Uthenga: 60-1211E M’badwo Wa Mpingo Wa Laodikaya
- 24-1208 M’badwo Wa Mpingo Wa Laodikaya
- 23-0618 M’badwo Wa Mpingo Wa Laodikaya
- 20-1227 M’badwo Wa Mpingo Wa Laodikaya
- 19-0310 M’badwo Wa Mpingo Wa Laodikaya
- 16-0410 M’badwo Wa Mpingo Wa Laodikaya
Wokondedwa Osankhidwa,
Taonani, ndaima pakhomo, ndi kugogoda: ngati wina amva mau Anga, ndikutsegula pakhomo, ndidzalowa mwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.
Utumiki, tsegulani makomo anu kwa mngelo wa Mulungu nthawi isanathe. Ikani Liwu la Mulungu libweleleso mu maguwa anu posewera matepi. Ndi Liwu lokhalo lotsimikiziridwa la Mulungu la tsiku lathu ndi Mawu osalephera. Ndi Mau okhawo omwe ali ndi PAKUTI ATERO AMBUYE. Ndi Liwu lokhalo Mkwatibwi aliyense angakhoze kunena AMEN kwa iye.
Ndi m’badwo waukulu kuposa nthawi zonse. Yesu akutipatsa kufotokoza kwa Iye mwini pamene masiku a chisomo chake akutha. Nthawi yafika kumapeto. Iye waulula makhalidwe Ake omwe kwa ife mu m’badwo wotsiriza uno. Watipatsa kuyang’ana komaliza pa Umulungu Wake Wachisomo ndi wapamwamba. M’badwo uwu uli vumbulutso la mwala wa pamutu la Iye mwini.
Mulungu anabwera mu m’badwo wa Laodikaya uwu ndipo anayankhula kupyolera mu thupi la munthu. Liwu Lake linalembedwa ndi kusungidwa kuti litsogolere ndi kupangitsa ungwiro Mkwatibwi wa Mawu Ake. Palibenso Liwu lina limene lingakhoze kupangitsa Mkwatibwi Wake kukhala wangwiro koma Liwu Lake Lomwe.
Mu m’badwo wotsiriza uno, Liwu Lake pa matepi layikidwa pambali; latulutsidwa kunja kwa mipingo. Iwo sasewera matepi. Chotero Mulungu akuti, “Ine ndikutsutsana nanu nonse. Ine ndidzakulavula iwe mkamwa Mwanga. Awa ndi mathero.
“Pa mibadwo isanu ndi iwiri mwa mibadwo isanu ndi iwiri, sindinawone kalikonse koma anthu olemekeza mawu awo omwe kuposa Anga. Chotero pa mapeto a m’badwo uwu Ine ndikulavula inu kutuluka mkamwa Mwanga. Zonse zatha. Ndilankhula inde cha bwino. Inde, ndili pano pakati pa Mpingo. Ameni wa Mulungu, wokhulupirika ndi woona adzadziulula Yekha ndipo izo zikhala NDI MNENERI WANGA.”
Monga mmene zinalili poyamba, iwo akuyenda moona mtima n’kukhala mmene anachitira makolo awo akale m’masiku a Ahabu. Anali mazana anai a iwo, ndipo onsewo anali mu m’gwirizano; ndipo mwa iwo onse kunena chinthu chomwecho, iwo anapusitsa anthu. Koma mneneri MMODZI, MMODZI YEKHA, anali wolondola ndipo ena onse olakwa chifukwa Mulungu anali atapereka vumbulutso kwa MMODZI YEKHA.
Izi sizikunena kuti mautumiki onse ndi abodza ndi kupusitsa anthu. Komanso sindikunena kuti munthu amene ali ndi mayitanidwe otumikira sangathe kulalikira kapena kuphunzitsa. Ine ndikunena kuti Utumiki wofutukuka usanu WOWONA udzayika MATEPI, Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi, ngati Liwu lofunika kwambiri lomwe inu MUYENERA KUMVA. Liwu la pa matepi liri Liwu LOKHALA limene latsimikiziridwa ndi Mulungu Mwiniwake kuti liri PAKUTI ATERO AMBUYE.
Chenjerani ndi aneneri onyenga, pakuti iwo ndi mimbulu yolusa.
Kodi mungadziwe bwanji njira yolondola ya lero? Pali kusiyana koteroko pakati pa okhulupirira. Gulu limodzi la anthu limati utumiki wofutukuka usanu udzachititsa Mkwatibwi kukhala wangwiro, pamene ena amati Kusewera matepi basi. Sitiyenera kugawanika; ife tiyenera kuti tigwirizane ngati MKWATIBWI MMODZI. Yankho lolondola ndi liti?
