26-0322 Chikwati Ndi Chilekano

Uthenga: 65-0221M Chikwati Ndi Chilekano

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi Wotengedwa, Wosankhidwa, ndinso Wokonzedweratu:

Ine ndikukumbukira pomwe ndinali mnyamata wachichepere ndikukula, ndikuyesera kusankha tepi yoti ndimvere. Pamene ndinali kuwerenga mitu yomwe ndimaganiza nthawi zonse, Ine sindinkafuna kumvera Chikwati ndi Chilekano, chifukwa zimenezo zinalibe chochita ndi ine; zinali za anthu okwatira okha.

Kenako tsiku lina, pamene ndimamvetsera Chikwati ndi Chilekano, Atate anandipatsa Vumbulutso la Uthenga umenewo. Kudzoza Kwake kunabwera mumtima mwanga. Iye akulankhula nane. Uthenga uwu NDI wa ine. Iye akundiuza ine kuti Iye anandisankha ine maziko a dziko la pansi asanakhazikitsidwe. Uwu ndi mwambo wa ukwati wanga. Ine Sindikufuna wina koma Iye. Ine ndine woona mtima komanso wokhulupirika kwa Iye, ndi Mawu Ake, ndi Liwu Lake, LOKHALO. Ife ndife M’MODZI.

Zoonadi Uthenga uwu unali kwa abale ndi alongo ambiri omwe anali okwatirana ndipo tsopano analekana, ndipo Iye anali kuwauza iwo chomwe anali kuyenera kuchita; koma panali tanthauzo la patali LOKWANIRA NDI LALIKULU kwambiri, lalikulu kwambiri, lamphamvu kwambiri.

Panali Mwamuna m’modzi, ndipo Iye anali kuyitana ndi kulankhula kwa Ake ambiri, mkwatibwi wosankhidwa. LIWU LA MULUNGU LINALI KUITANA WAKE WOYERA, WOSAWONONGEDWA, NAMWALI MKWATIBWI WA MAWU. Mmodzi amene sanakhudzidwe kapena kuipitsidwa ndi munthu. Mmodzi woona mtima komanso wokhulupirika kwa Iye ndi Mawu Ake okha. Mmodzi amene anakhutitsidwa kwathunthu ndi Iye ndi Mawu Ake.

Mwa Chisomo ndi Chifundo Chake, lero tinganene, popanda mthuzi umodzi wa kukayika, IFE NDIFE NAMWALI WAKE MKWATIBWI WA MAWU. ULEMERERO!!

Iye ankafuna kutsimikiza kuti sipadzakhala malire omasuka pankhani yoitana Mkwatibwi Wake, kotero Iye anabwera yekha ndikukhala m’thupi la munthu kuti awulule Mawu Ake ndikuitana Mkwatibwi Wake kwa Iyemwini. Iye anali Elieza amene akanasankha Mkwatibwi Wa Iyemwini.

Kuti titsimikizire kuti palibe njira yoti tisokonezedwe ndi amene anali kutifunsira ukwati, Iye mwini anatsimikizira chotengera chake chosankhidwa mwa kulankhula naye kuchokera mu mphepo yamkuntho yopachikidwa pamtengo. Kenako Iye analankhula naye moonekera pa Mtsinje wa Ohio pamaso pa anthu zikwizikwi.

Iye ngakhaleso anajambulidwa chithunzi chake pamodzi ndi Iye kotero onetsani ndi kuliwuza dziko lonse lapansi , INE NDINAKUWUZANI INU KUTI INE NDIKANADZABWERANSO NDI KUDZAKHALA NDI MOYO MU THUPI. IYE NDIYE AMENE INE NDINASANKHA KUKHALAMO NDI MOYO, KUTI NDIKUITANENI INU KUTI MUKHALE MKWATIBWI WANGA. SI IYE; NDI INE NDIKULANKHULA KUDUTSIRA MWA IYE. INE NDIKUNGOGWIRITSA NTCHITO LIWU LAKE KUTI LIKHALE LIWU LANGA KWA INU. INE NDIYE AMENE NDAKUYITANANI INU KUTI MUKHALE MKWATIBWI WANGA WANGWIRO.

Vumbulutso la Uthenga Uwu, Mawu Ake, Liwu Lake, ndipo tsopano chomwe amene IFE tili ndizopitirira mawu a munthu kuti ayesere kufotokoza. Ine ndikudziwa kuti inu mukudziwa chenicheni chomwe ine ndikunena. Kukwatulidwa mu Chikhulupiriro kukuchitika. Mkwatibwi akudzikonzekeretsa yekha pokhala mu mkupezeka kwa Mulungu Mwiniwake, kukhala wangwiro.

Ndi mwayi waukulu kwambiri wotani womwe dziko lapansi lili nawo womva Liwu la Mulungu likulankhula ndi iwo; kukhala pansi ndi kumvetsera Mawu pa Mawu pamene Iye akulankhula ndi kuwulula Mawu Ake ndikutiuza amene ife tili. Palibe china choponsa kukhala mumkupezeka Kwake, choncho bwerani mudzalumikizane nafe Lamlungu nthawi ya 12:00 P.M., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene ife tikumumva Iye akulankhula ndi Mkwatibwi Wake, Uthenga, “Chikwati Ndi Chilekano” 65-0221M.

M’bale Joseph Branham

Malemba owerenga musanamve Uthenga:

Mateyu Woyera 5:31-32 / 16:18 / 19:1-8 / 28:19
Machitidwe 2:38
Aroma 9:14-23
Timoteo Woyamba 2:9-15
Akorinto Woyamba 7:10-15 / 14:34
Ahebri 11:4
Chivumbulutso 10:7
Genesis mutu 3
Levitiko 21:7
Yobu 14:1-2
Yesaya 53
Ezekieli 44:22