Uthenga: 64-0830E Mafunso ndi Mayankho #4
- 26-0215 Mafunso ndi Mayankho #4
- 24-0519 Mafunso ndi Mayankho #4
- 22-1023 Mafunso ndi Mayankho #4
- 18-0225 Mafunso ndi Mayankho #4
Lokondedwa Banja La Chifumu,
Pali malo amodzi okha otsimikiziridwa komwe inu mungapite kukamva Ambuye akulankhula kudzera mwa mngelo Wake ndikukuuzani inu kuti, “Nthawi zonse kumbukirani, inu ndinu ana a Mulungu, Banja Lachifumu lokhala ndi Magazi Achifumu. Palibe Magazi abwino kuposa anu padziko lapansi. Inu ndinu ana anga, omwazikana padziko lonse lapansi, omwe ndawabalira kwa Khristu.”
Ife ndife Banja Lachifumu la Mulungu lokhala ndi Magazi Achifumu omwe akuyenda m’mitsempha yathu. Ana omwe abadwa kwa Khristu ndi Liwu la Mulungu likuyankhula kudzera mwa mneneri wake wamphamvu. Izo Sizingakhale bwino kuposa zimenezo abwenzi anga.
M’bale Branham, kodi Mkwatibwi adzafunika kusamukira ku Jeffersonville kapena ku Arizona kuti adzapite mu Mkwatulo?
Ndipo izo ndi zokayikitsa kwambiri ngati ziti zidzakhale mwanjira imeneyo, chifukwa Baibulo linati, “Adzakhala ali awiri mu kama; Ine ndidzatenga mmodzi ndi kumusiya mmodzi; ndi awiri ku munda, ndipo ine ndidzatenga mmodzi ndi kusiya mmodzi.” Mukuona? Kotero iwo mwinamwake…Kudutsa mdziko, iwo sadzakhala atasonkhana mu malo amodzi kuti akhale ochita zinthu mofanana. Koma magulu aang’ono a iwo adzakhala atamwazikana konse konse padziko lapansi.
Kotero mwakuthupi, sitidzakhala pamalo amodzi nthawi imodzi. Koma ulemerero kwa Mulungu, Iye anali ndi dongosolo lalikulu kwambiri lobweretsa pamodzi Mkwatibwi Wake.
Ife tikupempherera mipingo yonse ndi magulu amene asonkhana pozungulira zo—zo—zoyankhulira zazing’ono kunja kudutsa, kuchokera ku fukoli, njira yonse mpaka ku Gombe la Kumadzulo, kukwera mpaka ku mapiri a Arizona, kutsika mpaka ku zigwa za Texas, njira yonse mpaka ku Gombe la Kummawa, monse kudutsa dziko, Ambuye, kumene iwo asonkhana. Maora ambiri motalikana, ife tiri mu nthawi, koma, Ambuye, ife tiri limodzi usikuuno ngati chimango chimodzi, okhulupirira, tikuyembekezera Kudza kwa Mesiya.
Lero, sikuti Iye akusonkhanitsa Mkwatibwi Wake kuchokera ku dziko lino lokha, komanso Iye akutisonkhanitsa ife kuchokera ku ma kontinenti asanu ndi awiri a dziko lapansi. Kuchokera ku Africa mpaka ku Antarctica. North America ndi South America, Asia, Australia ndi Europe. Akusonkhanitsa ndikugwirizanitsa Mkwatibwi Wake ngati MMODZI kuti timve Liwu la Mulungu.
Iye anatiuza ife kuti tipite ku tchalitchi; ngakhale kumene amaphunzitsa theka la Mawu, kufikira MPAKA titapeza tchalitchi komwe amaphunzitsa MAWU ONSE. Mulungu alemekezeke Mkwatibwi tsopano wapeza malo amenewo, Mawu a Mulungu pa Tepi ndi MAWU ONSE.
Kaya inu muli ku tchalitchi chanu cha pa Nyumba cha Tape, tchalitchi chanu komwe mabanja ambiri amasonkhana, kapena m’nyumba m’nkhalango za Amazoni kapena Africa, kulikonse komwe mungathe Kukanikiza Kusewera kuti mumve Liwu la Mulungu likuyankhula nanu kuchokera ku kakamwa Kupita ku khutu, inu mudzakhala mu Tchalitchi cha MAWU ONSE.
Ife tapeza tchalitchi cha Mawu Onse ndipo ife tikukuyitanani inu kuti mudzalumikizane nafe Lamlungu lino nthawi ya 12:00 P.M., nthawi yaku Jeffersonville, pomwe tidzakhala tikumva: Mafunso ndi Mayankho #4 64-0830E.
M’bale Joseph Branham