Uthenga: 64-0823M Mafunso ndi Mayankho #1
- 26-0125 Mafunso ndi Mayankho #1
- 24-0428 Mafunso ndi Mayankho #1
- 22-1002 Mafunso ndi Mayankho #1
- 18-0204 Mafunso ndi Mayankho #1
Wokondedwa Branham Tabernacle,
Moni kwa Mkwatibwi wa Yesu Khristu kuchokera kuzungulira padziko lonse lapansi, omwe amakhulupirira kuti Branham Tabernacle, Liwu la Mulungu, ndi tchalitchi chawo cha kwawo komwe iwo akudyetsedwa mwauzimu ndi Mana obisika omwe asungidwa ndi kusungidwira Mkwatibwi wa Khristu.
Kuno ndi kwathu kokhazikika; kuno ndi likulu langa; kuno ndi kumene ife tinakhazikikako. Tsopano, sungani zimenezo mmalingaliro ziribe kanthu chomwe chingachitike. Tsopano, ngati ndinu anzeru, mugwira chinachake. Ziribe kanthu chomwe chingachitike, lino ndi likulu lathu, pomwe pano!
Okhulupirira ambiri nthawi zonse akhala osamvetsetsa kapena kuyika lingaliro lawo kapena kutanthauzira kwawo ku zomwe mneneri ananena apa, koma akuuza Mkwatibwi molunjika, “ngati Inu muli anzeru, mugwira china chake, ili ndiye likulu lathu, komwe kuno!”
Kodi Iye ankatanthauza chiyani pa zimenezo?
pomwe m’bale Branham anali pano, ambiri sanamumvetse bwino Iye ndipo ankaganiza kuti Mkwatibwi ayenera kupita ku Arizona ndi kumutsatira iye kumeneko, kuti adzapite mu Mkwatulo. M’bale Branham anawayankha momveka bwino kuti: KHALANI PANO, AWA NDIWO MALO.
gulu lalikulu lonse la iwo linanyamuka kupita njira imeneyo, ndipo iwo ankafuna kuti apite uku ndi kukachita izo, ine nditatha kuwauza iwo kuti akhale pamenepo. Mukhale pamenepo, mukhale pomwe pano; awa ndiwo malowo.
Anthu ananyamuka kuchokera kulikonse mu United States kupita ku Arizona, koma iye anawauza momveka bwino kuti: Khalani pomwe pano, awa ndiwo malowo!
Khalani ku Jeffersonville? Ndicho chimene ananena!
Vumbulutso langa ndi lakuti, anali Mulungu, akulankhula kudzera mwa mneneri wake ndikuuza anthu kuti, “KHALANI NDI MATEPI.” Awo NDIWO MALOWO!
Iye kotero anakwiya ndipo iye anati ankayenera kuchitapo chinachake ndi anthu onsewo.Kodi iye ayenera kuti anachita chiyani? Kodi ndi ku tchalitchi chiti komwe Iye akanawatumizako iwo? Kodi iwo ankayenera kupita kuti? Kodi M’bale Branham anati iye ayenera kuti anachita chiyani?
Kotero tsopano, ine ndikuyenera ndiwabweretse ana amenewo kuno kuti adzapeze chinachake choti adzadye. Iwo ali kumusi uko mchipululu akuvutika ndi njala.
Iye sananene kuti iwo ankafunikira kupita kutchalitchi chapafupi ndikukatengako tizidutswa tating’onoting’ono tomwe iwo angadye. Iye anati ankayenera KUWABWERETSELANSO KUNO chinachake choti adzadye, apo kupanda kutero AKANAFA NDI NJALA.
VUMBULUTSO LANGA, ABWENZI.
Tsopano, musatinso kachiwiri musamuvetsenso molakwika, kapena kunena zomwe iye sananene, ponena kuti, “M’bale Branham amafuna kuti wokhulupirira aliyense apite kukakhala ku Jeffersonville kuti akhale Mkwatibwi.” M’bale Branham ankadziwa anthu onsewo, ndipo wokhulupirira ALIYENSE wochokera padziko lonse lapansi, sakanatha kuchoka ndikukhala ku Jeffersonville. Zimenezo sizikanatheka. Ndiye iye ankatanthauza chiyani? Iye Anali KUGWIRIZANITSA Mkwatibwi wa Khristu mozungulira matepi omwe anajambulidwa ndi kusungidwa kuti Mkwatibwi adye.
