25-0504 Kukhazikitsidwa #1

Uthenga: 60-0515E Kukhazikitsidwa #1

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Iwo Okhazikitsidwa,

Ife tsopano tikudya zinthu zamphamvu za Mulungu ndi kumvetsa bwino Mawu ake. Mulungu watipatsa ife Vumbulutso loona la Mau ake. Malingaliro athu auzimu onse ndi osasokonezeka.

Ife TIKUDZIWA ndendende Yemwe Iye ali. Ife tikudziwa ndendende chimene Iye ali. Ife TIKUDZIWA ndendende kumene tikupita. Ife TIKUDZIWA ndendende amene ife tili. Ife TIKUDZIWA mwa Yemwe ife tinamukhulupirira ndi kuvomereza kuti Iye ali wokhoza kusunga chimene ife tapereka kwa Iye kufikira tsikulo.

Iye wayankhula ndi kuwulula zinsinsi zonse zomwe zakhala zili zobisika chikhazikitsireni maziko a dziko kwa ife. Iye anatiuza ife momwe ena nthawizonse akhala akukana njira Yake yoperekedwa ndi kukhumba utsogoleri wosiyana, koma Iye akanati akhale ndi kagulu kakang’ono kamene kadzakhala moona ku Mawu Ake.

Kudutsa mdziko, iwo sadzakhala atasonkhana mu malo amodzi kuti akhale ochita zinthu mofanana. Koma magulu aang’ono a iwo adzakhala atamwazikana konse konse padziko lapansi.

Ulemerero, tamwazikana padziko lonse lapansi, koma Ogwirizana monga Mmodzi mwa Kukanikiza kusewera ndikumvetsera ku Liwu la Mulungu likulankhula kwa ife.

Tiyeni tingosuzumira ndi kulawiratu zimene Iye adzatilankhula kudzera mwa mngelo wake wamphamvu pa Lamlungu.

Okondedwa anga osankhidwa, inu tsopano mukukhala pamodzi mu malo a Kumwamba. Osati kokha kulikonse, koma mu malo “Akumwamba”; ndi udindo wanu ngati wokhulupirira. Inu mwapemphereredwa ndi kukonzekera Uthenga. Inu mwadzisonkhanitsa nokha palimodzi monga oyera, wobatizidwa ndi Mzimu Woyera, odzazidwa ndi madalitso a Mulungu. Inu munaitanidwa, osankhidwa, ndipo mzimu wanu wabweretsedwa mu chikhalidwe cha Kumwamba.

Zomwe zingachitike. Mzimu wanga Woyera udzakhala ukusuntha pa mtima uliwonse. Inu Munabadwanso mwatsopano ndipo cholengedwa chatsopano mwa Khristu Yesu. Machimo anu onse ali pansi pa Mwazi. Inu muli mu kupembedza kwangwiro, ndi manja anu ndi mitima yokwezera kwa Ine, mukundipembedza Ine palimodzi mu malo ammwambamwamba.

Inu ndinu wokonzedweratu, Osankhidwa, mu Kudziwiratu Kwanga. Osankhidwa, Oyeretsedwa, Olungamitsidwa mwa Kuikidwiratu. N’zosatheka kuti munyengedwe. Ine ndinakuikani inu asanaikidwe maziko a dziko. Inu ndinu Mulungu wamng’ono, wosindikizidwa ndi Mzimu Woyera wa lonjezano; osati kungobadwira m’banja, Ana Anga aamuna ndi Aakazi.

Ine ndidzakudalitsani inu ndi machiritso Auzimu, kudziwiratu, vumbulutso, masomphenya, mphamvu, malirime, kutanthauzira, nzeru, chidziwitso, ndi madalitso onse a Kumwamba, ndi chisangalalo chosaneneka ndi chodzaza ndi Ulemerero.

Mtima uliwonse udzadzazidwa ndi Mzimu Wanga. Inu mudzakhala mukuyenda limodzi, mutakhala palimodzi, mu malo Ammwambamwamba. Palibe lingaliro limodzi loyipa pakati panu, palibe ndudu imodzi yomwe idzasutidwe, palibe diresi limodzi lalifupi, palibe ichi, icho kapena chimzake, palibe lingaliro limodzi loyipa, palibe yemwe ali ndi kalikonse kotsutsana wina ndi mzake, aliyense akuyankhula mu chikondi ndi chiyanjano, aliyense ndi mtima umodzi mu malo amodzi.

Kenako mwadzidzidzi padzabwera mkokomo wochokera Kumwamba ngati mphepo yothamanga yamphamvu ndipo ndidzakudalitsani inu ndi madalitso onse auzimu. Ndiye inu mudzakhala ngati Davide, kuvina pamaso pa Likasa, kuliwuza dziko kuti simukuchita manyazi, IWE NDIWE MKWATIBWI WANGA WA TEPI! Inu mumakanikiza kusewera ndi kukhulupirira MAWU ALIWONSE amene Ine ndimayankhula. Simudzasunthika, ndipo simungathe kusunthika!

Ena akhoza kuwakana Iwo, kapena osawamvetsa Iwo, koma kwa inu, Ndi Chizindikikiro chanu chaulemu. Monga Davide adanena kwa mkazi wake; “Inu mukuganiza kuti ichi chinali chinachake, ingodikirani mpaka mawa, ife tidzakhala tikumvetsera kwa matepi ngakhale ochuluka, kutamanda Ambuye, odzazidwa ndi Mzimu Wake; pakuti ife tikukhala mu Kenani, kupita ku dziko lolonjezedwa.”

Kenako ndidzayang’ana pansi kuchokera Kumwamba ndikukuuzani:

“Ndiwe Mkwatibwi wa pamtima Wanga Womwe.”

Madalitso amenewa angakhale anunso. Bwerani, kulumikizana nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, ndi kuona kukhalapo kwa Ambuye kuposa kale lonse pamene tikumvetsera Liwu la Mulungu la lero likulankhula kwa ife ndi kutibweretsera Uthenga: Kukhazikitsidwa #1 60-0515E.

Kumbukirani, izi ndi za kwa mpingo, osati kwa wakunja. Icho ndi chinsinsi mmafanizo kwa iye, samatha konse kuti amvetse, zimapita pamwamba pa mutu wake, iye samadziwa konse za icho kuposa kalikonse. Koma, kwa mpingo, icho ndi uchi mu thanthwe, icho ndi chimwemwe chosaneneka, icho ndi chitsimikizo chodala, icho ndi nangula ya solo, icho ndi chiyembekezo chathu ndi pokhalapo, icho ndi Thanthe la Mibadwo, oh, icho ndi chirichonse chimene chiri chabwino.Pakuti miyamba ndi dziko lapansi zidzapita, koma Mawu a Mulungu sadzapita.

Pakuti kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka, koma Mawu a Mulungu sadzachoka.

M’bale. Joseph Branham

Malemba oti muwerenge Uthenga usanayambe:
Yoweli 2:28
Aefeso 1:1-5
1 Akorinto 12:13
1 Peturo 1:20
Chivumbulutso 17:8
Chivumbulutso 13