25-0615 Chilumikizo Chosawoneka Cha Mkwatibwi Wa Khristu

Uthenga: 65-1125 Chilumikizo Chosawoneka Cha Mkwatibwi Wa Khristu

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkazi Wosankhidwa wa Mulungu,

Palibe njira yozungulira izo, inu ndinu Jini Lauzimu la Mulungu, chiwonetsero cha zikhumbo za maganizo Ake, ndipo munali mwa Iye asanaikidwe maziko a dziko.

Ife sitingapitirirenso, ndife ofanana ndendende ndi njere yomwe idapita munthaka. Ndife Yesu yemweyo, mu mawonekedwe a Mkwatibwi, ndi mphamvu yomweyo, Mpingo womwewo, Mawu omwewo amoyo ndi akukhala mwa ife kupanga mutu, KUKONZEKERA MKWATULO.

Anatiuza ife kuti talekanitsidwa ku mgwirizano wathu woyamba, ndi imfa yauzimu, ndipo tsopano tabadwanso, kapena takwatiwanso, ku mgwirizano wathu watsopano wauzimu. Osatinso moyo wathu wakale wachithupi ndi zinthu za mdziko, koma wa Moyo Wamuyaya. Nyongolosi yomwe inali mwa ife pachiyambi, yatipeza ife!

Zimatanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti bukhu lathu lakale lapita ndi mgwirizano wathu wakale, lasamutsidwa. TSOPANO ili mu “Bukhu Latsopano” la Mulungu; osati bukhu la moyo… ayi, ayi, ayi… koma mu Bukhu la Moyo wa Mwanawankhosa. Chimene Mwanawankhosa anachiombola. Ndi chiphaso chathu chaukwati chimene nyongilodzi yathu yaoyo osatha imagwirizirako.

Mwakonzeka? Apa izo zikubwera. Inu kulibwino mudzitsine nokha ndi kukonzekera kukuwa ndi kufuula ulemerero, aleluya, mulemekezeke Ambuye, ndi migolo iwiri ndi katundu wakumwamba.

“Kodi mukutanthauza kundiuza ine kuti buku langa lakale ndi zolakwa zanga zonse, zolephera zanga zonse …”

Mulungu anachiyika icho mu Nyanja ya Kuyiwala Kwake, ndipo inu simunakhululukidwe kokha, koma inu mwalungamitsidwa…Ulemerero!  “Kulungamitsidwa.”

Ndipo izi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti inu simunachite m’komwe ngakhale pa maso pa Mulungu.  Iwe umayima mwangwiro pamaso pa Mulungu. ULEMERERO!  Yesu, Mawu, anatenga malo anu. Iye anakhala inu, kuti inu, wochimwa wonyansa, mukhoze kukhala Iye, MAWU. Ife ndife MAWU.

Izo zimatipanga ife nyongolodzi Yake yaing’ono yomwe inakonzedweratu kuchokera pachiyambi. Ndife Mawu akubwera pa Mawu, pa Mawu, pa Mawu, pa Mawu, ndipo ife tikubwera mu thunthu lokwanila la Khristu kotero kuti Iye akhoze kubwera kudzatitenga ife kuti tikhale Mkwatibwi Wake.

Kodi chikuchitika ndi chiyani TSOPANO?

Ndi Chilumikizano Chosaoneka Cha Mkwatibwi Wa Khristu kusonkhana mozungulira Mawu, kuchokera kuzungulira dziko.

Ponena izi tsopano, izi zikupita mu fuko lonseli. Mu New York, tsopano ili twente-faifi minitsi pasiti leveni. Kutali uko mu Philadelphia ndi kuzungulira kumeneko, oyera okondedwa awo akhala ali uko akumvetsera, pakali pano, mu mipingo konse kozungulira. Kutali uko, kutali komwe kuzungulira Mexico, kutali uko mu Canada ndi konse kozungulira, kudutsa. Mailosi thuu handiredi, kulikonse mkati mwa dera la North America kuno, pafupifupi, anthu ali kumeneko, akumvetsera pakali pano. Zikwi kuchulukitsa ka zikwi, akumvetsera.

Ndiwo Uthenga wanga kwa inu, Mpingo, inu omwe muli mchilumikizano, chilumikizano chauzimu mwa Mawu,

Iye anati Icho chinali chilumikizano chauzimu cha Khristu ndi Mpingo Wake, ndipo Izo ZIKUCHITIKA PALI PANO. Thupi likukhala Mawu, ndipo Mawu akukhala thupi. Ife tawonetseredwa, ndi kutsimikiziridwa; zomwe Baibulo linanena kuti zidzachitika mu tsiku lino, ndipo Izo zikuchitika tsopano, tsiku ndi tsiku mwa aliyense wa ife.

Mulungu adzakhala ndi Mpingo waukoma. Mkwatibwi Wake woona, wokhulupirika wa Mawu. NDIFE AMAYI WOSANKHIDWA wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Ndi Nthawi Yanji Yino, Bwana?

Ife tiri nalo vumbulutso mu masiku otsiriza ano, la Uthenga wa Ambuye Mulungu kuti usonkhanitse Mkwatibwi Wake palimodzi. Palibe m’badwo wina umene iwo unalonjezedwapo. Izo zinalonjezedwa mu m’badwo uno: Malaki 4, Luka 17:30, Yohane Woyera 14:12, Yoweli 2:38. Malonjezo amenewo ali chimodzimodzi basi monga Yohane M’batizi anadzizindikiritsa yekha mu Lemba.

Ndani anakwaniritsa malemba amenewa?

Mngelo wake wamphamvu wachisanu ndi chiwiri, William Marrion Branham. Iye nthawizonse ankazichita izo mwa dongosolo. Iye ankazichita izo nthawi iliyonse mwa dongosolo. Iye akuchita izo kachiwiri mu tsiku lathu, kuitana ndi kusonkhanitsa Mkwatibwi Wake waukoma mu tsiku lotsiriza mwa mneneri Wake.

Ndi nthawi yaulemerero bwanji yomwe Mkwatibwi ali nayo. Kusonkhana kulikonse kumakulirakulira, kokoma komanso kokoma. Sipanakhalepo nthawi ngati iyi. Zokayikira zonse zatha.

Bwerani mudzajowinane nafe pamene tikumva Mawu olonjezedwa a tsiku lathu akuyankhula, ndi kutiuza ife chomwe ife tiri ndi zomwe zikuchitika mu tsiku lathu.  Chilumikizano Chosaoneka Cha Mkwatibwi Wa Khristu 65-1125.

M’bale. Joseph Branham 

Malemba:

Mateyu Woyera 24:24
Luka Woyera 17:30 / 23:27-31
Yohane Woyera 14:12
Machitidwe 2:38
Aroma 5:1/7:1-6
2 Timoteyo 2:14
1 Yohane 2:15
—Genesis 4:16-17; 25-26
Danieli 5:12
Yoweli 2:28
Malaki 4