Uthenga: 65-1205 Zinthu Zimene Ziti Zidzakakhaleko
- 25-0803 Zinthu Zimene Ziti Zidzakakhaleko
- 21-1205 Zinthu Zimene Ziti Zidzakakhaleko
- 20-0719 Zviitiko Zvanhasi Zvinojekeswa Nechiporofita
- 18-0114 Zinthu Zimene Ziti Zidzakakhaleko
- 15-1206 Zinthu Zimene Ziti Zidzakakhaleko
Wokondedwa Zikhumbo za Mulungu,
Mawu aliwonse amene analankhulidwa mu Uthenga uwu ndi kalata yachikondi kwa Mkwatibwi Wake. Kuganiza kuti Atate wathu wa Kumwamba amatikonda kwambiri, moti sikuti ankangofuna kuti tiziwerenga Mawu ake, koma ankafuna kuti tizimva Liwu lake likulankhula ku mitima yathu kuti atiuze kuti: “Inu ndinu liwu langa lamoyo, Chikhumbo changa chamoyo, chimene Ine ndingawonetsere pa dziko lapansi.
Ndiyeno kuganiza kuti pambuyo pa nsembe Yake yonse imene Iye anachita pano pa dziko lapansi, moyo umene Iye anakhala, njira imene Iye anayenda. Iye anapempha chinthu chimodzi,
“Kuti kumene Ine ndikakhale, iwonso akakhaleko.” Iye anapempha chiyanjano chathu. Ndicho chinthu chokhacho chimene Iye anawapempha Atate mu pemphero, ubwenzi wanu wosatha.
Kumene ine ndiri, “Mawu Ake,” ifeso tiyenera kukakhalako, kuti tikalandire chiyanjano Chake, Ubwezi Wake Wosatha, kwanthawizonse. Chotero, tiyenera kukhala moyo mwa Mawu aliwonse amene Iye analankhula kwa ife pa matepi kuti tikhale Namwali m’kwatibwi wa mawu, amene amatipanga ife gawo la Mkwati.
Ilo ndilo VUMBULUTSO la Yesu Khristu mu ora lino. Osati chimene Iye anali mu ora lina, yemwe Iye ali TSOPANO. Mawu a lero. Kumene Mulungu ali lero. Ndilo Vumbulutso la lero. Tsopano likukula mwa Mkwatibwi, kutipanga ife mu m’thunthu lokwana la mngwiro la ana aamuna ndi aakazi.
Ife timadziwona tokha mu Mawu Ake. Ife tikudziwa amene ife tili. Ife tikudziwa ife tiri mu dongosolo Lake. Iyi ndi Njira yoperekedwa ndi Mulungu ya lero. Ife tikudziwa Mkwatulo uli pafupi. Posachedwapa okondedwa athu adzawonekera. Kenako tidzadziwa: kuti Ife Tafika. Ife tonse tikupita Kumwamba…inde, Kumwamba, malo enieni monga awa.
Ife tikupita kumalo enieni kumene tizikachitako zinthu, kumene tikakhalako moyo. Ife tizikagwirako ntchito. Ife tikasangalalako. Ife tikakhalako moyo. Ife tikupita ku Moyo, ku Moyo Wamuyaya weniweni. Ife tikupita Kumwamba, paradiso. Chimodzimodzi monga momwe Adamu ndi Eva ankagwirira ntchito, ndi kumakhala moyo, ndi kumadya, ndi kumasangalalako, mmunda wa Edeni tchimo lisanabweremo, ife tiri panjira yathu tikubwerera kumeneko panonso, kulondola, tikubwerera kumeneko. Adamu woyamba, chifukwa cha tchimo, anatichotsako ife. Adamu Wachiwiri, kupyolera mu chirungamo, akutibwezeretsako ife kumeneko kachiwiri; akutilungamitsa ife ndi kutibwezeretsanso ife mmenemo.
Kodi aliyense anganene bwanji za izi pazomwe izo zikutanthauza kwa ife? Chowonadi ndi chakuti tikupita ku paradaiso kumene tikukakhala kwa Muyaya wonse pamodzi. Kulibenso chisoni, zowawa kapena Zokhumudwitsa, ungwiro basi pa ungwiro.
Mitima yathu ikukondwera, miyoyo yathu ili pamoto mkati mwathu. Satana akumayika mochuruka ndi mochuruka zopsinja pa ife tsiku lililonse , koma ife tikusangalalabe. Chifukwa:
- TIKUDZIWA, YEMWE IFE TILI.
- TIKUDZIWA, SITINAMULEPHERE, NDIPO SITIDZAMULEPHERA IYE.
- TIKUDZIWA, TILI MU CHIFUNIRO CHAKE CHANGWIRO.
- TIKUDZIWA, WATIPATSA IFE VUMBULUTSO LOWONA LA MAWU AKE.
M’bale Joseph, inu mumalemba chinthu chomwecho sabata iliyonse. ULEMERERO, ndidzalemba chimenecho sabata iliyonse chifukwa Iye akufuna kuti inu mudziwe mochuruka momwe Iye amakukonderani inu.Yemwe inu muli. Kumene inu mukupita. Chithunzi chikusandulika kukhala chenicheni. Inu ndinu Mawu mukusandulika kukhala Mawu.
Okondedwa dziko, bwerani mudzajowinane nafe Lamlungu lino pa 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, polumikizana, osati chifukwa “Ine” ndikukuitanani inu, koma chifukwa “IYE” akukuitanani inu. Osati chifukwa “Ine” ndinatenga tepiyo, koma kumva Mawu ndi gawo la Mkwatibwi kuzungulira dziko lonse nthawi imodzi.
Kodi Ife tingazindikire kuti n’zotheka kuti Mkwatibwi amve Liwu la Mulungu padziko lonse, pa nthawi yofanana? Ameneyo ayenera kukhala Mulungu. Mulungu anali ndi mneneri wake kuti achite izo pamene mngelo Wake anali pano pa dziko lapansi. Iye analimbikitsa Mkwatibwi kulumikizana mu m’pemphero, ONSE PA NTHAWI YOFANANA YA KU JEFFERSONVILLE, 9:00, 12;00, 3:00; Kodi icho ndi chinthu chachikulu motani tsopano, kuti Mkwatibwi akhoza kulumikizana ngati M’MODZI kuti amve Liwu la Mulungu likuyankhula kwa iwo onse pa nthawi imodzi?
M’bale. Joseph Branham
Uthenga: Zinthu Zimene Ziti Zidzakakhaleko 65-1205
Malemba:
Mateyu woyera 22:1-14
Yohane Woyera 14:1-7
Ahebri 7:1-10