25-1207 Kenako Yesu Anabwera Ndipo Anadzaitana

Uthenga: 64-0213 Kenako Yesu Anabwera Ndipo Anadzaitana

PDF

BranhamTabernacle.org

Wokondedwa Mkwatibwi wa Mawu,

Tikukhala mu nthawi yamdima kwambiri, koma tilibe MANTHA, Ambuye wabwera. Wabwera kudzakwaniritsa Mawu Ake mu tsiku lomaliza. Chimene Iye anali panthawiyo, Iye ali lero. Chimene kuonekera kwake ndi kudziwika kwake zinali, ndi lero. Iye akadali Mawu a Mulungu, akudziwonetsera Yekha mu thupi la munthu mwa mngelo wake wachisanu ndi chiwiri wamphamvu ndipo watiululila ife, ife ndife Mkwatibwi wake wa Mawu a moyo.

Tilibe nthawi ya mtsutso kapena mkangano; Ife tinadutsa tsiku limenelo; tikupita patsogolo, Ife tikuyenera kukafika kumeneko. Mzimu Woyera wabwera pakati pathu. Ambuye Yesu mu mawonekedwe a Mzimu wadziulula ndi kudziwonetsera Yekha kudzera mwa mneneri Wake kuti Iye ndi Liwu la Mulungu kwa Mkwatibwi Wake.

Iye anati adzabwera. Iye anati adzachita izi. Iye anati adzauka m’masiku otsiriza ndikuchita zinthu izi monga momwe Iye anachitira pamene anabwera m’thupi nthawi yoyamba, ndipo apa akuchita izi. Kodi inu mukuopa chiyani? PALIBE!!!

Tili pa njira ya kwathu yopita ku Ulemerero! Palibe chomwe ife chingatilepheretse. Mulungu adzatsimikizira Mawu Ake. Sindikusamala zomwe zikuchitika. Nthawi yafika yochitapo kanthu. Nthawi yafika yo khulupilira kapena kusakhulupirira. Mzere uja wolekanitsa umene umabwera kwa mwamuna ndi mkazi aliyense wafika.

Inu Munabadwira pa cholinga. Pamene Kuwala kunakukanthani inu, Kunachotsa kudetsedwa konse mkati mwa inu. Pamene munamva Liwu Lake likulankhula ndi inu pa matepi, chinachake chinachitika. Kunalankhula ndi moyo wanu. Kunati, “Ambuye wabwera ndipo akukuitanani inu. Musatope, musaope, Ine ndikukuitanani inu. Ndinu Mkwatibwi Wanga”.

Oh Anthu inu, onetsetsani! Musamangotenga chatheka chilichose pa izo. Mulungu ali ndi pologaramu: Mawu Ake Iye adawajambula pa matepi. Ambuye wabwera ndipo akukuitanani inu. Bwerani ku njira yoperekedwa ndi Mulungu.

Ambuye adzagwirizanitsanso Mkwatibwi Wake padziko lonse lapansi ndi Liwu Lake. Adzatilimbikitsa ife, kutitsimikizira ife, kutichiritsa ife, kutibweretsa mu mKukhalapo Kwake kwamphamvu ndikutiuza ife:

Mbuye wabwera ndipo Iye akuitana iwe. Oh, wochimwa, oh, munthu wodwala, kodi iwe sukuwona Mbuye akuwonetseredwa mwa anthu, pakati pa okhulupirira? Iye wabwera kuti adzaitane ana Ake okhulupirira kuti akhale athanzi. Iye wabwera kuti adzamuitanire wochimwa ku kulapa. Wobwerera mmbuyo, membala wa mpingo, Mbuye wabwera ndipo akukuitanani inu.

Kodi ndikutsanyulila kotani Kwa mzimu woyera komwe mkwatibwi adzakhale nako Lamlungu lino pamene Mulungu akusonkhanitsaso ana ake pamodzi kachiwiri ndi kulowa m’nyumba zathu, m’matchalitchi athu, m’misonkhano yathu, ndikutiyitana ife kunena kuti, “Ambuye wabwera ndipo akuitana. Chilichonse chomwe Inu mukuchifuna, ndi chanu.”

Lolani mawu amenewo alowe mozama m’mitima mwanu, abale ndi alongo. CHILICHONSE CHIMENE INU MUKUFUNA, AMBUYE WABWERA NDIPO APEREKA ICHO KWA INU.

Atate Akumwamba, O Ambuye, mulole izo zichitikenso. Zinthu zonse izi zimene ine ndanena, “Yesu wabwera ndipo akukuitanani inu.” Kodi Iye akuchita chiyani pamene Iye wabwera? Iye akuitana. Ndipo mulole izo zichitikenso, Ambuye. Mulole Mzimu Woyera Wanu ubwere pakati pa anthu usikuuno, Ambuye Yesu mu mmaonekedwe a—a Mzimu. Mulole Iye abwere usikuuno ndipo adzadziulule Yekha, ndipo potero adzadziwonetsere Yekha.

M’bale Joseph Branham

Uthenga: Kenako Yesu Anabwera Ndipo Anadzaitana
Nthawi:12:00 PM nthawi ya ku Jeffersonville
Malemba: Yohane Woyera 11:18-28