26-0301 Mbewu Sizilowa Ufumu Pamodzi Ndi Makoko

Uthenga: 65-0218 Mbewu Sizilowa Ufumu Pamodzi Ndi Makoko

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Namwali Mkwatibwi Wa Mawu,

Ine ndakhala pano m’mawa uno ndikumva kudzoza kumeneko pamene ndikumvetsera, kuwerenga ndikuphunzira Uthenga uwu umene Mkwatibwi adzamva Lamlungu. Thupi langa lonse ladzozedwa. Mtima wanga ukudzaza ndi chisangalalo chotelocho podziwa kuti, IFE TONSE TIDZASONKHANA PAMODZI KUCHOKERA PA DZIKO LONSE NDI KUDZOZA KOFANANA KOMWEKU. Ife Tidzakondwera, kutamanda Ambuye, nthawi imodzi, pamene IYE akulankhula ndi aliyense wa ife ndikuulula Mawu Ake.

Kudzoza kudzakhala kwakukulu kwambiri kotero kuti padzakhala kufuula ndi kukuwilira, “aleluya, ameni, lilemekezeke Dzina la Ambuye” padziko lonse lapansi nthawi imodzi, pamene tikukwera Kumwamba ndi matamando ndi kupembedza kwathu.

Kodi chidzakhala chikuchitika ndi n’chiyani? Mulungu adzakhala akugwirizanitsa ndi kulankhula ndi Mkwatibwi Wake.Ife tidzakhala Gawo limodzi, mu lingaliro limodzi ndi mgwirizano umodzi pamene Iye akudziulula ndi kudziwonetsera Yekha kwa ife.

Palibe malo akuluakulu omwe inu mungapiteko, palibe Liwu lalikulu lomwe inu mungamve; palibe kudzoza kwakukulu kuposa Liwu la Mulungu likulankhula nanu mwachindunji pa matepi.

Mulungu wakhala akuyang’anira Mawu Ake kuyambira pachiyambi ndipo wapereka malo omwe ana Ake onse angapiteko ndikumva Iye akulankhula ndikutanthawuzira Mawu Ake omwe. Malo omwe palibe kupenekera, chiyembekezo, kapena kudabwa; Iwo ndi malo operekedwa ndi Mulungu kuti mumve PAKUTI ATERO AMBUYE.

Zikakhala kuti izo Zavumbulutsidwa kwa inu, zimakhala ngati kuwala kwakukulu komwe kwayatsidwa mumtima mwanu ndi moyo wanu … Inu mumafuula, “icho ndi ichi. Ine Ndili kuchiwoona icho. Ine ndili MMODZI NDI MAWU. INE NDINE MAWU. INE NDINE MKWATIBWI. INE NDAFIKA.”

Icho Chikuchitika ndipo iwo sakudziwa. Ndi choncho. Mukuona? Inde bwana! Pakuti kumene kwafa nyama ndi kumene mphungu zidzasonkhana…?…Ndi zimene linanena. Kodi nyama yakufa kumene ndi chiyani? Mawu. Iye ndi Mawu, nyama yakufa, Khristu, Khristu mwa inu, yemweyo dzulo, lero ndi nthawi zonse. Izo zili zolondola bwanji!

Pamene ife tisonkhana kuti timve Mawu, zosamalira zathu zonse, nkhawa zathu zonse, mavuto athu onse, zimangotha momphweka. Ife timakondwera pamene tikuzindikira kuti ife tilibe chodela nkhawa nacho; ife ndife Mkwatibwi Wake. Iye siali nafe kokha, KOMA ALI MWA IFE. NDIFE MKWATIBWI WA MBEWU YA MAWU. Chilichonse ndi changwiro. Nthawi yake ndi yangwiro. Ife ndife angwiro.

Ife tili okhutira kwambiri ndi oyamikira kwambiri kunena kuti ife ndife Mawu Ake obadwa kwa namwali opangidwa kuwonetseredwa; Yesu Khristu yemweyo dzulo, lero, ndi kwa nthawi zonse, wokhala ndi moyo ndi kupezeka mkati mwathu. Aleluya!

Ife sitingathe kunyengelera pa MAWU AMODZI. Ife tiyenera kumva Mawu a Mulungu pa matepi.

Kodi inu munamuona mphungu akuvomerezera zosayenera? Ayi, bwana! Palibe zonyengerera mwa iye. Ndi momwenso Mkhristu weni weni amachitira. Iye siwolobodoka ayi. Amasaka mpakana atachipeza. Ameni. Inde, bwana! Iye mpakana atapeza chakudya chake. Iye amafuna manna atsopano. Adzafika pamenepo nakumba mpaka atachipeza Amauluka chokwera m’mwamba. Ngati sichiri m’chigwa chino, iye amakweranso m’mwamba pang’ono. Ukapita m’mwamba kwambiri, umaonanso kwambiri. Kotero ndi nthawi ya mphungu za tsiku lino kuti ziyambe kuuluka m’mwamba zedi, kukumba mu malonjezo a Mulungu, osati kumakhala moyo ndi chakudya cha akhwangwala chimene chinaphedwa zaka zapitazo. Tulukanimo m’menemo.

Khala okonzeka Mkwatibwi, ife tidzakhala tikudya Manna watsopano aja, titakhala pansi pa kudzoza kwakukulu komwe kulipo, Lamlungu lino nthawi ya 12:00 P.M, nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tikumva: 65-0218 Mbewu Si ili Yolandira Cholowa Pamodzi Ndi Makoko.

Ife tikuitana Mkwatibwi kuchokera kuzungulira padziko lonse lapansi kuti adzalumikizane nafe kudya pa Njira Yangwiro Yoperekedwa ndi Mulungu ya lero. Malo okhawo kumene MKWATIBWI anganene kuti ameni ku Mawu aliwonse. Kumene kudzoza kwakukulu kwa Mzimu Woyera kumalankhula ndi kupangitsa Mkwatibwi Wake kukhala wangwiro mwa Kukanikiza Kusewera ndi kumva ndi kulandira Mawu Ake.

M’bale Joseph Branham

Malemba:
Mateyu Woyera 24:24
Luka Woyera 17:30
Yohane Woyera 5:24 / 14:12
Aroma 8:1
Agalatiya 4: 27-31
Ahebri 13:8
1 Yohane 5:7
Chivumbulutso 10
Malaki 4