Uthenga uwu, Liwu ili, ndi Mawu Olankhulidwa ndi Mulungu lero ndipo ilo lidzagwirizanitsa ndi kumupanga Mkwatibwi wa Yesu Khristu kukhala wangwiro.
Nyama ndi chimene mphungu zimadya. Tsopano, mphungu imafanizidwa mu Baibulo, ngati mneneri. Mneneri ndi mphungu. Mulungu—Mulungu amadzitcha Yekha mphungu, ndipo ndife “ana a mphungu” ndiye, o—okhulupirira. Inu mukuona? Ndipo nyama imene izo zimadya ndi chiyani? Ndi Mawu. Kulikonse kumene kuli Mawu, chikhalidwe chenicheni cha mbalame chidzadziwonetsera chokha.
Kodi Mawu a Ambuye oyera ali kuti , otsimikizilidwa, osakhala osamvetsetseka, Pakuti Atero Ambuye wa lero? Pali malo amodzi okha, Matepi.
Ndikhoza kupitiriza, ndi chobwereza pa pachobwereza, koma Uthenga uwu ndi zomwe M’bale Branham ananena zimatenga vumbulutso kuchokera kwa Mulungu. Tiyenera kuwerenga pakati pa mizere ndi vumbulutso, koma muzinena zomwe iye adanena. Pakuti Ndi Mawu OYERA.
Mafunso ndi Mayankho a lero ndi zomwe NDIMAKHULUPIRIRA.
Masiku ano, atumiki ambiri akuuza anthu kuti pokhala ndi Tchalitchi cha Mnyumba cha Tepi ife tasiya Mawu ndi zomwe M’bale Branham anati ife tichite. Amavelera kuti ife tiyenera kupita ku zomwe iwo amazitcha ndikuzitenga ngati tchalitchi.
Zoona Zilipo zambiri ,zobwereza zambiri momwe M’bale Branham akunena momveka bwino izi.
“Tsopano, inu muzipita ku tchalitchi china chabwino cha Uthenga wonse ndipo mukazipezere tchalitchi cha kwanuko.”
Ndipo ine ndimakhulupirira zimenezo ndi mtima wanga wonse, chifukwa iye anatero. Koma ine ndikukhulupirira kuti ife tikuchita zimenezo mwa KUKHALA NDI TCHALITCHI CHA PA NYUMBA CHA TEPI. Malo athu si omwe ali ofunika kwa Ambuye. Imeneyo ndi nyumba chabe. Koma ntchito yathu kwa Ambuye ndikukhalabe ndi Mawu Ake, OSATI MALO KAPENA NYUMBA. Malowo sapulumutsa ndi kupangitsa Mkwatibwi kukhala wangwiro, MAWU AMACHITA.
Ngati ndipita ku nyumba ya tchalitchi, koma ayiwala CHINTHU CHACHIKULU: kumva Liwu la Mulungu mwa kukanikiza Kusewera, ndipo angolowetsapo m’malo mwake pongomva KOKHA atumiki akulalikira Uthenga, kodi zimenezo zidzakukhutiritsani kotheratu ndi kudyetsa moyo wanu wonse? Zingakhutiritse moyo wanu, m’bale wanga ndiso mlongo wanga, koma sizidzakhutiritsa Mkwatibwi.
Ndiloleni ine nditsindike apa ndikunena kuti pali anthu zikwizikwi omwe alibe nyumba ya tchalitchi yoti apiteko. Kodi iwo atayika? Ngati iwo alibe m’busa kapena tchalitchi, kodi zimenezo zikutanthauza kuti iwo sangakhale Mkwatibwi? Ngati inu mukukhala pamtunda wa makilomita 100 kuchokera ku nyumba ya tchalitchi, kodi inu mukuyenera kupita ku tchalitchi chimenecho? Koma ngati ine ndikukhala kutali, ine sindiyenera kutero? Ine Ndiyenera kulumikizidwa ku mlaliki, koma ine sindingathe kulumikizidwa ku matepi? Nyumba yowoneka ndi maso ndi imene mneneri akunena kuti ndi chinthu chofunika kwambiri chomwe ife tiyenera kupitako?
Kodi mneneriyo ankafuna kumubweretsa Mkwatibwi kuti?
Ngati inu simungathe kubwera kuno ku kachisi, kapezeni tchalitchi china kwinakwake; muzikapita kumeneko.
