25-0119 Chibvumbulutso, Mutu Faivi Gawo I

Uthenga: 61-0611 Chibvumbulutso, Mutu Faivi Gawo I

PDF

BranhamTabernacle.org

Okondedwa Wokhazikitsidwa, 

Ndi dzinja lodabwitsa bwanji lomwe tili nalo pomwe Mzimu Woyera akuwunikira Mau ake kwa Mkwatibwi kuposa kale. Zinthu zomwe mwina tazimva, kuwerenga ndi kuphunzira moyo wathu wonse tsopano zikuvumbulutsidwa ndi kuwululidwa kuposa kale. 

Munthu wakhala akuyembekezera kwa zaka masauzande ambiri za tsiku ili. Onse analakalaka ndi kupemphera kuti amve ndi kuona zinthu zimene timaona ndi kumva.  Ngakhale aneneri akale ankalakalaka tsikuli.  Momwe iwo ankafunira kuwona kukwaniritsidwa ndi kudza kwa Ambuye.

Ngakhale ophunzira a Yesu, Petro, Yakobo, ndi Yohane, amuna amene anayenda ndi kulankhula ndi Iye, analakalaka kuona ndi kumva zonse zobisika.  Iwo anapemphera kuti Izo ziwululidwe ndi kuwonetseredwa mu tsiku lawo, mu nthawi yawo.

Mu Mibadwo Isanu ndi iwiri Yonse ya Mipingo, mthenga aliyense, Paulo, Marteni, ndi Lutera, ankafuna kudziwa zinsinsi zonse zomwe zinali zitabisika. Chikhumbo chawo chinali kuona kukwaniritsidwa kwa Mawu kukuchitika m’moyo wawo. Iwo ankafuna kuti awone kudza kwa Ambuye.

Mulungu anali ndi dongosolo. Mulungu anali nayo nthawi. Mulungu anali ndi anthu Iye amawayembekezera pa…IFE. Kudutsa mu mumibadwo yonse, Onse anali atalephera.  Koma Iye anadziwa, mwa kudziwiratu Kwake, pakanadzakhala anthu: ulemerero Wake, Mkwatibwi wa Mawu wangwiro. IWO SAKANADZAMULEPHERA IYE. Iwo sakananyengerera PA MAWU AMODZI. Iwo adzakhala namwali woyera Mkwatibwi Wa Mau

Tsopano ino ndi nthawi. Tsopano ino ndi nyengo. Ndife osankhidwa amene iye wayembekezera kuchokera pamene Adamu anagwa ndi kutaya ufulu wake. NDIFE MKWATIBWI WAKE.

Mulungu anaonetsa Yohane chithunzithunzi cha zonse zimene zidzachitike, koma sanadziwe matanthauzo ake onse. Pamene adaitanidwa, adawona m’dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m’kati mwake, losindikizidwa ndi zisindikizo zisanu ndi ziwiri, koma panalibe wina woyenera kutsegula bukulo.

Yohane anakuwa ndi kulira momvetsa chisoni chifukwa zonse zinali zitatayika, panalibe chiyembekezo. Koma Ambuye alemekezeke, mmodzi wa akulu anati kwa iye, “Usalire, pakuti taonani, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika kutsegula bukhu, ndi kumasula zisindikizo zake zisanu ndi ziwiri.”

Iyo inali nthawi. Iyo inali nyengo. Ameneyo anali munthu amene Mulungu anamusankha kuti alembe zonse zimene anaona. Komabe, Izo zonse zinali zosadziwika tanthauzo Lake lonse. 

Mulungu anali kuyembekezera ndi kuyembekezera chotengera Chake chosankhidwa, mthenga Wake wa mngelo wachisanu ndi chiwiri, kuti abwere pa dziko lapansi, kotero kuti Iye akhoze kugwiritsa ntchito liwu Lake kuti likhale Liwu Lake, kwa Mkwatibwi Wake. Ankafuna kuti alankhule milomo kupita ku khutu kuti pasakhale KUSAMVETSETSA KULIKONSE. Iye Mwiniwake, ankafuna kulankhula ndi kuwulula zinsinsi Zake zonse kwa wokondedwa Wake, wokonzedweratu, wangwiro, Mkwatibwi wokoma wapamtima …IFE!!

Iye wakhala akulakalaka kutiuza zinthu zodabwitsa zonsezi. Monga mwamuna amauza mkazi wake kuti amamukonda iye mobwerezabwereza, ndipo iye samatopa kuzimva izo, Iye amakonda kutiuza mobwerezabwereza kuti amatikonda ife, anatisankha ife, kutiyembekezera ife, ndipo tsopano atidzera ife.

Iye anadziwa momwe ife tikanakondera kumamumva Iye akunena Izo mobwereza bwereza, kotero Iye anali ndi Liwu Lake lojambulidwa, chotero Mkwatibwi Wake angathe ‘Kusindikiza Kusewera’ tsiku lonse, tsiku lirilonse, ndi kumva Mawu Ake akudzaza mitima yawo. 

Mkwatibwi Wake wokondeka wadzikonzekeretsa Yekha mwa kudya pa Mawu Ake. Ife sitidzamvetsera kwa china chirichonse, Liwu Lake lokha basi. Ife tikhoza kungodya Mawu Ake Oyera amene aperekedwa.

Tili pansi pa kuyembekezera kwakukulu. Ife timazimverera Izo mkati mwa miyoyo yathu. Iye akubwera. Timamva nyimbo za ukwati zikuyimba. Mkwatibwi akukonzekera kuyenda pansi mu kanjira. Aliyense wayimirira, Mkwatibwi akubwera kudzakhala ndi Mkwati wake. Zonse zakonzedwa. Nthawi yafika.

Iye amatikonda Ife kuposa wina aliyense. Ife timamukonda Iye kuposa wina aliyense. Tidzakhala Mmodzi ndi Iye, ndi onse amene timawakonda, ku muyaya. 

Mukuitanidwa kuti mubwere mudzakonzekere ukwati nafe Lamlungu nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tidzakhala tikumva Liwu la Mulungu likuwululira Chivumbulutso, Chaputala Chachisanu Gawo I   61-0611.

M’bale. Joseph Branham