Tiyeni titsegule mitima yathu palimodzi ndi kumva zomwe Mulungu akunena kudzera mwa mneneri Wake kwa Mkwatibwi. Pakuti ife tonse tikuvomereza, kuti M’bale Branham ndi mngelo mthenga Wake wa wachisanu ndi chiwiri.
Pamaziko a khalidwe laumunthu lokha, aliyense amadziwa kuti pamene pali anthu ambiri pali ngakhale malingaliro ogawanika pa mfundo zazing’ono za chiphunzitso chachikulu chimene onse amagwirizira pamodzi. Ndani ndiye amene adzakhala nayo mphamvu ya kusalephera yomwe iti ibwezeretsedwe mu m’badwo wotsiriza uno, pakuti m’badwo wotsiriza uwu ubwereranso ku kuwonetsera Mkwatibwi wa Mawu Oyera? Izo zikutanthauza kuti ife tidzakhala nawo Mawu kamodzinso monga iwo anaperekedwa mwangwiro, ndi kumveka mwangwiro mu masiku a Paulo. Ndikuuzani amene adzakhala nayo. Iye adzakhala mneneri monga wotsimikiziridwa mwathunthu, kapena ngakhale wotsimikiziridwa mwathunthu kuposa momwe analiri mneneri aliyense mu mibadwo yonse kuchokera kwa Enoki mpaka tsiku lino, chifukwa munthu uyu mofunikila adzakhala nawo utumiki wa uneneri wa mwala wapamwamba, ndipo Mulungu adzamuwonetsa iye apo. Iye sadzasowa kuti aziyankhulire yekha, Mulungu adzayankhula mmalo mwa iye ndi liwu la chizindikiro. Ameni.
Chotero, Uthenga uwu wolankhulidwa ndi mthenga Wake unaperekedwa mwangwiro, ndipo umamveka mwangwiro.
Kodi Mulungu ananenanso chiyani china za mngelo Wake wachisanu ndi chiwiri wamthenga ndi Uthenga wake?
- Adzamvera kwa Mulungu yekha.
- Adzakhala ndi pakuti “atero Ambuye” ndi kuyankhula m’malo mwa Mulungu.
- Iye adzakhala kamwa ya Mulungu.
- IYE, MONGA KUNALEMBEDWA PA Malaki 4:6, ADZABWEZERETSA MITIMA YA ANA KUBWELERA KWA ATATE.
- Iye adzabwezeretsanso osankhidwa a tsiku lomaliza ndipo adzamva mneneri wotsimikiziridwa akupereka choonadi chenicheni monga momwe zinalili ndi Paulo.
- Adzabwezeretsa chowonadi monga adali nacho.
Ndiyeno kodi Iye ananena chiyani za ife?
Ndipo iwo osankhidwa pamodzi ndi iye mu tsiku limenelo adzakhala iwo amene moona adzawonetsera Ambuye ndi kukhala Thupi Lake ndi kukhala liwu Lake ndi kuchita ntchito Zake. Aleluya! Kodi inu mukuziwona izo?
Ngati mukadali mu kukaikira kulikonse, funsani Mulungu mwa Mzimu Wake kuti akudzazeni inu ndi kukutsogolerani inu, pakuti Mawu amati, “ OSANKHIDWA KUMENE KOKHA SADZAPUSITSIDWA”. Palibe mwamuna aliyense amene angakunyengeni inu ngati ndinu Mkwatibwi.
Pamene Amethodisti analephera, Mulungu anadzutsa ena ndipo kotero izo zapitirira kupyola mu zaka mpaka mu tsiku lotsiriza ili palinso anthu ena mu dziko, amene pansi pa mthenga wawo adzakhala liwu lotsiriza ku m’badwo wotsiriza.
Inde bwana. Mpingo sulinso “choyankhulira” cha Mulungu. Iyemwini ali kamwa payekha. Chotero Mulungu akutembenukira pa iye. Iye adzaphatikizana ndi iye kupyolera mwa mneneri ndi mkwatibwi, pakuti liwu la Mulungu lidzakhala mwa iye. Inde, chifukwa anena m’mutu wotsiriza wa Chivumbulutso vesi 17, “Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani.” Kamodzinso dziko lidzamva molunjika kuchokera kwa Mulungu monga pa zinalili pa Pentekosite; koma ndithudi Mkwatibwi wa Mawu uyo adzakanidwa monga zinalili mu m’badwo woyamba.
Mkwatibwi ali nalo liwu, koma ilo lidzangonena zomwe ziri pa matepi. Pakuti Liwu limenelo ndi LOLUNJIKA KUCHOKERA KWA MULUNGU, motero silikusowa kutanthauzira monga linaperekedwa mwangwiro ndipo limamveka mwangwiro.
Bwerani mudzajowine nafe Lamulungu lino pa 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, pamene ife tikumva Liwu lija likuwululira kwa ife: M’badwo wa Mpingo wa Laodikaya 60-1211E.
Mbale. Joseph Branham