Kamodzinso, kodi chisankho chake choyamba chotumiza anthu chili kuti? Ku Branham Tabernacle, Mawu, matepi. Ndicho chimene Mulungu wapereka Mkwatibwi Wake kuti achite mu nthawi ino yotsiriza, ndipo tikuchita izi tsiku lililonse NDI Lamlungu lililonse.
Kotero ine simukundiva molakwika. INE SINDIKUNENA KUTI muyenera muzilumikizidwa pa intaneti ku matepi ndi Branham Tabernacle kuti mukhale Mkwatibwi. Ine SINDINENA KUTI inu simukuyenera kupita kutchalitchi.Ine SINDIKUNENA KUTI simungamvere atumiki. Ngati inu mukukhulupirira zimenezo, Inu mwachoka pa Mawu. Ine ndikunena kuti kumva Liwu la Mulungu pa matepi ndilo Liwu lofunikira kwambiri lomwe MUYENERA KUMVA, ndipo ndikukhulupirira kuti m’busa aliyense ayenera kusewera Liwu limenelo, matepi, m’matchalitchi awo. Koma iwo apanga zifukwa zonse zomwe zilipo KUTI OSATI ASASEWERE MATEPI. Ngati umenewo ndiwomwe uli mpingo wanu, inu simukudya pa Mawu.
Izi n’zoonekeratu kuti izi ndi zomwe sankafuna kuti zichitike komanso zomwe anthu anali kuchita.
Ndipo inu muzipita ku tchalitchi; musati mudzikhala kunyumba, kumapita kukawedza, ndi kukasaka, ndi zinthu monga zimenezo Lamlungu.
Ife Sitili. Ife tikulumikizana mozungulira pa chinthu chokhacho chomwe chidzagwirizanitsa Mkwatibwi, Uthenga Uwu, Liwu ili.
Kachiwirinso, Ine ndimakhulupirira kupita kutchalitchi. Pali matchalitchi ambiri kuzungulira padziko lonse lapansi omwe akuika matepi moyambilira pa maguwa awo, Ambuye atamandike. Kodi ine ndikukhulupirira kuti muyenera kukhala panyumba kapena inu simuli Mkwatibwi? AYI, AYI, AYI….ine sindinaganizepo chimenecho, ine sindinakhulupirirepo chimenecho. Ine Ndikungofuna kuti MUZIKANIKIZA KUSEWERA mosatengela kuti kaya inu muli kuti kapena ndi tchalitchi chiti chomwe inu mukupita.
Ngati inu mulibe vumbulutso la zomwe iye akunena, ndiye kuti inu munganene momveka bwino kuti, “Ine Sindiyenera kumvera M’bale Branham ngakhaleso kapena KUVOMEREZA zonse zomwe iye akunena. Ngakhaleso Iye Ananena choncho, pali amuna ena ambiri oitanidwa ndi Mulungu.”
Kazipitaniko. Ife tikuzindikira apa, akuti, “Kodi ife tizipita ku mpingo wina umene sugwirizana ndi inu?” Ndithudi, ine sindi…Ine si nsangalabwi yokhayo mmphepete mwa nyanja, inu mukudziwa. Alipo—alipo amuna ena a umulungu konsekonse; ndikukhulupirira kuti ndine mmodzi wa iwo.
Mawu a Mulungu pa matepi ndiyo SANGALABWI YANGA, THANTHWE LANGA. Ndi Liwu lomwe ndikufuna kumva komanso Liwu lomwe ndikufuna kuti Branham Tabernacle imve.
Ngati inu mukufuna kulumikizana nafe, Inu muli olandiridwa kwambiri, abale ndi alongo anga. Mudzalumikizane nafe Lamlungu nthawi ya 12:00 p.m., nthawi ya ku Jeffersonville, pamene tidzava Liwu la Mulungu likulankhula ndikuyankha mafunso ambiri omwe mungakhale nawo mumtima mwanu. Ndipo mverani nokha ngati zomwe ine ndanena m’kalata iyi sizikugwirizana ndi Mawu ndiso ngati ine sindinamvetse bwino zomwe Mulungu akunena kwa Mkwatibwi Wake.
Zimene iye akunena pa matepi ndi Pakuti Atero Ambuye. Osati zomwe ine ndikunena ndi zomwe iye akunena, kapena zomwe ine ndikukhulupirira kuti iye akunena, ndipo Mulungu YEKHA ndi amene angakupatseni inu Vumbulutso lolondola.
M’bale Joseph Branham