwa a Mulungu.

Ndife chida chamoyo cha Mulungu chimene Iye akuyendamo, Iye akuwona mkati, Iye akulankhula, Iye akugwira ntchitomo. Ndi Mulungu akuyenda ndi mapazi awiri MWA IFE.

Ndife makalata ake olembedwa owerengedwa ndi anthu onse. Osankhidwa Ake, okonzedweratu, ana aamuna ndi aakazi otengedwa amene Iye akuwapanga kukhala munthu wamoyo, chifaniziro chamoyo, msinkhu wa munthu wangwiro.

koma kudzigwetsera tokha pamaso pa Mulungu Wamoyo, ukoma wamoyo, chidziwitso chamoyo, chipiriro chamoyo, umulungu wamoyo, mphamvu yamoyo, kubwera ndi Mulungu Wamoyo kumapangitsa munthu wamoyo fano lamoyo—thunthu la Mulungu!

Ndi Khristu, mu umunthu wa Mzimu Woyera pa ife, ndi ubatizo woona wa Mzimu Wake Woyera, ndi ukoma Wake wonse wosindikizidwa mwa ife. Mulungu, akukhala mwa ife mu Kachisi wotchedwa Nyumba. Kachisi wamoyo, wa mokhalamo Mulungu wamoyo; Mpingo wangwiro, kuti Mwalawapamutu Wangwiro utiphimbe ife.

Mulungu anatumiza mneneri kuti adzayitane ndi kutsogolera Mkwatibwi Wake. Anali Adamu Wake woyamba wobwezeretsedwa kwathunthu, msinkhu wa munthu wangwiro mu tsiku lathu, kuti awulule Mawu Ake kwa Mkwatibwi Wake.

Sindingathe kuchoka pamenepo. Palibe chomwe chingandisunthe. Sindisamala zomwe wina akunena; sizimandisuntha ngakhale pang’ono. Ndikhala pomwepo.

Ndidikirira, dikirani, dikirani, dikirani. Musapange kusiyana kulikonse. Iwo amakhala pomwepo. Ndiyeno, tsiku lina, ndidzafuula pamodzi ndi oyera mtima ena onse mogwirizana kuti: “Ife tikupumula ndi chitsimikizo pa Mawu aliwonse! Pa mtengo wa Kalvari.”

Ine ndikulonjeza mmawa uno kwa Iye ndi mtima wanga wonse kuti mwa chithandizo Chake ndipo mwa chisomo Chake, ine ndikupemphera kuti ndifunafuna tsiku ndi tsiku mosalekeza mpaka nditamverera chirichonse cha zofunikira zonsezi zikuyenderera mu kanthunthu kokalamba kangaka. Mpaka nditakhala kuwonekera kwa Khristu Wamoyo,

KWA INE, kumvetsera Mawu a Mulungu pa matepi ndi dongosolo la Mulungu la lero. Ndi Mawu amoyo a Yesu Khristu. Iwo ndiwo Mtheradi wanga molingana ndi Mawu a Mulungu. Ndi njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero.

Chotero, ine ndikufuna kukuitanani inu kuti mudzabwere kulumikizana nane Lamlungu pa 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ine ndidzamvetsera kwa William Marrion Branham, amene ine ndikukhulupirira kuti ndi Liwu la Mulungu la masiku athu ano, kuphunzitsa Mkwatibwi wa Khristu momwe angakhalire: Thunthu La Munthu Wangwiro 62-1014M.

M’bale. Joseph Branham